Lilime ndi Lamphamvu
Lilime ndi Lamphamvu
LILIME la kadyansonga n’lotalika masentimita 45 ndipo limatha kupindika mosavuta. Lilimeli n’lamphamvu kwambiri moti limatha kuthyola masamba a mitengo. Lilime la namgumi wotchedwa blue whale limalemera mofanana ndi njovu imodzi. Taganizirani mphamvu zomwe zingafunikire kuti muthe kusuntha lilimeli.
Tikayerekeza kukula, kulemera ndi mphamvu za malilime amenewa ndi lilime la munthu, la munthu n’lochepa kwambiri. Koma lilime la munthu litha kuchita zazikulu kuposa malilime enawo. Ponena za kachiwalo ka munthu kameneka, Baibulo limati: “Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo.” (Miyambo 18:21) Ndithudi, nthawi zambiri tamvapo kuti anthu agwiritsa ntchito lilime lawo kunena mabodza ndi kupereka umboni wonama umene wasokoneza moyo wa anthu osalakwa, ngakhale kuwapha kumene.
Mofananamo, kusalankhula bwino kwachititsa anthu amene akhala akugwirizana kwa nthawi yaitali kuti asagwirizanenso. Anthu ena akhumudwa kwambiri chifukwa cha mawu okhadzula. Yobu yemwe mabwenzi ake anamuneneza kwambiri anafuula kuti: “Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti, ndi kundithyolathyola nawo mawu?” (Yobu 19:2) Wophunzira Yakobe anafotokoza bwino kwambiri mmene lilime losalamulirika lingawonongere zinthu. Iye anati: “Lilime . . . ndi kachiwalo kakang’ono, koma limadzitama kwambiri. Tangoganizani mmene kamoto kakang’onong’ono kamayatsira nkhalango yaikulu! Inde, lilimenso ndi moto.”—Yakobe 3:5, 6.
Komabe, zinthu zina zimene lilime limatha kuchita zingapulumutse moyo. Mawu achifundo ndi olimbikitsa athandiza anthu ena kuti asavutike maganizo kapena kudzipha. Chifukwa chomvera malangizo abwino, zigawenga ndiponso anthu ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo athandizidwa kuti asafe mwamsanga. N’zoona kuti zimene lilime la munthu wolungama limanena ndizo “mtengo wa moyo” ndipo “mawu oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”—Miyambo 15:4; 25:11.
Koma tingachite bwino kwambiri kugwiritsa ntchito lilime lathu potamanda Yehova Mulungu, kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso kuphunzitsa anthu ena choonadi chofunika kwambiri cha m’Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3; Mateyo 24:14; 28:19, 20.