Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa

Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa

Barizilai Anali Munthu Wodzichepetsa

‘NDIKULEMERENI chifukwa chiyani?’ Munthu wa zaka 80 amene ananena mawu amenewa kwa Davide, mfumu ya Isiraeli anali Barizilai. Baibulo limati iyeyu anali “munthu womveka,” ndipo n’zachidziwikire kuti anali womveka chifukwa cha chuma chake. (2 Samueli 19:32, 35) Barizilai ankakhala m’chigawo chamapiri chotchedwa Gileadi, chomwe chinali kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano.​—2 Samueli 17:27; 19:31.

Kodi Barizilai ananeneranji mawu omwe ali pamwambawa kwa Davide? Ndipo kodi zinatani kuti munthu wachikulireyu alankhule motero?

Kuukira Mfumu

Panthawiyo n’kuti moyo wa Davide uli pangozi. Mwana wake Abisalomu anali ‘atakopa mitima ya Aisiraeli,’ n’kulanda mpando wachifumu. Zinali zoonekeratu kuti Abisalomu akanaseseratu aliyense amene anali pambuyo pa Davide, yemwe anali bambo ake. Motero, Davide ndi anthu ake anathawa mu Yerusalemu. (2 Samueli 15:6, 13, 14) Davide atafika m’dera lina la kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano, lotchedwa Mahanaimu, Barizilai anamuthandiza.

Barizilai limodzi ndi Sobi ndiponso Makiri, anapatsa Davide mowolowa manja zinthu zambiri zimene ankafunikira. Anthu atatu okhulupirika kwa Davidewa anasonyeza kuti ankamvetsa mikwingwirima imene Davide anali kukumana nayo. Tikutero chifukwa choti iwowa ataona Davide ndi anthu ake, anati: “Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m’chipululumo.” Barizilai, Sobi ndiponso Makiri anachita zonse zomwe akanatha pom’patsa Davide ndi anthu ake aja zinthu zofunikira monga zogonera, tirigu, barele, ufa, tirigu wokazinga, nyemba, uchi, mafuta, ndiponso nkhosa.​—2 Samueli 17:27-29.

Kuthandiza Davide kunali kuika moyo pachiswe. Chifukwatu n’zokayikitsa kwambiri kuti Abisalomu akanangom’siya munthu aliyense amene anali pambuyo pa Davide, osam’chita kalikonse. Motero, Barizilai analimba mtima kwambiri posonyeza kuti anali pambuyo pa Davide.

Zinthu Zinasintha

Posakhalitsa, gulu loukira la Abisalomu linakumanizana ndi anthu a Davide. Zitatero, panabuka nkhondo imene inachitikira m’tchire la ku Efraimu, mwina cha kufupi ndi ku Mahanaimu. Gulu la asilikali a Abisalomu linagonjetsedwa ndipo “kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo.” Abisalomu anaphedwabe ngakhale kuti anayesa kuthawa.​—2 Samueli 18:7-15.

Motero, Davide anakhalanso mfumu ya Isiraeli, popanda wopikisana naye. Anthu ake anapuma moyo womangothawathawa. Komanso Davide anayamba kuwalemekeza ndiponso kuwayamikira kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwawo.

Davide akubwerera ku Yerusalemu, “Barizilai, Mgileadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yorodano ndi mfumu, kuti akamuwolotse pa Yorodano.” Ndiyeno Davide ananena mawu otsatirawa kwa Barizilai, yemwe anali wokalamba: “Tiyeni muwoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.”​—2 Samueli 19:15, 31, 33.

N’zosakayikitsa kuti Davide anayamikira kwambiri thandizo la Barizilai lija. Zikuoneka kuti Davide sanamuitane Barizilai pofuna kungobweza zabwino zimene anam’chitirazo. Chifukwatu Barizilai anali munthu wachuma moti sakanafunikira thandizo lotere. N’kutheka kuti Davide ankafuna kuti Barizilai akakhale m’nyumba yachifumu chifukwa choti munthu wachikulireyu anali ndi makhalidwe abwino. Unali ulemu waukulu kwambiri kwa Barizilai kukakhala ku nyumba imeneyi nthawi zonse, n’kukhala paubwenzi ndi mfumu.

Kudzichepetsa ndiponso Kuzindikira Zinthu Kwake

Barizilai ananena mawu otsatirawa poyankha pempho la mfumu lija: “Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kumka ku Yerusalemu? Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mawu a amuna ndi akazi oyimba?” (2 Samueli 19:34, 35) Motero Barizilai anakana mwaulemu mwayi waukulu woterewu. Koma n’chifukwa chiyani anakana?

N’kutheka kuti chimodzi mwa zifukwa zimene Barizilai anakanira pempholi chinali chakuti iye anali wokalamba ndipo sakanatha kuchita zinthu zina ndi zina. Mwinanso ankaona kuti watsala pang’ono kufa. (Salmo 90:10) Iye anachita zonse zimene akanatha pothandiza Davide, komabe ankadziwanso kuti pali malire a zimene angathe kuchita malingana ndi msinkhu wake. Barizilai sanalole kuti kuganizira za ulemerero wake ndiponso kudziwika kwake kum’sokoneze maganizo n’kulephera kuona kuti sangathe kuchita zinthu zina. Mosiyana ndi Abisalomu, yemwe anali odzithemba kwambiri, Barizilai anachita zinthu mwanzeru podzichepetsa.​—Miyambo 11:2.

N’kuthekanso kuti Barizilai anakana mwayiwo chifukwa choti ankafunitsitsa kupewa kusokoneza zochita za mfumu yoikidwa ndi Mulunguyi, chifukwa cha mavuto ake a ukalamba. Barizilai anafunsa kuti: “Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu?” (2 Samueli 19:35) Ngakhale kuti anali wokhulupirikabe kwa Davide, n’kutheka kuti Barizilai ankaona kuti udindo umene Davide ankafuna kuti iye akachite ukanatha kuchitidwa mosavuta ndi munthu wachichepereko. Moti mwina ponena mawu otsatirawa, iye ankanena za mwana wake: “Koma suyu, Chimamu mnyamata wanu, iye awoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mum’chitire chimene chikukomerani.” Davide sanakhumudwe ndi yankho limeneli, moti anavomera kutero. Ndipotu asanawoloke mtsinje wa Yorodano Mfumu Davide “inapsompsona Barizilai nim’dalitsa.”​—2 Samueli 19:37-39.

Tiziona Zinthu Moyenera

Nkhani ya Barizilai ikutithandiza kuti tiziona zinthu m’njira yoyenera. Koma sikuti zimene iye anachitazi zizitipangitsa kukana mwayi wautumiki poganiza kuti sitingakwanitse, mwinanso pofuna kungokhala ndi moyo wosatanganidwa. Komanso zisamatipangitse kusafuna udindo mumpingo. M’malo mwake tiyenera kudalira Mulungu kuti atipatse mphamvu ndiponso nzeru kuti tim’tumikire.​—Afilipi 4:13; Yakobe 4:17; 1 Petulo 4:11.

Ngakhale zili choncho, tiyenera kuzindikira zinthu zomwe sitingakwanitse. Mwachitsanzo, zingatheke kuti munthu ali ndi maudindo ambiri mumpingo. N’zodziwikiratu kuti kulandira maudindo enanso owonjezera pamenepa, kungam’chititse kunyalanyaza maudindo ena a m’malemba monga kusamalira banja lake. Ngati zitakhala choncho, kodi sizingakhale bwino kukana maudindo ena owonjezerawo? Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti munthuyo amaona zinthu m’njira yoyenera ndiponso ndi wodzichepetsa.​—Afilipi 4:5; 1 Timoteyo 5:8.

Zimene Barizilai anachita ndi chitsanzo chabwino kwambiri chomwe tingatsatire. Iye anali wokhulupirika, wolimba mtima, wopatsa ndiponso wodzichepetsa. Koma choposa zonsezi n’chakuti, Barizilai ankaona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zake.​—Mateyo 6:33.

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ngakhale kuti Barizilai anali ndi zaka 80, anayenda ulendo wautali ndiponso wotopetsa kuti akathandize Davide

GILEADI

Rogelimu

Sukoti

Mahanaimu

Mtsinje wa Yorodano

Giligala

Yeriko

Yerusalemu

EFRAIMU

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi Barizilai anakaniranji zimene Davide anam’pempha?