Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Okalamba Ndi Dalitso kwa Anthu Ocheperapo Msinkhu

Okalamba Ndi Dalitso kwa Anthu Ocheperapo Msinkhu

Okalamba Ndi Dalitso kwa Anthu Ocheperapo Msinkhu

“Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.”​—SALMO 71:18.

1, 2. Kodi atumiki okalamba a Mulungu ayenera kudziwa chiyani, ndipo tikambirana chiyani m’nkhani ino?

TSIKU lina, mkulu wina wachikhristu kumadzulo kwa Africa anakacheza kwa m’bale wokalamba yemwe ndi wodzozedwa. Atapereka moni kwa m’baleyo kuti, “Nanga muli bwanji?” M’bale wokalambayo anayankha kuti, “Ayi, ndili bwino ndipo nditha kuthamanga, ngakhale kudumpha kumene.” Ponena mawuwa, anayerekeza kuthamanga ndi kudumpha. Kenako, anawonjezera kuti: “Koma sindingathe kukumba dzenje.” Mfundo yake inamveka, iye anatanthauza kuti, ‘Ndimachita zimene ndingathe, koma zimene sindingathe, sindichita.’ Panopa mkulu wachikhristu amene anakacheza ndi m’baleyo ali ndi zaka zoposa 80, ndipo amakumbukira bwino nthabwala za m’baleyo ndi kukhulupirika kwake.

2 Makhalidwe abwino a munthu wokalamba amakhudza kwambiri anthu ena. Pano sitikunena kuti munthu akakhala wamkulu ndiye kuti basi ali ndi nzeru ndipo ali ndi makhalidwe ngati a Khristu ayi. (Mlaliki 4:13) Baibulo limati: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, [ikapezedwa, NW] m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31) Ngati ndinu wokalamba, kodi mukudziwa kuti mawu ndi zochita zanu zingawathandize kwambiri anthu ena? Tiyeni tikambirane zitsanzo za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti okalamba ndi dalitso lalikulu kwa anthu ocheperapo msinkhu.

Chikhulupiriro Chimene Phindu Lake Silitha

3. Kodi kukhulupirika kwa Nowa kwakhudza bwanji anthu onse amene ali moyo lerolino?

3 Chikhulupiriro chosagwedera cha Nowa ndi chaphindu mpaka pano. Nthawi imene Nowa anamanga chingalawa, kusonkhanitsa zinyama, ndi kulalikira kwa anansi ake, anali ndi zaka pafupifupi 600. (Genesis 7:6; 2 Petulo 2:5) Chifukwa choopa Mulungu, Nowa limodzi ndi banja lake, anapulumuka Chigumula ndi kukhala makolo a anthu onse amene ali moyo lero. Ndi zoona kuti Nowa anakhalako nthawi imene anthu ambiri ankakhala ndi moyo wautali kuposa masiku ano. Koma ngakhale atakalamba kwambiri, Nowa anakhala wokhulupirikabe ndipo anadalitsidwa kwambiri. Kodi anadalitsidwa bwanji?

4. Kodi chikhulupiriro chosagwedera cha Nowa chawapindulitsa bwanji atumiki a Mulungu masiku ano?

4 Nowa anali ndi zaka pafupifupi 800 pamene Nimrode anayamba kumanga Nsanja ya Babele, kutsutsa lamulo la Yehova lakuti ‘adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 9:1; 11:1-9) Koma Nowa sanapanduke nawo. Choncho, ziyenera kuti Mulungu atasokoneza chinenero cha anthu opandukawo, chinenero cha Nowa sichinasinthe. Nowa anali ndi chikhulupiriro chosagwedera osati paukalamba wake wokha, komanso pamoyo wake wonse wautaliwo ndipo ndi chitsanzodi chabwino kwa atumiki a Mulungu amisinkhu yonse.​—Aheberi 11:7.

Okalamba Amathandiza Banja Lawo

5, 6. (a) Kodi Abulahamu ali ndi zaka 75, Yehova anamuuza kuchita chiyani? (b) Kodi Abulahamu anatani Mulungu atamuuza zimenezo?

5 Makolo amene anakhalako pambuyo pa Nowa amapereka umboni wakuti okalamba amathandiza banja lawo kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Abulahamu anali ndi zaka pafupifupi 75 pamene Mulungu anamuuza kuti: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kumka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso.”​—Genesis 12:1, 2.

6 Tangoganizani kuti mwauzidwa kuti musiye nyumba yanu, mabwenzi anu, dziko lanu ndi achibale anu kupita ku dziko limene simukulidziwa. Izitu ndi zimene Abulahamu anauzidwa kuti achite. Iye “anamuka . . . monga Yehova ananena kwa iye,” ndipo moyo wake wonse, anakhala m’mahema ngati mlendo wongokhalira kusamukasamuka m’dziko la Kanani. (Genesis 12:4; Aheberi 11:8, 9) Ngakhale kuti Yehova ananena kuti Abulahamu adzakhala “mtundu waukulu,” iye anamwalira kukali zaka zambiri kuti mbadwa zake zichuluke. Sara mkazi wake, anangobereka mwana mmodzi yekha Isake, ndipo izi zinachitika Abulahamu atakhala zaka 25 m’dziko limene analonjezedwa. (Genesis 21:2, 5) Koma sanataye mtima ndi kuganiza zobwerera ku mzinda umene anachokera. Chikhulupiriro chake ndi kupirira kwake ndi chitsanzo chabwino kwa ife.

7. Kodi kupirira kwa Abulahamu kunathandiza bwanji Isake mwana wake, ndipo phindu lake ndi lotani kwa anthu onse?

7 Kupirira kwa Abulahamu kunathandiza kwambiri Isake mwana wake, amene anakhala mlendo m’dziko la Kanani moyo wake wonse wa zaka 180. Isake anapirira chifukwa chokhulupirira lonjezo la Mulungu, ndipo chikhulupiriro chimenechi anachitenga kwa makolo ake ndiponso chinalimbikitsidwa ndi mawu amene Yehova anamuuza pambuyo pake. (Genesis 26:2-5) Chifukwa cha kulimbikira kwake, Isake anathandiza kwambiri kuti kudzera m’banja la Abulahamu, lonjezo la Yehova la “mbewu” imene idzadalitsa anthu onse, likwaniritsidwe. Patadutsa zaka mazana ambiri, Yesu Khristu, amene ndi mbali yoyamba ya “mbewu” imeneyo, anatsegula njira kuti onse okhulupirira iye ayanjidwe ndi Mulungu ndi kukhala ndi moyo wosatha.​—Agalatiya 3:16; Yohane 3:16.

8. Kodi Yakobo anasonyeza bwanji chikhulupiriro champhamvu, ndipo zotsatira zake n’zotani?

8 Isake nayenso anathandiza Yakobo mwana wake kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu chimene chinamuthandiza mpaka ukalamba wake. Yakobo anali ndi zaka 97 pamene analimbana ndi mngelo usiku wonse pofuna kuti mngeloyo amudalitse. (Genesis 32:24-28) Yakobo anamwalira ali ndi zaka 147, koma asanamwalire, anadzilimbitsa ndi kupeza mphamvu zodalitsa ana ake onse 12 mmodzimmodzi. (Genesis 47:28) Mawu olosera za kutsogolo amene iye ananena, olembedwa pa Genesis 49:1-28, anakwaniritsidwa ndipo akukwaniritsidwabe mpaka pano.

9. Kodi okalamba okhwima mwauzimu angathandize bwanji banja lawo?

9 Zoonadi, atumiki a Mulungu okhulupirika ndi okalamba, angathandizedi banja lawo. Nzeru zawo ndi malangizo a m’Malemba komanso chitsanzo chawo cha kupirira zingathandize kwambiri mwana kukula ndi chikhulupiriro champhamvu. (Miyambo 22:6) Okalamba asamadziderere, koma azidziwa kuti iwowo ndiwo angathandize kwambiri banja lawo.

Okalamba Amathandiza Olambira Anzawo

10. Kodi Yosefe “anapereka lamulo lokhudza mafupa ake” lotani, ndipo linathandiza bwanji?

10 Okalamba angathandizenso okhulupirira anzawo. Paukalamba wake, Yosefe mwana wa Yakobo ananena chinthu chosonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Ali ndi zaka 110, “anapereka lamulo lokhudza mafupa ake,” kuti Aisiraeli akadzatuluka mu Iguputo, adzatenge mafupa akewo. Zimenezi zinathandiza kwambiri olambira oona mamiliyoni ambiri amene anakhalako pambuyo pake. (Aheberi 11:22; Genesis 50:25) Lamulo limenelo linathandiza Aisiraeli kusataya chiyembekezo chawo pazaka zambiri za ukapolo umene analowamo Yosefe atamwalira, ndipo linawatsimikizira kuti adzalanditsidwa.

11. Kodi Mose wokalambayo ayenera kuti anamuthandiza bwanji Yoswa?

11 Munthu wina amene analimbikitsidwa ndi chikhulupiriro cha Yosefe anali Mose. Ali ndi zaka 80, Mose anakhala ndi mwayi wonyamula mafupa a Yosefe kutuluka nawo mu Iguputo. (Eksodo 13:19) Ziyenera kuti ndi panthawi imeneyi, pamene anadziwana ndi Yoswa, amene anali wamng’ono kwa iye. Yoswa anakhala mtumiki wa Mose pazaka 40 zotsatira. (Numeri 11:28) Iye anakwera phiri la Sinai limodzi ndi Mose ndipo anamudikirira m’phiri momwemo mpaka Mose atatsika ndi miyala ya Mboni. (Eksodo 24:12-18; 32:15-17) Mose wokalambayo ayenera kuti anali nkhokwe ya nzeru ndi uphungu kwa Yoswa.

12. Kodi Yoswa anathandiza bwanji mtundu wa Isiraeli panthawi yonse ya moyo wake?

12 Yoswa nayenso analimbikitsa mtundu wa Isiraeli panthawi yonse ya moyo wake. Lemba la Oweruza 2:7 limati: “Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israyeli.” Koma Yoswa ndi akuluakulu ena atafa, mtunduwo unali wosakhazikika moti umangoti pena kulambira Mulungu woona, pena milungu yonama. Izi zinachitika zaka 300 mpaka masiku a mneneri Samueli.

Samueli “Anachita Chilungamo”

13. Kodi Samueli “anachita chilungamo” m’njira yotani?

13 Baibulo silinena kuti Samueli anali ndi zaka zingati pamene anamwalira, koma zinthu zimene buku la Samueli Woyamba limasimba zinatenga zaka 102, ndipo Samueli anaona zambiri za izo. Tikawerenga Aheberi 11:32, 33, timamva kuti oweruza okhulupirika ndi aneneri “anachita chilungamo.” Choncho, Samueli anathandiza anthu ambiri kupewa ndi kusiya zoipa. (1 Samueli 7:2-4) Kodi anachita bwanji zimenezi? Anali wokhulupirika kwa Yehova moyo wake wonse. (1 Samueli 12:2-5) Sanaope kudzudzula ngakhale mfumu. (1 Samueli 15:16-29) Ndiponso Samueli, pokhala “wokalamba waimvi,” anali chitsanzo chabwino pa kupempherera anzake. Iye anati sakanatha ‘kuchimwira Yehova ndi kuleka kupempherera’ Aisiraeli anzake.​—1 Samueli 12:2, 23.

14, 15. Kodi okalamba masiku ano angatsanzire bwanji Samueli pankhani ya kupemphera?

14 Zonsezi zikungosonyezeratu kuti okalamba atha kuthandiza atumiki a Yehova anzawo m’njira yapadera. Ngakhale kuti sangachite zambiri chifukwa cha mmene thanzi lawo ndi moyo wawo zilili, okalamba angapempherere anzawo. Inu agogo, kodi mukudziwa kuti mapemphero anu amathandiza kwambiri mpingo? Chifukwa cha chikhulupiriro chanu m’magazi okhetsedwa a Khristu, Yehova amakuyanjani, ndiponso chifukwa cha mbiri yanu ya kupirira, chikhulupiriro chanu chakhala cholimba ‘poyesedwa.’ (Yakobe 1:3; 1 Petulo 1:7) Musaiwale kuti: “Pembedzero la munthu wolungama, limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”​—Yakobe 5:16.

15 Ntchito yolalikira za Ufumu wa Yehova imafuna mapemphero anu. Abale athu ena ali m’ndende chifukwa chosalowerera ndale. Ena akuvutika chifukwa cha masoka achilengedwe, nkhondo, ndi ziwawa. Ngakhalenso mumipingo mwathu, muli anthu amene akukumana ndi mayesero ndipo ena amatsutsidwa. (Mateyo 10:35, 36) Nawonso amene akutsogolera ntchito yolalikira ndi kuyang’anira mipingo amafuna kuti muziwapempherera nthawi zonse. (Aefeso 6:18, 19; Akolose 4:2, 3) Mumachita bwino kutchula okhulupirira anzanu m’mapemphero anu, ngati mmene anachitira Epafura.​—Akolose 4:12.

Kuphunzitsa Mbadwo Wakudza M’mbuyo Mwawo

16, 17. Kodi lemba la Salmo 71:18 linalosera chiyani, ndipo kodi zimenezi zachitika bwanji?

16 Anthu okhulupirika a “kagulu ka nkhosa” oitanidwa kumwamba, akugwirira ntchito limodzi ndi a “nkhosa zina” omwe akuyembekeza kudzakhala pa dziko lapansi kosatha. Zimenezi zathandiza kuti “nkhosa zina” ziphunzire zinthu zambiri. (Luka 12:32; Yohane 10:16) Lemba la Salmo 71:18 linalosera zimenezi kuti: “Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.” Akhristu odzozedwa ndi mzimu, ali ndi khama pophunzitsa anzawo a nkhosa zina maudindo akuluakulu asanawasiye kuti akalandire ulemerero wawo limodzi ndi Yesu Khristu.

17 Mfundo ya pa Salmo 71:18, yonena za kuphunzitsa “onse akudza m’mbuyo,” ingagwirenso ntchito kwa a nkhosa zina, amene alandira malangizo kwa odzozedwa a Mulungu. Yehova walemekeza okalamba powapatsa udindo wofotokoza za iye kwa anthu amene akulandira choonadi masiku ano. (Yoweli 1:2, 3) A nkhosa zina akuona kuti ndi odala chifukwa cha zimene aphunzira kwa odzozedwa ndipo nawonso ali ndi mtima wofuna kuphunzitsabe Malemba anthu amene akufuna kutumikira Yehova.​—Chivumbulutso 7:9, 10.

18, 19. (a) Kodi ndi mfundo zamtengo wapatali zotani zimene atumiki okalamba a Yehova angafotokozere ena? (b) Kodi Akhristu okalamba sayenera kukayikira chiyani?

18 Atumiki okalamba a Yehova, odzozedwa ndi a nkhosa zina, ndiwo njira imene tingadziwire zochitika zapadera za m’mbuyomu. Adakalipobe okalamba ena amene anaonerera nawo filimu yoyamba ya “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” Ena anaonanapo ndi abale otsogolera gulu amene anaponyedwa m’ndende mu 1918 ndipo ankawadziwa bwino. Ena anagwirapo nawo ntchito youlutsa mawu pawailesi ya Watchtower ya WBBR. Ambiri atha kusimba za milandu yozengedwa m’makhoti akuluakulu kalelo yomenyera ufulu wa chipembedzo wa Mboni za Yehova. Enanso anakhulupirikabe pa kulambira koona m’mayiko omwe munali ulamuliro wankhanza. Ndithudi, okalamba atha kufotokoza mmene kamvedwe kathu ka choonadi kapitira patsogolo. Baibulo limatilimbikitsa kutapako nzeru m’nkhokwe zimenezi.​—Deuteronomo 32:7.

19 Akhristu okalamba akulimbikitsidwa kukhala zitsanzo zabwino kwa anthu ocheperapo msinkhu. (Tito 2:2-4) Mwina panopa simukuona kuti kupirira kwanu, mapemphero anu, ndi uphungu wanu zikuthandiza bwanji ena. Chimodzimodzinso Nowa, Abulahamu, Yosefe, Mose, ndi ena, ayenera kuti sanadziwe kuti kukhulupirika kwawo kudzathandiza kwambiri mibadwo yakudza m’mbuyo mwawo. Koma chitsanzo chawo cha chikhulupiriro ndi umphumphu chinathandiza kwambiri anthu ena; nanunso chitsanzo chanu chikutero.

20. Kodi anthu amene amakhalabe ndi chiyembekezo cholimba mpaka mapeto, adzapeza madalitso otani?

20 Kaya mudzachita kupulumuka “chisautso chachikulu” kapena kuukitsidwa, zidzakhala zosangalatsa kupeza “moyo weniweniwo.” (Mateyo 24:21; 1 Timoteyo 6:19) Pajatu mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, Yehova adzathetsa ukalamba. Nthawi imeneyi matupi athu sadzakalamba, koma tizidzati tikadzuka tsiku lililonse, thanzi lathu liziwongokera. Tidzakhala ndi mphamvu zambiri, tidzayambanso kuona kwambiri, kumva kwambiri, ndiponso tidzakhala ndi maonekedwe okongola. (Yobu 33:25; Yesaya 35:5, 6) Podziwa kuti anthu amene adzadalitsidwe kukhala m’dziko latsopano la Mulungu adzakhala ndi moyo wamuyaya, tinganene kuti adzakhalabe ngati ana nthawi zonse. (Yesaya 65:22) Choncho, tiyeni tonse tikhalebe ndi chiyembekezo cholimba mpaka mapeto ndipo tipitirizebe kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse. Tikukhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa zonse zimene walonjeza ndi kuti adzachitanso zambiri kuposa zimene tikuyembekezera.​—Salmo 37:4; 145:16.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi anthu onse adalitsidwa bwanji ndi kukhulupirika kwa Nowa?

• Kodi chikhulupiriro cha makolo akale chinathandiza bwanji mbadwa zawo?

• Kodi Yosefe, Mose, Yoswa, ndi Samueli paukalamba wawo, analimbikitsa bwanji olambira anzawo?

• Kodi ndi zinthu zotani zimene okalamba angasiyire mibadwo yakudza m’mbuyo mwawo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Kupirira kwa Abulahamu kunathandiza kwambiri Isake

[Chithunzi patsamba 28]

Uphungu wanzeru umene Mose anapereka unalimbikitsa Yoswa

[Chithunzi patsamba 29]

Kupempherera ena kumathandiza kwambiri

[Chithunzi patsamba 30]

Ana zimawathandiza akamamvetsera kwa agogo okhulupirika