Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikhulupiriro cha Mayi Wina Chinapambana Vuto Lalikulu

Chikhulupiriro cha Mayi Wina Chinapambana Vuto Lalikulu

Chikhulupiriro cha Mayi Wina Chinapambana Vuto Lalikulu

“Ngati mukuwerenga kalatayi, ndiye kuti opaleshoni yanga sinayende bwino, ndipo sitionananso.”

AMENEWA ndi mawu oyamba a kalata yomwe mayi wina wachikhristu, dzina lake Carmen, analembera ana ake aakazi atatu a zaka 25, 19 ndi 16. Ndipotu opaleshoniyo sinayendedi bwino, moti n’zomvetsa chisoni kuti Carmen anamwalira.

Kusiya ana aakazi atatu mwanjira imeneyi n’kopweteka kwambiri kwa wina aliyense. Komabe, mayiyu ankakhulupirira kwambiri Yehova ndiponso malonjezo ake, motero anapambana vutoli chifukwa chikhulupiriro chakecho chinkamupatsa mtendere wa mumtima. Zimenezi zikuonekera bwino m’kalata yokhudza mtima yomwe mayiyu analemba. Taonani zimene analembera ana akewo.

“Choyamba, ndikufuna kukuuzani kuti ndimakukondani ndi mtima wanga wonse. . . . Ndinu ana abwino kwambiri, ndipo ndimakunyadirani.

“Ndikanakonda kukhalabe nanu mpaka dziko latsopano limene Mulungu walonjeza . . . , komabe popeza mwina sizingatheke, ndapempha Mulungu kuti akuthandizeni kukhalabe okhulupirika kwa iye. Tapirira limodzi mavuto ambiri, ndipo Yehova sanayambe watitayapo. . . . Chotero pitirizani kudalira malangizo amene Yehova amapereka kudzera m’gulu lake, ndiponso pitirizani kuchita zinthu limodzi ndi mpingo komanso akulu. Ngati mungathe muzilalikira nthawi zonse, ndipo muzikonda abale onse.

“Tingosiyana kwa kanthawi kochepa. . . . Ndikupempha kuti mundikhululukire pa zonse zomwe ndinakulakwirani, ndiponso panthawi zomwe sindinakumvetsetseni, kapena panthawi zimene sindinakuuzeni kuti ndimakukondani kwambiri. . . . Ndikudziwa kuti pali zinthu zimene aliyense wa inu amafunikira. Yehova amadziwa bwino zimenezo kuposa inuyo, ndipo adzakupatsani zonse zimene mumafunikirazo, komanso adzakufupani pa zonse zimene mwakhala mukupirira.

“Musaiwale cholinga chanu chodzalowa m’dziko latsopano, ndipo pitirizani kuchita zonse zomwe mungathe kuti mudzalowe m’dzikolo. Yehova akudalitseni ndiponso akupatseni mphamvu kuti mukhalebe okhulupirika mpaka mapeto. . . . Ana anga okondedwa, musakhumudwe. Ndimakukondani.”

Munthu aliyense angakumane ndi tsoka panthawi ina iliyonse. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.” (Mlaliki 9:11) Komabe, anthu amene amakhulupirira kwambiri Mulungu, angavomereze mawu amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, kapena moyo, . . . kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 8:38, 39; Aheberi 6:10.