Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Iwo Ndi Okalamba Koma Akubalabe Zipatso Zauzimu

Iwo Ndi Okalamba Koma Akubalabe Zipatso Zauzimu

Iwo Ndi Okalamba Koma Akubalabe Zipatso Zauzimu

“Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova, . . . atakalamba adzapatsanso zipatso.”​—SALMO 92:13, 14.

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri amaganiza za chiyani akamva mawu akuti nkhalamba? (b) Kodi Malemba amati chiyani za mavuto obwera ndi tchimo la Adamu?

MUKAMVA mawu akuti nkhalamba, kodi mumaganiza za chiyani? Za munthu wamakwinya, wovutika kumva, kapena wa manja ndi miyendo yofooka? Kodi kapena mumaganiza za vuto linanso la “masiku oipa” a ukalamba amenewa lofotokozedwa mwatsatanetsatane pa Mlaliki 12:1-7? Ngati mumaganiza choncho, ndi bwinonso kukumbukira kuti ukalamba wofotokozedwa pa Mlaliki chaputala 12, sunali cholinga cha Yehova Mulungu, Mlengi wathu, koma unabwera chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu.​—Aroma 5:12.

2 Ngakhale zili choncho, kukula pakokha si temberero. Tikutero chifukwa chakuti, pamadutsa zaka kumene munthu akamakula. Pajatu kukula ndi chibadwa cha zamoyo zonse. Kwa zaka 6,000, uchimo ndi kupanda ungwiro kwawononga zinthu zambiri. Koma posachedwapa zimenezi zidzakhala mbiri yakale, ndipo anthu onse omvera adzakhala ndi moyo umene Mulungu anafuna, wopanda zopweteka za ukalamba ndi imfa. (Genesis 1:28; Chivumbulutso 21:4, 5) Nthawi imeneyo, ‘wokhala m’dziko sadzanena, Ine ndidwala.’ (Yesaya 33:24) Okalamba adzabwerera ku masiku a “ubwana” wawo, ndipo mnofu wawo udzakhala “se, woposa wa mwana.” (Yobu 33:25) Koma panopa, anthu onse akulimbanabe ndi cholowa chimene analandira kwa Adamu. Izi zili choncho, atumiki a Yehova amadalitsidwa mwapadera akamakalamba.

3. Kodi Akhristu ‘amapatsanso zipatso atakalamba’ m’njira yotani?

3 Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti “iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova, . . . atakalamba adzapatsanso zipatso.” (Salmo 92:13, 14) Ndi mawu ophiphiritsa amenewa, wamasalmo anatchula mfundo yofunika kwambiri yakuti atumiki a Mulungu angapitirize kukula mwauzimu ngakhale pamene akukalamba. Pali zitsanzo zambiri za m’Baibulo ndiponso za masiku ano zotsimikizira zimenezi.

“Sanali Kusowa pa Kachisi”

4. Kodi Anna, mneneri wokalamba, anasonyeza bwanji kudzipereka kwake kwa Mulungu, ndipo anadalitsidwa motani?

4 Chitsanzo chimodzi ndi Anna, mneneri wamkazi. Ali ndi zaka 84, “sanali kusowa pa kachisi, kuchita utumiki wopatulika usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupereka mapembedzero.” Anna sanali kugonera pakachisi pomwepo chifukwa chakuti atate wake sanali Mlevi koma anali wa “fuko la Aseri.” Mutha kuona kuti anali kuchita khama kuti azipezeka pa kachisi tsiku ndi tsiku kuyambira popereka nsembe ya m’mawa mpaka ya madzulo. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwake, Anna anadalitsidwa kwambiri. Anali ndi mwayi woona Yesu wakhanda pamene Yosefe ndi Mariya anabwera naye kwa Yehova kukachisi, malinga ndi Chilamulo. Atangomuona Yesuyo, Anna ‘anayamba kuyamika Mulungu, ndi kulankhula za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.’​—Luka 2:22-24, 36-38; Numeri 18:6, 7.

5, 6. Kodi okalamba ambiri masiku ano akusonyeza bwanji mtima ngati wa Anna?

5 Masiku anonso, okalamba ambiri pakati pathu ali ngati Anna. Iwo saphonya misonkhano, amapemphera ndi mtima wonse kuti kulambira koona kupite patsogolo, ndipo ali ndi mtima wokonda kulalikira uthenga wabwino. M’bale wina wazaka 80, yemwe ndi mkazi wake saphonya misonkhano, anati: “Kupita ku misonkhano ndi chizolowezi chathu. Sitifuna kupita kwina kulikonse nthawi ya misonkhano. Kumene kuli anthu a Mulungu, ifenso timafuna kukhala komweko. Tikakhala kumeneko, mtima wathu umakhala m’malo.” Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwa ife tonse.​—Aheberi 10:24, 25.

6 Nayenso Jean, mlongo wamasiye wazaka 80, akuti: “Sindilephera kudzipereka pa nkhani iliyonse ya kupembedza yoti nditha kuchita nawo.” Imeneyi ndi mfundo imene amayendera. Popitiriza, iye anati: “Ndi zoona kuti nthawi zina zinthu zimandivuta, koma nanga kodi pali chifukwa choti aliyense azikhala wachisoni ngati ine ndili ndi chisoni?” Akusekerera, anafotokoza kuti amasangalala kupita ku mayiko ena kukakhala pa misonkhano yolimbikitsa yauzimu. Paulendo wina posachedwapa ali kudziko lina kumene anakaonanso malo, anauza anzake kuti: “Kuona malo kwandikwana. Ndikufuna kupita mu utumiki wa kumunda.” Ngakhale kuti sanadziwe chinenero cha kumeneko, Jean anatha kukopa chidwi cha anthu kuti amve uthenga wa m’Baibulo. Ndiponso, kwa zaka zambiri, anatumikira mu mpingo umene unafunikira thandizo, ngakhale kuti zimenezi zinafuna kuti aphunzire chinenero chatsopano ndi kumayenda ola limodzi popita ku misonkhano.

Sasiya Kuphunzira

7. Kodi Mose atakalamba, anati chiyani kusonyeza kuti ankafuna kuti ubale wake ndi Mulungu uzikula?

7 Munthu akamakula, nzeru zake zimawonjezereka. (Yobu 12:12) Koma kupita patsogolo mwauzimu sikubwera chabe chifukwa chakuti munthu wakula. Choncho, atumiki okhulupirika a Mulungu sadalira nzeru zimene apeza pa zaka zambiri m’mbuyomo, koma amayesetsa ‘kuwonjezera kuphunzira.’ (Miyambo 9:9) Mwachitsanzo, Mose anali ndi zaka 80 pamene Yehova anamutuma. (Eksodo 7:7) Masiku amenewo, si anthu ambiri amene anali kufika zaka zimenezi, chifukwa chakuti iye analemba kuti: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, . . . tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu.” (Salmo 90:10) Ngakhale zinali choncho, Mose sanaganize kuti wakalamba kwambiri moti sangathe kuphunzira. Atatumikira Mulungu zaka zambiri, kuchita ntchito zambiri zapadera, ndi kulandira maudindo akuluakulu, Mose anachondererabe Yehova kuti: “Mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni.” (Eksodo 33:13) Nthawi zonse Mose ankafuna kuti ubale wake ndi Yehova ukule.

8. Kodi Danieli anayesetsa bwanji kuphunzira mpaka ali ndi zaka zoposa 90, ndipo pamapeto pake chinachitika ndi chiyani?

8 Nayenso mneneri Danieli, mwina ali ndi zaka zoposa 90, ankawerengabe mozama malemba opatulika. Zimene anazindikira powerenga “mabuku” amenewo, omwe ena a iwo angakhale anali Levitiko, Yesaya, Yeremiya, Hoseya, ndi Amosi, zinamulimbikitsa kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. (Danieli 9:1, 2) Poyankha pemphero lake limenelo, Mulungu anamuuza za kubwera kwa Mesiya ndi za tsogolo la kulambira koyera.​—Danieli 9:20-27.

9, 10. Kodi anthu ena achita zotani kuti apitirize kuphunzira?

9 Ifenso, mofanana ndi Mose komanso Danieli, tiyenera kuyesetsa mmene tingathere kuphunzira zinthu zauzimu. Ambiri akuchitadi zimenezi. Mwachitsanzo, Worth ali ndi zaka zoposa 80 ndiponso ndi mkulu mumpingo. Koma amayesetsa kuti asaphonye chakudya chauzimu choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyo 24:45) Iye anati: “Choonadi ndimachikonda kwambiri, ndipo ndimachita chidwi kuona kuunika kwa choonadi kukuwalirawalira.” (Miyambo 4:18) Fred nayenso wakhala mu utumiki wa nthawi zonse zaka zoposa 60, ndipo amasangalala kuyambitsa nkhani za m’Baibulo akamacheza ndi okhulupirira anzake. Zimenezi zimamulimbikitsa mwauzimu. Iye anati: “Ndimafuna kuganizira za Baibulo nthawi zonse. Ukamalimvetsa Baibulo ndi kulumikiza zimene ukuphunzira ndi ‘chitsanzo cha mawu opindulitsa,’ sumangodziwa mfundo za choonadi mwa apa ndi apo, koma umatha kuona bwinobwino kugwirizana kwa mfundo zonsezo.”​—2 Timoteyo 1:13.

10 Munthu akakalamba, sindiye kuti basi sangathe kuphunzira mfundo zatsopano ndi zovuta. Anthu ena aphunzira kuwerenga ndi kulemba, enanso aphunzira chinenero chatsopano ali ndi zaka zoposa 60, 70, ndi 80. Mboni za Yehova zambiri zachita zimenezi ndi cholinga cholalikira uthenga wabwino kwa anthu amitundu yosiyanasiyana. (Maliko 13:10) Mwachitsanzo, Harry ndi mkazi wake anali ndi zaka zoposa 60 pamene anaganiza zokathandiza kudera la Chipwitikizi. Harry anati: “Kunena zoona, ntchito iliyonse imavuta ukamakalamba.” Komabe, chifukwa cha khama lawo, anatha kuphunzitsa anthu Baibulo m’Chipwitikizi. Ndipo kwa zaka zambiri tsopano, Harry wakhala akukamba nkhani pamsonkhano wachigawo m’Chipwitikizi.

11. N’chifukwa chiyani tikukambirana zimene okalamba ena okhulupirika achita?

11 Sikuti aliyense angachite zimene enawa achita, chifukwa moyo wa anthu ndi thanzi lawo zimasiyanasiyana. Nangano ndi chifukwa chiyani tikukambirana zimene anthu ena okalamba achita? Cholinga chake sichakuti tonsefe tizichita zofanana ndi zimene enawa achita. Koma tikungotsatira mfundo imene mtumwi Paulo analembera Akhristu achiheberi yokhudza akulu mumpingo. Iye anati: “Poonetsetsa mmene khalidwe lawo likukhalira, tsanzirani chikhulupiriro chawo.” (Aheberi 13:7) Tikamaonetsetsa changu cha okalamba amene akutumikira Mulungu, zimatilimbikitsa kutsanzira chikhulupiriro chawo cholimba chimene chimawathandiza potumikira Mulungu. Pofotokoza chifukwa chake amachita zimene akuchita, Harry, amene panopa ali ndi zaka 87, anati: “Ndikufuna kugwiritsa ntchito zaka zanga zotsala mwanzeru ndi kuthandiza kwambiri pa utumiki wa Yehova.” Fred, amene tamutchula uja, ali pa Beteli ndipo amasangalala kwambiri ndi ntchito yake. Iye anati: “Uyenera kuganizira njira imene ungatumikire Yehova ndi kusaisiya.”

Amadziperekabe Ngakhale Zinthu Zikusintha

12, 13. Kodi Barizilai anasonyeza bwanji kudzipereka kwake kwa Mulungu ngakhale kuti anali wokalamba?

12 Munthu akamakula, zambiri zimasintha pamoyo wake ndipo zimamuvuta kuvomereza zimenezo. Ngakhale zili choncho, ndi zotheka kukhalabe wodzipereka kwa Mulungu. Chitsanzo chabwino pankhani imeneyi ndi Barizilai wa ku Gileadi. Ali ndi zaka 80, anasamalira Davide ndi asilikali ake mwapadera kwambiri, powapatsa chakudya ndi pogona, nthawi imene Abisalomu anagaluka. Davide akubwerera ku Yerusalemu, Barizilai anamuperekeza mpaka kumtsinje wa Yordano. Davide anapempha kuti Barizilai apite naye kuti azikakhala m’bwalo la mfumu. Barizilai atamva zimenezi anati: “Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu . . . Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mawu a amuna ndi akazi oimba? . . . Suyu, Chimamu mnyamata wanu, iye awoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mum’chitire chimene chikukomerani.”​—2 Samueli 17:27-29; 19:31-40.

13 Ngakhale kuti anali atakalamba, Barizilai anachita zonse zomwe akanatha kuthandiza mfumu yoikidwa ndi Yehova. Iye anazindikira kuti sangathenso kumva kukoma kwa chakudya ndi kumva zinthu ngati mmene ankachitira kale, koma sanakhumudwe. Ponena kuti Chimamu apite m’malo mwake, Barizilai anaonetsa kuti anali ndi mtima wosadzikonda. Mofanana ndi Barizilai, okalamba ambiri masiku ano ali ndi mtima wopatsa ndi wosadzikonda. Amachita zonse zomwe angathe kuti apititse patsogolo kulambira koona, podziwa kuti “nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” Kunena zoona, ndi dalitso lalikulu kukhala ndi anthu okhulupirika amenewa pakati pathu.​—Aheberi 13:16.

14. Kodi kutchula msinkhu wa Davide kumathandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la mawu a pa Salmo 37:23-25?

14 Pamoyo wa Davidenso, zinthu zinasintha kambirimbiri koma iye anakhulupirirabe kuti Yehova sasiya kusamalira atumiki ake okhulupirika. Chakumapeto kwa moyo wake, Davide analemba nyimbo imene masiku ano ndi Salmo 37. Tayerekezani Davide akusinkhasinkha atakhala pansi, kwinaku akuimba nyimbo ndi zeze kuti: “Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu: pakuti Yehova agwira dzanja lake. Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Salmo 37:23-25) Yehova anaona kuti ndi bwino kutchula msinkhu wa Davide mu salmo limeneli. Zimenezi zimawonjezera mphamvu ya mawu a Davide amenewa ochokera pansi pa mtima.

15. Kodi mtumwi Yohane anakhala bwanji chitsanzo chabwino cha kukhulupirika, moyo wake utasintha komanso atakalamba?

15 Mtumwi Yohane ndi chitsanzo chinanso chabwino cha munthu amene anakhalabe wokhulupirika moyo wake utasintha komanso atakalamba. Atatumikira Mulungu zaka pafupifupi 70, Yohane anaponyedwa m’ndende pachilumba cha Patimo chifukwa “cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Koma ntchito yake sinathere pamenepo, chifukwatu mabuku onse a m’Baibulo amene analembedwa ndi Yohane, anawalemba atakalamba. Ali pa chilumba cha Patimo, anaona masomphenya ochititsa nthumanzi ochokera kwa Mulungu amene anawalemba bwinobwino m’buku la Chivumbulutso. (Chivumbulutso 1:1, 2) Ambiri amakhulupirira kuti Yohane anamasulidwa mu ulamuliro wa Nerva, Mfumu Yaikulu ya Roma. Kenako pofika mu 98 C.E., Yohane analemba buku lake la Uthenga Wabwino ndi makalata atatu odziwika ndi dzina lake. Apa n’kuti ali ndi zaka 90 kapena 100.

Ali ndi Mbiri Yosaiwalika ya Kupirira

16. Kodi anthu amene afika posatha kulankhula bwinobwino angaonetse bwanji kudzipereka kwawo kwa Yehova?

16 Pamoyo, zinthu zimasintha mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, anthu ena afika mpaka posatha kulankhula bwinobwino. Komabe, amakumbukirabe chikondi cha Mulungu ndi kukoma mtima kwake kwa m’chisomo. Ngakhale kuti sangalankhule ndi pakamwa pawo, mumtima mwawo amakhala akumuuza Yehova kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Yehova nayenso amadziwa anthu amene ‘amakumbukira dzina lake,’ ndipo amazindikira kuti iwo ndi osiyana kwambiri ndi anthu ena onse, amene alibe nazo ntchito njira zake. (Malaki 3:16; Salmo 10:4) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amakondwera ndi zimene timasinkhasinkha mu mtima mwathu.​—1 Mbiri 28:9; Salmo 19:14.

17. Kodi atumiki a Yehova amene amutumikira zaka zambiri, apeza chinthu chapadera chotani?

17 Komanso tisaiwale kuti anthu onse amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, apeza chinthu chapadera kwambiri chomwe sichingapezeke m’njira ina iliyonse. Chinthu chimenechi ndi mbiri yosaiwalika ya kupirira. Yesu anati: “Ngati inu mudzapirira, mudzapeza miyoyo yanu.” (Luka 21:19) Kupirira ndi kofunikiradi kuti munthu apeze moyo wosatha. Inu amene ‘mwachita chifuniro cha Mulungu’ ndipo mwaonetsa kukhulupirika pamoyo wanu, mungayembekezere kuona “kukwaniritsidwa kwa lonjezolo.”​—Aheberi 10:36.

18. (a) Kodi Yehova amasangalala ndi chiyani akaona okalamba? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Yehova amayamikira utumiki wanu umene mukuchita ndi mtima wonse, kaya zimene mukuchitazo ndi zambiri kapena ndi zochepa. Ngakhale kuti ‘munthu wakunja’ akutha ndi ukalamba, ‘munthu wam’kati’ akukhala watsopano tsiku ndi tsiku. (2 Akorinto 4:16) Sitikukayika kuti Yehova amayamikira zimene mwachita m’mbuyomu, ndipo n’zodziwikiratu kuti akuyamikiranso zimene mukuchitira dzina lake panopa. (Aheberi 6:10) M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mmene kukhulupirika kotereku kwathandizira ena ambiri.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Anna ndi chitsanzo chabwino chotani kwa Akhristu okalamba masiku ano?

• N’chifukwa chiyani ukalamba sungalepheretse munthu kuchita zambiri?

• Kodi okalamba angatani kuti asonyezebe kudzipereka kwa Mulungu?

• Kodi Yehova amauona bwanji utumiki wa anthu okalamba?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Danieli, mwa kuwerenga “mabuku,” anazindikira za kutha kwa zaka za ukapolo wa Ayuda

[Zithunzi patsamba 25]

Okalamba ambiri ndi zitsanzo zabwino pa kusaphonya misonkhano, kulalikira mwachangu, ndi kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira