Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu Yolimbitsa Chikhulupiriro

Sukulu Yolimbitsa Chikhulupiriro

Sukulu Yolimbitsa Chikhulupiriro

“NDI mwayi waukulu zedi umene takhala nawo kwa miyezi isanu yapitayi chifukwa takhala tikulingalira mwakuya mfundo za Mlengi wathu ndiponso kuphunzira kuona zinthu m’njira imene iyeyo amaonera.” Anatero mmodzi mwa anthu amene analowa kalasi ya nambala 122, patsiku lomaliza maphunziro awo a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Panali pa March 10, 2007, tsiku losaiwalika kwa anthu 56 a m’kalasi imeneyi, amene anali atangotsala pang’ono kuti apite kukatumikira ku mayiko 26.

Atanena mawu a malonje kwa anthu 6,205, omwe anafika pa mwambowu, Theodore Jaracz, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira anati: “Tili ndi chikhulupiriro kuti mulimbikitsidwa mwauzimu ndiponso chikhulupiriro chanu chilimba chifukwa chofika pa mwambo uno.” Kenaka M’bale Jaracz anaitana abale anayi omwe anakamba motsatizana nkhani za m’Baibulo zolimbikitsa ndiponso zapanthawi yake. Nkhani zimenezi zinali zothandizadi kwa ophunzirawo kuti akwaniritse bwino utumiki wawo wa umishonale.

Kulimbikitsa Amishonalewo Kuti Akalimbitse Chikhulupiriro cha Ena

M’bale Leon Weaver, yemwe ndi wa m’Komiti ya Nthambi ku United States, anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Pitirizani Kuchita Zabwino.” M’baleyu anauza ophunzirawo kuti asaiwale kuti aliyense wa iwo, pa avereji watha zaka 13 ali mu utumiki wa nthawi zonse, akupititsa patsogolo ntchito yophunzitsa Baibulo imene imalimbitsa chikhulupiriro. M’baleyu anati: “Ndi ntchito yabwino chifukwa imapulumutsa moyo wa anthu, komanso chofunika kwambiri n’choti imalemekezetsa Atate wathu wa kumwamba, Yehova.” Kenaka M’bale Weaver analimbikitsa ophunzirawo kuti apitirize ‘kufesa mu mzimu’ ndiponso kuti ‘asaleke kuchita zabwino.’​—Agalatiya 6:8, 9.

Ndiyeno M’bale David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yothandiza kwambiri yakuti, “Yesetsani Kuponya Mwendo Patsogolo.” M’bale Splane analimbikitsa amishonale atsopanowo powapatsa malangizo kuti akayambe bwino utumiki wawo kumadera amene atumizidweko. Iye anati: “Pitirizani kuona zinthu moyenerera. Musamafulumire kutaya mtima kapena kuganizira ena molakwika. Muzikhala ansangala. Musamakonde kuona zolakwika zokhazokha za ena. Khalani odzichepetsa, ndiponso lemekezani abale a m’dzikolo.” Ndiyeno m’baleyo anawonjezera kuti: “Mukangotsika ndege, ponyani mwendo patsogolo, ndipo tikupempha Yehova kuti adalitse mapazi anu okongolawo, amene atenga ‘uthenga wabwino wa zinthu zabwino,’ n’kuupititsa kwa anthu ena.”​—Yesaya 52:7.

Kenaka Lawrence Bowen, yemwe ndi mlangizi wa sukuluyi anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Cholowa Chodalirika Kwambiri.” M’bale Bowen anakumbutsa ophunzirawo kuti kuyambika kwa Sukulu ya Gileadi panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndi umboni wosonyeza kuti Mawu a ulosi a Yehova akukwaniritsidwa. (Aheberi 11:1; Chivumbulutso 17:8) Kungoyambira nthawi imeneyo, Sukulu ya Gileadi yathandiza ophunzira kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Chikhulupiriro cholimba n’chomwe chimathandiza amishonale kupitirizabe kulengeza choonadi molimba mtima.

Ndiyeno Mark Noumair, yemwenso ndi mlangizi wa Sukulu ya Gileadi, anakamba nkhani yochititsa chidwi ya mutu wakuti, “Mwandikumbutsa za Munthu Winawake.” M’baleyu anafotokoza za chitsanzo cha mneneri Elisa, amene anasonyeza chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima pochita utumiki wake. Pofotokoza mfundo za pa 1 Mafumu 19:21, M’bale Noumair anati: “Elisa ankafunitsitsa kusintha zinthu pamoyo wake mwa kuika zofuna zake pambuyo, n’cholinga choti apititse patsogolo ntchito ya Yehova.” Kenaka m’baleyu anayamikira ophunzirawo chifukwa chosonyeza mzimu wofanana ndi wa Elisa, ndiponso anawalimbikitsa kuti akapitirizebe kusonyeza mzimu umenewu kumene akupitako.

Chikhulupiriro Chimathandiza Kukhala ndi Ufulu wa Kulankhula

Kuwonjezera pa kulimbitsa chikhulupiriro chawo panthawi yomwe anali pasukuluyi, ophunzirawo analinso ndi mwayi wolalikira uthenga wabwino, Loweruka ndi Lamlungu lililonse. Motero m’nkhani ina ya patsiku lomaliza maphunziro awoli, iwo anachita zitsanzo ndiponso anasimba nkhani zosangalatsa zimene anakumana nazo muutumiki. Nkhani imeneyi inakambidwa ndi M’bale Wallace Liverance, yemwenso ndi mlangizi wa Gileadi. Mutu wa nkhaniyi unali woti, “Timalankhula Zomwe Timakhulupirira,” wogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo a pa 2 Akorinto 4:13.

Pambuyo pa nkhani imeneyi, abale awiri a m’banja la Beteli, Daniel Barnes ndi Charles Woody, anafunsa mafunso abale amene kale anali amishonale ndi enanso amene akutumikirabe monga amishonale. Abale ofunsidwawo analongosola mmene Yehova amasamalilira ndiponso kudalitsira anthu amene akum’tumikira mokhulupirika. (Miyambo 10:22, 1 Petulo 5:7) Mmishonale wina anati: “Chifukwa cha mfundo zimene tinaphunzira ku Gileadi, ine ndi mkazi wanga tinaona ndi maso athu kuti Yehova amatisamaliriradi. Sukuluyi inalimbitsadi chikhulupiriro chathu. Chikhulupiriro n’chofunika kwambiri chifukwa atumiki onse a Mulungu, kuphatikizapo amishonale, amakumana ndi mayesero, mavuto ndiponso nkhawa.”

Pitirizani Kulimbikitsa Anthu Kutsatira Mfundo za M’Baibulo Zolimbitsa Chikhulupiriro

Pulogalamu ya patsikuli inafika pachimake pamene M’bale Samuel Herd, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yakuti, “Pitirizani Kulimbikitsa Abale Anu.” Kodi cholinga cha maphunziro amene amishonalewa analandira n’chotani? M’bale Herd anati: “Cholinga chake n’choti akuphunzitseni kugwiritsa ntchito lilime lanu kutamandira Yehova, kuphunzitsa choonadi chake kwa ena kumadera atsopano kumene akutumizeni, ndiponso kulimbikitsana chikhulupiriro ndi abale anu.” Komabe, m’baleyu anachenjeza ophunzirawo kuti nthawi zina lilime lingalankhule zinthu zosalimbikitsa. (Miyambo 18:21; Yakobe 3:8-10) M’baleyu analimbikitsa amishonale atsopanowo kuti atsanzire Yesu pogwiritsa ntchito bwino lilime lawo. Panthawi ina ophunzira ake atamvetsera zimene Yesu ankanena, ophunzirawo anati: “Kodi mitima yathu sinali kunthunthumira pamene anali . . . kutisanthulira Malemba momveka bwino?” (Luka 24:32) M’bale Herd anati: “Mukamalankhula zinthu zolimbikitsa, abale ndi alongo anu a kumadera amene mukupita mukawalimbikitsa kwambiri ndipo mukawafika pa mtima.”

Kenako ophunzirawo analandira madipuloma. Pambuyo pa zimenezi, anawerenga kalata yoyamikira yolembedwa ndi ophunzirawo. Kalatayo inati: “Tikuona kuti tili ndi udindo waukulu woti tigwiritse ntchito zimene taphunzirazi pochita mokhulupirika utumiki wathu wa umishonale. Ndife ofunitsitsa kupita kwina kulikonse, mpaka kumapeto a dziko lapansili, ndipo tikupemphera kuti khama lathuli lichititse anthu kutamanda kwambiri Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu.” Anthu onse amene anasonkhana pa mwambo umenewu anayamikira kwambiri kalatayi mwa kuwomba m’manja kwa nthawi yaitali. Indedi, pulogalamu ya mwambo wotsazikana ndi ophunzira a kusukuluyi inalimbitsadi chikhulupiriro cha anthu onse amene anasonkhanawo.

[Mawu Otsindika patsamba 17]

“Mukamalankhula zinthu zolimbikitsa, abale ndi alongo anu a kumadera amene mukupita mukawalimbikitsa kwambiri ndipo mukawafika pa mtima”

[Bokosi patsamba 15]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira achokera: 9

Chiwerengero cha mayiko amene atumizidwa: 26

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Avereji ya zaka za kubadwa: 33.4

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 16.8

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13

[Chithunzi patsamba 16]

Kalasi ya Nambala 122 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Howitt, R.; Smith, P.; Martinez, A.; Pozzobon, S.; Kitamura, Y.; Laud, C. (2) Fiedler, I.; Beasley, K.; Matkovich, C.; Bell, D.; Lippincott, W. (3) Sites, W.; Andersen, A.; Toevs, L.; Fusano, G.; Rodríguez, C.; Yoo, J. (4) Sobomehin, M.; Thomas, L.; Gasson, S.; Dauba, V.; Bertaud, A.; Winn, C.; Dobrowolski, M. (5) Yoo, J.; Dauba, J.; Mixer, H.; Newton, M.; Rodríguez, F.; Mixer, N. (6) Laud, M.; Lippincott, K.; Martinez, R.; Haub, A.; Schamp, R.; Pozzobon, L.; Toevs, S. (7) Howitt, S.; Kitamura, U.; Newton, D.; Haub, J.; Sites, J.; Thomas, D. (8) Sobomehin, L.; Matkovich, J.; Fusano, B.; Winn, J.; Schamp, J.; Andersen, D.; Dobrowolski, J. (9) Fiedler, P.; Bell, E.; Beasley, B.; Smith, B.; Bertaud, P.; Gasson, M.