Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zozizwitsa” Ziwiri pa Msonkhano Umodzi ku Georgia

“Zozizwitsa” Ziwiri pa Msonkhano Umodzi ku Georgia

“Zozizwitsa” Ziwiri pa Msonkhano Umodzi ku Georgia

M’CHAKA cha 2006, ku Georgia kunachitika msonkhano wosaiwalika, chifukwa panachitika “zozizwitsa” ziwiri. Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti “Chipulumutso Chayandikira” unachitika kwa masiku atatu kuyambira pa 7 mpaka pa 9 July, m’madera 6 a dzikolo. Anthu 17,000 anasangalala ndi phwando lauzimu limeneli.

Mu January 2006, anayamba kufufuza malo oyenerera oti anthu masauzande ambiri adzasonkhaneko mu mzinda wa Tbilisi, likulu la dziko la Georgia, komwe kunali kudzachitikira msonkhanowu. M’madera enawo, msonkhanowu anthu anali kudzaumvera kudzera pa telefoni.

Ufulu wa kulambira wakhala ukuwonjezereka pang’onopang’ono m’dziko la Georgia pa zaka zingapo zapitazo. Choncho, mosasamala kanthu za chitsutso chimene chinalipo m’dzikolo, Mboni zinafufuza mwakhama malo ochitirako msonkhano, zili ndi chikhulupiriro choti awapeza mu likulu la dzikolo. Anthu a ku Georgia ndi ansangala ndiponso okonda kuchereza mwachikhalidwe chawo. Komabe pankhani za chipembedzo, tsankho linazika mizu m’mitima ya anthu ena a maudindo. Ndiye kodi akanasintha maganizo awo n’kulola kuti Mboni zipeze malo ochitirako msonkhano?

Abale a mu Komiti ya Msonkhano anakafufuza mabwalo a masewera angapo ndiponso maholo akuluakulu. Oyang’anira malowo analonjeza kuti adzawabwereka, koma kenako anasintha maganizo abalewo atatchula masiku enieni omwe ankafuna kugwiritsa ntchito malowo. Motero, abale a mu komitiyi anadabwa ataona kuti akuluakulu oyang’anira holo ya gulu lina lake loimba la ku Tbilisi avomera kuti Mboni za Yehova zidzagwiritse ntchito holo yawo. Holoyi ili pakatikati pa mzindawu, ndipo kumachitikira zinthu zambiri zotchuka.

Polimbikitsidwa kuti khama lawo lapindula, komitiyi inayamba kukonza msonkhano wa ku Tbilisi, komanso misonkhano ya m’matawuni ndi m’mizinda ina m’dziko lonselo, monga ku Tsnori, Kutaisi, Zugdidi, Kaspi, ndi ku Gori. Panali ntchito yaikulu yolumikiza matelefoni m’malo onsewa kuti anthu onse azidzamvera msonkhanowo panthawi imodzi. Chilichonse chinali m’malo mwake. Mwadzidzidzi, patangotsala sabata imodzi kuti msonkhano uyambe, akuluakulu oyang’anira holo ija anati Mboni zisagwiritse ntchito malowo. Iwo sanafotokoze chifukwa chimene anasinthira maganizo.

“Chozizwitsa” Choyamba

Kodi abalewa akanatani popeza nthawi inali itatha? Zomwe akanachita n’kupita ku Marneuli basi, dera laulimi lomwe lili pa mtunda wa makilomita 40 kuchokera mu mzinda wa Tbilisi. Kumeneko kwakhala kukuchitikira misonkhano yambiri panyumba ya banja lina la Mboni za Yehova. Poyamba, malowo anali munda waukulu kwambiri. Kwa zaka 10, anali malo okhawo omwe mipingo ya ku Tbilisi inkachitirako misonkhano. Komabe, ku Marneuli ndi komwenso Mboni za Yehova zakhala zikuvutitsidwa kwambiri ndi magulu a anthu achiwawa.

Chimodzi mwa ziwawa zimenezi chinachitika pa September 16, 2000. Apolisi a mu mzinda wa Marneuli anatseka misewu kuti Mboni zisafike ku malo a msonkhano. Kenako kunafika mabasi odzadza ndi anthu osokoneza, otsogoleredwa ndi Vasili Mkalavishvili, yemwe anachotsedwa pa unsembe m’tchalitchi cha Orthodox. Anthuwa anaimitsa magalimoto ndi mabasi omwe ankapita ku msonkhano wa ku Marneuli, anakokera kunja anthu omwe anali m’magalimotowo ndi kuwamenya mopanda chifundo, ndipo ena anawabera zinthu zonse kuphatikizapo Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo.

Nakonso kumalo a msonkhano ku Marneuli kunafika gulu la anthu ochita zachiwawa okwanira pafupifupi 60. Mboni pafupifupi 40 zinavulazidwa. M’bale wina anam’baya pamtima ndi mpeni. Ena mwa anthu a chiwawawo ankaopseza ndi mfuti zomwe ankawombera m’mwamba mosalekeza. M’modzi mwa anthuwa analozetsa mfuti mwini wa malowo, n’kumulamula kuti am’patse ndalama ndi zinthu zina zonga mphete, ndolo, ndi zibangiri zomwe ndi zamtengo wapatali. Gulu la chiwawali linafufuza pena paliponse m’nyumba ya mwini malo uja, yomwe inali kumapeto kwa mbali ina ya malowo, ndi kuba zinthu zake zofunikira. Ataswa mawindo onse a nyumbayo, anatentha mabuku ofotokoza za m’Baibulo ndi mabenchi omwe anakonzedwa kuti anthu adzakhalire pa msonkhanowo. Anthuwa anawononga mabuku okwana tani imodzi ndi theka. M’malo moletsa chiwawachi, apolisi omwe anali pamalowa ankathandiza gululi kuvutitsa Mboni. *

Kuwonjezera pa ziwawazi, Komiti ya Msonkhano inafunikiranso kuthana ndi vuto la kuchepa kwa malo. Malowa ankakwana anthu 2,500 koma panthawiyi ankayembekezera anthu 5,000. Ndiyeno akanatani popeza nthawi inali itatha kale? Zinangokhala ngati chozizwitsa kuona eni minda ina iwiri yoyandikana akuuza abalewa kuti awabwereka malo awo.

Sinali ntchito yophweka kusandutsa mindayo kukhala malo abwino ochitirapo msonkhano. Ntchitoyi inavuta kwambiri chifukwanso nyengo sinali bwino. Kutatsala mlungu umodzi kuti msonkhano uyambe, kunagwa mvula mlungu wonsewo. M’minda iwiri ija munali mbatata ndipo zinafunika kukumbidwa. Choyamba, anthu odzipereka anabwera mvula ili puu kudzakumba mbatatazo. Kenako anachotsa mipanda yotchinga mindayo ndipo anaimika mitengo kuti akhome denga loteteza anthu ku dzuwa ndi mvula. Pankafunika kukhoma mabenchi ena ndipo anawonjezeranso zokuzira mawu. Anthu ongodziperekawa ankacheka, kukhoma ndiponso kuboola matabwa usana ndi usiku, ndipo ena tulo sankationa n’komwe.

Aliyense ankadera nkhawa n’kumati, “Kodi zikhala bwanji ngati mvulayi ingapitirize kugwa mpaka masiku a msonkhano? Kodi anthu omwe adzabwere ku msonkhanowo sadzamira m’matope?” Anagula udzu kuti aike pansi ponyowapo. Kenako dzuwa linawala! Kwa masiku onse atatu a msonkhanowo, pansi panawombedwa dzuwa bwino.

Anthu odzamvera msonkhano atafika, anasangalala ndi mmene malowa ankaonekera. Ankangokhala ngati ali m’dziko latsopano pamalo a bata amenewa. Anthu omwe anafika ku msonkhanowu anakhala pa malo abwino ndipo kuzungulira malowa, kunali mitengo ya mkuyu, ya zipatso zina, komanso minda ya chimanga ndi tomato. Kuseli kwa pulatifomu anakongoletsako ndi mipesa. Pulogalamu ili mkati, anthu ankamva kulira kwa nkhuku mwa apa ndi apo pamene eni ake amatolera mazira. Kunkamvekanso phokoso losiyanasiyana la kumudzi, koma kwa anthu amene anali pa msonkhanopo, phokosoli limangokhala ngati nyimbo yosangalatsa. Silinkawasokoneza chifukwa ankamvetsera mwachidwi nkhani zabwino za m’Baibulo zomwe zinkakambidwa pa msonkhanowo. Komatu sizokhazi zomwe zinachititsa msonkhanowu kukhala wosaiwalika.

“Chozizwitsa” Chachiwiri

Pamapeto pa chigawo cha m’mawa cha tsiku Lachisanu, anthu osonkhana anadabwa kwambiri kumva M’bale Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, akulengeza za kutuluka kwa Baibulo lonse la Baibulo la Dziko Latsopano mu Chijojiya. * Anthu ambiri analibe chonena ndipo m’maso mwawo munalengeza misozi. Banja lina linanena mosangalala kuti: “Ntchito yaikulu yonseyi yagwirika pa nthawi yochepa yomweyi? Chimenechi n’chozizwitsa cha Yehova ndithu. Sitingaleke kuyamikira.”

Mlongo wina wochokera ku tawuni ya Tsalendjikha yemwe anamvetsera msonkhanowu pa telefoni atamufunsa anayankha kuti: “Sindingathe kufotokoza chimwemwe chomwe ndinali nacho pamene tinalandira Baibulo lonse lathunthu m’chinenero chathu. Ndikukuthokozani chifukwa cha msonkhano wosangalatsa kwambiri wa masiku atatu umenewu. Kunena zoona unalidi wosaiwalika.” Banja lina lochokera ku mpingo wina wa kumadzulo kwa Georgia, m’malire ndi Nyanga Yakuda, linati: “Kuyambira kalekale tinali ndi Baibulo limodzi lokha m’banja mwathu, koma tsopano tonse anayi aliyense ali ndi Baibulo lakelake la Baibulo la Dziko Latsopano. Tsopano aliyense angaphunzire Baibulo payekha.”

Komatu, kuti Baibuloli lituluke, panali zovuta zina zimene anthu ena sanazidziwe. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Mabaibulowa anasindikizidwa ndi kutumizidwa ku Georgia nthawi idakalipo pokonzekera msonkhano, akuluakulu oona za katundu wolowa ndi kutuluka m’dziko, analetsa zoti Mabaibulowa alowe m’dzikolo. Abale anakadandaula ku ofesi yomva madandaulo a anthu. Mkulu wa mu ofesiyi anathandiza abalewo ndipo Mabaibulowo anafika m’nthawi yabwino ndithu. Mpaka mkuluyu anatuma womuthandiza wake kupita ku msonkhano wa ku Marneuli kuti akalandire Mabaibulo atsopanowo odzaika mu ofesi yawo.

Kulandiridwa ndi Anthu a ku Georgia

Msonkhano wachigawo wa ku Marneuli unali wosaiwalika kwa Mboni za Yehova pachifukwa chinanso. Pamsonkhanopo panali m’bale wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Anthu onse pamsonkhanopo anasangalala kwambiri moti aliyense ankafunitsitsa kulonjerana naye mogwirizana ndi mwambo wa kumeneko. M’bale Jackson anafunika kuimirira ndi kupereka moni kwa abale ndi alongowo kwa nthawi yaitali, koma iye sanakhumudwe nazo.

Kalelo mu 1903, pamapeto pa msonkhano ngati womwewu, m’bale wina anati: “Ine ndine wosauka, koma sindingalole kusinthanitsa zabwino zomwe ndapeza pamsonkhanowu ndi ndalama zokwana madola 1,000.” Pambuyo pa zaka zoposa 100, Mboni zimene zinafika pa misonkhano yosaiwalika yomwe inachitika m’chilimwe cha chaka cha 2006, ku Georgia zinamvanso chimodzimodzi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kuti mumve zambiri za mmene Mboni za Yehova zinazunzikira ku Georgia, onani Galamukani! ya Chingelezi ya January 22, 2002, masamba 18 mpaka 24.

^ ndime 16 Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikristu mu Chijojiya linatulutsidwa mu 2004.

[Bokosi patsamba 19]

“Wamng’ono” Wakula

Mawu omwe ali pa Yesaya 60:22 akwaniritsidwa ku Georgia. Mawuwo amati: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthawi yake.” M’zaka zosakwana 20, chiwerengero cha ofalitsa Ufumu ku Georgia chakula kuchokera pa ofalitsa osakwana 100 kufika pa ofalitsa pafupifupi 16,000. Atumiki achangu a Mawu a Mulungu amenewa akuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba pafupifupi 8,000 mlungu uliwonse. Zimenezitu zikusonyeza kuti chiwerengero cha ofalitsa ku Georgia chipitiriza kukula.

[Chithunzi/Mapu patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

RUSSIAN FEDERATION

GEORGIA

⇨ Zugdidi

⇨ Kutaisi

Marneuli ⇨ Gori

⇨ Kaspi

⇨ Tsnori

TBILISI

TURKEY

ARMENIA

AZERBAIJAN

[Mawu a Chithunzi]

Globe: Based on NASA/​Visible Earth imagery

[Chithunzi patsamba 16]

Chosema cha ku Tbilisi

[Zithunzi patsamba 17]

Msonkhano wa ku Marneuli anaulumikiza ndi misonkhano ya m’madera ena asanu kudzera pa telefoni za m’manja

[Zithunzi patsamba 18]

Anthu pamsonkhanowo anasangalala kwambiri ndi kutuluka kwa Baibulo lonse la “Baibulo la Dziko Latsopano” mu Chijojiya