Kodi Zoipa Zingathetsedwe?
Kodi Zoipa Zingathetsedwe?
Mnyamata wamng’ono akutola chinthu chinachake m’munda, koma chinthucho ndi bomba ndipo likum’phulikira ku maso moti tsopano mnyamatayo ndi wakhungu ndiponso wolemala. Mayi wina akutaya mwana wake wongobadwa kumene m’zinyalala zomwe zili m’mphepete mwa msewu. Munthu wina yemwe wachotsedwa ntchito wabwerera kumene ankagwira ntchitoko ndipo akuwombera aliyense amene wam’peza, kenako akudzipha. Munthu wolemekezeka akugwirira ana.
N’ZOMVETSA chisoni kuti nkhani zoipa zoterezi zafala kwambiri masiku ano. Ndipo n’zomvetsanso chisoni kwambiri kuti nkhanizi sizimvekamveka chifukwa chakuti zimaphimbika ndi nkhani zina monga za kupha anthu onse a fuko lina kapena uchigawenga. M’chaka cha 1995, nkhani ina m’nyuzi inati: “Zinthu zaipa koposa, moti tingati zakazi zakhala zikulamulidwa ndi Satana. Kuposa kale lonse, anthu ali ndi luso ndiponso mtima wofuna kupha anthu mamiliyoni ambiri chifukwa chosiyana mtundu, chipembedzo kapena kuchuluka kwa chuma.”
Ndiponso anthu akuipitsa mpweya, akuipitsanso malo ndipo akusakaza zachilengedwe moti mitundu ina ya nyama ikutha. Kodi anthu angathetsedi zoipa zonsezi kuti dziko likhale labwino ndi lotetezeka? Kodi kuyesa kuchita zimenezi sikungafanane ndi kugwiritsa ntchito tsache pofuna kuimitsa madzi amene akuyenda mwamphamvu? Pulofesa wina amene walemba nkhani zambiri zokhudza kuipa anati: “Ndakhala ndikulakalaka kwambiri kusintha zinthu m’dzikoli kuti zikhale zabwino. Koma palibe chimene chikuoneka kuti chikusintha.” Mwina inunso mukuona chimodzimodzi.
Mmene dziko likuyendera zikufanana ndi chombo chimene chikuyenda pa nyanja yamkuntho ndi yoopsa imene ikuipiraipira. Ngakhale kuti palibe munthu amene akufuna kupita komwe chombo chikulowera, zoyesayesa zonse zosintha komwe akulowera zikulephereka. Chombocho chikungopitabe komwe kuli mphepo yamkunthoyo.
Chinthu china chimene chikuchititsa zinthu kuipiraipira ndi kupanda ungwiro kwa anthu. (Aroma 3:23) Komabe, sangakhale anthu okha amene akuchititsa zimenezi, chifukwa chakuti zoipa zikuwonjezereka kwambiri, zikufalikira paliponse ndipo zikuchitika nthawi zonse. Kodi n’kutheka kuti anthu akulamulidwa ndi mphamvu inayake yoipa kwambiri ndiponso yosaoneka? Ngati zili choncho, kodi mphamvuyo n’chiyani ndipo tingadziteteze bwanji? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
© Heldur Netocny/Panos Pictures