Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino”

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino”

“Pitirizani Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino”

“Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.”​—AROMA 12:21.

1. Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kugonjetsa choipa?

KODI n’zotheka kulimbana ndi anthu amene mwankhanza amatsutsa kulambira koona? Kodi n’zotheka kugonjetsa mphamvu zofuna kuti tiyambenso kutsatira anthu osaopa Mulungu a m’dzikoli? Yankho la mafunso onse awiriwa ndi lakuti inde. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa cha zimene mtumwi Paulo ananena m’kalata yake ya kwa Aroma. Analemba kuti: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Tikamakhulupirira Yehova ndiponso kukhala ofunitsitsa kusatsatira dzikoli, zoipa zake sizingatigonjetse. Mawu akuti “pitirizani kugonjetsa choipa” amasonyeza kuti tingagonjetse choipa ngati sitisiya kulimbana nacho. Anthu omwe angagonje ndi okhawo amene amasiya kukhala tcheru ndiponso kulimbana ndi dziko loipali komanso wolamulira wake, Satana Mdyerekezi.​—1 Yohane 5:19.

2. N’chifukwa chiyani tikambirana zinthu zina zimene zinam’chitikira Nehemiya?

2 Pafupifupi zaka 500 Paulo asanakhalepo, mtumiki wina wa Mulungu yemwe ankakhala ku Yerusalemu anasonyeza kuti mawu a Paulo onena za kulimbana ndi choipa analidi oona. Mtumiki wa Mulungu ameneyo, Nehemiya, sanangopirira kutsutsidwa ndi anthu osaopa Mulungu koma anagonjetsanso choipa mwa kuchita chabwino. Kodi anakumana ndi mavuto otani? N’chiyani chinam’thandiza kupambana? Kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zinam’chitikira Nehemiya. *

3. Kodi zinthu zinali bwanji pamoyo wa Nehemiya ndipo ndi ntchito yodabwitsa yotani imene anachita?

3 Nehemiya ankatumikira pa nyumba ya Mfumu Aritasasta ya ku Perisiya. Ngakhale kuti Nehemiya ankakhala limodzi ndi anthu osakhulupirira, ‘sanatengere nzeru za dongosolo la zinthu’ la masiku amenewo. (Aroma 12:2) Ataona kuti zinthu sizinali kuyenda bwino ku Yuda, Nehemiya anasiya moyo wake wapamwamba n’kupita ku Yerusalemu, ulendo umene unali wovuta kwambiri. Atafika kumeneko, anayamba ntchito yaikulu yomanganso linga. (Aroma 12:1) Ngakhale kuti Nehemiya anali kazembe ku Yerusalemu, anagwira ntchito tsiku lililonse limodzi ndi Aisiraeli anzake “kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.” Chifukwa cholimbikira kugwira ntchito, anamaliza ntchitoyo patapita miyezi iwiri yokha. (Nehemiya 4:21; 6:15) Zimenezi zinalidi zodabwitsa kwambiri chifukwa pamene anali kugwira ntchitoyo, Aisiraeli ankatsutsidwa m’njira zosiyanasiyana. Kodi ndani ankatsutsa Nehemiya ndipo anali ndi cholinga chotani?

4. Kodi otsutsa Nehemiya anali ndi cholinga chotani?

4 Anthu amene ankatsutsa kwambiri Nehemiya anali Sanibalati, Tobiya, ndi Gesemu, anthu olemekezeka omwe ankakhala pafupi ndi Yuda. Popeza kuti anali adani a anthu a Mulungu, “chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israyeli chokoma.” (Nehemiya 2:10, 19) Adani amenewo ankafuna kwambiri kuletsa ntchito yomanga imene Nehemiya ankachita moti anagwiritsa ntchito ziwembu zoopsa. Kodi Nehemiya ‘analola kugonjetsedwa ndi choipa’ chimenechi?

“Kudamuipira, Nakwiya Kwakukulu”

5, 6. (a) Kodi adani a Nehemiya anatani ataona kuti ntchito yomanga yayambika? (b) N’chifukwa chiyani Nehemiya sanachite mantha ndi otsutsawo?

5 Nehemiya analimbikitsa anthu ake molimba mtima kuti: “Tiyeni, timange linga la Yerusalemu.” Anthuwo anayankha kuti: “Timange.” Nehemiya anati: ‘Analimbitsa manja mokoma,’ koma otsutsa “anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?” Nehemiya sanachite mantha anthuwo atamunyoza ndi kumunamizira. Iye anauza otsutsawo kuti: “Mulungu Wam’mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga.” (Nehemiya 2:17-20) Nehemiya anafunitsitsa kuti apitirize kugwira ntchito yabwino imeneyi.

6 Mmodzi mwa otsutsawo, dzina lake Sanibalati, “kudamuipira, nakwiya kwakukulu” ndipo anayamba kulankhula monyoza kwambiri. Iye anati: “Alikuchitanji Ayuda ofookawa? . . . Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?” Tobiya nayenso ananyoza kuti: “Ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lawo lamiyala.” (Nehemiya 4:1-3) Kodi Nehemiya anatani?

7. Kodi Nehemiya anatani anthu omutsutsa atamunamizira?

7 Nehemiya anangonyalanyaza zonena zawozo. Iye anamvera lamulo la Mulungu ndipo sanafune kubwezera. (Levitiko 19:18) M’malo mwake, anasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndipo anapemphera kuti: “Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezera chitonzo chawo pamtu pawo.” (Nehemiya 4:4) Nehemiya anakhulupirira mawu a Mulungu akuti: “Kubwezera chilango n’kwanga.” (Deuteronomo 32:35) Nehemiya ndi anthu ake anapitiriza ‘kumanga lingali.’ Sanalole kuti zimenezi ziwasokoneze. Ndipotu “linga lonse linalumikizana kufikira pakati m’pakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.” (Nehemiya 4:6) Anthu odana ndi kulambira koona amenewo analephera kuletsa ntchito yomanga linga imeneyi. Kodi ifeyo tingatsanzire motani Nehemiya?

8. (a) Kodi tingatsanzire motani Nehemiya otsutsa akamatinamizira? (b) Fotokozani zimene zinakuchitikirani kapena zimene munamva zosonyeza ubwino wosabwezera.

8 Masiku ano, anthu amene amatitsutsa ku sukulu, ku ntchito, ngakhale panyumba angatinyoze ndi kutinamizira. Koma akatinamizira, nthawi zambiri ndi bwino kutsatira mfundo ya m’Malemba yakuti: ‘Pali nthawi yakutonthola.’ (Mlaliki 3:1, 7) Motero, mofanana ndi Nehemiya, timapewa kubwezera ndi mawu okhadzula. (Aroma 12:17) Timapemphera kwa Mulungu ndi kumukhulupirira chifukwa anatilonjeza kuti: “Ndidzawabwezera ndine.” (Aroma 12:19; 1 Petulo 2:19, 20) Mwa kutero, sitilola anthu amene amatitsutsa kuti atidodometse pa ntchito imene tapatsidwa masiku ano yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kupanga ophunzira. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Nthawi iliyonse imene timalalikira ndi kupewa kusokonezedwa ndi otitsutsa, timasonyeza kuti ndife okhulupirika mofanana ndi Nehemiya.

‘Tikuphani’

9. Kodi adani a Nehemiya anayamba kutsutsa m’njira yotani ndipo Nehemiya anachita chiyani?

9 Anthu otsutsa kulambira koona m’nthawi ya Nehemiya atamva kuti “makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula,” anatenga malupanga awo “kudzathira nkhondo ku Yerusalemu.” Zinthu zinaoneka ngati siziwayendera bwino Ayuda. Kumpoto kunali Asamariya, kum’mawa kunali Aamoni, kum’mwera kunali Aarabu, ndipo kumadzulo kunali Aasidodi. Mzinda wa Yerusalemu unazingidwa ndipo zinaoneka kuti omangawo analibe kothawira. Kodi akanatani? Nehemiya anati: “Tinapemphera kwa Mulungu wathu.” Adaniwo anaopseza kuti: ‘Tiwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.’ Nehemiya anauza omanga kuti ateteze mzindawo ndi “malupanga awo, nthungo zawo, ndi mauta awo.” N’zoonadi, malinga ndi kuona kwa anthu, gulu laling’ono la Ayudalo silikanatha kugonjetsa gulu lalikulu kwambiri la adanilo, koma Nehemiya anawalimbikitsa kuti: “Musamawaopa . . . ; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa.”​—Nehemiya 4:7-9, 11, 13, 14.

10. (a) N’chifukwa chiyani adani anasintha mwadzidzidzi? (b) Kodi Nehemiya anachita chiyani?

10 Kenako, zinthu zinasintha mwadzidzidzi ndipo adaniwo anasiya nkhondo. N’chifukwa chiyani anatero? Nehemiya anati: “Mulungu adapititsa pachabe uphungu wawo.” Koma Nehemiya anazindikira kuti adaniwo aziwaopsezabe. Choncho, mwanzeru anasintha njira imene omangawo ankagwirira ntchito. Kuyambira nthawi imeneyo, “anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida.” Nehemiya anapatsanso munthu wina udindo “woomba lipenga” kuti achenjeze anthu omanga, adani akawaukira. Ndipo chofunika kwambiri n’choti Nehemiya anawatsimikizira anthuwo kuti: “Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.” (Nehemiya 4:15-20) Atalimbikitsidwa ndiponso atakonzeka kulimbana ndi adani awo, omangawo anapitiriza kugwira ntchito. Kodi nkhaniyi ingatiphunzitse chiyani?

11. Kodi kumayiko kumene ntchito ya Ufumu n’njoletsedwa, n’chiyani chimathandiza Akhristu oona kuti apirire, ndipo iwowo amagonjetsa bwanji choipa mwa kuchita chabwino?

11 Nthawi zina, Akhristu oona amatsutsidwa mwankhanza. Ndithudi kumayiko ena, otsutsa moopsa kulambira koona angakhale gulu lalikulu lochititsa mantha. Ndipo kwa anthu, zingaoneke ngati okhulupirira anzathu kumayiko amenewo sangapambane. Komabe, a Mboni amenewo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti ‘Mulungu adzawagwirira nkhondo.’ Anthu amene amazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo aona nthawi zambiri kuti Yehova amayankha mapemphero awo ndipo ‘amapititsa pachabe uphungu’ wa adani amphamvuwo. Ngakhale kumayiko kumene ntchito ya Ufumu n’njoletsedwa, Akhristu amapezabe njira zoti apitirize kulalikira uthenga wabwino. Mofanana ndi mmene anthu omanga ku Yerusalemu anasinthira njira yawo yogwirira ntchito, masiku ano Mboni za Yehova zikaukiridwa, mochenjera zimasintha njira yawo yolalikira. Koma n’zodziwikiratu kuti amapewa kugwiritsa ntchito zida. (2 Akorinto 10:4) Ngakhale ataopsezedwa kuti awachitira chiwawa, sasiya ntchito yawo yolalikira. (1 Petulo 4:16) Koma abale ndi alongo olimba mtima amenewo ‘amapitiriza kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.’

“Tiyeni Tikumane”

12, 13. (a) Kodi adani a Nehemiya anagwiritsa ntchito njira yotani? (b) N’chifukwa chiyani Nehemiya anakana kukakumana ndi adani akewo?

12 Adani a Nehemiya ataona kuti njira zomutsutsa mwachindunji zalephera, anayamba kugwiritsa ntchito njira zosaonekera. Ndipotu, anayesa njira zitatu zachiwembu. Kodi njirazi zinali zotani?

13 Choyamba, adani a Nehemiya anayesa kumunyenga. Anamuuza kuti: “Tiyeni tikumane ku midzi ya ku chigwa cha Ono.” Chigwa cha Ono chinali pakati pa mzinda wa Yerusalemu ndi wa Samariya. Choncho, adaniwo anauza Nehemiya kuti akumane nawo pakati kuti athetse kusiyana maganizo kumene kunalipo. Nehemiya akanaganiza kuti: ‘Zimenezi ndi zomveka, ndi bwino kukambirana kusiyana ndi kumenyana.’ Koma Nehemiya anakana ndipo anafotokoza chifukwa chake kuti: “Analingirira za kundichitira choipa.” Anazindikira chiwembu chawo ndipo sananyengedwe. Anauza omutsutsawo kanayi konse kuti: “Sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?” Adaniwo analephera kuchititsa Nehemiya kusiya ntchito yake. Iye anapitirizabe kuika mtima wake pantchito yomangayo.​—Nehemiya 6:1-4.

14. Kodi Nehemiya anachita chiyani pa zimene adani ake anachita?

14 Chachiwiri, adani a Nehemiya anayamba kufalitsa mabodza onena za iye kuti anali ‘kulingirira za kupandukira’ Mfumu Aritasasta. Anauzanso Nehemiya kuti: “Tiyeni tsono tipangane pamodzi.” Nehemiya anakananso chifukwa anazindikira cholinga cha adaniwo. Nehemiya anafotokoza kuti: “Anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja awo adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika.” Koma panthawiyi, Nehemiya anatsutsa mabodza a adani ake ponena kuti: “Koma ndinam’tumizira mawu, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.” Ndiponso Nehemiya anapemphera kwa Yehova kuti am’thandize, anati: “Mulimbitse manja anga.” Iye anakhulupirira kuti atathandizidwa ndi Yehova, angalepheretse chiwembu chimenechi ndi kupitiriza ntchito yake yomanga.​—Nehemiya 6:5-9.

15. N’chiyani chimene mneneri wonyenga anauza Nehemiya ndipo n’chifukwa chiyani Nehemiya anakana?

15 Chachitatu, adani a Nehemiya anagwiritsa ntchito Semaya, Mwisiraeli wopanduka, kuti achititse Nehemiya kuswa Malamulo a Mulungu. Semaya anauza Nehemiya kuti: “Tikumane ku nyumba ya Mulungu m’kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe.” Semaya anauza Nehemiya kuti moyo wake uli pangozi koma akhoza kupulumuka mwa kubisala m’kachisi. Koma popeza Nehemiya sanali wansembe, akanachimwa ngati akanabisala m’nyumba ya Mulungu. Kodi Nehemiya anaswa Malamulo a Mulungu chifukwa chofuna kupulumutsa moyo wake? Nehemiya anayankha kuti: “Ndani wonga ine adzalowa m’Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.” N’chifukwa chiyani Nehemiya sanagwere m’msampha umene anam’tchera? Chifukwa anazindikira kuti ngakhale Semaya anali Mwisiraeli mnzake, ‘sanatumidwe ndi Mulungu.’ Ndipotu, mneneri woona sangamuuze kuti aswe Malamulo a Mulungu. Nehemiya sanalolenso kuti agonjetsedwe ndi anthu oipa amene ankam’tsutsa. Patapita nthawi yochepa anatha kunena kuti: “Linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli.”​—Nehemiya 6:10-15; Numeri 1:51; 18:7.

16. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani ndi mabwenzi onyenga, anthu otinamizira ndiponso abale onyenga? (b) Kodi mungasonyeze bwanji kuti simungasiye kumvera Yehova kusukulu, kuntchito kapena panyumba?

16 Mofanana ndi Nehemiya, ifenso tingatsutsidwe ndi mabwenzi onyenga, anthu otinamizira, kapena abale onyenga. Anthu ena angafune kuti tichite zimene iwowo akufuna. Angamatiuze kuti tisachite khama kwambiri potumikira Yehova kuti tithe kuchitanso zinthu zimene anthu ena a m’dzikoli akuchita. Koma popeza kuti timaika Ufumu wa Mulungu poyamba m’moyo wathu, timakana kutero. (Mateyo 6:33; Luka 9:57-62) Anthu amene amatitsutsa amafalitsanso mabodza onena za ife. Monga mmene ananamizira Nehemiya kuti anali kupandukira mfumu, ifenso kumayiko ena, amatinamizira kuti tikufuna kuukira boma. Koma makhoti agamula kuti milandu ina yotere ndi yabodza. Ndipo mulimonse mmene zinthu zingayendere, timapemphera ndi chikhulupiriro kuti Yehova atsogolere zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake. (Afilipi 1:7) Tingatsutsidwenso ndi anthu amene amanamizira kutumikira Yehova. Mofanana ndi mmene Myuda mnzake anayesera kuchititsa Nehemiya kuswa Malamulo a Yehova kuti apulumutse moyo wake, ampatuko omwe kale anali Mboni angafune kuti tichite zinthu zina zosemphana ndi malamulo a Mulungu. Komabe, sitingamvere ampatuko chifukwa timadziwa kuti tingapulumutse moyo wathu mwa kumvera malamulo a Mulungu osati mwa kuwaswa. (1 Yohane 4:1) N’zoonadi, tikhoza kugonjetsa choipa chilichonse, Yehova akatithandiza.

Kulengeza Uthenga Wabwino Ngakhale Tikukumana ndi Zoipa

17, 18. (a) Kodi Satana ndiponso amene amamuimira amafuna kuchita chiyani? (b) Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchitanji ndipo n’chifukwa chiyani?

17 Mawu a Mulungu amanena za abale odzozedwa a Khristu kuti: “Anam’gonjetsa [Satana] chifukwa cha . . . mawu a umboni wawo.” (Chivumbulutso 12:11) Motero, pali kugwirizana kwambiri pakati pa kugonjetsa Satana, yemwe amayambitsa zoipa, ndi kulalikira uthenga wa Ufumu. N’zosadabwitsa kuti Satana nthawi zonse amaukira otsalira odzozedwa ndiponso “khamu lalikulu” mwa kusonkhezera anthu ena kuti awatsutse.​—Chivumbulutso 7:9; 12:17.

18 Monga mmene taonera, anthu angatitsutse mwa kugwiritsa ntchito mawu onyoza kapena kutiopseza kuti atichitira chiwawa kapenanso angagwiritse ntchito njira zosaonekera. Chilichonse chimene angagwiritse ntchito, nthawi zonse cholinga cha Satana ndi chimodzi, kuletsa ntchito yathu yolalikira. Koma adzalephereratu chifukwa anthu a Mulungu akufunitsitsa ‘kupitiriza kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino,’ monga mmene kalelo Nehemiya anachitira. Adzapitiriza kulalikira uthenga wabwino mpaka Yehova atawauza kuti amaliza ntchitoyo.​—Maliko 13:10; Aroma 8:31; Afilipi 1:27, 28.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Kuti mudziwe mmene zinthu zinalili nthawi imeneyo, werengani Nehemiya 1:1-4; 2:1-6, 9-20; 4:1-23; 6:1-15.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi atumiki a Mulungu kalelo anatsutsidwa motani, ndipo masiku ano Akhristu akutsutsidwa motani?

• Kodi cholinga chachikulu cha adani a Nehemiya chinali chotani, ndipo masiku ano cholinga cha adani a Mulungu n’chotani?

• Kodi masiku ano timapitiriza motani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 29]

Zimene Buku la Nehemiya Limatiphunzitsa

Atumiki a Mulungu

• amanyozedwa

• amaopsezedwa

• amachitiridwa chinyengo

Amene amachita chinyengo ndi

• mabwenzi onyenga

• anthu otinamizira

• abale onyenga

Atumiki a Mulungu amagonjetsa choipa mwa

• kupitiriza kuchita ntchito imene Mulungu wawapatsa

[Chithunzi patsamba 27]

Nehemiya ndi antchito anzake anamanganso linga la Yerusalemu ngakhale kuti anatsutsidwa moopsa

[Chithunzi patsamba 31]

Akhristu oona amalalikira uthenga wabwino mopanda mantha