Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amakuonani?

Kodi Mulungu Amakuonani?

Kodi Mulungu Amakuonani?

KODI Yehova yemwe ndi Mlengi Wamkulu amaona? Inde. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti: “Kodi Iye wakuumba diso n’ngosapenya?” (Salmo 94:9) Yehova amaona kwambiri kuposa anthu. Sikuti amangoona mmene timaonekera kunja, komanso ‘amayesa mitima.’ (Miyambo 17:3; 21:2) Ndithudi, iye amatha kudziwa zimene tikuganiza, zolinga zathu komanso zimene mtima wathu ukukhumba.

Yehova amadziwanso mavuto amene timakumana nawo pamoyo wathu, ndipo amatipatsa zimene tapempha. Wamasalmo analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:15, 18) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amamvetsa zimene timakumana nazo ndiponso kuti amayankha mapemphero athu ochokera pansi pamtima.

Yehova Mulungu amaona ngakhale zinthu zomwe timachita m’malo obisika. Indedi, “zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (Aheberi 4:13) Choncho kaya zochita zathu ndi zabwino kapena zoipa, Mulungu amaona zonsezo. (Miyambo 15:3) Mwachitsanzo, lemba la Genesis 6:8, 9 limati, “Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova” ndiponso kuti “anayendabe ndi Mulungu.” Yehova anayanja ndi kudalitsa Nowa chifukwa ankamumvera ndiponso ankatsatira mfundo zake zolungama. (Genesis 6:22) Mosiyana ndi Nowa, anthu a m’nthawi yake anali achiwawa ndiponso amakhalidwe oipa. Zimenezi Mulungu ankazidziwa. “Anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” Pamapeto pake, Yehova anawononga anthu oipawo koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake.​—Genesis 6:5; 7:23.

Kodi inuyo, Yehova adzakuyanjani? Maso a Yehova “ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Ndipotu posachedwapa adzachotsa anthu onse oipa padziko lapansi ndi kupulumutsa anthu ofatsa.​—Salmo 37:10, 11.