Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi njoka imene inalankhula ndi Hava inali ndi miyendo?

Pa Genesis 3:14, Yehova Mulungu analankhula ndi njoka imene inanyenga Hava m’munda wa Edene. Mulungu anati: “Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako.” Baibulo silinena kuti njoka imene inagwiritsidwa ntchito poyesa Hava poyamba inali ndi miyendo. Ngakhale kuti mawu a pa Genesis 3:14 angachititse ena kuganiza choncho, sikuti tinganene kuti temberero limeneli lisanaperekedwe, njoka zinali ndi miyendo. N’chifukwa chiyani tikutero?

Tikutero makamaka chifukwa chakuti temberero limenelo linali kupita kwa Satana, mzimu wosaoneka umene unagwiritsa ntchito njoka yosadziwa chilichonse. Baibulo limati Satana ndi “tate wake wa bodza” ndiponso “njoka yakale ija.” Zikuoneka kuti mayina amenewa akunena zimene Satana anachita pogwiritsa ntchito njoka yeniyeni polankhula ndi Hava kuti amunyengerere kuphwanya lamulo la Mulungu.​—Yohane 8:44; Chivumbulutso 20:2.

Njoka zinalengedwa ndi Mulungu, ndipo Adamu ayenera kuti ndiye anazipatsa dzina, Satana asanachite zachinyengozo. Njoka yosadziwa chilichonse imene inalankhula ndi Hava inalibe mlandu. Sinadziwe kuti Satana akuigwiritsa ntchito, ndipo sinadziwe chilichonse za chiweruzo chimene Mulungu anapereka kwa opandukawo.

Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu anatemberera njokayo? Zimene njoka imachita malinga ndi chilengedwe chake, monga kuyenda ndi pamimba ndiponso kutulutsa lilime ngati kuti ikudya fumbi, zimaimira bwino lomwe kutembereredwa ndi kutsitsidwa kwa Satana. Poyamba Satanayo anali mngelo wapamwamba wa Mulungu, koma kenako anatsitsidwa kukhala mu mkhalidwe wonyozeka umene Baibulo limatcha Tatalasi.​—2 Petulo 2:4.

Ndiponso, mofanana ndi mmene njoka imalumira chitende cha munthu, Satana mumkhalidwe wake wonyozeka ‘adzalalira chitende’ cha “mbewu” ya Mulungu. (Genesis 3:15) Mbali yoyamba ya mbewuyo ndi Yesu Khristu, amene atumiki a Satana anamuvutitsa kwakanthawi. Koma Khristu limodzi ndi anzake odzozedwa, adzatswanyiratu mutu wa njoka yophiphiritsayo. (Aroma 16:20) Choncho, Mulungu potemberera njoka, analosera za kutsitsidwa kwa Satana Mdyerekezi, “njoka yakale ija,” ndi kuwonongedwa kwake.