Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pita Ukasambe M’dziwe la Siloamu”

“Pita Ukasambe M’dziwe la Siloamu”

“Pita Ukasambe M’dziwe la Siloamu”

YESU atachiritsa munthu wosaona ndi dothi lonyowa, anauza munthuyo kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu.” Munthuyo anachita zimene anauzidwazo ndipo “anabwerako akuona.” (Yohane 9:6, 7) Kodi dziwe la Siloamu linali kuti? Zimene akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza posachedwapa zingathandize kuyankha funsoli.

Alendo ambiri okacheza ku Yerusalemu amakafika ku malo otchedwa Dziwe la Siloamu, poganiza kuti limeneli ndilo dziwe la Siloamu lotchulidwa m’Baibulo pa Yohane 9:7. Malowa ali cha kumapeto kwa ngalande ya Hezekiya, yomwe ndi yayitali mamita 530 ndipo inakumbidwa cha m’ma 700 B.C.E. Komatu dziwe limeneli lakhala lilipo kuyambira cha m’ma 300 C.E. Dziweli linakumbidwa ndi anthu omwe ankanena kuti ndi Akhristu mu ufumu wa Byzantine, omwe ankaganiza kuti dziwe lotchulidwa m’buku la uthenga wabwino wa Yohane linali pamenepa.

Komabe m’chaka cha 2004, akatswiri ofukula za m’mabwinja anapeza malo amene akuti ndi pamene panali Dziwe la Siloamu la m’nthawi ya Yesu. Malowa ali pamtunda wa mamita pafupifupi 100 kuchokera kum’mwera chakum’mawa kwa malo amene anthu ankaganiza kuti ndiye dziwe la Siloamu. Kodi zinatani kuti akatswiriwa atulukire malo amenewa? Akuluakulu a boma anaganiza zokonza paipi yotulutsa zonyansa za mderali. Choncho, anatumiza antchito okhala ndi zimagalimoto zokumbira. Katswiri wofukula za m’mabwinja yemwe ankagwira ntchito pafupi ndi malowa, ankaonetsetsa zomwe zimachitika ndipo anaona masitepe awiri. Ntchito yokonza paipiyo inaimitsidwa kaye ndipo bungwe loona za zinthu zakale la kumeneko (Israeli Antiquities Authority) linavomereza zoti malowo afukulidwe. Mbali imodzi ya dziwelo inali yozama mamita pafupipafupi 70, ndipo panopa afukula kale mbali ziwiri za dziwelo.

Pofukula malowa, anapeza ndalama zingapo zachitsulo ndipo zina mwa ndalamazo n’zomwe Ayuda ankagwiritsa ntchito panthawi yomwe anapandukira Aroma m’zaka za pakati pa 66 ndi 70 C.E. Zaka zimene zinalembedwa pa ndalamazi zimapereka umboni wakuti Dziwe la Siloamu linkagwirabe ntchito mpaka mu 70 C.E., pamene Aroma anawononga mzinda wa Yerusalemu. Buku lina (Biblical Archaeology Review) limati: “Zikuoneka kuti dziweli linkagwirabe ntchito mpaka pamene Ayuda anapanduka, ndipo kenako linasiyidwa. Malowa ali m’dera lotsika kwambiri la m’Yerusalemu. Anthu sanadzakhalenso ku malo amenewa mpaka mu ufumu wa Byzantine. Chaka ndi chaka, madzi a mvula ankabweretsa matope omwe ankakwirira dziweli. Ndipo pamene Aroma anawononga mzindawo, dziweli silinasamalidwenso. Patatha zaka zambiri, matope anadzadza ndipo dziwelo linakwiririka. Kuti apeze dziweli, akatswiriwa anachita kufukula matope ozama pafupifupi mamita atatu.”

N’chifukwa chiyani anthu amene amaphunzira Baibulo mwakhama ayenera kuchita chidwi ndi malo enieni amene panali Dziwe la Siloamu? N’chifukwa choti zimenezi zingawathandize kumvetsa bwino kumene kunali mzinda wa Yerusalemu, womwe umatchulidwatchulidwa m’mauthenga abwino onena za moyo wa Yesu ndi utumiki wake ali pa dziko lapansi.

[Chithunzi patsamba 7]

Dziwe la Siloamu limene alitulukira posachedwa

[Mawu a Chithunzi]

© 2003 BiblePlaces.com