Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pirirani Poyembekezera Tsiku la Yehova

Pirirani Poyembekezera Tsiku la Yehova

Pirirani Poyembekezera Tsiku la Yehova

‘Wonjezerani chipiriro pa chikhulupiriro chanu.’​—2 PETULO 1:5, 6.

1, 2. Kodi kupirira n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani Akhristu afunika kupirira?

TSIKU lalikulu la Yehova layandikira kwambiri. (Yoweli 1:15; Zefaniya 1:14) Panthawi imeneyi Yehova adzaonetsa kuti ulamuliro wake ndi woyenerera. Ife Akhristu amene timayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu, tikuyembekezera mwachidwi nthawi imeneyo. Pakali pano, timadedwa, kunyozedwa, kuzunzidwa, ndi kuphedwa kumene chifukwa cha chikhulupiriro chathu. (Mateyo 5:10-12; 10:22; Chivumbulutso 2:10) Zimenezi zimafuna kupirira, kapena kuti kukhalabe olimba pokumana ndi mavuto. Mtumwi Petulo akutilimbikitsa kuti: ‘Wonjezerani chipiriro pa chikhulupiriro chanu.’ (2 Petulo 1:5, 6) Timafunika kupirira chifukwa Yesu anati: “Iye amene adzapirira mpaka mapeto, ndiye amene adzapulumuka.”​—Mateyo 24:13.

2 Nthawi zinanso timadwala, timaferedwa, komanso timakumana ndi mavuto ena ambiri. Satana amasangalala kwambiri tikataya chikhulupiriro chathu. (Luka 22:31, 32) Koma Yehova angatithandize kupirira mavuto osiyanasiyana. (1 Petulo 5:6-11) Pali zitsanzo zambiri zosonyeza kuti titha kupirira poyembekezera tsiku la Yehova popanda kutaya chikhulupiriro chathu.

Akupirira Ngakhale Akudwala

3, 4. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti n’zotheka kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale tikudwala.

3 Tikamadwala, Mulungu satichiritsa mozizwitsa koma amatipatsa mphamvu yoti tithe kupirira. (Salmo 41:1-3) Mlongo wina dzina lake Sharon anati: “Ndakhala ndikuyenda pa njinga ya anthu olemala kuyambira kalekale. Ndinabadwa ndi matenda opha ziwalo ndipo sindinasangalale ndi moyo ngati ana anzanga.” Sharon analimba mtima ataphunzira kuti Yehova walonjeza kudzapatsa anthu thanzi labwino. Ngakhale kuti amalankhula ndi kuyenda movutikira, amasangalala ndi utumiki wake wachikhristu. Zaka 15 zapitazo, iye anati: “Inde, ndine wodwaladwala koma kukhulupirira Mulungu ndi ubale wanga ndi iye, zimandithandiza kukhalabe wolimba. Ndikusangalala kwambiri kukhala ndi anthu a Yehova ndi kuona Yehova akundithandiza nthawi zonse.”

4 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Tesalonika ‘kulankhula molimbikitsa kwa a mtima wachisoni.’ (1 Atesalonika 5:14) Zinthu monga kukhumudwa kwambiri zingachititse munthu kuvutika maganizo. Mu 1993, Sharon analemba kuti: “Chifukwa chodziona ngati munthu wolephereratu, ndinadwala matenda ovutika maganizo kwa zaka zitatu. . . . Akulu anandilimbikitsa ndi kundilangiza. . . . Kudzera mu Nsanja ya Olonda, Yehova anatithandiza kudziwa zambiri za matenda ovutika maganizo. Umenewu ndi umboni wakuti iye amasamalira anthu ake ndipo amamvetsa mavuto awo.” (1 Petulo 5:6, 7) Sharon akutumikirabe Mulungu mokhulupirika ndipo akuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova.

5. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Akhristu atha kupirira akamasowa mtendere?

5 Akhristu ena amasowa mtendere chifukwa cha zimene zinawachitikira m’mbuyomo. Mwachitsanzo Harley anamenya nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse motero ankalota maloto oopsa a nkhondoyo. Ali m’tulo, ankafuula kuti: “Thawa akuwombera! Bisala!” Akadzidzimuka, ankapezeka kuti wanyoweratu ndi thukuta. Ngakhale kuti anali ndi moyo wotere, anayamba kutumikira Mulungu, ndipo patapita nthawi maloto otere anachepa.

6. Kodi Mkhristu wina anapirira bwanji vuto lake losokonezeka maganizo?

6 Mkhristu wina atamupeza ndi matenda osokonezeka maganizo, zinkamuvuta kulalikira khomo ndi khomo. Koma analimbikira podziwa kuti iyeyo, ndi anthu olabadira uthenga, adzapeza moyo chifukwa cha kulalikira. (1 Timoteyo 4:16) Nthawi zina zinkamuvuta ngakhale kugogoda pa chitseko. Iye ananena kuti: “Ndikalephera kugogoda panyumba ina, ndinkadzilimbitsa ndi kupita pa nyumba yotsatira n’kukayesanso kugogoda. Chifukwa chosasiya kulalikira, thanzi langa lauzimu linakhalabe lolimba.” M’bale ameneyu zinkamuvutanso kuti apezeke pa misonkhano koma ankadziwa ubwino wa mayanjano achikhristu. Choncho, ankayesetsabe kupitako.​—Aheberi 10:24, 25.

7. Kodi anthu amene amaopa kulankhula pa gulu kapena kupita ku misonkhano, amasonyeza bwanji kupirira?

7 Akhristu ena ali ndi vuto lochita mantha kwambiri. Mwachitsanzo, ena amaopa kulankhula pa gulu kapena kupita ku misonkhano. Zimakhala zovuta kwa anthu amenewa kuyankha pa misonkhano kapena kukamba nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Komabe, akuyesetsa ndipo timawayamikira kwambiri chifukwa chobwera ku misonkhano ndi kulankhulapo.

8. Kodi chimathandiza kwambiri n’chiyani kuti munthu apirire ngati akuvutika maganizo?

8 Kupuma ndi kugona mokwanira kungathandize munthu kupirira ngati akuvutika maganizo. Mwinanso angafunikire thandizo la kuchipatala. Komanso kudalira Mulungu ndi kupemphera kumathandiza kwambiri. Lemba la Salmo 55:22 limati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Choncho, ‘khulupirirani Yehova ndi mtima wanu wonse.’​—Miyambo 3:5, 6.

Kupirira Panthawi Yachisoni

9-11. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira munthu amene timakondana naye akamwalira? (b) Kodi chitsanzo cha Anna chingatithandize bwanji kupirira tikaferedwa?

9 Wina m’banja akamwalira, banjalo limakhala ndi chisoni chachikulu. Abulahamu analira Sara mkazi wake atamwalira. (Genesis 23:2) Ngakhale Yesu, munthu wangwiro, “anagwetsa misozi” Lazaro bwenzi lake atamwalira. (Yohane 11:35) Choncho ndi chibadwa kumva chisoni munthu amene mumakondana naye akamwalira. Komabe, Akhristu amadziwa kuti akufa adzauka. (Machitidwe 24:15) N’chifukwa chake iwo ‘sachita chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo amachitira.’​—1 Atesalonika 4:13.

10 Kodi tingapirire bwanji panthawi yachisoni? Mwachitsanzo, mnzathu akapita paulendo, sitikhala achisoni mpaka kalekale popeza timadziwa kuti tidzaonana naye akadzabwera. Motero munthu amene anali Mkhristu wokhulupirika akamwalira, sitikhala ndi chisoni chachikulu chifukwa chodziwa kuti iye adzauka.​—Mlaliki 7:1.

11 Kudalira “Mulungu wa chitonthozo chonse” ndi mtima wathu wonse kungatithandize kupirira panthawi yachisoni. (2 Akorinto 1:3, 4) Kuganiziranso zimene Anna mkazi wamasiye anachita kungatithandize. Mwamuna wake anamwalira atakhala m’banja zaka 7 zokha. Koma ankachitabe utumiki wopatulika kwa Yehova pakachisi mpaka ali ndi zaka 84. (Luka 2:36-38) Mosakayikira, moyo wopembedza unamuthandiza kuti apirire chisoni ndi kusungulumwa kwake. Ifenso tikamachita ntchito zachikhristu nthawi zonse, kuphatikizapo kulalikira za Ufumu, timapirira panthawi yachisoni.

Kupirira Mavuto Osiyanasiyana

12. Kodi Akhristu ena apirira vuto lotani lokhudza banja?

12 Akhristu ena amapirira mavuto okhudzana ndi banja. Mwachitsanzo, mwamuna kapena mkazi akachita chigololo, banja lonse limavutika kwambiri. Chifukwa cha kuwawidwa mtima, wosalakwayo angamasowe tulo ndipo atha kumangolira. Angamavutike kugwira ntchito ngakhale zing’onozing’ono moti angamangolakwitsa zinthu kapena kuchita ngozi. Angamalephere kudya, angaonde, ndipo angamavutike maganizo. Ngakhalenso kugwira ntchito zachikhristu kungavute. Ndipo zimenezi zingasokonezenso ana kwambiri.

13, 14. (a) Kodi pemphero la Solomo potsegulira kachisi limakulimbikitsani bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha mzimu woyera?

13 Tikakhala pa mavuto otere, Yehova amatithandiza. (Salmo 94:19) Mulungu amamva mapemphero a anthu ake. Pemphero limene Mfumu Solomo anapereka potsegulira kachisi wa Yehova limatsimikizira zimenezi. Popemphera, Solomo anati: “Pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisiraeli, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake ku nyumba ino; pamenepo mverani inu m’mwamba mokhala inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene inu mum’dziwa mtima wake, popeza inu, inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu; kuti aope inu masiku onse akukhala iwowo m’dziko limene inu munapatsa makolo awo.”​—1 Mafumu 8:38-40.

14 Zimathandizanso kwambiri kupempha mzimu woyera. (Mateyo 7:7-11) Zipatso zina za mzimu ndi chimwemwe ndi mtendere. (Agalatiya 5:22, 23) Atate wathu wakumwamba akayankha mapemphero athu, timapeza mpumulo kwambiri. M’malo mwa chisoni, timakhala ndi chimwemwe ndiponso m’malo mwa kuwawidwa mtima, timakhala ndi mtendere.

15. Kodi ndi malemba ati amene angatithandize kuchepetsa nkhawa?

15 M’pake kukhala ndi nkhawa tikamapirira mavuto. Koma nkhawa zathu zina zingachepe ngati titakumbukira mawu a Yesu akuti: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu chimene mudzadya kapena chimene mudzamwa, kapena matupi anu chimene mudzavala. . . . Chotero pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu], ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyo 6:25, 33, 34) Mtumwi Petulo akutilimbikitsa ‘kutulira Mulungu nkhawa zathu zonse, pakuti amasamala za ife.’ (1 Petulo 5:6, 7) Tikakhala ndi vuto, ndi bwino kuyesetsa kuthana nalo. Koma ngati tachita zonse zimene tingathe, ndi bwino kupemphera chifukwa kungoda nkhawa sikuthandiza. Wamasalmo anaimba kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.”​—Salmo 37:5.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani sizingatheke kukhala opandiratu nkhawa? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tikatsatira lemba la Afilipi 4:6, 7?

16 Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Popeza ndife mbadwa za Adamu zopanda ungwiro, sizingatheke kukhala opanda nkhawa. (Aroma 5:12) Mwachitsanzo, Esau atakwatira akazi Achihiti, “anapweteka mtima” wa Isake ndi wa Rebeka, makolo ake oopa Mulungu. (Genesis 26:34, 35) Akhristu ena monga Timoteyo ndi Terofimo anali ndi nkhawa chifukwa cha matenda. (1 Timoteyo 5:23; 2 Timoteyo 4:20) Paulo ankaderanso nkhawa okhulupirira anzake. (2 Akorinto 11:28) Koma “wakumva pemphero” sataya anthu amene amamukonda.​—Salmo 65:2.

17 Pamene tikuyembekezera tsiku la Yehova, “Mulungu wa mtendere” amatithandiza ndi kutitonthoza. (Afilipi 4:9) Yehova ndi “wachifundo ndi wachisomo,” ndi “wabwino, ndi wokhululukira,” ndipo “akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Eksodo 34:6; Salmo 86:5; 103:13, 14) Chotero, ‘zopempha zathu zidziwike kwa iye’ kuti tikhale ndi “mtendere wa Mulungu” wopambana nzeru za anthu.

18. Mogwirizana ndi Yobu 42:5, kodi zimatheka bwanji ‘kupenya’ Mulungu?

18 Mapemphero athu akayankhidwa, timadziwa kuti Mulungu ali nafe. Yobu atapirira mayesero ake anati: “Kumva ndidamva mbiri yanu [Yehova], koma tsopano ndikupenyani maso.” (Yobu 42:5) Poganizira zimene Mulungu watichitira, tingathe ‘kumupenya’ ndi maso ozindikira, achikhulupiriro, ndi oyamikira, mosiyana ndi mmene tinkamuonera poyamba. Tikadziwa Mulungu motere, timakhala ndi mtendere mumtima ndi m’maganizo.

19. Kodi chimachitika ndi chiyani ‘tikatulira Yehova nkhawa zathu zonse’?

19 ‘Tikatulira Yehova nkhawa zathu zonse,’ titha kupirira mavuto tili ndi mtendere umene umateteza mtima ndi maganizo athu. Timamva mumtima mwathu kuti tamasuka ku nkhawa ndi mantha ndipo maganizo athu amakhazikika.

20, 21. (a) Kodi nkhani ya Sitefano imasonyeza bwanji kuti titha kukhala osatekeseka pozunzidwa? (b) Perekani chitsanzo cha masiku ano cha anthu amene sanatekeseke pozunzidwa.

20 Wophunzira Sitefano anaonetsa mtima wosatekeseka popirira chiyeso choopsa cha chikhulupiriro chake. Asanapereke umboni womaliza, onse a mu Bungwe Lalikulu la Ayuda “anaona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.” (Machitidwe 6:15) Nkhope yake inali yosatekeseka ngati ya mngelo, mthenga wa Mulungu. Sitefano atawanena poyera kuti ndiwo anapha Yesu, oweruzawo “zinawalasa mu mtima nayamba kum’kukutira mano.” Koma Sitefano, “pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemerero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.” Masomphenyawo anamulimbikitsa ndipo anakhulupirika mpaka imfa. (Machitidwe 7:52-60) Ngakhale kuti ife sitiona masomphenya, Mulungu atha kutipatsa mtima wosatekeseka pozunzidwa.

21 Tamverani mawu onenedwa ndi Akhristu amene anaphedwa ndi Anazi panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Pofotokoza zimene zinachitika ali m’khoti, wina analemba kuti: “Atagamula kuti ndikaphedwe, ine ndinakhala duu. Ndipo nditanena mu mtima kuti, ‘Khala wokhulupirika mpaka imfa,’ ndi mawu enanso a Ambuye wathu, ndinati basi zateremu zatha. . . . Koma musadandaule. Chifukwa ndili ndi mtendere wosasimbika moti mtima wanga uli zii!” Mkhristu winanso wachinyamata ataweruzidwa kuti akanyongedwe, analembera makolo ake kuti: “Pano nthawi yadutsa kale 12 koloko pakati pa usiku. Ndidakali ndi nthawi yoti ndisinthe maganizo anga. Koma kodi ndingakhalenso wokondwa m’dzikoli ngati nditakana Ambuye? Ayi ndithu. Ndikukutsimikizirani kuti ndikusiyana nalo dzikoli ndili ndi mtendere ndiponso chimwemwe.” Sitikukayika kuti Yehova amathandiza atumiki ake okhulupirika.

Nanunso Mutha Kupirira

22, 23. Kodi mungakhale ndi chikhulupiriro chotani ngati mukupirira poyembekezera tsiku la Yehova?

22 Mwina inu simungakumane ndi mavuto amene tafotokozawa. Komabe, munthu woopa Mulungu Yobu ananena zoona kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Mwina ndinu bambo kapena mayi amene mukuyesetsa kuphunzitsa ana anu malangizo a m’Baibulo. Anawo afunika kupirira mayesero kusukulu. Koma mudzasangalala kwambiri kuona ana anu akumvera Yehova ndi kutsatira mfundo zake zolungama. Mwinanso mukukumana ndi mavuto kapena mayesero kuntchito. Mutha kupirira mavuto amenewa ndi enanso ambiri chifukwa chakuti ‘tsiku ndi tsiku, Yehova akukusenzerani katundu.’​—Salmo 68:19.

23 Mungadzione ngati munthu wamba, koma musaiwale kuti Yehova sadzaiwala ntchito yanu ndi chikondi chimene mwasonyeza pa dzina lake loyera. (Aheberi 6:10) Mothandizidwa ndi Mulungu, mutha kupirira ziyeso za chikhulupiriro chanu. Choncho, muziona kuti nkhani yochita chifuniro cha Mulungu ndi yofunika kwambiri popemphera ndi posankha zochita. Mukatero, mudzakhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu adzakudalitsani ndi kukuthandizani ndipo mudzapirira poyembekezera tsiku la Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu amafunika kupirira?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira tikamadwala kapena tikaferedwa?

• Kodi pemphero limatithandiza bwanji kupirira mavuto?

• N’chifukwa chiyani tingati n’zotheka kupirira poyembekeza tsiku la Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Kudalira Yehova kumatithandiza kupirira pa nthawi yachisoni

[Chithunzi patsamba 31]

Pemphero lochokera pansi pa mtima limatithandiza kupirira ziyeso za chikhulupiriro chathu