Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nzeru Itchinjiriza”

“Nzeru Itchinjiriza”

“Nzeru Itchinjiriza”

LEMBA la Miyambo 16:16 limati: “Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golidi, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?” N’chifukwa chiyani nzeru ili yamtengo wapatali kwambiri? N’chifukwa choti “nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Kodi nzeru imasunga bwanji “moyo wa eni ake” a anzeruyo?

Kukhala ndi nzeru yaumulungu, kapena kuti kudziwa Mawu a Mulungu molondola n’kumawatsatira, kumatithandiza kuyenda m’njira yovomerezeka kwa Yehova. (Miyambo 2:10-12) Mfumu Solomo ya Isiraeli wakale inati: “Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.” (Miyambo 16:17) N’zoonadi, nzeru imateteza eni ake kunjira zoipa ndiponso imasunga moyo wawo. Mawu anzeru ndiponso osapita m’mbali a pa Miyambo 16:16-33, amasonyeza mmene tingapindulire ndi nzeru yaumulungu m’moyo wathu watsiku ndi tsiku, m’zolankhula zathu, ndi m’zochita zathu. *

“Kufatsa Mtima”

Nzeru akuiyerekezera ndi munthu, ndipo nzeruyo ikuti: “Kunyada, ndi kudzikuza . . . ndizida.” (Miyambo 8:13) Kunyada sikuyenderana ndi nzeru ngakhale pang’ono. Tiyenera kusamala kwambiri kuti tisakhale ndi mtima wodzikuza kapena wosamva za ena. Tiyenera kusamala makamaka ngati zinthu zina zikutiyendera bwino pamoyo wathu kapena ngati tapatsidwa udindo winawake mumpingo.

Lemba la Miyambo 16:18 limachenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” Taganizirani za munthu amene anawonongeka m’njira imeneyi, kapena kuti kugwera m’vuto lalikulu kwambiri m’chilengedwe chonse. Munthu ameneyu anali mngelo wangwiro wa Mulungu ndipo anadzipanga yekha kukhala Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9) Iyeyutu anasonyeza mtima wonyada asanagwe m’vutolo. Baibulo limanena za mtima umenewu likamati munthu amene watembenuka posachedwa asaikidwe kukhala woyang’anira mu mpingo “kuwopera kuti angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada n’kugwa m’chiweruzo chimene chinaperekedwa kwa Mdyerekezi.” (1 Timoteyo 3:1, 2, 6) Ndi bwino kusamala kwambiri kuti tisamachite zinthu zolimbikitsa ena kukhala ndi mtima wonyada, komanso ifeyo tiziyesetsa kusakhala ndi mtima wonyada.

“Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.” Limatero lemba la Miyambo 16:19. Sitingavutike kuvomereza mawu amenewa tikaona zomwe zinam’chitikira Nebukadinezara, yemwe anali wolamulira wa ufumu wakale wa Babulo. Chifukwa chonyada, mfumuyi inaimika fano lalikulu kwambiri, mwinamwake loimira iyeyo, kuchigwa cha Dura. Mwina fanolo analiimika pa malo okwera zedi moti linkaonekera m’mwamba kwambiri, mamita 27 kuchokera pansi. (Danieli 3:1) Cholinga cha Nebukadinezara poimika fano lalitali kwadzaonenili chinali choti likhale chizindikiro chogometsa anthu cha ufumu wake. N’zoona ndithu kuti anthu amagoma ndi zinthu zoterezi monga zipilala, ndiponso nyumba zosanja zitalizitali, koma zinthu zimenezi Mulungu saziona ngati kanthu. N’chifukwa chake wamasalmo anaimba kuti: “Angakhale Yehova n’ngokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziwira kutali.” (Salmo 138:6) Ndipotu “chimene chili chapamwamba kwa anthu n’chonyansa m’maso mwa Mulungu.” (Luka 16:15) Ndi bwino kuti ifeyo tizichita zinthu modzichepetsa m’malo ‘modziyesa anzeru.’​—Aroma 12:16.

‘Phunzitsani Milomo Yanu’

Kodi kukhala ndi nzeru kumasintha bwanji zimene timalankhula? Mfumu yanzeruyi inati: “Wolabadira mawu adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala. Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera; ndipo kukoma kwa milomo kuyenjezera kuphunzira. Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru. Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake.”​Miyambo 16:20-23.

Nzeru imachenjeza m’kamwa mwathu ndi kuphunzitsa milomo yathu, kutanthauza kuti imatithandiza kulankhula zinthu moganizira bwino ndiponso mokopa. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa choti munthu amene ali wanzerudi amayesetsa ‘kupeza zabwino,’ kapena kuti kuona zabwino m’nkhani inayake, ndipo ‘amakhulupirira Yehova.’ Tikamayesetsa kupeza zabwino mwa ena, sizivuta kulankhula zabwino zokhudza iwowo. Sitilankhula mosaganizira ena, kapena mwamtopola, koma mwaulemu ndiponso mokopa. Kumvetsa bwino zimene zikuchitika m’moyo wa anthu ena kumatithandiza kumvetsetsa mavuto amene iwowo akulimbana nawo.

Kulankhula mwanzeru n’kofunikanso kwambiri tikamagwira ntchito yathu yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Tikamaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu, cholinga chathu sikungowauza Malemba ayi, koma kuwafika pamtima. Zimenezi zimafuna kuti tiphunzitse milomo yathu kulankhula mokopa. Mtumwi Paulo analimbikitsa mnzake Timoteyo kuti apitirize kuchita zinthu zimene ‘anakhutitsidwa nazo.’​—2 Timoteyo 3:14, 15.

Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo, (An Expository Dictionary of New Testament Words) lolembedwa ndi W.E. Vine, limati mawu a Chigiriki otanthauza kuti ‘kukhutitsidwa’ amatanthauza, “kusintha maganizo chifukwa choganizira mfundo zinazake kapena kuona makhalidwe enaake.” Kuti tithe kukhutiritsa, kapena kuti kukopa munthu amene tikulankhula naye, timafunika kumvetsa bwino maganizo ake, zimene amakonda, mmene zinthu zilili pamoyo wake, ndiponso mmene anakulira. Kodi tingatani kuti timvetse zinthu zimenezi? Mtumwi Yakobe anati: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobe 1:19) Tingathe kudziwa zimene zili mumtima mwa munthuyo mwa kumufunsa mafunso ndiponso kumvetsera bwino zimene akunena.

Mtumwi Paulo anali ndi luso zedi pankhani yokopa anthu. (Machitidwe 18:4) Moti ngakhale Demetiriyo, munthu wosula siliva yemwe ankatsutsa Pauloyo, anafika ponena kuti “si mu Efeso mokha mmene wakopa anthu ambirimbiri ndi kuwapatutsira ku chikhulupiriro china. Wachita zimenezi pafupifupi m’chigawo chonse cha Asiya. Akumanena kuti yopangidwa ndi manja si milungu ayi.” (Machitidwe 19:24-26) Kodi Paulo ankadzitama chifukwa cha luso lake lolalikira? Ayi. Iye ankaona kuti ntchito yake yolalikira ndi “mphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 2:4, 5) Nafenso timathandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova. Chifukwa choti timakhulupirira Yehova, sitikayikira ngakhale pang’ono kuti angatithandize tikamayesetsa kulankhula mwanzeru ndiponso mokopa muutumiki wathu.

Motero n’zosabwitsa kuti “wanzeru mtima”amatchedwa wochenjera,”kapena kuti wozindikira. (Miyambo 16:21) Inde, nzeru yotereyi ndi “kasupe wa moyo” kwa anthu amene ali nayo. Nanga bwanji anthu opusa? Iwo ‘amanyoza nzeru ndi mwambo.’ (Miyambo 1:7) Kodi kusamvera chilango cha Yehova kumawabweretsera zotani? Amapitiriza kulangidwa, ndipo nthawi zambiri chilango chake chimakhala chachikulu kwambiri. Monga tanenera pamwambapa, Solomo anati: “Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.” (Miyambo 16:22) Anthu opusa angathenso kudziika m’mavuto, kudzichititsa manyazi, kudziputira matenda, ndiponso kufa msanga.

Popitiriza kunena mmene nzeru zimasinthira zolankhula zathu, mfumu ya Isiraeli inati: “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” (Miyambo 16:24) Monga uchi wotsekemera, mawu okoma amalimbikitsa ndi kutsitsimula. Uchi umathandizanso kuti munthu akhale wathanzi ndiponso ndi mankhwala. Ndi mmene mawu okoma alili; amathandiza munthu kukhala wathanzi mwauzimu.​—Miyambo 24:13, 14.

Chenjerani ndi ‘Njira Yooneka Ngati Yoongoka’

Solomo anati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 16:25) Limeneli ndi chenjezo lakuti tisamaganize molakwika ndiponso tisamachite zinthu zotsutsana ndi malamulo a Mulungu. Njira inayake ingaoneke ngati yoongoka kwa munthu koma kwenikweni ingakhale yotsutsana ndi mfundo zolungama za Mawu a Mulungu. Komanso, Satana angathe kulimbikitsa chinyengo choterechi moti munthu angalimbikire kuchita zinthu zimene akuganiza kuti n’zolondola, koma kwenikweni zili zoika moyo pachiswe.

Njira yabwino kwambiri yodzitetezera kuti tisadzinyenge tokha ndiyo kukhala ndi mtima wanzeru ndiponso wozindikira, komanso kukhala ndi chikumbumtima chabwino chimene munthu amakhala nacho chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu. Posankha zochita pamoyo, kaya n’zokhudza makhalidwe abwino, kupembedza kapena nkhani zina zilizonse, njira yabwino kwambiri yodzitetezera kuti tisamadzinyenge ndiyo kutsatira mfundo za Mulungu pankhani ya zabwino ndi zoipa.

“Wantchito Adzigwirira Yekha Ntchito”

Mfumu yanzeruyi inapitiriza kunena kuti: “Wantchito adzigwirira yekha ntchito; pakuti m’kamwa mwake mum’fulumiza.” (Miyambo 16:26) Pamenepa Solomo ankatanthauza kuti wantchito amalimbikira ntchito yake chifukwa choopa njala. Baibulo lina (An American Translation ) limamasulira lembali kuti: “Njala imam’chititsa munthu kulimbikira kugwira ntchito kuti apeze chakudya.” Zinthu zachibadwa monga kufuna kudya, zingatithandize kulimbikira ntchito. Zinthu zimenezi zingathe kutipindulitsa. Komano, kodi chingachitike n’chiyani tikamafuna chinthu chinachake mopitirira muyezo? Zimene zimachitika n’zofanana ndi zimene zimachitika ngati moto umene mumawotha panja wagwira tchire n’kusanduka moto wolusa. Dyera ndilo chilakolako cha munthu chimene chapitirira malire ndipo lingathe kupweteketsa anthu. Poganizira zoopsa zimenezi, munthu wanzeru amasamala ngakhale ndi zilakolako zabwino zimene ali nazo.

‘Musayende M’njira Yosakhala Bwino’

Mawu amene timalankhula angathe kukhala oononga ngati moto wolusa. Ponena za kuopsa kwa mtima wokonda kuona zolakwa za ena n’kumazilengeza, Solomo ananena kuti: “Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa; ndipo m’milomo mwake muli moto wopsereza. Munthu wokhota amautsa makani; kazitape afetsa ubwenzi.”​Miyambo 16:27, 28.

Munthu amene amachita zinthu zofuna kuipitsa mbiri ya mnzake ndi “wopanda pake.” Tiziyesetsa kuona zabwino za anzathu ndi kunena zinthu zochititsa ena kuwapatsa ulemu. Nanga bwanji zomamvetsera anthu amene amafalitsa miseche? M’posavuta kuti miseche yawoyo ichititse anthu kuyamba kukayikirana, kudana ndiponso kuchititsa anthu kugawikana mumpingo. Nzeru imatipangitsa kupewa kumvetsera anthu amenewa.

Pochenjeza za chinthu china chimene chingathe kukopa munthu mosavuta, n’kutsatira njira yolakwika, Solomo anati: “Munthu wachiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m’njira yosakhala bwino. Wotsinzina ndiye aganizira zokhota; wosunama afikitsa zoipa.”​Miyambo 16:29, 30.

Kodi zingatheke kuti olambira oona akopeke ndi zachiwawa? Anthu ambiri masiku ano akhala akukodwa mumsampha ‘woganizira zokhota.’ Amachita kapena kulimbikitsa anzawo kuchita zachiwawa. N’kutheka kuti sizitivuta kupewa kuchita zinthu zachiwawa. Komatu n’zotheka kukopeka ndi zachiwawa mosadziwa. Ndipotu pali anthu ambiri amene akopeka n’kuyamba kuonerera zachiwawa kapena masewera olimbikitsa chiwawa. Malemba amachenjeza momveka bwino kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Ndithu, nzeru yaumulungu imatiteteza kwambiri.

Kodi tinganene chiyani za munthu amene wakhala moyo wake wonse akuyenda mwanzeru ndiponso mozindikira, ‘wosayendapo m’njira yosakhala bwino’? Mulungu amasangalala ndi munthu amene akukhala moyo wolungama ndipotu munthu wokhala moyo woterewu n’ngofunika kulemekezedwa. Lemba la Miyambo 16:31 limati: “Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m’njira ya chilungamo.”

Komano mkwiyo wosaletseka ulibe pabwino pake. Kaini, yemwe anali mwana woyamba wa Adamu ndi Hava ‘anam’kwiyira kwambiri’ m’bale wake Abele ndipo anamumenya n’kumupha.’ (Genesis 4:1, 2, 5, 8) Ngakhale kuti nthawi zina timatha kukwiya pa zifukwa zomveka, tizipewa kukwiya mosadziletsa. Lemba la Miyambo 16:32 limanena momveka bwino kuti: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” Kukwiya mosadziletsa sikusonyeza uchamuna kapena khalidwe lililonse losiririka. Kumangosonyeza kuti munthuyo ali ndi vuto ndipo kungathe kum’chititsa ‘kuyenda m’njira yosakhala bwino.’

Kulola ‘Yehova Kuti Alongosole Zonse’

“Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse,” inatero mfumu ya Isiraeli. (Miyambo 16:33) Mu Isiraeli wakale, nthawi zina Yehova ankalola anthu kugwiritsa ntchito maere pofuna kuwadziwitsa chifuniro chake. Anthuwo ankachita maere pogwiritsira ntchito miyala kapena matabwa. Choyamba, ankapempha Yehova kuti awauze chochita ndipo kenaka miyala kapena matabwawo ankawapukusa m’thumba la mkanjo ndiyeno n’kuwatulutsa. Choncho, chilichonse chimene maerewo asonyeze ankachiona kuti chachokera kwa Mulungu.

Yehova anasiya kugwiritsa ntchito maere pouza anthu ake zimene akufuna. Ananena zofuna zake m’Mawu ake, Baibulo. Kudziwa molondola zinthu zofotokozedwa m’Baibulo n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi nzeru yaumulungu. Motero, tisamalole m’pang’ono pomwe tsiku kudutsa popanda kuwerenga Malemba ouziridwa.​—Salmo 1:1, 2; Mateyo 4:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Lemba la Miyambo 16:1-15, lafotokozedwa mwatsatanetsatane mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2007, masamba 17-20.

[Chithunzi patsamba 8]

N’chifukwa chiyani nzeru imapambana golidi?

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi n’chiyani chimathandiza kuti tiphunzitse milomo yathu tikakhala mu utumiki?

[Chithunzi patsamba 10]

“Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa”

[Chithunzi patsamba 11]

Mkwiyo wosaletseka ungachititse munthu ‘kuyenda m’njira yosakhala bwino’

[Chithunzi patsamba 12]

Zachiwawa zingathe kukopa munthu