Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha

Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha

Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha

KWINA kulikonse anthu amatsatira mfundo zinazake za makhalidwe abwino. Kodi simukuvomereza kuti anthu padziko lonse amasangalala ndi munthu yemwe ndi woona mtima, wokoma mtima, wachifundo, ndiponso woganizira ena?

Ndani Anayambitsa Makhalidwewa?

Saulo anali wophunzira kwambiri, ndipo ankakhala pakati pa Ayuda, Agiriki, ndi Aroma. Mitundu yonseyi inali ndi zikhalidwe zawo. Kuwonjezera pa miyambo yambirimbiri ndiponso zikhalidwe zosiyanasiyana za mitunduyi, Saulo anazindikiranso kuti anthu onse amakhala ndi chibadwa chofuna kutsatira makhalidwe enaake abwino. Chibadwa chimenechi chimatchedwa chikumbumtima. Motero Saulo atakhala mtumwi Paulo, analemba kuti: “Nthawi zonse anthu a mitundu amene alibe chilamulo akamachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo, anthu amenewa, ngakhale kuti alibe chilamulo, ali chilamulo kwa iwo eni. Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’chilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo, pamene chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi nawo.”​—Aroma 2:14, 15.

Ndiyeno, kodi n’kokwanira kuti tizingochita zinthu “mwachibadwa” basi posiyanitsa chabwino ndi choipa? Muyenera kuti mukudziwa za anthu ambirimbiri m’dzikoli amene agwera m’mavuto chifukwa chongochita zinthu mwachibadwa. Zimenezi zikusonyeza kuti kudalira chibadwa chathu chokha pochita zinthu si kokwanira. Ambiri amavomereza kuti Mlengi wathu ndi amene ayenera kutipatsa mfundo zodalirika zosasinthasintha. Dr. Carl Jung analemba m’buku lake (The Undiscovered Self) kuti: “Munthu amene sadalira Mulungu sangathe kupewa ziyeso zovuta kwambiri zokhudza makhalidwe oipa a m’dzikoli.”

Mawu amenewatu akugwirizana ndi zomwe mneneri wina wakale analemba. Iye anati: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ndipotu Mlengi wathu akuti: ‘Ndikuphunzitsa kupindula, ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’​—Yesaya 48:17.

Kumene Tingapeze Mfundo Zodalirika

Mawu amene agwidwa pamwambawa amapezeka m’buku lofala kwambiri la makhalidwe abwino, lomwe ndi Malemba Oyera. Anthu ambiri zedi padziko lonse, ngakhale amene si Akhristu ndiponso amene sapembedza, akhala akudalira Malemba kuti apeze nzeru pankhani zosiyanasiyana. Wolemba ndakatulo wina wa ku Germany, dzina lake Johann Wolfgang von Goethe, analemba kuti: “[Baibulo] ndimalipatsa ulemu kwambiri, chifukwa choti pafupifupi mfundo zanga zonse zamakhalidwe abwino n’zochokera m’Baibulo.” Akuti mtsogoleri wa Chihindu, Mohandas Gandhi anati: “Yesetsani mulimonse mmene mungathere kumwa madzi a m’kasupe amene anakupatsani mu ulaliki wa paphiri [wa Yesu womwe uli m’Baibulo] . . . Chifukwa choti zimene anaphunzitsa pa ulaliki umenewu n’zothandiza tonsefe.”

Mtumwi Paulo, amene mawu ake tawatchulapo m’nkhani ino, ananena za kufunika kwa Malemba Oyera pankhani ya mfundo zodalirika. Iye anati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Koma kodi ndi mmene zililidi?

Bwanji osaona nokha? Taonani mfundo zimene zatchulidwa pa tsamba lotsatirali. Onani makhalidwe abwino amene mfundozo zikulimbikitsa. Sinkhasinkhani mmene mfundo zimene zili m’nkhani ino zingakuthandizireni pa moyo wanu ndiponso ubwenzi wanu ndi anthu ena.

Kodi Muchitapo Kanthu Kuti Mupindule?

Mfundo zimene tatchulazi ndi zochepa chabe pamalangizo othandiza opezeka m’Malemba Oyera. Kuphatikiza pa mfundo zimenezi, Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zambiri zotichenjeza kuti tisamakhale ndi maganizo oipa, kunena mawu oipa, ndi kuchita zinthu zimene zingavulaze moyo wathu.​—Miyambo 6:16-19.

Inde, Baibulo limaphunzitsa zinthu zimene anthu ochuluka akuzisowa kwambiri. Zinthu zake ndizo malangizo amene amathandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri. Anthu amene amavomereza ndi kutsatira ziphunzitso zimenezi amasintha kwambiri. Maganizo awo amasintha n’kukhala abwino. (Aefeso 4:23, 24) Amayamba kukhala ndi zolinga zabwino. Kuphunzira mfundo za Mulungu zolembedwa m’Baibulo kwathandiza anthu ambiri kuthetsa maganizo oipa monga kusankhana mitundu, kusala anthu ena, ndiponso chidani. (Aheberi 4:12) Malemba ndiponso makhalidwe amene Malembawo amalimbikitsa athandiza anthu kusiya makhalidwe osiyanasiyana achiwawa n’kukhala anthu amtendere.

Inde, makhalidwe a m’Baibulo athandiza anthu mamiliyoni ambiri kuthetsa zizolowezi zimene akhala nazo kwa nthawi yaitali monga zizolowezi zimene zasokoneza moyo wa ena. (1 Akorinto 6:9-11) Ziphunzitso za m’Baibulo zakhala zikuthandiza anthu amenewa kusintha m’njira zinanso, osati zizolowezi zawo chabe. Zasintha mitima yawo, zimene amalakalaka, ndiponso mabanja awo. Ngakhale kuti dzikoli likuipiraipira kwambiri, pali anthu ena padziko lonse amene akusintha khalidwe lawo kuti likhale labwino. Ndipotu zimenezi zipitirirabe chifukwa Baibulo limati: “Udzu unyala, duwa lifota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.”​—Yesaya 40:8.

Komabe, kodi inuyo panokha mupindulapo chilichonse pa “mawu a Mulungu wathu”? Mboni za Yehova zingasangalale kwambiri kukusonyezani zimene mungachite kuti mfundo za m’Baibulo zikupindulitseni. Kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zimenezi kungachititse kuti Mulungu akukondeni panopa ndiponso kuti mudzakhale ndi moyo wosatha, woyendera mfundo zodalirika, osati zosinthasintha.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 6, 7]

MFUNDO ZODALIRIKA NDIPONSO ZOSASINTHASINTHA

Lamulo la Chikhalidwe. “Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.”​—Mateyo 7:12.

Kondani anansi. “Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyo 22:39) “Chikondi sichikuchititsa zoipa kwa mnansi wako; chotero chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.”​—Aroma 13:10.

Lemekezani ena. “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.”​—Aroma 12:10.

Khalani amtendere. “Sungani mtendere pakati panu.” (Maliko 9:50) “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) “Tiyeni titsatire zinthu zodzetsa mtendere.”​—Aroma 14:19.

Khalani okhululuka. “Mutikhululukire zolakwa zathu, pakuti ifenso takhululukira amene atilakwira.” (Mateyo 6:12) “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”​—Aefeso 4:32.

Khalani okhulupirika. “Imwa madzi a m’chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m’kasupe mwako . . . Ukondwere ndi mkazi wokula naye . . . Mawere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere, ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?” (Miyambo 5:15-20) “Munthu wokhulupirika m’chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu, ndipo munthu wosalungama m’chaching’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) “Komanso pamenepa, chofunika kwa mdindo ndicho kukhala wokhulupirika.”​—1 Akorinto 4:2.

Khalani oona mtima. “Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?” (Mika 6:11) “Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

Pewani chinyengo ndiponso kukondera. “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata.” (Amosi 5:15) “Nena choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m’zipata zanu.” (Zekariya 8:16) “Popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake, chifukwa ndife ziwalo kwa wina ndi mnzake.”​—Aefeso 4:25.

Limbikirani ntchito. “Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.” (Miyambo 22:29) “Musakhale aulesi m’machitidwe anu.” (Aroma 12:11) “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.”​—Akolose 3:23.

Khalani ofatsa ndi achifundo. “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”​—Akolose 3:12.

Gonjetsani choipa pochita chabwino. “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyo 5:44) “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”​—Aroma 12:21.

Muzikonda kwambiri Mulungu. “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba.”​—Mateyo 22:37, 38.

[Zithunzi]

Kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo kungatithandize kuti tikhale ndi mabanja abwino, tizigwirizana ndi anthu a m’banja mwathu, ndiponso kuti tizisangalala ndi anzathu