Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsankho Lingathe Bwanji?

Kodi Tsankho Lingathe Bwanji?

Kodi Tsankho Lingathe Bwanji?

KU Spain woimbira mpira anaimitsa masewera a mpira. Anatero chifukwa chakuti anthu ambiri oonera mpirawo anatukwana wosewera mpira wa ku Cameroon mpaka wosewerayo anafuna kutuluka mu mpira. Anthu akuda, amwenye, ndi anthu a kumayiko a kum’mwera kwa America akhala akumenyedwa ku Russia. Mwachitsanzo mu 2004, mchitidwe umenewu womenya anthu amitundu ina unawonjezeka ndi 55 peresenti moti kunali ziwawa 394 mu 2005. Pakafukufuku wina ku Britain, munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse achimwenye ndi achikuda akuti anachotsedwa ntchito chifukwa cha tsankho. Zimenezi zikungosonyeza kuti vutoli lafala pa dziko lonse.

Tsankho limachitika m’njira zosiyanasiyana, kuyambira pa kungonyozana mpaka kufika pokhazikitsa lamulo lopululutsa fuko lonse la anthu. Kodi muzu wa tsankho n’chiyani? Kodi tingalipewe bwanji? Kodi tingayembekezere kuti tsiku lina mitundu yonse ya anthu idzakhala pamodzi mwamtendere? Baibulo lingatithandize kumvetsa nkhani imeneyi.

Chidani ndi Kuponderezana

Baibulo limati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Choncho anthu ena amasangalala kuzunza anzawo. Baibulo limanenanso kuti: “Taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu.”​—Mlaliki 4:1.

Baibulo limasonyezanso kuti tsankho linayamba kalekale. Mwachitsanzo, zaka zoposa 3,700 zapitazo Farao anaitana Yakobo Mheberi ndi banja lake kuti akakhale ku Iguputo. Koma kenako kunabwera Farao wina amene anachita mantha ndi alendo ambirimbiri amenewa. Choncho, Baibulo limati: “Ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, achuluka, natiposa mphamvu. Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke. . . . Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu awo.” (Eksodo 1:9-11) Aiguputowo mpaka analamula kuti ana onse aamuna obadwa kwa mbumba ya Yakobo aphedwe.​—Eksodo 1:15, 16.

Kodi Muzu wa Tsankho N’chiyani?

Zipembedzo za dzikoli sizikuthandiza kuthetsa tsankho. Ngakhale kuti anthu ena alimba mtima ndi kutsutsa kuponderezana, zipembedzo nthawi zambiri zimachirikiza anthu opondereza anzawo. Umu ndi mmene zinalili ku United States kumene malamulo ankalola kupondereza anthu akuda ndi kuwapha. Kunalinso malamulo oletsa anthu akuda ndi azungu kukwatirana omwe anatha mu 1967. Nakonso ku South Africa kunali tsankho ndipo atsamunda anateteza ulamuliro wawo ndi malamulo amene ena a iwo analetsa ukwati wa anthu akuda ndi azungu. Kumayiko onsewa anthu amene ankalimbikitsa tsankho anali olimbikira kupembedza.

Komatu Baibulo limatiuza chifukwa chachikulu chimene chimachititsa tsankho. Limatiuza chifukwa chake mitundu ina imapondereza anzawo. Limati: “Wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Ngati wina anena kuti: ‘Ndimakonda Mulungu,’ koma amada m’bale wake, ndi wonama. Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yohane 4:8, 20) Mawu amenewa akusonyeza muzu wa vuto la tsankho. Anthu, kaya akhale opembedza kapena ayi, amachita tsankho chifukwa chakuti sadziwa kapena sakonda Mulungu.

Kudziwa Mulungu Kumagwirizanitsa Anthu

Kodi kudziwa ndi kukonda Mulungu kumathetsa bwanji tsankho? Kodi ndi mfundo ziti zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa zomwe zimaletsa anthu kupweteka anzawo amtundu wina? Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova ndi Atate a anthu onse. Limanena kuti: “Kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate. Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye.” (1 Akorinto 8:6) Limanenanso kuti: “Kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Choncho tingati anthu onse ndi pachibale.

Mitundu yonse iyenera kuthokoza kuti Mulungu anaipatsa moyo. Koma mitundu yonse iyenera kuchita chisoni ndi zimene kholo lawo loyamba linachita. Paulo analemba kuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi.’ N’chifukwa chake “onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23; 5:12) Yehova Mulungu amakonda zinthu zamitundumitundu, n’chifukwa chake cholengedwa chilichonse ndi chosiyana ndi chinzake. Koma sananene kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa unzake. Maganizo amene anthu ambiri ali nawo akuti mtundu wawo ndi wapamwamba kuposa mitundu ina ndi osagwirizana ndi Malemba. Apa ndi zoonekeratu kuti zimene Mulungu amatiphunzitsa zimalimbikitsa mitundu yonse kugwirizana.

Mulungu Amakonda Mitundu Yonse

Ena amaganiza kuti Mulungu analimbikitsa tsankho poyanja Aisiraeli ndi kuwaphunzitsa kuti adzipatule ku mitundu ina. (Eksodo 34:12) Panthawi ina, Mulungu anasankha Aisiraeli kukhala mtundu wake wapadera. Anatero chifukwa cha chikhulupiriro champhamvu chimene kholo lawo Abulahamu anasonyeza. Mulungu mwiniyo ankalamulira Aisiraeli, kuwasankhira atsogoleri ndi kuwapatsa malamulo. Panthawi imene Aisiraeli anatsatira zimenezi, mitundu ina inkatha kuona ubwino wa boma la Mulungu poyerekezera ndi maboma a anthu. Yehova anaphunzitsanso Aisiraeli kalelo kuti panafunika nsembe yoyanjanitsa anthu onse ndi Mulungu. Choncho zochita za Yehova ndi Aisiraeli zinapindulitsa mitundu yonse. Zimenezi zinali zogwirizana ndi zimene Mulungu anauza Abulahamu kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.”​—Genesis 22:18.

Ndiponso, Ayuda anakhala ndi mwayi wolandira malemba opatulika ochokera kwa Mulungu ndipo Mesiya anadzabadwira mu mtundu umenewu. Koma zonsezi cholinga chake chinali chakuti mitundu yonse ipindule. Malemba Achiheberi amene Ayuda anapatsidwa ali ndi mawu olimbikitsa onena za nthawi imene mitundu yonse idzadalitsidwa kwambiri. Mawuwo amati: “Amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake . . . Mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.”​—Mika 4:2-4.

Ngakhale kuti Yesu Khristu analalikira Ayuda, iye ananenanso kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyo 24:14) Palibe mtundu umene sudzamva uthenga wabwino. Chotero Yehova anapereka chitsanzo chabwino pochitira mitundu yonse chilungamo. “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Malamulo amene Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli amasonyezanso kuti iye amakonda mitundu yonse. Onani kuti Chilamulo chinapempha Aisiraeli kuchita zambiri koposa kungolandira alendo m’dziko lawo. Chilamulocho chinati: ‘Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aiguputo.’ (Levitiko 19:34) Malamulo ambiri amene Mulungu anapatsa Aisiraeli anawaphunzitsa kukomera mtima alendo. Choncho, pamene Boazi, agogo a Yesu, anaona mkazi wosauka wachilendo akukunkha m’munda mwake, anaonetsetsa kuti antchito ake akusiya tirigu wambiri kuti mkaziyo akunkhe. Anachita zimenezi potsatira zimene Mulungu anaphunzitsa.​—Rute 2:1, 10, 16.

Yesu Anaphunzitsa Anthu Kukomerana Mtima

Yesu anaphunzitsa anthu za Mulungu kuposa wina aliyense. Anaphunzitsa otsatira ake kukomera mtima anthu amitundu ina. Tsiku lina analankhulana ndi mkazi wachisamariya. Mkaziyo anadabwa chifukwa Ayuda ambiri ankadana ndi Asamariya. Akukambirana, Yesu mokoma mtima anathandiza mkaziyo kudziwa mmene angapezere moyo wosatha.​—Yohane 4:7-14.

Yesu anatiphunzitsanso kukomera mtima anthu amitundu ina pamene anapereka fanizo la Msamariya wachifundo. Munthu ameneyu anapeza Myuda atavulazidwa kwambiri ndi achifwamba panjira. Msamariyayu akanatha kungonena kuti: ‘Ine sindingathandize Myuda. Pajatu Ayuda amadana ndi mtundu wathu.’ Koma Yesu anafotokoza kuti Msamariyayo ankakonda anthu amitundu ina. Ngakhale kuti anthu ena apaulendo anangomudutsa munthu wovulalayo, Msamariya uja “chifundo chinam’gwira” ndipo anachita zinthu zambiri kumuthandiza. Pomaliza fanizoli, Yesu ananena kuti aliyense amene akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu azichita zimenezi.​—Luka 10:30-37.

Mtumwi Paulo anaphunzitsa anthu ofuna kukondweretsa Mulungu kusintha makhalidwe awo ndi kutsanzira mmene Mulungu amachitira ndi anthu. Iye analemba kuti: “Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo muvale umunthu watsopano, umene kudzera mwa kudziwa zinthu molondola ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha Iye amene anaulenga. Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, mdulidwe kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti . . . Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.”​—Akolose 3:9-14.

Kodi Anthu Amasinthadi Akadziwa Mulungu?

Kodi anthu akadziwa Mulungu amasinthadi mmene amaonera anthu a mitundu ina? Taganizirani za mmwenye wina ku Canada amene anakhumudwa kwambiri chifukwa chakuti anthu ankamusankha. Kenako mayi ameneyu anakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira nazo Baibulo. Pambuyo pake anawalembera kalata yowathokoza, kuti: ‘Ndinu azungu abwino ndi okoma mtima. Ndinkadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani muli osiyana zedi ndi azungu anzanu. Nditaganiza kwambiri, ndinazindikira kuti ndinu osiyana chifukwa chakuti ndinu Mboni za Mulungu. Zikuoneka kuti m’Baibulo muli mfundo zothandiza. Pamisonkhano yanu ndinaonapo anthu oyera, akuda, oyererapo, ndi achikasu onse amtima wofanana, osaona khungu la munthu, popeza onse anali abale ndi alongo. Panopa ndazindikira kuti Mulungu wanu ndi amene wachititsa kuti mukhale anthu otere.’

Mawu a Mulungu amanena za nthawi imene “dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova.” (Yesaya 11:9) Ngakhale pakali pano, pokwaniritsa ulosi wa Baibulo, a khamu lalikulu mamiliyoni ambiri ‘ochokera m’dziko lililonse, fuko, mtundu, ndi lilime lililonse,’ akugwirizana pa kulambira koona. (Chivumbulutso 7:9) Akuyembekezera kudzaona chidani chikulowedwa m’malo ndi chikondi m’dziko limene Yehova adzakwaniritsa lonjezo limene anauza Abulahamu lakuti: “Mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa.”​—Machitidwe 3:25.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Chilamulo cha Mulungu chinaphunzitsa Aisiraeli kukonda alendo

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi tikuphunzira chiyani pafanizo la Msamariya wachifundo?

[Zithunzi patsamba 6]

Mulungu sananene kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa unzake