Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinafunitsitsa Kukwaniritsa Utumiki Wathu

Tinafunitsitsa Kukwaniritsa Utumiki Wathu

Mbiri ya Moyo Wanga

Tinafunitsitsa Kukwaniritsa Utumiki Wathu

Yosimbidwa ndi Lena Davison

“Ndikulephera kuona. Sindikuona ngakhale pang’ono.” Woyendetsa ndege imene tinakwera ananena mawu amenewa movutikira. Posakhalitsa anasiya chiwongolero cha ndegeyo, n’kukomoka. Mwamuna wanga sankadziwa kuyendetsa ndege motero anayesetsa umu ndi umu kuti am’dzutse. Ndithudi, tinapulumuka lokumbakumba. Koma ndisanakuuzeni mmene tinapulumukira, taimani ndikufotokozereni zimene zinachitika kuti tipezeke m’ndege m’dziko lakutali kwambiri, lotchedwa Papua New Guinea.

NDINABADWIRA ku Australia mu 1929 koma ndinakulira mumzinda wa Sydney, womwe ndi likulu la chigawo cha New South Wales. Bambo anga, a Bill Muscat, anali achikomyunizimu, koma n’zodabwitsa kuti ankakhulupiriranso Mulungu. Moti mu 1938 iwo anavomera kukhala m’gulu la anthu a ku Australia amene anasaina nawo pempho loti a Joseph F. Rutherford, a ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova aloledwe kukalalikira ku holo yotchedwa Sydney Town Hall.

Panthawiyo bambo anatiuza kuti: “Mkulu ameneyu ayenera kuti ali ndi mfundo zinazake zochititsa chidwi.” Patatha zaka eyiti tinamva mfundo zikuluzikulu za uthenga umene ankalalikirawo. Bambo anaitana Norman Bellotti, mpainiya wanthawi zonse wa Mboni za Yehova, kuti abwere ku nyumba n’kudzakambirana nafe za m’Baibulo. Posakhalitsa banja lathu lonse linavomereza choonadi cha m’Baibulo ndipo linayamba kuchita nawo mwakhama utumiki wachikhristu.

Cha m’ma 1945 ndinasiya sukulu kuti ndisamalire mayi pa matenda awo aakulu. Ndiye ndinayamba kusoka zovala kuti ndizipeza ndalama zodzisamalira. Loweruka madzulo, ine ndi mkulu wanga Rose tinkayenda ndi gulu la apainiya n’kumalalikira mumsewu, panja pa holo ya Sydney Town Hall. Mu 1952, mchimwene wanga John, anamaliza maphunziro ake ku sukulu yaumishonale ya Gileadi ku United States ndipo anatumizidwa ku Pakistan. Inenso ndinkakonda kwambiri utumiki ndipo ndinkafuna kutsatira chitsanzo chake. Motero, chaka chotsatira ndinakhala mpainiya wokhazikika.

Ndinakwatiwa N’kuyamba Umishonale

Posakhalitsa, ndinakumana ndi John Davison, amene ankagwira ntchito pa ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ya ku Australia. Ndinagoma naye chifukwa cha kudzichepetsa kwake, khama lake pochita zinthu mosadzionetsera, ndiponso kusalola kuphwanya mfundo zolungama. M’nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, iye anamangidwa katatu chifukwa choti anakana kulowerera pa nkhondoyo poti anali Mkhristu. Tinagwirizana zoti moyo wathu wonse, ntchito yathu ikhala ya utumiki wachikhristu.

Tinakwatirana mu June 1955. Tinagula basi n’cholinga choti tiisandutse nyumba yotha kuyenda nayo. Tinkafuna kuti tizitha kupita m’madera akumidzi a ku Australia n’kumakakhala m’basiyi panthawi yonse imene tikulalikira kumeneko. Chaka chotsatira, analengeza kuti ku New Guinea kukufunika Mboni. Ili ndi dera la kumpoto cha kum’mawa kwa chilumba china chachikulu chomwe chili kumpoto kwa dziko la Australia. * Kumeneku kunali kusanafike uthenga wa Ufumu. Nthawi yomweyo tinadzipereka kuti tipita.

Nthawi imeneyi, panali njira imodzi yokha yolowera m’dziko la New Guinea. Njira yake inali kupeza ntchito ya nthawi zonse m’dzikolo. Motero John anayamba kufunafuna ntchito. Posakhalitsa anapeza ntchito ku kampaniyi inayake yocheka matabwa ku kachilumba kakang’ono kotchedwa New Britain, komwe kali mbali ya New Guinea. Patatha milungu ingapo, tinayambapo ulendo wopita ku gawo lathu latsopanoli, ndipo tinafika ku Rabaul, ku New Britain, mu July 1956. Kumeneku tinadikirira kwa masiku sikisi kuti boti lititenge n’kutipititsa ku Waterfall Bay.

Utumiki Wathu ku Waterfall Bay

Panyanja sipanali bwino komabe titayenda masiku angapo, tinafika ku Waterfall Bay dera lalikulu makilomita 240, lomwe lili m’mbali mwanyanja. Kumeneku kunali macheka aakulu omwe anawaika pa malo enaake olambulidwa bwino m’nkhalango. Tsiku limenelo usiku, antchito onse atakhalakhala kuti azidya chakudya chamadzulo, bwana woyang’anira machekawo anati: “Pepanitu bambo ndi mayi Davison, malingana ndi malamulo a kampani ino, wantchito aliyense amayenera kunena chipembedzo chimene ali.”

Ifeyo tinkadziwa kuti kampaniyo inalibe lamulo lililonse lotere, koma zikuoneka kuti anthuwa anayamba kutikayikira chifukwa choti tinakana kusuta. Komabe, John anayankha kuti: “Ndife Mboni za Yehova.” Kenaka aliyense anangoti zii, osanena kanthu. Anthu onsewa anamenya nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse motero ankadana ndi a Mboni chifukwa choti anakana kulowerera nawo pankhondoyo. Ndiyetu kungoyambira pamenepa, anthuwo ankayesetsa zedi kutichitira zamtopola.

Poyamba bwana uja anakana kutipatsa firiji ndi chitofu, ngakhale kuti kampaniyo imayenera kutipatsa zinthu zonsezi. Zimenezi zinachititsa kuti zakudya zathu ziwonongeke, komanso kuti tiziphikira pa chitofu chinachake chowonongeka chomwe tinatola m’nkhalango. Kenaka anthu akumidzi ya m’derali anawaletsa kutigulitsa zinthu monga ndiwo zamasamba ndi zina zotere, moti tinkangodya ndiwo zilizonse za masamba zimene tapeza. Komanso anauza anthu kuti ndife akazitape moti anthu ankationetsetsa kuti aone ngati tikuphunzitsa munthu aliyense Baibulo. Kenaka ndinadwala malungo.

Ngakhale tinakumana ndi zinthu zonsezi, tinali ofunitsitsa zedi kukwaniritsa utumiki wathu. Ndiye tinapempha anyamata awiri a kumeneku, omwe ankagwira ntchito pamachekapo komanso omwe ankalankhula Chingelezi, kuti azitiphunzitsa chinenero cha dzikolo chotchedwa Chipijini cha ku Melaneziya. Ifeyo tinkawaphunzitsa Baibulo. Loweruka ndi Lamlungu tinkapita m’madera a kutalikutali ndipo tinkanamizira kuti tikukaona malo. M’njira, tinkalalikira mosaonetsera kwa anthu aliwonse amene tinkawapeza pa mudzi uliwonse, ndipo anyamata amene tinkaphunzira nawo Baibulo aja ankamasulira zimene tikunena. Tinawoloka mitsinje yokhala ndi madzi othamanga komanso ng’ona zazikulu kwadzaoneni, zomwe zinkawothera dzuwa m’mphepete mwa mitsinjeyo. Ng’onazo sizinkativuta ayi, kupatulapo nthawi imodzi yokha imene tinapulumukira m’kamwa mwambuzi.

Kupanga Zipangizo Zothandiza Polalikira

Titapeza njira zina zochitira utumiki, tinaganiza zolemba pa taipi uthenga wa m’Baibulo wosavuta kumva kuti tizigawira anthu achidwi. Ndiye ophunzira Baibulo athu a pamacheka aja anatithandiza kumasulira uthenga woyamba. Masiku ambiri tinkagona mochedwa chifukwa cholemba timapepalati ndipo tinalemba timapepala tambirimbiri toteleti n’kumagawira anthu m’midzi ndiponso anthu ogwira ntchito m’maboti.

Mu 1957, John Cutforth, yemwe anali woyang’anira woyendayenda wodziwa bwino ntchito yake, anadzatichezera ndi kutilimbikitsa kwambiri. * Anatiuza kuti kugwiritsa ntchito zithunzi kungathandize kwambiri pophunzitsa choonadi cha m’Baibulo anthu amene satha kuwerenga. Motero iyeyo ndi mwamuna wanga anakonza zithunzi zosavuta kujambula, pofuna kufotokoza ziphunzitso zikuluzikulu za m’Baibulo. Kenaka, tinakhala kwa maola ambirimbiri tikukopera zithunzi zimenezi m’makope. Wophunzira Baibulo aliyense tinam’patsa kope lakelake kuti aziphunzitsiranso anzake. Patsogolo pake, njira imeneyi inayamba kugwiritsidwa ntchito dziko lonselo.

Patatha zaka ziwiri ndi theka tili ku Waterfall Bay, zaka zimene tinayenera kugwira ntchito pakampaniyo zinatha komabe tinaloledwa kupitiriza kukhala m’dzikolo. Motero tinavomera atatipempha kuti tiyambe upainiya wapadera.

Kubwerera Ku Rabaul

Tinalowera cha kumpoto ku Rabaul, ndipo boti lathu linaima kwa usiku umodzi pafamu ina yomwe ankalimapo mtundu winawake wa kokonati ndi koko ku Wide Bay. Eni ake, anali bambo ndi mayi achikulire. Iwowa ankafuna kupuma pa ntchito yawoyo n’kubwerera ku Australia, motero anamuuza John kuti akhale bwana woyang’anira famuyo. Nkhaniyi inali yosangalatsa kwambiri komano titakambirana bwinobwino usiku umenewo, tinagwirizana zoti tisalole chifukwa choti sitinabwere ku New Guinea kudzafuna chuma ayi. Cholinga chathu chinali kuchita utumiki waupainiya basi. Motero mawa lake, tinauza banjalo kuti sititha kuyamba ntchito ndipo titatero tinakweranso boti lija.

Titafika ku Rabaul, tinapeza kagulu ka Mboni zochokera m’mayiko ena zimene zinasamukira m’derali. Anthu kumeneku ankachita chidwi zedi ndi uthenga wa Ufumu, ndipo tinayambitsa maphunziro ambiri a Baibulo. Panthawiyi misonkhano yachikhristu tinkachitira mu holo yalendi, ndipo nthawi zina tinkasonkhana mpaka anthu 150. Ambiri mwa anthuwa anayamba choonadi ndipo anathandiza kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’madera ena a dzikolo.​—Mateyo 24:14.

Tinafikanso ku mudzi wa Vunabal, womwe uli pa mtunda wa makilomita 50 kuchoka ku Rabaul. Kumeneku tinapezako kagulu ka anthu amene anachita chidwi zedi ndi choonadi cha m’Baibulo. Posakhalitsa nkhaniyi inafika kwa Mkatolika wina wotchuka m’derali. Iyeyu anakusa anzake n’kudzatisokoneza pa maphunziro athu a Baibulo a mlungu ndi mlungu n’kutithamangitsa m’mudzimo. Titamva kuti anthuwa akonza zodzativutitsa kwambiri mlungu wotsatira, tinapempha apolisi kuti adzatiteteze.

Tsiku limenelo msewu wonsewo unali Akatolika okhaokha, akutiwowoza kwambiri. Ambiri anali atakonzeka kuti adzatigende. Kumudziko kunali wansembe amene anali atasonkhanitsa anthu mazanamazana. Apolisi anatiuza kuti ndi ufulu wathu kuchita misonkhano, motero anakankha anthuwo kuti ife tidutse. Komano titangoyamba misonkhano yathu, wansembe uja anaphyephyerezera anthu aja kuti atikhaulitse. Apolisi analephera kuletsa chiguluchi, motero mkulu wa apolisiwo anatiuza kuti tichoke pamalopo n’kutiperekeza kumene kunali galimoto yathu.

Chigulucho chinatizungulira, n’kumatitukwana, kutilavulira ndi kutikungira zibakera, kwinaku wansembe uja ali manja pindire n’kumasekerera. Titathawa, mkulu wa apolisi uja anatiuza kuti sanakumanepo ndi zinthu zoopsa ngati zimenezi. Ngakhale kuti anthu ambiri ku Vunabal anachita mantha ndi zimenezi, wophunzira Baibulo wina analimba mtima n’kupitiriza kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Tikunena pano, anthu enanso ochuluka zedi ku New Britain achita chimodzimodzi.

Mwayi Wolalikira ku New Guinea

Mu November 1960, anatitumiza ku tauni ina yaikulu yotchedwa Madang, yomwe ili m’mphepete mwa nyanja, cha kumpoto kwa chilumba cha New Guinea, chomwe chili chilumba chachikulu kwambiri m’derali. Tili kuno, ine ndi John tinapatsidwa mwayi wosiyanasiyana wopeza ntchito. Kampani ina inandinyengerera kuti ndikhale woyang’anira sitolo yawo ya zovala. Ina inafuna kuti ndiziithandiza kukonza zovala. Azimayi ena ochokera kunja ankafuna kuti andithandize kukhazikitsa shopu yangayanga yosoka zovala. Koma chifukwa chokumbukira cholinga chathu, tinakana zinthu zonsezi mwaulemu.​—2 Timoteyo 2:4.

Dera la ku Madang linali lobala zipatso kwambiri, ndipo posakhalitsa kunapangika mpingo wolimba. Popita kolalikira m’midzi yakutali, nthawi zina tinkayenda wapansi, nthawi zina panjinga yamoto. Kumeneko tinkakhalako masiku angapo tikulalikira. M’njira, munali tinyumba topanda anthu ndipo ifeyo tinkagona m’tinyumbati paudzu womwe tinkamweta m’tchire. Tinkatenga zinthu zochepa chabe kuphatikizapo zakudya zam’chitini, mabisiketi, ndi maneti a udzudzu.

Paulendo wina woterewu, tinayendera gulu la anthu achidwi m’mudzi wa Talidig, womwe uli makilomita 50 kumpoto kwa Madang. Gululo litayamba kupita patsogolo, mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya kumeneko analiletsa kuphunzira Baibulo pasukulupo. Kenaka mphunzitsiyo anakanena mabodza kupolisi ndipo apolisiwo anaphwasula nyumba za anthu achidwiwo n’kuwathamangitsira m’thengo. Komabe, mfumu ya mudzi wina wapafupi inalola kuti gululi lizikhala m’mudzi mwakemo. Patsogolo pake mfumuyi inayamba choonadi ndipo m’mudzimo anamangamo Nyumba ya Ufumu yamakono.

Ntchito Yomasulira ndi Yoyendayenda

Patangotha zaka ziwiri zokha chifikireni ku New Britain mu 1956, John ndi ine anatiitana kuti tikamasulire mabuku osiyanasiyana ofotokoza Baibulo m’Chipijini cha ku Melaneziya. Ntchito imeneyi inapitirira kwa zaka zambiri. Kenaka mu 1970, anatiitana ku ofesi yanthambi ku Port Moresby, likulu la Papua New Guinea, kuti tikatumikire monga omasulira a nthawi zonse. Tinkaphunzitsanso ena chinenero cha m’dzikoli.

Mu 1975 tinabwerera ku New Britain kuti tikachite utumiki woyendayenda. Kwa zaka 13 zotsatira, tinayenda pafupifupi paliponse m’dzikoli pandege, paboti, pagalimoto, ndiponso wapansi. Nthawi zambiri tinkapulumuka lokumbakumba, monga mmene zinachitikira nthawi inayake imene ndailongosola kumayambiriro kwa nkhaniyi. Panthawiyi, woyendetsa ndege uja anakomoka tikuyandikira ku kabwalo kandege ka ku Kandrian ku New Britain chifukwa choti matenda enaake a m’mimba anam’tengetsa kwambiri. Ndegeyo inayamba kuuluka payokha, ndipo inali pendapenda kuzungulira dera la nkhalangolo. Apa n’kuti John akuyesa umu ndi umu kuti atsitsimutse woyendetsayo. Kenaka, iye anadzuka ndipo anayamba kuona pang’ono moti anatha kuteletsa ndegeyo movutikira. Kenaka anakomokanso.

Tinapeza Mwayi Winanso Wotumikira

Mu 1988 anatitumiza ku nthambi ku Port Moresby kuti tikathandize pa ntchito yomasulira yomwe inali kukulirakulira. Tinaliko anthu pafupifupi 50 ndipo tinkagwira ntchito panthambipo monga banja, ndipo tinkaphunzitsanso omasulira atsopano. Banja lililonse linali ndi chipinda chawochawo chokhalamo, chomwe chinali chaching’ono ndithu. John ndi ine tinaganiza zoti nthawi zonse chitseko chathu tizichisiya chili chotsegula pang’ono pofuna kuti anthu am’banjali ndiponso alendo azikhala omasuka kutiyendera nthawi iliyonse n’kumacheza nafe. Mwanjira imeneyi, tinayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu am’banja lathuli ndipo tinkakondana ndi kuthandizana nawo kwambiri.

Kenaka mu 1993, John anamwalira ndi matenda a mtima. Ndinamva ngati kuti mbali inayake ya thupi langa yafa. Tinali titakhala m’banja kwa zaka 38 ndipo tinakhala nthawi yonseyi tikuchita utumiki. Komabe, ndinkafunitsitsa kwambiri kupitiriza utumikiwu, mothandizidwa ndi Yehova. (2 Akorinto 4:7) Mpaka panopo khomo la chipinda changa limakhalabe lotsegula, ndipo achinyamata amabwerabe m’chipinda changa. Kucheza kolimbikitsa kumeneku kwandithandiza kukhala wosangalala.

M’chaka cha 2003 ananditumiza ku ofesi ya nthambi ya ku Sydney, m’dziko la Australia. Panopo ndili ndi zaka 77, ndipo ndimatumikira mu Dipatimenti Yomasulira komanso ndimalalikira mwakhama. Ndimasangalala kwambiri ndi anzanga ndiponso ana ndi zidzukulu zanga zauzimu.

Mpaka panopo chitseko cha chipinda changa ku Beteli chimakhala chotsegula, ndipo masiku ambiri ndimakhala ndi alendo. Ndipotu, ndikatseka chitseko changa, nthawi zambiri anthu amagogoda kuti adziwe ngati pali vuto linalake. Panthawi yonse imene ndili moyo ndikufuna ndikhalebe wofunitsitsa kukwaniritsa utumiki wanga ndi kutumikira Mulungu wanga, Yehova.​—2 Timoteyo 4:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Panthawiyi, dera la kum’mawa la chilumbachi linagawidwa pawiri; chakum’mwera kunali Papua ndipo chakumpoto kunali New Guinea. Masiku ano, dera la kumadzulo kwa chilumbachi limatchedwa Papua, ndipo ndi mbali ya dziko la Indonesia. Dera la kum’mawa limatchedwa Papua New Guinea.

^ ndime 19 Nkhani ya moyo wa John Cutforth mungaipeze mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya June 1, 1958, tsamba 333 mpaka 336.

[Mapu patsamba 18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

NEW GUINEA

AUSTRALIA

Sydney

INDONESIA

PAPUA NEW GUINEA

Talidig

Madang

PORT MORESBY

NEW BRITAIN

Rabaul

Vunabal

Wide Bay

Waterfall Bay

[Mawu a Chithunzi]

Map and globe: Based on NASA/​Visible Earth imagery

[Chithunzi patsamba 17]

Ndili ndi John pamsonkhano wa ku Lae, ku New Guinea, mu 1973​

[Chithunzi patsamba 20]

Ndili pa nthambi ku Papua New Guinea, mu 2002