Kulemba Kunali Kofunika Kwambiri ku Isiraeli
Kulemba Kunali Kofunika Kwambiri ku Isiraeli
KODI munawerengapo mabuku awiri akale andakatulo zotamanda ngwazi za ku Girisi otchedwa Iliad kapena Odyssey? Akuti mabuku amenewa analembedwa pakati pa zaka za m’ma 800 ndi 700 B.C.E. Kodi tikayerekeza mabuku amenewa ndi Baibulo, limene linayamba kulembedwa zaka mazana ambiri m’mbuyomo, timapeza zotani? Buku lina limati: “Baibulo limatchula za nkhani yolemba ndi zikalata zolembedwa maulendo osachepera 429. Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi makamaka tikakumbukira kuti buku la Iliad limatchula za kulemba kamodzi kokha pamene la Odyssey silitchulako n’komwe.”—The Jewish Bible and the Christian Bible.
Buku linanso limati “zikuoneka kuti kale ku Isiraeli, kulemba kunali kofunika kwambiri pachipembedzo chawo.” (The Oxford Encyclopedia of Archaeology in the Near East) Mwachitsanzo, pangano la Chilamulo linachita kulembedwa ndipo linkawerengedwa kwa anthu onse, amuna, akazi ndi ana. Anthu ankaliwerenganso ndi kuliphunzira paokha kapena m’magulu. Ataunika mfundo zina za Chilamulo, Alan Millard, mphunzitsi wamkulu wa pa Yunivesite ya Liverpool, anati: “Zikuoneka kuti kuwerenga ndi kulemba kunali kofunika kwambiri pamoyo wa anthu onse.”—Deuteronomo 31:9-13; Yoswa 1:8; Nehemiya 8:13-15; Salmo 1:2.
Mtumwi Paulo anafotokoza mmene Akhristu ayenera kuonera malemba oyera amenewa. Anati: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri, ndipo kodi mumaliwerenga nthawi zonse?—Aroma 15:4.