N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
CHRISTINE atakhala pa banja zaka 20, mwadzidzidzi tsiku lina mwamuna wake anamuthawa. Anamusiya ndi ana 8, aamuna 7 ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamng’ono anali ndi zaka 7 ndipo wamkulu anali ndi zaka 18. Christine anati: “Kuyambira pamenepo, ndinayamba kuyendetsa ndekha banja. Ndinapanikizika ndi udindo umenewu ndipo ndinalakalaka nditapeza munthu wondilangiza ndi kundilimbikitsa.” Kodi anapeza kuti thandizo limene ankafunalo?
Christine anati: “Ine ndi ana anga tinapulumukira ku misonkhano yachikhristu. Kumeneko, tinkalimbikitsidwa ndi anzathu ndipo tinkalandira malangizo a m’Mawu a Mulungu. Kusaphonya misonkhano kunatithandiza kwambiri m’zonse pabanja pathu.”
“Nthawi yovuta” ino, tonsefe tikulimbana ndi mavuto osiyanasiyana. (2 Timoteyo 3:1) Monga Christine, inunso mungaone misonkhano ya Mboni za Yehova ngati kasupe wauzimu wofunika kwambiri pa kulambira Yehova. N’zosakayikitsa kuti misonkhano isanu imene imakhalako mlungu uliwonse, imakulimbikitsani kukonda Mulungu, imalimbitsa chiyembekezo chanu cha m’tsogolo, ndipo imakupatsani malangizo a m’Baibulo okuthandizani kulimbana ndi mavuto.
Koma alipo anthu ena amene zimawavuta kupita ku misonkhano nthawi zonse. Akaweruka ku ntchito zawo, amakhala atatopa, ndipo akaganiza zosintha zovala kuti avale zabwino ndi kupita ku misonkhano, amagwa ulesi. Ena ntchito yawo siwalola kusonkhana bwinobwino. Ngati atati azipezeka pa misonkhano yonse, ndiye kuti azikhala ndi ndalama zochepa kapena angachotsedwe ntchito. Ena angaphonye misonkhano chifukwa choganiza kuti kusangalala pang’ono kungawatsitsimule kwambiri kusiyana ndi kusonkhana ndi mpingo.
Kodi pali zifukwa zomveka zomwe tiyenera kupezekera pa misonkhano yachikhristu? Kodi inu mungatani kuti misonkhano izikhala yotsitsimula? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane mawu olimbikitsa a Yesu a pa Mateyo 11:28-30. Iye akutipempha kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”
“Bwerani kwa Ine”
Yesu akutiitana ndi mawu akuti: “Bwerani kwa ine.” Timalabadira pempho limeneli tikamapezeka pa Mateyo 18:20.
misonkhano nthawi zonse. Ndi bwino kupezeka pa misonkhano, chifukwa nthawi ina Yesu anati: “Kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pawo.”—Pamene anali padziko lapansi, Yesu anapempha yekha anthu osiyanasiyana kumutsatira. Potero, anawapatsa anthu amenewa mwayi wokhala mabwenzi ake apamtima. Ena sanazengereze, analabadira nthawi yomweyo. (Mateyo 4:18-22) Koma ena sanalabadire chifukwa chokonda zinthu zakuthupi. (Maliko 10:21, 22; Luka 9:57-62) Yesu analimbikitsa anthu amene anamutsatirawo ndi mawu akuti: “Inu simunandisankhe ine, koma ine ndinakusankhani.”—Yohane 15:16.
Atamwalira ndi kuukitsidwa, Khristu sanakhalenso ndi ophunzira ake padziko lapansi. Koma anali nawobe m’njira yakuti anali kuwatsogolera ndi kuona mmene iwo ankalabadirira uphungu wake. Mwachitsanzo, patadutsa zaka pafupifupi 70 kuchokera pamene anaukitsidwa, Yesu anapereka uphungu ndi chilimbikitso kumipingo 7 ya ku Asiya Mina. Mawu ake akusonyeza kuti iye ankadziwa bwino zabwino ndi zofooka za munthu aliyense m’mipingoyo.—Chivumbulutso 2:1–3:22.
Yesu amaganizirabe kwambiri wophunzira wake aliyense. Akulonjeza kuti: “Dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 28:20) Lero tili m’nthawi ya mapeto, ndipo tiyenera kulabadira pempho la Yesu lakuti timutsatire. Mwa zina, kutsatira Yesu kumafuna kuti tizipita ku misonkhano nthawi zonse. Yesu akufuna kuti tizimumvera ndi ‘kuphunzitsidwa mwa iye’ kudzera m’maphunziro a Baibulo ndi nkhani zimene zimakambidwa pa misonkhano. (Aefeso 4:20, 21) Kodi inuyo mukulabadira pempho la Yesu lakuti: “Bwerani kwa ine”?
“Nonsenu Ogwira Ntchito Yolemetsa ndi Olemedwa”
Chifukwa chachikulu chimene tiyenera kupezekera pa misonkhano yachikhristu n’chakuti imatilimbikitsa. (Aheberi 10:24, 25) Ambirife ‘tikugwiradi ntchito yolemetsa ndipo ndife olemedwa’ m’njira zosiyanasiyana. Mwina ndinu olemedwa ndi nkhawa zokhudza thanzi lanu kapena zinthu zina. Koma tikakhala pa misonkhano yachikhristu, timalimbikitsana. (Aroma 1:11, 12) Mwachitsanzo, timamva ndemanga zolimbikitsa mwauzimu, timakumbutsidwa za chiyembekezo chathu cha m’Baibulo, ndipo timaona chikhulupiriro chimene anzathu omwe akupirira mavuto ali nacho. Zonsezi zingatithandize kupirira ndi kusada nkhawa kwambiri ndi mavuto athu.
Tamverani zimene mkazi wina wachikhristu, amene amavutika ndi matenda, ananena. Anati: “Nthawi zambiri ndimagonekedwa m’chipatala chifukwa cha matenda anga. Zimandivuta kupita ku misonkhano ndikangotuluka m’chipatala, koma ndi zimene zimandithandiza. Ndimasangalala kuona mtima waubwenzi ndi chikondi zimene abale ndi alongo ali nazo, ndipo maphunziro ndi malangizo amene Yehova ndi Yesu amapereka, amathandiza kuti moyo wanga ukhale wofunika.”
“Goli Langa Ndi Lofewa Ndipo Katundu Wanga Ndi Wopepuka”
Onani kuti m’ndime imene tikukambiranayi, Yesu anati: “Phunzirani kwa ine.” Tikamaphunzira kwa Yesu, timakhala ophunzira ake, ndipo timayamba kusenza goli lake tikadzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa. (Mateyo 28:19, 20) Kuti tikhalebe ophunzira a Yesu, tiyenera kutenga nawo mbali pamisonkhano. Zimenezi ndi zofunika chifukwa chakuti ndi pamisonkhano yachikhristu pamene timaphunzira za Yesu, ziphunzitso zake, ndi mmene ankaphunzitsira anthu.
Kodi katundu amene Khristu akufuna kuti tisenze ndi chiyani? Ndi katundu amene iye mwiniwakeyo wasenza, yemwe ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. (Yohane 4:34; 15:8) Timafunika khama kuti timvere malamulo a Mulungu, koma sikuti katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri woti sitingamusenze. Amalemera tikamayesa kumusenza tokha. Koma ngati tipempha mzimu wa Mulungu ndi kudya chakudya chauzimu chimene chimaperekedwa pa misonkhano, Mulungu amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akorinto 4:7) Tikamakonzekera misonkhano ndi kutenga nawo mbali, chikondi chathu pa Yehova chimalimbiralimbira. Ndiyeno chikondi chikamatilamulira, malamulo a Mulungu sakhala “olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
Anthu masiku ano amavutika ndi matenda, kupeza zofunika pamoyo, ndiponso ndi zothetsa nzeru zina. Koma kuti ife tithane ndi mavutowo, sitimangodalira nzeru zathu. Misonkhano ya mpingo imatithandiza ‘kuleka kuda nkhawa,’ chifukwa chakuti Yehova amatipatsa zimene timafunikira ndipo amatithandiza kupirira mavuto. (Mateyo 6:25-33) Ndithudi, misonkhano yachikhristu ndi umboni wakuti Mulungu amatikonda.
“Ndine Wofatsa ndi Wodzichepetsa”
Yesu anali ndi chizolowezi chopita ku sunagoge, kumene anthu ankakambirana Mawu a Mulungu. Ulendo wina ali kumeneko, Yesu anatenga mpukutu wa Yesaya ndi kuyamba kuwerenga kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi za kuchiritsidwa kwa akhungu. Inde, kudzamasula oponderezedwa kuti apite monga mfulu, kudzalalikira chaka chokomera Yehova.” (Luka 4:16, 18, 19) Tikanasangalala kwambiri tikanakhalapo ndi kumva Yesu akufotokoza kuti: “Lero lemba ili limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”—Luka 4:21.
Yesu, “m’busa wamkulu” ndi wofatsa, akusamalirabe mwauzimu otsatira ake. (1 Petulo 5:1-4) Motsogoleredwa ndi Yesu, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wasankha amuna kukhala abusa m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse. (Mateyo 24:45-47; Tito 1:5-9) Amuna amenewa ‘amaweta mpingo wa Mulungu’ mofatsa ndipo amakhala zitsanzo zabwino posaphonya misonkhano. Mungasonyeze kuti mumayamikira “mphatso za amuna” zimenezi mwa kupezeka pa misonkhano. Ndiponso kupezekapo kwanu ndi ndemanga zanu zimalimbikitsa ena.—Machitidwe 15:30-33; 20:28; Aefeso 4:8, 11, 12.
“Mudzapeza Chitsitsimutso cha Miyoyo Yanu”
Mukakhala pa misonkhano yachikhristu, kodi mungatani kuti misonkhanoyo ikhale yotsitsimula? Muyenera kutsatira uphungu wa Yesu wakuti: “Samalani ndi kamvedwe kanu.” (Luka 8:18) Anthu amene anali ndi mtima wofuna kuphunzira anamvetsera mosamala zimene Yesu ankanena. Iwo anamupempha kuti afotokoze mafanizo ake ndipo, mapeto ake, anamvetsetsa zimene Yesu anaphunzitsa.—Mateyo 13:10-16.
Mungatengere chitsanzo cha anthu anjala yauzimu amenewo mwa kumvetsera mosamala nkhani zokambidwa pa misonkhano. (Mateyo 5:3, 6) Kuti maganizo asamayendeyende, yesetsani kutsatira mmene wokamba nkhani akufotokozera mfundo zake mwatsatanetsatane. Mukumvetsera nkhani, dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito bwanji pamoyo wanga? Ndingawathandize nazo bwanji anthu ena? Ndingazifotokoze bwanji mfundo zimenezi?’ Ndiponso, werengani malemba amene wokamba nkhaniyo akugwiritsa ntchito kufotokoza mfundo zake zazikulu. Mukamasamala kwambiri ndi kamvedwe kanu, ndi pamene misonkhano imakhala yotsitsimula kwambiri.
Misonkhano ikatha, kambiranani zimene mwaphunzira ndi mmene mungazigwiritsire ntchito. Kukambirana kotere kungathandize kuti misonkhano izikhala yotsitsimula kwambiri.
Kunena zoona, tili ndi zifukwa zomveka zopezekera pamisonkhano. Pokhala kuti mwawerenga za ubwino wa misonkhano, bwanji osadzifunsa kuti, ‘Kodi ine ndikulabadira pempho la Yesu lakuti: “Bwerani kwa ine”?’
[Zithunzi patsamba 11]
Kodi zinthu zina zimakulepheretsani kusonkhana bwinobwino?