Mungakhale ndi Chiyembekezo M’dziko Lamavutoli
Mungakhale ndi Chiyembekezo M’dziko Lamavutoli
“MASIKU ano kusiyana ndi kale, anthu wamba ali ndi mphamvu yothandiza anzawo ndi kuthetsa mavuto amene tonse tikukumana nawo.” Mawu amenewa ananenedwa ndi Bill Clinton, pulezidenti wakale wa dziko la United States, pamsonkhano umene unachitikira ku Ottawa, m’dziko la Canada, mu March 2006. Pomaliza, iye ananena kuti kuyambira chaka cha 2004 pamene kunachitika ngozi ya tsunami, anthu ayamba kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza anzawo padziko lonse. Kenako, iye analankhula molimba mtima kuti masiku ano, dziko lafika pa “nthawi imene anthu akudalirana kwambiri kuposa kale.”
Kodi tingayembekeze kuti anthu padziko lonse adzagwirizana kuti akonze tsogolo lathu chifukwa cha masoka achilengedwe? Kodi tingayembekeze
tsogolo lamtendere weniweni ndi chitetezo chosatha chifukwa chakuti “anthu akudalirana kwambiri kuposa kale”?Kodi Chiyembekezo Chodalirika Tingachipeze Kuti?
Mbiri ya anthu pazaka zoposa 6,000, imasonyeza kuti anthu amagwiritsana mwala. Ndiye chifukwa chake Malemba amatiuza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Inde, kudalira mabungwe a dzikoli, chuma chake, ndi zolinga zake kumangogwiritsa munthu fuwa la moto. Tikutero chifukwa chakuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.”—1 Yohane 2:17.
Kuyambira kale, Mulungu wakhala chiyembekezo cha anthu olungama. Baibulo limati iye anali “chiyembekezo cha Israyeli” wakale ndiponso “chiyembekezo cha atate,” kapena kuti makolo a Israyeli. Limanenanso zambiri pankhani ya kuyembekeza Mulungu, kumukhulupirira, ndi kumudalira. (Yeremiya 14:8; 17:13; 50:7) Ndithudi, Malemba amatilimbikitsa ‘kuyembekeza Yehova.’—Salmo 27:14.
Lemba la Miyambo 3:5, 6 limatilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” M’pomveka kukhulupirira lonjezo limeneli ndi mtima wanu wonse chifukwa chakuti Yehova Mulungu sasintha, ndi wodalirika, ndiponso amakwaniritsa malonjezo ake. (Malaki 3:6; Yakobe 1:17) Iye amakufunirani zabwino, ndipo mukamamvera zimene Mawu ake, Baibulo, amanena, amakutsogolerani bwinobwino m’nthawi yovuta ino.—Yesaya 48:17, 18.
Munthu amene amamvera malangizo a Mulungu ndi mtima wonse, angadalire lonjezo lakuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.” (Yesaya 41:10) Anthu okondadi Yehova Mulungu akamapemphera kuchokera pansi pa mtima ndi kusinkhasinkha lonjezo limeneli, amalimba mtima chifukwa zimawathandiza kulimbana ndi mavuto ndi nkhawa zawo.
Tiyeni tione chitsanzo cha Andrea, amene ndi wa Mboni za Yehova ndiponso ali ndi ana awiri. Mayi ameneyu anati: “Ndikamada nkhawa pamoyo wanga, pemphero ndi kusinkhasinkha malonjezo a Yehova zimandithandiza kulimba mtima. Ndikamadalira Yehova, sizindivuta kupirira.”
Limbitsani Chiyembekezo Chanu mwa Yehova
Kuti asonyeze kufunika koyembekeza Yehova, wamasalmo anati: “Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.” (Salmo 119:165) Ngati muphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, mungadzaze maganizo ndi mtima wanu ndi zinthu ‘zoona, zofunika kwambiri, zolungama, zoyera, za chikondi, zoneneredwa zabwino, zakhalidwe labwino, ndi zotamandika,’ zimene zili zolimbikitsa mwauzimu. Mukamayesetsa kumva, kuphunzira, kulandira, ndi kuchita zinthu zimenezi, “Mulungu wa mtendere adzakhala nanu.”—Afilipi 4:8, 9.
Malinga ndi zimene waona pa zaka zambiri, John anati: “Kuti ndisinthe mmene ndinkaonera tsogolo langa, ndinafunika kukhala pa ubale wabwino ndi Mulungu wangwiro ndi wosaoneka. Koma kuti ndichite zimenezi, ndinayenera kusintha kwambiri umunthu ndi maganizo anga kuti ndikhale munthu wokonda zauzimu. Ndinasintha maganizo anga kuti afanane ndi a Mulungu mwa kuwerenga Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha.”
Mukamamwa madzi otsitsimula ndi opatsa moyo a choonadi opezeka m’Malemba ouziridwa, mumakhala ngati mukumwa mankhwala amphamvu ndi odalirika amene angakuthandizeni kulimbana ndi zinthu zoipa zambirimbiri zimene zimafalitsidwa tsiku ndi tsiku. Kutsatira zimene Baibulo limanena kungalimbitsenso banja lanu ndi kukuthandizani kuchepetsa nkhawa. Ndiponso, Mulungu akulonjeza “kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Choncho, palibe chifukwa chokhalira ndi mantha chifukwa Mulungu adzakuthandizani.
Phinehas, amene wapulumuka nkhondo ndi ziwembu zopha anthu ambirimbiri, anati: “Ndaphunzira kudalira Yehova ndi kuika moyo wanga Salmo 18:29) Mwana wamng’ono amene amakondana ndi makolo ake amawakhulupirira kwambiri ndipo sada nkhawa podziwa kuti makolo ake amusamalira ngakhale atadwala kapena atakumana ndi mavuto. Inunso mungamve chimodzimodzi ngati muyesetsa kulabadira chilimbikitso chakuti muyembekeze Yehova.—Salmo 37:34.
m’manja mwake. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwanditeteza ku mavuto ambiri.” Mukakhulupiriradi Yehova Mulungu, iye angakuthandizeni kugonjetsa mavuto onga linga. (Maziko Olimba a Chiyembekezo
Yesu Khristu anauza otsatira ake kuti: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.’” (Mateyo 6:9, 10) Ufumu wa kumwamba umenewu, womwe ndi boma limene Yesu Khristu ndiye wolamulira wake, ndi njira imene Mulungu wakhazikitsa kuimira ulamuliro wake padziko lapansi.—Salmo 2:7-12; Danieli 7:13, 14.
Mantha osiyanasiyana amene anthu masiku ano amakhala nawo ndi umboni wakuti Mulungu akufunika kulowererapo. Mwayi wake, Mulungu watsala pang’ono kuchita zimenezi. Panopa, Yesu Khristu waikidwa kale ndi Mulungu kukhala Mfumu Mesiya, ndipo ali ndi ulamuliro wotsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso woyeretsa dzina Lake. (Mateyo 28:18) Posachedwapa, Ufumuwo udzayamba kulamulira dziko lapansi ndi kuchotsa zinthu zonse zoyambitsa mantha ndi nkhawa. Lemba la Yesaya 9:6 limasonyeza kuti Yesu ndiye Wolamulira woyenereradi amene angatichotsere mantha. Mwachitsanzo, limati iye ndi “Atate Wosatha,” “Wauphungu,” ndi “Kalonga wa Mtendere.”
Taonani dzina losonyeza chikondi limeneli lakuti “Atate Wosatha.” Dzina limeneli likusonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu ndi ulamuliro, komanso mtima wofuna kupatsa anthu omvera, moyo wosatha padziko lapansi pamaziko a nsembe yake ya dipo. Zimenezi zikutanthauza kuti anthuwo adzamasuka ku moyo wauchimo ndi wopanda ungwiro umene analandira kwa Adamu, munthu woyamba kuchimwa. (Mateyo 20:28; Aroma 5:12; 6:23) Khristu adzagwiritsanso ntchito ulamuliro wake umene Mulungu anamupatsa kuti aukitse anthu ambiri amene anafa.—Yohane 11:25, 26.
Ali pa dziko lapansi, Yesu analidi “Wauphungu.” Yesu ankadziwa kuthetsa mavuto a anthu chifukwa chakuti amadziwa Mawu a Mulungu ndipo amamvetsa kwambiri chibadwa cha anthu. Kuyambira pamene analandira Ufumu kumwamba, Khristu akupitiriza kukhala “Wauphungu,” chifukwa ndiye amene Yehova akumugwiritsa ntchito kwambiri kulankhula ndi anthu. Uphungu wa Yesu wa m’Baibulo ndi wanzeru ndiponso sulephera. Mukadziwa zimenezi ndi kuzikhulupirira, mudzakhala ndi moyo wopanda nkhawa ndi mantha.
Lemba la Yesaya 9:6 limatinso Yesu ndi “Kalonga wa Mtendere.” Paudindo umenewu, Khristu posachedwapa adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuthetsa kupanda chilungamo konse pankhani zandale, zachikhalidwe, ndi zachuma. Adzachita zimenezi mwa kukhazikitsa pakati pa anthu ulamuliro umodzi wamtendere, Ufumu wa Mesiya.—Danieli 2:44.
Ufumuwo ukadzayamba kulamulira, padziko lonse lapansi padzakhala mtendere wosatha. Kodi zimenezi zidzachitikadi? Inde, chifukwa lemba la Yesaya 11:9 limati: “[Nzika za Ufumuwo] sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” M’kupita kwa nthawi, munthu aliyense padziko lapansi adzadziwa Mulungu molondola ndi kumumvera. Kodi mukusangalala kumva za chiyembekezo chimenechi? Ngati mukutero, musazengereze kuphunzira kuti ‘mudziwe Yehova.’
Mungadziwe mfundo za Mulungu zolimbitsa chikhulupiriro ndi zopatsa moyo mwa kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni pa zimene zikuchitika masiku ano ndi zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolo. Choncho tikukulimbikitsani kuphunzira Baibulo kwaulere ndi Mboni za Yehova m’dera lanu. Imeneyi ndiyo njira imene mungapewere mantha ndi kukhala ndi chiyembekezo chodalirika ngakhale m’dziko lamavutoli.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
Boma la Mulungu Limatipatsa Chiyembekezo
Yesu Khristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, wapatsidwa mphamvu ndi ulamuliro wonse. (Mateyo 28:18) Adzabwezeretsa zinthu zonse zachilengedwe zimene zawonongedwa. Alinso ndi mphamvu yothetsa matenda onse. Zozizwitsa zimene anachita ali pa dziko lapansi zinali ngati kutilawitsako madalitso ankhaninkhani amene iye monga Mfumu yangwiro ndi yodalirika, adzapereka kwa anthu muulamuliro wake. Kodi ndi makhalidwe ati m’munsimu a Mfumu imeneyi amene mukukopeka nawo kwambiri?
▪ Wochezeka.—Maliko 10:13-16.
▪ Womvetsa zinthu ndi wosakondera.—Maliko 10:35-45.
▪ Wodalirika ndi wosadzikonda.—Mateyo 4:5-7; Luka 6:19.
▪ Wokonda chilungamo.—Yesaya 11:3-5; Yohane 5:30; 8:16.
▪ Woganizira ena ndi wodzichepetsa.—Yohane 13:3-15.
[Chithunzi patsamba 4]
Kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha kungatithandize kuyembekeza Yehova