Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mdulidwe Umasonyeza Kuti Ndiwe Mwamuna Weniweni?

Kodi Mdulidwe Umasonyeza Kuti Ndiwe Mwamuna Weniweni?

Kodi Mdulidwe Umasonyeza Kuti Ndiwe Mwamuna Weniweni?

M’MADERA ambiri padziko lonse anyamata amawadula pofuna kuti apewe matenda. M’madera ena, amuna sadulidwa kwa moyo wawo wonse. Kwa ena, monga Ayuda ndi Asilamu, mdulidwe si nkhani yongopewa matenda ayi, komanso ndi nkhani yachipembedzo.

Komabe m’mayiko ena, ana aamuna amawadula akafika paunyamata. Nthawi zambiri anyamatawo amawatumiza ku simba, kumene amakawadula n’kuwabindikiritsa kwa milungu ingapo mpaka zilonda zawozo zitapola. Panthawiyi, anyamatawa amatsatira miyambo inayake ndipo amawaphunzitsa kuchita zinthu ngati mwamuna wamkulu. Kodi mnyamata ayenera kuchitidwa mdulidwe woterewu kuti aoneke kuti wafika pokhala mwamuna weniweni? Tiyeni tione maganizo a Mulungu pa nkhaniyi m’Baibulo.​—Miyambo 3:5, 6.

Mmene Mulungu Amaonera Mdulidwe

Anthu ena kale, monga Aiguputo, ankachita mdulidwe, kapena kuti ankadula amuna khungu la kunsonga kwa chokodzera. Komatu Abulahamu sanabadwire pakati pa anthu achikhalidwe chotero. Ndipo anakhala mbali yaikulu ya moyo wake, ali wosadulidwa. Komanso anachita zinthu zosonyeza chamuna zedi ali wosadulidwa. Ndi kagulu kochepa chabe ka anthu, iye anathamangitsa ndi kugonjetsa magulu ankhondo a mafumu anayi amene anagwira Loti, yemwe anali mphwake. (Genesis 14:8-16) Patatha zaka pafupifupi 14, Mulungu analamula Abulahamu kuti adulidwe ndi kutinso adule mbumba yake yonse. N’chifukwa chiyani Mulungu analamula zimenezi?

Ndithu, si chifukwa choti panthawi imeneyi m’pamene Abulahamu anakhala munthu wamkulu, chifukwatu apa n’kuti iye ali kale ndi zaka 99. (Genesis 17:1, 26, 27) Mulungu ananena chifukwa chimene analamulira zimenezi. Iye anati: “Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi inu.” (Genesis 17:11) Pangano la Abulahamuli linalinso ndi lonjezo lakuti m’tsogolo Mulungu adzadalitsa “mabanja onse a dziko lapansi,” kudzera mwa Abulahamu. (Genesis 12:2, 3) Motero, kwa Mulungu nkhani ya mdulidwe sinali chizindikiro cha kukhala mwamunamuna ayi. Ankachita mdulidwe posonyeza kuti munthuyo ndi mbadwa ya Abulahamu wa mtundu wa Isiraeli, amene anali ndi mwayi woikizidwa “mawu opatulika a Mulungu.”​—Aroma 3:1, 2.

Patapita nthawi, mtundu wa Isiraeli unasonyeza kuti sunali woyenerera kuikizidwa zimenezi ndipo unatero pokana Yesu Khristu, yemwe ndi Mbewu ya Abulahamu yeniyeni. Motero, Mulungu anawasiya ndipo mdulidwe wawowo unalibenso tanthauzo lililonse kwa Mulungu. Komabe, Akhristu ena m’nthawi ya atumwi ankakakamirabe mfundo yakuti Mulungu ankafunabe kuti anthu ake azidulidwa. (Machitidwe 11:2, 3; 15:5) Choncho, mtumwi Paulo anatumiza Tito kuti ‘akakonze zinthu zosalongosoka,’ m’mipingo ingapo. M’kalata imene analembera Tito, Paulo anatchulamo vuto lawo limodzi: “Pali anthu ambiri osaweruzika, olankhula zopanda pake, ndi opotoza maganizo a ena, makamaka anthu amene akusungabe mdulidwe. N’kofunika kuwatseka pakamwa amenewa, pakuti anthu amenewa, pofuna kupeza phindu mwachinyengo, akuwonongabe mabanja athunthu mwa kuphunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa.”​—Tito 1:5, 10, 11.

Malangizo a Paulowa akugwirabe ntchito panopo. N’kusemphana ndi Malemba kuti Mkhristu woona azilimbikitsa ena kuti ana awo adulidwe. M’malo mwa “kulowerera nkhani za ena,” Mkhristu amasiya nkhani zimenezi kwa makolowo, kuti adziwe okha chochita. (1 Petulo 4:15) Komanso Mulungu anauzira Paulo kulemba mawu otsatirawa onena za mdulidwe wa m’Chilamulo cha Mose: “Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Alipo kodi amene anaitanidwa ali wosadulidwa? Asadulidwe. Mdulidwe sutanthauza kalikonse, ndipo kusadulidwa sikutanthauza kanthu, koma kusunga malamulo a Mulungu ndiko kofunika. Wina aliyense akhalebe mmene analili poitanidwa.”​—1 Akorinto 7:18-20.

Nanga Bwanji Zotumiza Ana ku Simba?

Kodi bwanji ngati makolo achikhristu aganiza zoti mwana wawo adulidwe? Kodi Baibulo limavomereza zoti makolo azitumiza ana awo kusimba? Ana akapita kusimba si kuti amangowadula basi. Kwa milungu ingapo, nthawi zonse mwanayo amakhala ndi anyamata ndiponso anamkungwi amene salambira Yehova. Zinthu zambiri zimene amawaphunzitsa kumeneko n’zosemphana ndi mfundo zapamwamba za m’Baibulo. Baibulo limachenjeza kuti: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.”​—1 Akorinto 15:33.

Komanso nthawi zambiri anawo amavulazidwa ku simbako. M’chaka cha 2003, magazini ina ya zachipatala (South African Medical Journal) inachenjeza kuti: “Chaka chinonso pali zoopsa zambiri zomwe zachitika m’masimba odula ana, ndipo talandira malipoti apadziko lonse onena za ana amene afa ndi kuvulazidwa. Malipotiwa achokera ku mabungwe onse otchuka ofalitsa nkhani. . . . Mwachidule, tingati masimba ambiri amasiku anowa n’ngachabechabe, ndiponso n’ngoopsa.”

Kuphatikiza pa kuvulaza mwanayo mwakuthupi, choopsa kwambiri n’chakuti mwanayo angavulazidwenso zedi mwauzimu. Ziphunzitso ndiponso miyambo ya kusimba imakhala yogwirizana kwambiri ndi zokhulupirira mizimu ndiponso zolambira makolo akufa. Mwachitsanzo, anawo akavulala kapena kufa, ambiri amangoti zachitika chifukwa choti achesulidwa kapena kulozedwa, kapenanso chifukwa choti mizimu ya makolo yakwiya. Savomereza kuti n’chifukwa choti odulawo sachita ntchitoyo mosamala ndiponso amachita zinthu mwauve. Pankhani yochita zinthu zogwirizana ndi kupembedza konyenga, Baibulo limalamula kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira. Pali ubale wanji pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kuyanjana kwanji pakati pa kuwala ndi mdima? . . . ‘Choncho tulukani pakati pawo, dzilekanitseni kwa iwo,’ atero Yehova, ‘ndipo musakhudze chonyansacho’; ‘ndipo ndidzakulandirani.’” (2 Akorinto 6:14-17) Poganizira za malangizo amenewa, n’kupanda nzeru kwakukulu ngati makolo achikhristu atalola kuti mwana wawo wamwamuna apite kusimba.

Kodi N’chiyani Chimachititsa kuti Mkhristu Akhale Mwamuna Weniweni?

Kudulidwa kapena kusadulidwa sikusonyeza kuti Mkhristu ndi mwamuna weniweni kapena ayi. Akhristu oona amaganizira kwambiri zosangalatsa Mulungu osati “kudzionetsa ngati abwino pamaso pa anthu.”​—Agalatiya 6:12.

Komabe, kuti Mkhristu asangalatse Mulungu, ayenera ‘kudula khungu la mtima wake.’ (Deuteronomo 10:16; 30:6; Mateyo 5:8) Khungu la mtima wakelo salidula ndi lumo ayi, koma amalidula pokana maganizo oipa ndi odzikuza, monga maganizo akuti kudulidwa kwenikweni kuja kumapangitsa mwamuna kukhala woposa ena. Kaya akhale wodulidwa kapena wosadulidwa, Mkhristu angathe kusonyeza kuti ndi mwamuna weniweni popirira ziyeso ndiponso ‘pochirimika m’chikhulupiriro.’​—1 Akorinto 16:13; Yakobe 1:12.