Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliro
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliro
MNENERI Yeremiya anaona kukwaniritsidwa kwa uthenga wa chiweruzo umene iyeyo anakhala akuuza anthu kwa zaka 40. Kodi mneneriyu anamva bwanji pamene anaona yekha mzinda umene iye ankaukonda ukuwonongedwa? M’mawu ake oyamba ofotokoza za buku la Maliro, Baibulo lina la Chigiriki (Septuagint) linati: “Yeremiya anakhala pansi n’kumalilira Yerusalemu ndi mawu amenewa.” Bukuli linalembedwa mu 607 B.C.E. Apa n’kuti mneneriyu asanaiwale ngakhale pang’ono zoti Yerusalemu anazingidwa kwa miyezi 18 kenaka n’kuwotchedwa. Motero buku la Maliro limanena momveka bwino chisoni chachikulu chimene Yeremiya anali nacho. (Yeremiya 52:3-5, 12-14) Uwu ndi mzinda wokhawo m’mbiri yonse ya anthu umene unaliridwapo mokhudza mtima ndiponso momvetsa chisoni chonchi.
Buku la Maliro kwenikweni ndi ndakatulo zisanu. Ndakatulo zinayi zoyambirira ndi nyimbo zolira maliro ndipo yachisanuyo ndi pemphero.
“MASO ANGA ALEFUKA NDI MISOZI”
“Ha! mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m’madera a dziko wasanduka wolamba!” Umu ndi mmene mneneri Yeremiya anayambira ndakatulo yake yolilira Yerusalemu. Mneneriyu ananena mawu otsatirawa potchula chifukwa chimene mzindawu unaona zoopsazi: “Yehova wam’sautsa pochuluka zolakwa zake.”—Maliro 1:1, 5.
Pokhala ngati kuti ndi mkazi wamasiye yemwenso ana ake anafa, Yerusalemu anafunsa kuti: “Kodi chilipo chisoni china ngati changachi?” Ponena za adani ake, Yerusalemu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Zoipa zawo zonse zidze pamaso panu, muwachitire monga mwandichitira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse, pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga.”—Maliro 1:12, 22.
Chifukwa chovutika mtima kwambiri, Yeremiya anati: “[Yehova] pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Isiraeli; wabweza m’mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo, natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.” Posonyeza chisoni chake chachikulu mneneriyu akudandaula kuti: “Maso anga alefuka ndi misozi mkati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi.” Ngakhale anthu ongodutsa ankadabwa nazo, n’kumanena kuti: “Kodi uwu ndi mudzi wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse” uja?—Maliro 2:3, 11, 15.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:15—Kodi mawu akuti “Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Ziyoni, monga mopondera mphesa” akutanthauza chiyani? Powononga mzindawo, womwe unayerekezeredwa ndi namwali, Ababulo anakhetsa magazi ochuluka zedi. N’chifukwa chake Yeremiya anayerekezera zimenezi ndi kuponda mphesa. Popeza kuti Yehova ndiye analosera zimenezi n’kulola kuti zichitike, tingathe kunena kuti iyeyo ndiye ‘anaponda mphesa.’
2:1—Kodi ‘kukoma kwake kwa Isiraeli kunagwetsedwa pansi kuchoka kumwamba’ m’njira yotani? Popeza kuti “kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,” nthawi zina Baibulo likamanena za kuipitsidwa kwa zinthu zopatulika limanena kuti zinthuzo ‘zagwetsedwa pansi kuchoka kumwamba.’ ‘Kukoma kwake kwa Isiraeli,’ kapena kuti ulemerero ndiponso mphamvu zomwe mtunduwu unali nazo panthawi imene Yehova anali kuuyanja, kunagwetsedwa pansi pamene Yerusalemu anawonongedwa komanso Yuda anasanduka bwinja.—Yesaya 55:9.
2:1, 6—Kodi “poponda mapazi” ndiponso “dindiro” la Yehova n’chiyani? Wamasalmo anayimba kuti: “Tidzalowa mokhalamo iye; tidzagwadira ku mpando wa mapazi ake.” (Salmo 132:7) Motero, mawu akuti “poponda mapazi” omwe ali pa Maliro 2:1 akutanthauza nyumba yolambiriramo Yehova, kapena kuti kachisi wake. Ababulo “anatentha nyumba ya Yehova” ngati dindiro, kapena msasa wa kumunda.—Yeremiya 52:12, 13.
2:17—Kodi ndi “mawu” ati kwenikweni amene Yehova anatsiriza, kapena kuti anawachitadi onena za Yerusamu? Apa zikuoneka kuti akunena za mawu a pa Levitiko 26:17, akuti: “Nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.”
Zimene Tikuphunzirapo:
1:1-9. Yerusalemu analira kwambiri usiku, ndipo misozi inali chuchuchu pamasaya pake. Zipata zake zinasiyidwa zokha, ndipo ansembe ake anausa moyo. Anamwali ake anasauka mtima ndipo Yerusalemuyo anali ndi nkhawa yosaneneka. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa choti Yerusalemu anachita tchimo lalikulu zedi. Udyo wake, kapena kuti kudetsedwa kwake kunali m’nsalu zake, kapena kuti zovala zake. Kuchita zoipa sikubweretsa chimwemwe ayi, koma misozi, kuusa moyo, nkhawa yosaneneka, ndiponso kuwawidwa mtima.
1:18. Popereka chilango kwa wolakwa, Yehova nthawi zonse amatero mwachilungamo.
2:20. Aisiraeli anachenjezedwa kuti akapanda kumvera mawu a Yehova, adzakumana ndi zoopsa, monga kudya ‘nyama ya ana awo aamuna ndi aakazi.’ (Deuteronomo 28:15, 45, 53) Ndithudi, n’kupusa kwambiri kusamvera Mulungu mwadala.
“MUSABISE KHUTU LANU POPUMA NDI POFUULA INE”
Mu chaputala 3 cha Maliro, mtundu wa Isiraeli umatchedwa “munthu.” Ngakhale kuti mtunduwu unakumana ndi mavuto, munthuyu anaimba motere: “Yehova akhalira wabwino om’lindirira, ndi moyo wom’funafuna.” Popemphera kwa Mulungu woona, iye anapempha kuti: “Munamva mawu anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.” Popempha Yehova kuti asaiwale zoipa zimene adani anawachita, Yeremiya anati: “Mudzawabwezera chilango, Yehova, monga mwa machitidwe a manja awo.”—Maliro 3:1, 25, 56, 64.
Yeremiya ananena mmene ankamvera mumtima mwake chifukwa cha zoopsa zimene mzinda wa Yerusalemu unakumana nazo panthawi imene unazingidwa kwa miyezi 18. Iye anati: “Mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m’kamphindi, anthu osauchitira kanthu.” Yeremiya anapitiriza kuti: “Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m’munda.”—Maliro 4:6, 9.
Ndakatulo yachisanu imamveka ngati kuti anthu a mumzinda wa Yerusalemu ndiwo akulankhula. Iwo anati: “Yehova, kumbukirani chotigwerachi, penyani nimuone chitonzo chathu.” Pokumbukira mavuto amene anakumana nawo, iwo anapempha kuti: “Inu, Yehova, mukhala chikhalire, ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwo mibadwo. Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi, mukonzenso masiku athu ngati kale lija.”—Maliro 5:1, 19, 21.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
3:16—Kodi mawu akuti “wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi,” akutanthauza chiyani? Buku lina limati: “Ayuda ali paulendo wopita kuukapolo, sakanachitira mwina koma kuphika mikate yawo m’timauvuni tochita kukumba pansi, motero mkatewo unkakhala ndi mchenga.” Anthu ena ankabenthuka mano akamadya mkate umenewu.
4:3, 10—N’chifukwa chiyani Yeremiya anayerekezera ‘mwana wamkazi wa anthu a mtundu wake’ ndi “nthiwatiwa za m’chipululu”? Nthiwatiwa ‘imaumira mtima ana ake monga ngati si ake,’ limatero lemba la Yobu 39:16. Mwachitsanzo, nthiwatiwa yaikazi ikaswa, imachoka n’kumakayenda ndi zinzake n’kungosiya anapiyewo m’manja mwa yaimuna. Nanga chimachitika n’chiyani pakabwera zoopsa? Yaimuna ndi yaikazi ija zimathawa pa chisapo, anapiyewo n’kuwasiya okha. Panthawi imene Ababulo anazinga mzindawo, ku Yerusalemu kunali njala yoopsa zedi moti azimayi oti ankakonda ana awo bwinobwino anayamba kuwachita nkhanza anawo, ngati mmene zimachitira nthiwatiwa za m’chipululu. Ngakhale nkhandwe zinkawaposa kwambiri azimayiwa posamalira ana awo.
5:7—Kodi Yehova amaimba anthu mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo awo akale? Ayi, Yehova salanga anthu mwachindunji chifukwa cha machimo a makolo awo. Baibulo limati: “Aliyense wa ife adzadziyankhira yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Komabe, zotsatirapo za uchimo zingathe kukhala kwa nthawi yaitali ndithu mpaka kukhudza mibadwo yam’tsogolo. Mwachitsanzo, chifukwa choti Aisiraeli akale ankalambira mafano, mibadwo yawo yam’tsogolo inavutika kupitiriza kuchita zinthu zolungama.—Eksodo 20:5.
Zimene Tikuphunzirapo:
3:8, 43, 44. Panthawi ya zoopsa zimene zinachitika ku Yerusalemu, Yehova anakana kumvera madandaulo a anthu a mumzindawo. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa choti anthuwo anachita zosamvera ndipo sanalapebe. Ngati tikufuna kuti Yehova ayankhe mapemphero athu, tizimumvera.—Miyambo 28:9.
3:20. Yehova, yemwe ndi “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” ndi wokwezeka kwambiri moti amachita kudzichepetsa kuti “apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi.” (Salmo 83:18; 113:6) Koma Yeremiya ankadziwa bwino kuti Wamphamvuyonseyu amalolera kudzitsitsa pamaso pa anthuwa, kapena kuti amadzitsitsa kufika pa mlingo wawo, pofuna kuti awalimbikitse. Tizisangalala kwambiri kuti Mulungu woona ndi wodzichepetsa osati chabe wamphamvuyonse ndiponso wanzeruzonse!
3:21-26, 28-33. Kodi tingatani kuti tithe kupirira mavuto aliwonse, angakule bwanji? Yeremiya anatiuza mmene tingachitire. Tisamaiwale kuti Yehova ndi wokoma mtima zedi ndiponso n’ngwachifundo chosaneneka. Tizikumbukiranso kuti kukhala ndi moyo n’chifukwa chokwanira choti tisamataye mtima ndiponso kuti tizileza mtima ndi kudikira mwa phee kuti Yehova adzatipulumutsa, ndipo tizitero mosadandaula. Komanso tiyenera ‘kuika kamwa lathu m’fumbi,’ kutanthauza kuti tizilola kupirira ziyeso modzichepetsa, pozindikira kuti Mulungu amakhala ndi zifukwa zabwino zololera zinazake kuchitika.
3:27. Kuti tithane ndi ziyeso tili achinyamata tiyenera kupirira zovuta ndiponso kunyozedwa. Koma ‘n’kokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.’ Chifukwa chiyani? Chifukwa choti kuphunzira kupirira zovuta muli mwana kumakukonzekeretsani kuthana ndi mavuto m’tsogolo.
3:39-42. ‘Kudandaula’ tikamakumana ndi mavuto obwera chifukwa cha machimo athu si kwanzeru. M’malo modandaula ndi zotsatirapo za zoipa zimene tinachita, “tisanthule n’tiyese njira zathu n’tibwerenso kwa Yehova.” N’chinthu chanzeru kulapa ndi kusintha njira zathu.
Dalirani Yehova
Buku la m’Baibulo la Maliro limasonyeza bwino mmene Yehova anaonera Yerusalemu ndi dziko la Yuda pamene Ababulo anatentha mzindawu ndiponso kuwonongeratu dzikoli. M’buku limeneli, zikuonekeratu kuti Yehova analola anthu ake kukumana ndi zoopsazi chifukwa cha zolakwa zawo. Ndakatulo yomaliza m’bukuli, ili ndi mawu osonyeza kuti anthu ankadalirabe Yehova ndipo anali ndi cholinga choyambanso kuchita zinthu zabwino. Si anthu onse a m’nthawi ya Yeremiya amene anali ndi chiyembekezo chimenechi, koma ndi Yeremiya yekha ndiponso Ayuda ena otsala amene analapa moona mtima.
Zimene zalongosoledwa m’buku la Maliro zokhudza mmene Yehova ankaonera Yerusalemu, zikutiphunzitsa zinthu ziwiri zofunika kwambiri. Choyamba, kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi Yuda kukutithandiza kuona kufunika kokhala anthu omvera Yehova ndiponso zikutipatsa chenjezo loti tisanyalanyaze chifuniro chake. (1 Akorinto 10:11) Phunziro lachiwiri tikulipeza m’zochita za Yeremiya. (Aroma 15:4) Mneneriyu anali ndi chisoni chachikulu koma anadalirabe Yehova ngakhale panthawi yovuta kwambiri, pamene zinthu zinaoneka ngati kuti sizingakhalenso bwino. M’pofunikatu kuti nafenso tizidalira kwambiri Yehova ndiponso Mawu ake.—Aheberi 4:12.
[Chithunzi patsamba 9]
Mneneri Yeremiya anaona kukwaniritsidwa kwa uthenga wake wa chiweruzo
[Chithunzi patsamba 10]
Mboni za ku Korea izi zinayesedwa chikhulupiriro chifukwa chokana kulowerera m’zandale