Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• M’Malemba Achigiriki Achikhristu, kodi mawu akuti “mpingo” agwiritsidwa ntchito m’njira zinayi ziti?

Mawuwa kwenikweni amanena za gulu lonse la Akhristu odzozedwa (m’mavesi ena amaphatikizaponso Khristu). Nthawi zina, mawu akuti “mpingo wa Mulungu” amatanthauza Akhristu onse omwe anakhalapo panthawi inayake. Tanthauzo lachitatu ndi la Akhristu onse okhala ku dera linalake. Pomaliza, mawuwa angathe kugwiritsidwa ntchito kutanthauza anthu a mumpingo umodzi wokha.​—4/15, masamba 21 mpaka 23.

• Kodi kusankha Akhristu opita kumwamba kunatha liti?

Baibulo silipereka yankho lachindunji la funso limeneli. Kuitana kumeneku kunayamba mu 33 C.E. ndipo kunapitirira mpaka masiku ano. Pambuyo pa chaka cha 1935 cholinga chachikulu cha ntchito yolalikira chinali kusonkhanitsa khamu lalikulu. Mzimu woyera wakhala ukuchitira umboni Akhristu ena amene anabatizidwa pambuyo pa 1935, kuti akakhala kumwamba. Motero, sitingatchule tsiku lenileni la kutha kwa ntchito yosankha Akhristu opita kumwamba. Odzozedwa enieni sakhala ndi mzimu woyera wambiri kuposa anzawo a nkhosa zina ndipo safunanso kuwachitira mautumiki ena apadera. Mosasamala kanthu kuti chiyembekezo chawo n’chotani, Akhristu onse ayenera kukhala okhulupirika ndi kupitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu.​—5/1, masamba 30 mpaka 31.

• Pamene Yefita ankawinda, kodi anali wokonzeka kupereka mwana wake wamkazi nsembe yopsereza kwa Mulungu?

Ayi sichoncho. Yefita ankatanthauza kuti adzapereka munthu amene adzakumane naye kuti azitumikira Mulungu nthawi zonse. Amenewa anali makonzedwe a Chilamulo cha Mose. (1 Samueli 2:22) Pokwaniritsa chowindacho, mwana wa Yefita anapitiriza kutumikira pa chihema. Chimenechi chinali chowinda chachikulu kwa mwanayo, chifukwa sakanadzakwatiwa moyo wake wonse.​—5/15, masamba 9 mpaka 10.

• Kodi mabuku akale anathandiza bwanji Akhristu oyambirira?

Zikuoneka kuti Akhristu ankagwiritsira ntchito kwambiri mipukutu mpaka cha m’ma 100 C.E. Koma m’zaka zina 100 zotsatira, panabuka mkangano pakati pa anthu amene ankakonda kugwiritsa ntchito mabuku akale ndi ena okonda kugwiritsa ntchito mipukutu. Akatswiri ena a nkhaniyi amakhulupirira kuti mabuku akalewa anatchuka kwambiri chifukwa choti Akhristu ankawakonda.​—6/1, masamba 14 mpaka 15.

• Kodi Kalendala ya ku Gezeri n’chiyani?

Kameneka ndi kamwala komwe kanatulukiridwa pa malo ena mu mzinda wa Gezeri m’chaka cha 1908. Anthu ambiri amaganiza kuti mwana wa sukulu ndiye analemba pakamwalako kuti akachongetse kwa aphunzitsi. Kamwalako kamasonyeza ndandanda yachidule yosonyeza kalendala ya zaulimi. M’kalendalayo anayamba n’kulemba za ntchito yokolola, m’mwezi womwe umayenderana ndi miyezi ya September ndi October, ndipo anatchula za mbewu zosiyanasiyana komanso ntchito zosiyanasiyana zomwe zinkachitika panthawiyo.​—6/15, tsamba 8.

• Kodi kuchimwira mzimu woyera kumatanthauza chiyani?

N’zotheka kuchimwira mzimu woyera wa Yehova, lomwe ndi tchimo losakhululukidwa. (Mateyo 12:31) Mulungu ndiye amadziwa ngati tachita tchimo losakhululukidwa ndipo angatichotsere mzimu wake. (Salmo 51:11) Ngati tili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha tchimo limene tachita, n’kutheka kuti ndife olapadi ndipo sitinachimwire mzimu.​—7/15, masamba 16 mpaka 17.

• Popeza Mfumu Sauli ankam’dziwa kale Davide, nanga n’chifukwa chiyani anamufunsa kuti anali mwana wa yani? (1 Samueli 16:22; 17:58)

Sauli sanali kungofuna kudziwa dzina la bambo ake a Davide. Sauli anafuna kudziwa kuti ndi munthu wotani amene anabereka mnyamata wotereyu, chifukwa tsopano anaona Davide, yemwe anali atangogonjetsa Goliati, kuti anali ndi chikhulupiriro zedi ndiponso anali wolimba mtima kwambiri. Mwina Sauli anali kuganiza zoti aike Jese, kapena anthu ena a m’banja lake, m’gulu la asilikali ake.​—8/1, tsamba 31.