Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Mupitiriza Kuyenda mwa Mzimu’?

Kodi ‘Mupitiriza Kuyenda mwa Mzimu’?

Kodi ‘Mupitiriza Kuyenda mwa Mzimu’?

“Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.”​—AGALATIYA 5:16.

1. Kodi nkhawa yoopa kuti tachimwira mzimu tingaithetse bwanji?

PALI njira imene tingathetsere nkhawa yoopa kuti tachimwira mzimu woyera wa Yehova. Njira yake ndi kuchita zimene mtumwi Paulo ananena kuti: “Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.” (Agalatiya 5:16) Tikamalola mzimu wa Mulungu kutitsogolera, zilakolako za thupi sizingatigonjetse.​—Aroma 8:2-10.

2, 3. Kodi kupitiriza kuyenda mwa mzimu kumatithandiza m’njira yotani?

2 ‘Tikamapitiriza kuyenda mwa mzimu,’ mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imatithandiza kumvera Yehova. Timasonyeza makhalidwe abwino mu utumiki, mumpingo, kunyumba, ndi kwina kulikonse. Ndiponso timasonyeza kuti tili ndi zipatso za mzimu pochita zinthu ndi mnzathu wamuukwati, ana athu, anzathu amumpingo ndi anthu enanso.

3 Kukhala “ndi moyo mwa mzimu kwa Mulungu” kumatithandiza kupewa kuchita tchimo. (1 Petulo 4:1-6) Ngati mzimu ukutitsogolera, sitingachite tchimo losakhululukidwa. Koma kodi kuyenda mwa mzimu kumatithandiza m’njira zinanso zotani?

Khalani pa Ubale Wolimba ndi Mulungu Ndiponso Khristu

4, 5. Kodi ife amene timayenda mwa mzimu, timamuona bwanji Yesu?

4 Popeza kuti timayenda mwa mzimu woyera, tili ndi ubale wolimba ndi Mulungu ndiponso Mwana wake. Polemba za mphatso zauzimu, Paulo anauza okhulupirira anzake ku Korinto kuti: “Ndikufuna mudziwe [kunena anthu amene kale ankapembedza mafano] kuti palibe wolankhula mwa mzimu wa Mulungu amene anganene kuti: ‘Yesu ndi wotembereredwa!’ Palibenso anganene popanda mzimu woyera kuti: ‘Yesu ndiye Ambuye!’” (1 Akorinto 12:1-3) Maganizo alionse amene amachititsa anthu kutemberera Yesu amachokera kwa Satana Mdyerekezi. Koma Akhristufe amene timayenda mwa mzimu woyera, timakhulupirira kuti Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa ndi kumukweza kuposa zolengedwa zina zonse. (Afilipi 2:5-11) Timakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu ndipo timamuvomereza kukhala Ambuye wathu woikidwa ndi Mulungu.

5 M’nthawi ya atumwi, anthu ena amene ankati ndi Akhristu anakana kuti Yesu sanabwere m’thupi. (2 Yohane 7-11) Chifukwa chotengera maganizo amenewa ena anakana ziphunzitso zoona zonena za Yesu, Mesiya. (Maliko 1:9-11; Yohane 1:1, 14) Koma ife amene timayenda mwa mzimu woyera timapewa mpatuko ngati umenewo. Ngakhale zili choncho, tifunika kukhala atcheru mwauzimu kuti tipitirize kulandira chisomo cha Yehova ndi “kuyendabe m’choonadi.” (3 Yohane 3, 4) Choncho, tiyeni tikanitsitse mpatuko uliwonse kuti tikhale pa ubale wolimba ndi Atate wathu wakumwamba.

6. Kodi mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene akuyenda mwa mzimu kukhala ndi makhalidwe otani?

6 Paulo anatchula mpatuko wopembedza mafano limodzi ndi “ntchito za thupi” monga dama ndi khalidwe lotayirira. Koma anafotokoza kuti: “Anthu amene ali a Khristu Yesu, anapachika thupi pamodzi ndi zikhumbo zake, ndi zilakolako zake. Ngati tikukhala mwa mzimu, tiyeninso tipitirize kuyenda molongosoka mwa mzimu womwewo.” (Agalatiya 5:19-21, 24, 25) Kodi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imathandiza anthu amene akukhala komanso kuyenda mwa mzimu, kukhala ndi makhalidwe otani? Paulo analemba kuti: “Zipatso za mzimu ndizo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa.” (Agalatiya 5:22, 23) Tiyeni tikambirane zipatso za mzimu zimenezi.

‘Kondanani Wina ndi Mnzake’

7. Kodi chikondi ndi chiyani, ndipo tingachidziwe bwanji?

7 Munthu amene ali ndi chikondi, chimene ndi chimodzi mwa zipatso za mzimu, amasangalala kwambiri ndi anthu ena ndipo sadzikonda, ndiponso amapanga ubwenzi wolimba ndi anthuwo. Malemba amanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” Amatero chifukwa chakuti iye ndiye chimake cha chikondi. Chikondi chachikulu chimene Mulungu ndi Mwana wake ali nacho pa anthu chimaonekera pa nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. (1 Yohane 4:8; Yohane 3:16; 15:13; Aroma 5:8) Ife amene timatsatira Yesu timadziwika ndi chikondi chimene tili nacho pa wina ndi mnzake. (Yohane 13:34, 35) Pajatu timalamulidwa “kukondana wina ndi mnzake.” (1 Yohane 3:23) Ndiponso Paulo ananena kuti chikondi n’choleza mtima ndi chokoma mtima. Sichichita nsanje, ndipo sichidzitama, sichichita zosayenera, kapena kusamala zofuna zake zokha. Chikondi sichikwiya ndipo sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekeza zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Ndiponso chikondi sichitha konse.​—1 Akorinto 13:4-8.

8. Kodi ndi chifukwa chiyani tiyenera kukonda anzathu amene timalambira nawo Yehova limodzi?

8 Tikalola mzimu wa Mulungu kubala chikondi mwa ife, chikondicho chimaonekera pa ubale wathu ndi Mulungu komanso anthu anzathu. (Mateyo 22:37-39) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake akali mu imfa. Aliyense amene amada m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu kulibe moyo wosatha kwa iye.” (1 Yohane 3:14, 15) Kale ku Isiraeli, munthu wopha mnzake ankapeza chitetezo m’mudzi wopulumukira pokhapokha ngati sanali kudana ndi munthu wophedwayo. (Deuteronomo 19:4, 11-13) Mzimu woyera ukamatitsogolera, timakonda Mulungu, olambira anzathu, ndi anthu ena.

“Chimwemwe cha Yehova Ndicho Mphamvu Yanu”

9, 10. Kodi chimwemwe n’chiyani, ndipo ndi zinthu zotani zimene zimatipatsa chimwemwe?

9 Mawu akuti chimwemwe amatanthauza chisangalalo chachikulu. Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo.” (1 Timoteyo 1:11; Salmo 104:31) Mwana wake amakondwera kuchita chifuniro cha Atate wake. (Salmo 40:8; Aheberi 10:7-9) Ndipo “chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu” yathu.​—Nehemiya 8:10.

10 Tikamachita chifuniro cha Mulungu, ngakhale m’nthawi ya mavuto, chisoni, kapena chizunzo, timakhala osangalala chifukwa cha chimwemwe chimene Mulungu amatipatsa. Timasangalala ‘tikamudziwadi Mulungu.’ (Miyambo 2:1-5) Timakhala pa ubale wosangalatsa ndi Mulungu ngati timamudziwa bwino ndiponso ngati timamukhulupirira ndi kukhulupiriranso nsembe ya dipo ya Yesu. (1 Yohane 2:1, 2) Ndifenso achimwemwe chifukwa chakuti tili ndi ubale weniweni padziko lonse. (Zefaniya 3:9; Hagai 2:7) Chiyembekezo chathu cha Ufumu ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino zimatipatsanso chimwemwe. (Mateyo 6:9, 10; 24:14) Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha chimatipatsanso chimwemwe. (Yohane 17:3) Popeza tili ndi chiyembekezo chodabwitsa chimenechi, tiyenera ‘kukondwera monsemo.’​—Deuteronomo 16:15.

Khalani Munthu Wamtendere ndi Woleza Mtima

11, 12. (a) Kodi mungati mtendere ndi chiyani? (b) Kodi mtendere wa Mulungu umatithandiza bwanji?

11 Munthu amene ali ndi mtendere, womwe ndi chipatso chinanso cha mzimu, amakhala munthu wa mtima waphee ndipo sada nkhawa. Atate athu a kumwamba ndi Mulungu wa mtendere, ndipo tikutsimikiziridwa kuti: “Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Salmo 29:11; 1 Akorinto 14:33) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga.” (Yohane 14:27) Kodi mtendere ukanathandiza bwanji otsatira ake?

12 Mtendere umene Yesu anapatsa ophunzira ake unakhazika pansi mitima ndi maganizo awo ndipo nkhawa zawo zinachepa. Mtenderewo unachuluka kwambiri atalandira mzimu woyera umene analonjezedwa. (Yohane 14:26) Popeza kuti timatsogoleredwa ndi mzimu ndiponso mapemphero athu amayankhidwa, ife masiku ano tili ndi “mtendere wa Mulungu” wosayerekezeka umene umakhazika pansi mitima ndi maganizo athu. (Afilipi 4:6, 7) Ndiponso mzimu wa Yehova umatithandiza kuchita zinthu modekha ndi mwamtendere tikakhala ndi okhulupirira anzathu komanso anthu ena.​—Aroma 12:18; 1 Atesalonika 5:13.

13, 14. Kodi kuleza mtima ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima?

13 Kuleza mtima kumafanana ndi mtendere, chifukwa ndi kupirira kwathu moleza mtima wina akatiputa kapena kutilakwira, tili ndi chikhulupiriro chakuti zinthu zikhala bwino. Mulungu ndi woleza mtima. (Aroma 9:22-24) Nayenso Yesu ali ndi mtima umenewu. Ifenso titha kupindula ndi mtima wa Yesuwo, chifukwa Paulo analemba kuti: “Anandichitira chifundo kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa koposa, monga chitsanzo kwa amene adzam’khulupirira iye kuti akapeze moyo wosatha.”​—1 Timoteyo 1:16.

14 Kuleza mtima kumatithandiza kupirira, ena akatilankhulira kapena kutichitira zinthu mopanda chifundo kapena nzeru. Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Atesalonika 5:14) Popeza kuti tonsefe ndi opanda ungwiro ndipo timalakwa, m’pake kuti timafuna kuti anzathu azileza nafe mtima tikalakwa. Choncho, tiziyesetsa “kukhala oleza mtima mwachimwemwe.”​—Akolose 1:9-12.

Sonyezani Kukoma Mtima ndi Ubwino

15. Nenani tanthauzo la kukoma mtima, ndipo tchulani zitsanzo zake.

15 Munthu wokoma mtima amakhala ndi chidwi ndi anzake ndipo amawalankhula bwino ndi kuwathandiza. Yehova ndi Mwana wake ndi okoma mtima. (Aroma 2:4; 2 Akorinto 10:1) Atumiki a Mulungu ndi Khristu ayeneranso kukhala okoma mtima. (Mika 6:8; Akolose 3:12) Ngakhalenso anthu oti sali pa ubale ndi Mulungu asonyeza kwambiri “kukoma mtima kwa umunthu.” (Machitidwe 27:3; 28:2) Ngati anthu ena amatero, kuli bwanji ifeyo? Tiyenera kukhala okoma mtima ngati ‘tikupitiriza kuyenda mwa mzimu.’

16. Kodi tiyenera kusonyeza kukoma mtima pakachitika zinthu zotani?

16 Timasonyeza kukoma mtima ngakhale ngati wina watipsetsa mtima potilankhula mawu opweteka kapena potichitira zinthu mosatiganizira. Paulo anati: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi. . . . Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aefeso 4:26, 27, 32) Ndi bwino makamaka kukomera mtima anthu amene ali ndi mayesero. Komabe, mkulu mumpingo sikuti angakhale akusonyeza kukoma mtima ngati akulephera kupereka uphungu wa m’Malemba chifukwa choopa kukhumudwitsa munthu amene zikuonekeratu kuti akusiya njira ya ‘chabwino ndi cholungama ndi choona.’​—Aefeso 5:9.

17, 18. Kodi ubwino ndi chiyani, ndipo khalidwe limeneli ndi lofunika bwanji pamoyo wathu?

17 Ubwino ndiwo khalidwe labwino limene munthu wabwino amakhala nalo. Mulungu ndi wabwino pa chilichonse. (Salmo 25:8; Zekariya 9:17) Yesunso ndi wabwino. Komabe, iye sanalole kuti atchedwe “Wabwino,” munthu wina atamutchula kuti “Mphunzitsi Wabwino” pofuna kumulemekeza. (Maliko 10:17, 18) Sanalole chifukwa chakuti anazindikira kuti Mulungu ndiye chimake cha ubwino.

18 Ife timalephera kukhala abwino chifukwa cha uchimo wobadwa nawo. (Aroma 5:12) Ngakhale ndi choncho, tingasonyeze khalidwe limeneli ngati tipemphera kwa Mulungu kuti ‘atiphunzitse ubwino.’ (Salmo 119:66, NW) Paulo anauza okhulupirira anzake ku Roma kuti: “Inenso ndine wotsimikiza mtima za inu kuti inunso ndinu odzala ubwino, mmene mwakhalira odziwa zinthu zonse.” (Aroma 15:14) Woyang’anira wachikhristu ayenera kukhala “wokonda zabwino.” (Tito 1:7, 8) Tikamatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, tidzadziwika ndi ubwino, ndipo Yehova adzakumbukira zabwino zimene timachita.​—Nehemiya 5:19; 13:31.

“Chikhulupiriro Chopanda Chinyengo”

19. Malinga ndi Aheberi 11:1, kodi chikhulupiriro ndi chiyani?

19 Chikhulupiriro, chomwenso ndi chipatso cha mzimu, “ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) Ngati tili ndi chikhulupiriro, timadziwa kuti zonse zimene Yehova walonjeza zidzachitikadi. Umboni wotsimikizika wa zinthu zosaonekazo ndi wamphamvu kwambiri moti umboniwo ukunenedwa kukhala chikhulupiriro. Mwachitsanzo, chilengedwe chimatitsimikizira kuti Mlengi alipo. Chikhulupiriro chathu chidzakhala chotere ngati tipitiriza kuyenda mwa mzimu.

20. Kodi ‘tchimo lotikola mosavuta’ ndi chiyani, ndipo tingalipewe bwanji pamodzi ndi ntchito za thupi?

20 Kusowa chikhulupiriro ndi ‘tchimo lotikola mosavuta.’ (Aheberi 12:1) Tifunikira kudalira mzimu wa Mulungu kuti tipewe ntchito za thupi, kukonda chuma, ndi ziphunzitso zonama zimene zingawononge chikhulupiriro chathu. (Akolose 2:8; 1 Timoteyo 6:9, 10; 2 Timoteyo 4:3-5) Mzimu wa Mulungu umathandiza atumiki amakono a Yehova kukhala ndi chikhulupiriro ngati chimene mboni zakale Chikhristu chisanayambe ndi anthu enanso a m’Baibulo anali nacho. (Aheberi 11:2-40) Ndipo “chikhulupiriro [chathu] chopanda chinyengo” chingalimbitse chikhulupiriro cha ena.​—1 Timoteyo 1:5; Aheberi 13:7.

Khalani Ofatsa ndi Odziletsa

21, 22. Kodi kufatsa ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ofatsa?

21 Kufatsa ndiko kukhala ndi mtima ndi khalidwe lodekha. Ndipo Mulungu ndi wofatsa. Tikudziwa zimenezi chifukwa chakuti Yesu, amene anali munthu wofatsa, anaonetsa mwangwiro umunthu wa Yehova. (Mateyo 11:28-30; Yohane 1:18; 5:19) Kodi pamenepa chofunika ndi chiyani kwa ife atumiki a Mulungu?

22 Akhristufe tiyenera ‘kusonyeza kufatsa kwa anthu onse.’ (Tito 3:2) Timaonetsa kufatsa muutumiki wathu. Anthu oyenerera mwauzimu amalangizidwa kuwongolera Mkhristu amene walakwa “ndi mzimu wachifatso.” (Agalatiya 6:1) Tonsefe tikamasonyeza ‘kudzichepetsa ndi kufatsa,’ timakhala tikulimbikitsa umodzi ndi mtendere wachikhristu. (Aefeso 4:1-3) Timakhala ofatsa ngati sitisiya kuyenda mwa mzimu ndi kukhala odziletsa.

23, 24. Kodi kudziletsa ndi chiyani, ndipo kumatithandiza bwanji?

23 Kudziletsa kumatithandiza kuganiza, kulankhula, ndi kuchita zinthu mosamala. Yehova anakhala ‘wodziletsa’ kwa Ababulo amene anawononga Yerusalemu. (Yesaya 42:14, Malembo Oyera) Mwana wake ‘anatisiyira chitsanzo’ cha kudziletsa povutika. Ndipo mtumwi Petulo analangiza Akhristu anzake ‘kuwonjezera kudziletsa pa kudziwa zinthu.’​—1 Petulo 2:21-23; 2 Petulo 1:5-8.

24 Akulu mumpingo ayenera kukhala odziletsa. (Tito 1:7, 8) Ndipotu, onse amene amatsogoleredwa ndi mzimu woyera amakhala odziletsa ndipo amapewa chiwerewere, kutukwana, kapena zinthu zilizonse zimene Yehova amadana nazo. Tikalola mzimu wa Mulungu kutithandiza kukhala odziletsa, anthu ena amaona zimenezi chifukwa cha kalankhulidwe ndi khalidwe lathu labwino.

Pitirizani Kuyenda mwa Mzimu

25, 26. Kodi tikamayenda mwa mzimu, zinthu zimakhala bwanji panopa ndipo zidzakhala bwanji m’tsogolo?

25 Tikamayenda mwa mzimu, timakhala alaliki achangu a Ufumu. (Machitidwe 18:24-26) Timakhala mabwenzi abwino, ndipo anthu onse, makamaka odzipereka kwa Mulungu, amakonda kucheza nafe. Popeza timatsogoleredwa ndi mzimu woyera, timalimbikitsanso mwauzimu anzathu amene timalambira nawo Yehova. (Afilipi 2:1-4) Kodi pali Mkhristu amene sangafune kukhala wotere?

26 M’dziko limene Satana akulamulirali, ndi zovuta kuyenda mwa mzimu. (1 Yohane 5:19) Ngakhale zili choncho, anthu mamiliyoni akuchita zimenezi masiku ano. Ngati tikhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, tidzakhala ndi moyo wabwino panopa ndipo tidzapitiriza mpaka muyaya kuyenda m’njira zolungama za Mulungu wachikondi amene amapereka mzimu woyera.​—Salmo 128:1; Miyambo 3:5, 6.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ‘tikamayenda mwa mzimu,’ ubale wathu ndi Mulungu ndi Mwana wake umakhala wotani?

• Kodi ndi makhalidwe ati amene ali zipatso za mzimu woyera?

• Kodi tingasonyeze bwanji zipatso za mzimu wa Mulungu?

• Kodi tikamayenda mwa mzimu, moyo wathu umakhala bwanji panopa, nanga m’tsogolo zinthu zidzakhala bwanji?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Mzimu woyera wa Yehova umatilimbikitsa kukonda okhulupirira anzathu

[Chithunzi patsamba 24]

Sonyezani kukoma mtima mwa kulankhula mawu olimbikitsa ndi kuthandiza ena