Kodi Mungatani Kuti Mukhaledi Munthu Wauzimu?
Kodi Mungatani Kuti Mukhaledi Munthu Wauzimu?
MTUMWI Paulo analemba kuti: “Kuika maganizo pazinthu za thupi ndiko imfa, koma kuika maganizo pazinthu za mzimu ndiko moyo ndi mtendere.” (Aroma 8:6) Mawu amenewa akusonyeza kuti kukhala munthu wauzimu si nkhani yamakonda a munthu chabe. Koma ndi nkhani ya moyo kapena imfa. Nangano kodi munthu wauzimu amakhala bwanji ndi “moyo ndi mtendere”? Malinga ndi zimene Baibulo limanena, munthu wotero amakhala wopanda nkhawa ndipo amakhala pa mtendere ndi Mulungu panopa. Komanso adzakhala ndi moyo wosatha m’tsogolo. (Aroma 6:23; Afilipi 4:7) N’chifukwa chake Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.
Kuwerenga kwanu magazini imeneyi ndi umboni wakuti mumakonda zinthu zauzimu, ndipo mukuchita bwino. Komabe, anthu amasiyana maganizo kwambiri pankhani imeneyi, choncho mungafune kudziwa kuti: ‘Kodi munthu wauzimu tingamudziwe bwanji?’
“Maganizo a Khristu”
Mtumwi Paulo atatchula za kufunika ndiponso ubwino wokonda zauzimu, anafotokozanso zambiri za mmene tingadziwire munthu wauzimu. Polankhula ndi Akhristu a mumzinda wakale wa Korinto, iye anafotokoza kusiyana pakati pa munthu wa thupi, amene amatsata zilakolako za thupi, ndi munthu wauzimu, amene amakonda kwambiri zinthu zauzimu. Analemba kuti: “Munthu wa kuthupi salandira zinthu za mzimu wa Mulungu, chifukwa amaziona ngati zopusa.” Kenako Paulo anafotokoza kuti munthu wauzimu amakhala ndi “maganizo a Khristu.”—1 Akorinto 2:14-16.
Kukhala ndi “maganizo a Khristu” kumatanthauza kukhala ndi ‘mtima umene unalinso mwa Khristu Yesu.’ (Aroma 15:5; Afilipi 2:5, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu) Kunena kwina, munthu wauzimu ndi munthu amene amaganiza ngati Yesu ndipo amatsatira mapazi Ake. (1 Petulo 2:21; 4:1) Choncho, munthu amakhala wauzimu akamaganiza kwambiri ngati Khristu ndipo n’chapafupi kwa iye kupeza “moyo ndi mtendere.”—Aroma 13:14.
Mmene Mungadziwire “Maganizo a Khristu”
Kuti munthu akhale ndi maganizo a Khristu, afunika choyamba kudziwa maganizo amenewo. Choncho, choyamba chimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wauzimu ndi kudziwa mmene Yesu amaganizira. Komabe kodi mungadziwe bwanji maganizo a munthu amene anakhalako zaka 2,000 zapitazo? Mwina tifunse chonchi, kodi mumadziwa bwanji anthu akale otchuka a m’dziko lanu? Mosakayikira, mumachita kuwerenga za iwo. Mofananamo, kuwerenga mbiri ya Yesu ndiko njira yaikulu imene mungadziwire maganizo a Khristu.—Yohane 17:3.
Pali mabuku anayi odalirika onena mwatsatanetsatane mbiri ya moyo wa Yesu. Mabuku amenewa ndi Uthenga Wabwino wa Mateyo, Maliko, Luka, ndi Yohane. Mukamawerenga nkhani zimenezi, zidzakuthandizani kuzindikira kaganizidwe ka Yesu, mtima wake, ndiponso cholinga cha zinthu zimene anachita. Mukamawerenga ndi kusinkhasinkha za Yesu, mumakhala ndi chithunzi chonse cha mmene iye analili. Ngakhale ngati panopa mumaona kuti ndinu wotsatira wa Khristu, kuwerenga ndi kusinkhasinkha kumeneko kudzakuthandizani ‘kupitiriza kukula m’kukoma mtima kwa m’chisomo ndi kum’dziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’—2 Petulo 3:18.
Kuti timvetse chifukwa chake Yesu anali munthu Yohane 13:15.
wauzimu, tiyeni tione ndime zina za m’Mauthenga Abwino. Kenako, yesani kuona kuti mungatengere bwanji chitsanzo chake.—Munthu Wauzimu Amaonetsa “Zipatso za Mzimu”
Uthenga Wabwino wa Luka umati Yesu atabatizidwa, mzimu woyera wa Mulungu unatsanulidwa pa iye ndipo anakhala ‘wodzazidwa ndi mzimu woyera.’ (Luka 3:21, 22; 4:1) Yesu nayenso anawaphunzitsa otsatira ake za kufunika kotsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. (Genesis 1:2; Luka 11:9-13) Kodi n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwambiri? N’chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu uli ndi mphamvu yosintha maganizo a munthu kuti akhale ngati a Khristu. (Aroma 12:1, 2) Mzimu woyera umathandiza munthu kukhala ndi makhalidwe ngati “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa.” Makhalidwe amenewa, amene Baibulo limawatcha “zipatso za mzimu,” ndi amene amasonyeza kuti munthuyo alidi wauzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Mwachidule tingati munthu wokonda zinthu zauzimu, ndi munthu amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu.
Yesu anasonyeza zipatso za mzimu pautumiki wake wonse. Mmene ankachitira ndi anthu amene ankaonedwa ngati otsika, zimasonyeza bwino kuti anali munthu wachikondi, wokoma mtima, ndi wabwino. (Mateyo 9:36) Mwachitsanzo, taganizirani nkhani imene mtumwi Yohane analemba. Timawerenga kuti: “Pamene [Yesu] anali kuyenda anaona munthu wakhungu chibadwire.” Ophunzira a Yesu anaonanso munthu ameneyo koma anangoti ndi wochimwa. Choncho iwo anafunsa Yesu kuti: ‘Anachimwa ndani? Ndi iyeyu kapena makolo ake?’ Nawonso anansi a munthuyo ankamuona, koma onse ankangoti ndi wopemphapempha. Iwo anati: “Si uyu kodi amene anali kukhala pansi n’kumapemphapempha?” Koma Yesu ataona munthuyo, anazindikira kuti ndi munthu wofunika thandizo. Analankhula naye munthu wakhunguyo ndi kumuchiritsa.—Yohane 9:1-8.
Kodi nkhani imeneyi imatiphunzitsa chiyani za maganizo a Khristu? Choyamba, Yesu sananyalanyaze anthu otsika koma anawachitira chifundo. Chachiwiri, ankayamba ndi iye kuthandiza ena. Kodi inuyo mukutsatira chitsanzo cha Yesu chimenechi? Kodi mumaona anthu ngati mmene Yesu ankawaonera, n’kuwathandiza kuti atukule moyo wawo ndi kukhala ndi tsogolo labwino? Kapena kodi mumakonda anthu opeza bwino ndi kunyalanyaza anthu osauka? Ngati mumaona anthu mmene Yesu ankawaonera, ndiye kuti mukutsatira chitsanzo chake.—Salmo 72:12-14.
Munthu Wauzimu Amakonda Kupemphera
Nkhani za m’Mauthenga Abwino zimasonyeza kuti Yesu ankapemphera kwa Mulungu nthawi zambiri. (Maliko 1:35; Luka 5:16; 22:41) Ali pa dziko lapansi, Yesu ankachita kupatula nthawi yopemphera. Wophunzira Mateyo analemba kuti: “Atauza anthuwo kuti apite, [Yesu] anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.” (Mateyo 14:23) Yesu ankapeza mphamvu akamalankhula kwayekha ndi Atate wake wakumwamba. (Mateyo 26:36-44) Masiku anonso, anthu auzimu amayesetsa kupeza mpata wolankhula ndi Mulungu. Amadziwa kuti kuchita zimenezi kumalimbitsa ubale wawo ndi Mlengi ndi kuwathandiza kukhala ndi maganizo a Khristu.
Nthawi zambiri Yesu ankapemphera nthawi yaitali. (Yohane 17:1-26) Mwachitsanzo, asanasankhe atumwi ake 12, Yesu “anapita ku phiri kukapemphera, ndipo anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.” (Luka 6:12) Ngakhale kuti kwenikweni anthu auzimu sapemphera usiku wonse, iwo amatsatirabe chitsanzo cha Yesu. Asanapange zosankha zazikulu pamoyo wawo, amakhala ndi nthawi yokwanira yopemphera kwa Mulungu kuti mzimu woyera uwathandize kupanga zosankha zimene zingalimbitse moyo wawo wauzimu.
M’mapemphero ake, Yesu anasonyezanso mtima umene ife tiyenera kutengera popemphera. Taonani zimene Luka analemba za mmene Yesu anapempherera usiku kutatsala tsiku limodzi kuti afe. ‘Pokhala Iye m’chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu.’ (Luka 22:44, Buku Lopatulika) M’mbuyomo, Yesu anali atapempherapo kolimba. Koma nthawiyi atakumana ndi chiyeso chachikulu kwambiri pamoyo wake, anapemphera “kolimba koposa ndithu” ndipo pemphero lake linayankhidwa. (Aheberi 5:7) Munthu wauzimu amatsatira chitsanzo cha Yesu. Akakumana ndi mavuto aakulu kwambiri, amapemphera “kolimba koposa ndithu” kuti Mulungu amupatse mzimu woyera, amutsogolere, ndi kumuthandiza.
Popeza kuti Yesu ankapemphera kwambiri, n’zosadabwitsa kuti ophunzira anafunitsitsa kutengera chitsanzo chake. N’chifukwa chake anamupempha kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Masiku anonso, anthu amene amaona kufunika kwa zinthu zauzimu ndipo amafuna kutsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu amatengera chitsanzo cha Yesu popemphera. Munthu amene alidi wauzimu amapemphera.
Munthu Wauzimu Amalalikira Uthenga Wabwino
Uthenga Wabwino wa Maliko umasimba nkhani yakuti Yesu anachiritsa anthu ambiri odwala mpaka usiku. Kutacha m’mawa mwake Yesu ali yekha kokapemphera, atumwi ake anabwera ndi kumuuza kuti anthu ambiri akumufunafuna, mwina kuti awachiritse. Koma Yesu anawauza kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire kumenekonso.” Kenako anapereka chifukwa chake kuti: “Pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.” (Maliko 1:32-38; Luka 4:43) Ngakhale kuti kuchiritsa anthu kunali kofunika kwa Yesu, ntchito yake yaikulu inali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Maliko 1:14, 15.
Masiku ano, anthu amene ali ndi maganizo a Khristu amadziwika chifukwa chouza ena za Ufumu wa Mulungu. Yesu analamula onse ofuna kukhala otsatira ake kuti: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyo 28:19, 20) Ndiponso, Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” (Mateyo 24:14) Popeza kuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ntchito yolalikira imatheka ndi mphamvu ya mzimu woyera, aliyense amene amachita nawo ntchitoyo mwachangu amasonyeza kuti alidi munthu wauzimu.—Machitidwe 1:8.
Kuti uthenga wa Ufumu ulalikidwe pa dziko lonse, pamafunika anthu mamiliyoni ambiri kuti agwirizane pogwira ntchito imeneyi. (Yohane 17:20, 21) Anthuwo amafunika kukhala okonda zinthu zauzimu komanso ayenera kukhala ndi dongosolo labwino logwirira ntchitoyi padziko lonse. Kodi mukuwadziwa anthu amene akutsatira mapazi a Khristu ndipo amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse?
Kodi Ndinu Munthu Wauzimu?
Kunena zoona, pali zinthu zambiri zimene tingadziwire munthu wauzimu. Koma pa zimene takambiranazi, kodi mungati inuyo ndinu munthu wauzimu? Ngati mukufuna kudziwa, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimawerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, tsiku ndi tsiku ndi kusinkhasinkha zimene ndawerengazo? Kodi ndimaonetsa zipatso za mzimu pamoyo wanga? Kodi ndimakonda kupemphera? Kodi ndimalakalaka kugwirizana ndi anthu amene akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse?’
Ngati mutadzifufuza nokha moona mtima, mungathe kudziwa ngati ndinu munthu wauzimu kapena ayi. Tikukulimbikitsani kuchita zimene mungathe panopa kuti mupeze “moyo ndi mtendere.”—Aroma 8:6; Mateyo 7:13, 14; 2 Petulo 1:5-11.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
MMENE MUNGADZIWIRE MUNTHU WAUZIMU
◆ Amakonda Mawu a Mulungu
◆ Amaonetsa zipatso za mzimu
◆ Amapemphera kwa Mulungu ndi mtima wonse
◆ Amauza ena uthenga wabwino wa Ufumu
[Chithunzi patsamba 5]
Baibulo limathandiza munthu kudziwa “maganizo a Khristu”