Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ernst Glück Anagwira Ntchito Yaikulu Zedi

Ernst Glück Anagwira Ntchito Yaikulu Zedi

Ernst Glück Anagwira Ntchito Yaikulu Zedi

ZAKA zoposa 300 zapitazo, Ernst Glück anayamba kugwira ntchito imene anthu ambiri m’mbuyo monse ankaizemba. Iye anaganiza zomasulira Baibulo kuti likhale m’chinenero chimene ngakhale iyeyo sankachidziwa.

Glück anabadwa cha m’ma 1654 m’tauni yaing’ono ya Wettin, kufupi ndi mzinda wa Halle, m’dziko la Germany. Bambo ake anali m’busa wa mpingo wa Lutheran, motero Ernst anakulira m’banja lokonda za mawu a Mulungu. Ali ndi zaka 21, anamaliza maphunziro ake a za mawu a Mulungu ku Germany n’kusamukira m’dziko limene masiku ano limatchedwa Latvia. Panthawiyo anthu ambiri kumeneko anali osaphunzira, ndipo panali mabuku ochepa chabe m’chinenero chawo. Glück analemba kuti: “Panthawi imene ndinafika m’dziko limeneli ndili wachinyamata, vuto loyamba limene ndinaona linali loti matchalitchi a ku Latvia analibe Baibulo . . . Zimenezi zinandichititsa kuti ndilumbire kwa Mulungu kuti ndiphunzira chinenero chimenechi ndi kuchidziwa chonse bwinobwino.” Iyeyu anali wofunitsitsa kuwakonzera anthu a ku Latvia, Baibulo la chinenero chawo.

Kukonzekera Kulimasulira

Dziko la Latvia linkadziwika kuti Livonia ndipo linkalamulidwa ndi dziko la Sweden. Panthawiyi Johannes Fischer ndiye anali nthumwi ya ku Livonia ya mfumu ya Sweden. Nthumwiyi inkafuna kupititsa patsogolo maphunziro m’dzikolo komanso kupeza ndalama. Glück analankhula nayo zoti akufuna kumasulira Baibulo m’Chilativiya. Fischer anali ndi fakitale yosindikiza mabuku mumzinda wa Riga, likulu la dzikolo. Iye anadziwa kuti akasindikiza Baibulo m’chinenerocho ndiye kuti apha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi chifukwa alimbikitsa ntchito yophunzitsa anthu komanso n’kupezapo kangachepe. Nthumwiyi inapempha Mfumu Charles wachileveni, yemwe anali mfumu ya Sweden, kuti avomereze ntchito yomasulirayi. Mfumuyo inavomereza ndipo inati ipereka ndalama zothandizira pantchitoyi. Motero, pa August 31, 1681, mfumuyo inasayinira zoti ntchito yomasulirayi iyambe.

Panthawiyi n’kuti Glück ali jijirijijiri kukonzekera. Poti anali Mjeremani, akanatha kungomasulira Baibulo la Chijeremani la Martin Luther kuti likhale m’Chilativiya. Koma Glück ankafuna kuti Baibulo limene amasulirelo likhale mbambande, motero anaona kuti m’pofunika kumasulira Chiheberi ndiponso Chigiriki choyambirira. Glück sankadziwa bwinobwino zinenero za m’Baibulozi, motero anapita ku Hamburg, m’dziko la Germany, kuti akaphunzire Chiheberi ndi Chigiriki. Ali kumeneko, n’kutheka kuti m’busa wina wa ku Livonia, dzina lake Jānis Reiters anamuthandiza kumvetsa Chilativiya komanso Chigiriki cha m’Baibulo.

Zaka Zambiri Akugwira Ntchito Ndiponso Akudikirira

Atamaliza kuphunzira zinenerozi mu 1680, Glück anabwerera ku Latvia n’kukayamba ntchito yaubusa. Posakhalitsa anayamba ntchito yake yomasulira. Mu 1683, iye anatumizidwa ku parishi yaikulu ya ku Alūksne kuti akakhale m’busa kumeneko. Amenewa ndiwo malo amene anadziwika kuti anachitirako ntchito yake yomasulira.

Panthawi imeneyo, m’Chilativiya munalibe mawu ambiri a zinthu ndiponso mfundo zosiyanasiyana zopezeka m’Baibulo. Motero mwina ndi mwina Glück anangoikamo mawu a Chijeremani. Koma anayesetsa ndithu kuti Mawu a Mulungu akhale m’chinenerochi, ndipo akatswiri amavomereza kuti anamasulira Baibulolo mwambambande. Mwina ndi mwina Glück anangoikamo mawu amene anangowapeka yekha ndipo mawu ambiri ndithu oterewa amagwiritsidwa ntchito panopo m’chinenerochi. Mawu ake ndi mawu monga akuti “chitsanzo,” “madyerero,” “chimphona,” “kuchita ukazitape,” ndi “kuchitira umboni.”

Johannes Fischer, yemwe anali nthumwi ya mfumu ya ku Sweden uja, ankaiuza mfumuyo za mmene ntchito yomasulirayo inali kuyendera, ndipo makalata amene ankalemberana amasonyeza kuti pofika chaka cha 1683, Glück anali atamasulira Malemba Achigiriki Achikristu. Iye anamaliza kumasulira Baibulo lonse mu 1689, ndipo analimaliza m’zaka eyiti zokha. * Zinatenga nthawi kuti Baibuloli lifalitsidwe, koma mu 1694 iye anakwanitsa cholinga chake pamene boma linavomereza kuti Baibuloli liyambe kugulitsidwa kwa anthu.

Akatswiri ena a maphunziro a mbiri yakale amakayikira kuti Glück anamasulira yekha Baibuloli. N’zosachita kufunsa kuti iye ankaona zina ndi zina m’Baibulo la Luther ndipo zinthu zinanso anazitenga m’mbali zina za Baibulo zimene zinali zitamasuliridwa kale m’Chilativiya. Komabe imeneyi inali mbali yochepa kwambiri ya Baibulo lakeli. Kodi panali omasulira ena amene anam’thandiza? Glück anali ndi munthu wom’thandiza pantchitoyi ndipo ena anam’thandiza kupeza zinthu zofunika kukonza m’Baibulolo. Koma zikuoneka kuti anthuwa sanam’thandize kumasulira kwenikweniko ayi. Motero zikuoneka kuti Glück anamasulira yekha Baibulolo.

Baibulo la Glück linathandiza kwambiri kupititsa patsogolo Chilativiya cholembedwa, ndiponso linathandiza m’njira inanso yofunika kuposa pamenepa. Njira yake inali yakuti linathandiza kuti anthu a ku Latvia ayambe kuwerenga Mawu a Mulungu m’chinenero chawochawo n’kuyamba kudziwa ziphunzitso zake zopatsa moyo. Ndipotu mpaka panopa anthuwa sanaiwalebe zimene Ernst Glück anawachitira. Kwa zaka zoposa 300, anthu a ku Alūksne akhala akusamalira mitengo iwiri ya misolo yotchedwa Glika ozoli, kutanthauza kuti misolo ya Glück. Glück anadzala mitengoyi pofuna kuti ikhale chikumbutso cha Baibulo limene anamasulirali. Ku Alūksne kuli nyumba inayake yaing’ono yosungiramo zinthu zakale zochititsa chidwi imene muli Mabaibulo osiyanasiyana, ndipo limodzi mwa Mabaibulo amenewa ndi limodzi mwa Mabaibulo a Glück oyambirira kusindikizidwa. Ndipo pachizindikiro cha Alūksne anajambulapo Baibulo n’kulembapo kuti 1689, chaka chimene Glück anamaliza ntchito yake.

Ntchito Imene Anachita Patsogolo Pake

Atafika ku Latvia, Glück anayamba kuphunzira Chirasha. M’chaka cha 1699 iye analemba kuti akufuna kukwaniritsa cholinga chake chinanso, choti amasulire Baibulo m’Chirasha. M’kalata yake ya mu 1702, iye analembamo kuti wayamba kukonza zina ndi zina m’Baibulo lake la m’Chilativiya lija. Komano apa n’kuti ntchito yomasulira Baibulo itayamba kuvuta chifukwa choti ku Latvia kunayambika nkhondo, ngakhale kuti kunali mtendere kwa zaka zambiri. M’chaka cha 1702 magulu a asilikali a ku Russia anagonjetsa asilikali a Sweden n’kulanda Alūksne. Motero Glück ndi banja lake anawatulutsa m’dzikoli n’kuwapititsa ku Russia. * Chifukwa cha chipwirikiti cha panthawiyi Glück anataya mapepala a Baibulo lomwe amakonza lija komanso a Baibulo la Chirasha limene amayamba kumasulira. Iyeyu anamwalira mu 1705, mumzinda wa Moscow.

Mapepala amene anatayika aja anali ofunika kwambiri. Koma mpaka panopo aliyense amene amawerenga Baibulo m’Chilativiya amapindula ndithu ndi Baibulo loyamba limene Glück anamasulira.

Ernst Glück ndi mmodzi chabe mwa anthu ambiri amene anachita ntchito yaikulu kwadzaoneni, yomasulira Baibulo m’zinenero za anthu wamba. Motero, pafupifupi anthu azinenero zonse padziko pano angathe kuwerenga Mawu a Mulungu n’kumwa madzi ake a choonadi amtengo wapatali. Inde, pogwiritsira ntchito Mabaibulo a zinenero zosiyanasiyana zokwana 2,000, Yehova akupitiriza kudzidziwikitsa kwa anthu padziko lonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Iyi inali nthawi yochepa zedi poyerekezera ndi Baibulo la Chingelezi la Authorized Version, kapena kuti King James Version lomwe linamasuliridwa ndi akatswiri 47 koma anatha zaka 7 kuti alimalize, mu 1611.

^ ndime 14 Patsogolo pake, mwana yemwe Glück anangom’tenga n’kumulera anadzakwatiwa ndi mfumu ya ku Russia, yotchedwa Peter Wamkulu. Mu 1725, Peter anamwalira ndipo mkazi wakeyo anakhala mfumukazi Catherine Woyamba, ya dziko la Russia.

[Chithunzi patsamba 13]

Baibulo la Glück

[Chithunzi patsamba 14]

Mboni za Yehova zikuphunzitsa anthu Baibulo m’tauni imene Glück anamasulira Baibulo lake