Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Woipitsa Zinthu Waonekera Ng’amba!

Woipitsa Zinthu Waonekera Ng’amba!

Woipitsa Zinthu Waonekera Ng’amba!

M’ZAKA 100 zoyambirira, Ayuda ambiri anali kuyembekezera Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 6:14) Yesu atayamba utumiki wake, analimbikitsa ndi kuthandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu. Anachiritsa odwala, anadyetsa anjala, analamulira mphepo, ndipo anaukitsa akufa. (Mateyo 8:26; 14:14-21; 15:30, 31; Maliko 5:38-43) Anaphunzitsanso mawu a Yehova ndipo anauza anthu za chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 3:34) Ndipo iye anasonyeza mwa zimene ananena ndi kuchita kuti analidi Mesiya, amene adzamasule anthu kuuchimo ndi zotsatirapo zake zonse zoipa.

Atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda ndi amene anafunikira kukhala oyamba kulandira Yesu, kumumvetsera, ndi kukhala ofunitsitsa kutsatira malangizo ake. Koma sanatero. M’malo mwake anadana naye, anamuzunza, ndipo anakonza chiwembu choti amuphe.​—Maliko 14:1; 15:1-3, 10-15.

Moyenerera, Yesu anadzudzula amuna oipawo. (Mateyo 23:33-35) Komabe, anazindikira kuti panalinso wina amene ankachititsa kuti amunawo akhale ndi mitima yoipa. Anawauza kuti: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu. Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Ngakhale kuti Yesu m’mawu ake anasonyeza kuti anthu akhoza kuchita zoipa, iye anatchula amene anayambitsa zoipazo, kuti ndi Satana Mdyerekezi.

Mwa kunena kuti Satana “sanakhazikike m’choonadi,” Yesu anatanthauza kuti panthawi ina Satanayo anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu koma anapanduka. N’chifukwa chiyani Satana anapandukira Yehova? Chifukwa chakuti anali ndi mtima wodzikweza moti anayamba kufuna kuti anthu azimulambira m’malo molambira Mulungu yekha. *​—Mateyo 4:8, 9.

Kupanduka kwa Satana kunaonekera m’munda wa Edene pamene ananyenga Hava kuti adye chipatso choletsedwa. Satana anadzipanga kukhala ‘tate wa bodza’ pamene ananena bodza loyambirira ndiponso kuneneza Yehova. Mwa kupangitsa Adamu ndi Hava kusamvera Yehova, Satana anachititsa kuti uchimo uwalamulire. Ndipo chifukwa cha uchimowo, Adamu ndi Hava pamodzi ndi ana awo onse anayamba kufa. Motero, Satana anadzipanganso kukhala “wopha anthu” wankhanza koposa m’chilengedwe chonse.​—Genesis 3:1-6; Aroma 5:12.

Satana anasokoneza ngakhale angelo ena kumwamba, moti mpaka anawakopa kuti nawonso apanduke. (2 Petulo 2:4) Mofanana ndi Satana, angelo oipawa anayamba kuchita chidwi chosayenera ndi anthu. Koma mosiyana ndi Satanayo, angelowa anali kufuna kugonana ndi anthuwo. Ndipo zimenezi zinayambitsa mavuto aakulu kwambiri.

Dziko Linadzaza Zoipa

Baibulo limatiuza kuti: “Pamene anthu anayamba kuchuluka . . . ndi ana aakazi anawabadwira iwo, . . . ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” (Genesis 6:1, 2) Kodi “ana aamuna a Mulungu” amenewa anali ndani? Sanali anthu koma angelo. (Yobu 1:6; 2:1) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Mfundo imodzi n’njakuti anthu anakhala akukwatirana kwa zaka 1,500, motero panalibe chifukwa chotchulira za kukwatirana kwa anthu. Choncho, mwa kutchula za kukwatirana kwa “ana aamuna a Mulungu,” amene anabwera pa dziko lapansi n’kudzitengera okha “ana aakazi a anthu,” lembali likufotokoza chinthu chachilendo ndi chosayenera chimene sichinachitikepo n’kale lonse.

Ana amene anabadwa anasonyezanso kuti maukwatiwo anali achilendo ndi osayenera. Anawo anatchedwa Anefili ndipo anali zimphona. Analinso ankhanza kwambiri. Ndipotu, mawu akuti “Anefili” amatanthauza kuti “Ogwetsa,” kapena “anthu okonda kugwetsa anzawo.” Zimphonazi anazifotokoza kuti zinali “anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.”​—Genesis 6:4.

Anefili pamodzi ndi abambo awo anachita zinthu zoipa kwambiri zimene sizinachitikepo n’kale lonse. Lemba la Genesis 6:11 limati: “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu . . . ndipo linadzala ndi chiwawa.” Ndithudi, anthu anatengera khalidwe lachiwawa ndi loipa la Anefili ndi abambo awo.

Kodi Anefili pamodzi ndi abambo awowo anatani kuti anthu ayambe kutengera khalidwe lawo loipa? Iwo anakopa anthu pogwiritsa ntchito chibadwa chimene anthuwo ali nacho chokonda kuchita zoipa. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? “Anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.” Pamapeto pake, Yehova anawononga dzikolo ndi Chigumula ndipo anangopulumutsa Nowa ndi banja lake. (Genesis 6:5, 12-22) Koma angelo amene anabwera pa dziko lapansi anabwerera kumwamba ndipo sanakhalenso ndi ulemu umene anali nawo kale. Pokhala ziwanda zoipa kwambiri, anapitiriza kutsutsa Mulungu ndi banja lake lolungama la angelo okhulupirika. Zikuoneka kuti kuyambira nthawi imeneyo, Mulungu analetsa mizimu yoipayi kuvalanso matupi a anthu. (Yuda 6) Koma yapitirizabe kulamulira zinthu zambiri zimene anthu amachita.

Woipayo Waonekera Ng’amba!

Lemba la 1 Yohane 5:19 limasonyeza mphamvu zimene Satana ali nazo, mwa kunena kuti: “Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu, koma dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Mdyerekezi akupangitsa anthu kulowa m’mavuto owonjezereka. Ndipo iye watsimikiza kwambiri kuchita zoipa kuposa n’kale lonse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iyeyo ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba, Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa mu 1914. Ponena za kuchotsedwa kumeneku, Baibulo linaneneratu kuti: “Tsoka dziko lapansi . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ali ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:7-12) Kodi Satana akulamulira motani anthu masiku ano?

Satana akutero makamaka mwa kulimbikitsa maganizo enaake amene amalamulira zochita za anthu. N’chifukwa chake lemba la Aefeso 2:2 limati, Mdyerekezi ndiye “wolamulira wa mphamvu ya mumpweya, mzimu [kapena kuti maganizo] umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” M’malo molimbikitsa anthu kuopa Mulungu ndi kuchita zinthu zabwino, “mpweya” woipawu umachititsa anthu kupandukira Mulungu ndi kuswa malamulo ake. Motero, Satana ndi ziwanda zake amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zoipa kwambiri.

‘Tchinjirizani Mtima Wanu’

Chimodzi mwa zinthu zimene “mpweya” umenewu umaonekeramo ndi khalidwe lokonda zinthu zolaula. Khalidweli limalimbikitsa anthu kukhala ndi zilakolako zoipa zogonana ndipo limachititsa kuti zinthu zoipazi zioneke monga n’zosangalatsa. (1 Atesalonika 4:3-5) Zina mwa zinthu zimene zithunzi zolaula zimaonetsa kukhala monga zosangalatsa ndizo kugwirira achikulire ndi ana omwe, kugona nyama, kuchitira anthu nkhanza, ndiponso anthu angapo kugwirira munthu mmodzi. Munthu akamawerenga kapena kuonera zinthu zolaula, ngakhale zimene amati si zoipa kwenikweni, amayamba kuzikonda kwambiri mpaka n’kukhala ndi chizolowezi choonera kapena kuwerenga zinthuzi nthawi zonse. * Khalidwe loipali limawononga ubwenzi umene munthu ali nawo ndi anzake ndiponso umene ali nawo ndi Mulungu. Ziwanda zinayamba kukhala ndi zilakolako zoipa zogonana m’nthawi ya Nowa, Chigumula chisanachitike. Ndipo ziwandazo ndi zimene zimalimbikitsa kukonda zinthu zolaula. Motero zinthu zolaula zimaonetsa maganizo oipa a ziwanda.

Pazifukwa zomveka, munthu wanzeru Solomo analangiza kuti: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Kunena zoona, kutchinjiriza mtima wanu ku msampha wa kuonera zinthu zolaula kungafune kuti musinthe zimene mukuonera pa TV kapena kuzimitsa kompyuta ikamaonetsa zithunzi zolaula. N’kofunika kuti muchite zimenezi mwamsanga ndiponso motsimikiza. Dziyerekezeni kuti ndinu msilikali yemwe akudziteteza ku muvi umene walunjikitsidwa pa mtima wake. Satana amafuna kuipitsa mtima wanu wophiphiritsa, kutanthauza zimene munthu amakonda ndi kulakalaka.

Muyenera kutchinjirizanso mtima wanu kuti usakonde chiwawa chifukwa chakuti Mdyerekezi akudziwa kuti Yehova ‘amada okonda chiwawa.’ (Salmo 11:5) Satana safunikira kukupangitsani kukhala munthu wochita zachiwawa kuti Mulungu adane nanu, koma amangofunika kukulimbikitsani kukhala ndi mtima wokonda chiwawacho. Choncho n’zomveka kuti chiwawa, chimene nthawi zambiri chimakhudza zamatsenga, chimaonekeraonekera pa TV, m’mabuku, m’magazini, ndipo ngakhale kumveka pa wailesi. Anefili anafa kalekale koma makhalidwe awo adakalipo ndipo ndi ofala kwambiri lerolino. Kodi zosangalatsa zimene mumakonda zimasonyeza kuti mumapewa machenjera a Satana?​—2 Akorinto 2:11.

Zimene Tingachite Kuti Tipewe Mphamvu Yoipa ya Satana

Satana ndi ziwanda zake angaoneke ovuta kwambiri kulimbana nawo. Baibulo limanena kuti anthu amene akuyesetsa kusangalatsa Mulungu ‘akulimbana ndi . . . makamu a mizimu yoipa,’ kuwonjezera pa kulimbana ndi kupanda ungwiro kwawo. Ngati tikufuna kupambana nkhondoyi ndi kuyanjidwa ndi Mulungu, tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Mulungu amatipatsa.​—Aefeso 6:12; Aroma 7:21-25.

Chimodzi mwa zinthu zimene Mulungu watipatsazi ndi mzimu wake woyera, umene ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse. Mtumwi Paulo analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.” (1 Akorinto 2:12) Anthu amene mzimu wa Mulungu umawatsogolera amaphunzira kukonda zimene Mulungu amakonda ndi kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Amosi 5:15) Kodi munthu angatani kuti alandire mzimu woyera? Angalandire mzimuwu makamaka mwa kupemphera, kuphunzira Baibulo, limene linauziridwa ndi mzimu woyera, ndiponso mwa kusonkhana ndi anthu amene amakondadi Mulungu.​—Luka 11:13; 2 Timoteyo 3:16; Aheberi 10:24, 25.

Mukamagwiritsa ntchito zinthu zimene Mulungu watipatsazi, mumayamba kuvala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” Zidazi ndi zokhazo zimene zingakutetezeni ku “machenjera a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11-18) Masiku ano, kuposa n’kale lonse, tifunika kugwiritsa ntchito bwino kwambiri zinthu zimene Mulungu watipatsazi. N’chifukwa chiyani tikutero?

Zoipa Zitha Posachedwapa!

Wamasalmo anati: “Chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzawonongeke kosatha.” (Salmo 92:7) Ndithudi, mofanana ndi nthawi ya Nowa, kuchuluka kwa zoipa masiku ano ndi umboni woti chiweruzo cha Mulungu chayandikira. Sadzaweruza anthu oipa okha komanso adzaweruza Satana ndi ziwanda zake, amene asanawonongedwe choyamba adzaponyedwa m’phompho, kutanthauza kuti sadzatha kuchita chilichonse. (2 Timoteyo 3:1-5; Chivumbulutso 20:1-3, 7-10) Kodi ndani amene adzapereke chiweruzo chimenechi? Palibenso wina kusiyapo Yesu Khristu, amene timawerenga za iye kuti: “Mwana wa Mulungu anaonekera, kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”​—1 Yohane 3:8.

Kodi mumalakalaka zoipa zitatha? Ngati n’choncho, malonjezo a m’Baibulo angakulimbikitseni. Ndipotu ndi buku lokhali limene limanena mosapita m’mbali kuti Satana ndiye anayambitsa zoipa, ndiponso limene limasonyeza mmene iye adzawonongedwera limodzi ndi zochita zake zonse zoipa. Tikukulimbikitsani kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zolondola n’cholinga chakuti panopa mudziteteze ku mphamvu yoipa ya Satana ndiponso kuti mukhale ndi chiyembekezo chodzakhala m’dziko lopanda zoipa.​—Salmo 37:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Dzina lenileni la mngelo amene anakhala Satana silikudziwika. Mayina akuti “Satana” ndi “Mdyerekezi” amatanthauza “Wotsutsa” ndi “Woneneza.” Zimene Satana anachita zimafananako ndi zomwe mfumu yakale ya Turo inachita. (Ezekieli 28:12-19) Poyamba onse anali angwiro m’zochita zawo koma anayamba kudzikuza.

^ ndime 17 Onani nkhani yonena za zithunzi zolaula imene ili mu Galamukani! ya August 8, 2003, masamba 19 mpaka 26, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Nthano Zokhala ndi Mfundo Zina Zoona

Nkhani zonena za anthu okhala ngati milungu, zimphona, ndiponso chigumula chachikulu zimasimbidwa m’nthano zakale padziko lonse. Mwachitsanzo, nthano ya Ababulo yonena za Gilgamesh imatchula za chigumula, chombo, ndiponso anthu amene anapulumuka. Imafotokoza Gilgamesh kuti anali wokonda zachiwerewere, wankhanza, ndiponso wokhala ngati mulungu. Nthano ya a Aztec imasimba za dziko lakale la zimphona ndiponso chigumula chachikulu. Nthano ya ku dziko la Norway imakamba za mtundu wa zimphona ndi munthu wina wanzeru wotchedwa Bergelmir, yemwe anapanga bwato lalikulu momwe iye ndi mkazi wake anapulumukiramo. Zimene nthano zonsezi zimanena zimatsimikizira mawu a m’Baibulo akuti anthu onse anachokera kwa anthu amene anapulumuka chigumula chimene chinawononga dziko loipa lakale.

[Chithunzi]

Nthano ya Gilgamesh yolembedwa pa mwala

[Mawu a Chithunzi]

The University Museum, University of Pennsylvania (neg. # 22065)

[Chithunzi patsamba 5]

Anthu masiku ano ali ndi makhalidwe onga a Anefili

[Chithunzi patsamba 7]

Kudziwa Baibulo molondola kumatithandiza kupewa zinthu zoipa