Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake

Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake

Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake

“Anthu amene anapirira timawatcha osangalala.”​—YAKOBE 5:11.

1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti sichinali cholinga cha Yehova kuti anthufe tizivutika?

PALIBE munthu wanzeru zake amene amafuna kuvutika, ndipo ngakhale Yehova Mulungu, Mlengi wathu, safuna kuti anthufe tizivutika. Umboni wa zimenezi timaupeza tikawerenga Mawu ake ndi kuona zimene zinachitika atalenga mwamuna ndi mkazi. Mulungu anayamba ndi kulenga mwamuna. “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Adamu analengedwa ali ndi maganizo ndi thupi langwiro, ndipo sanali woti atha kudwala kapena kufa.

2 Koma nanga bwanji za malo amene Adamu anali kukhala? “Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakum’mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.” (Genesis 2:8, 9) Indedi, Adamu anali ndi mudzi wabwino kwambiri. Mu Edene munalibe mavuto.

3. Kodi anthu awiri oyamba anali ndi tsogolo lotani?

3 Lemba la Genesis 2:18 limatiuza kuti: “Yehova Mulungu ndipo anati, Sikwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzam’pangira wom’thangatira iye.” Yehova analengera Adamu mkazi wangwiro, choncho zinali zotheka kukhala ndi banja losangalala. (Genesis 2:21-23) Baibulo limatiuzanso kuti: “Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Anthu awiri oyambawo anali ndi ntchito yapadera yoti afutukule munda wa Edene mpaka dziko lonse lapansi litakhala paradaiso. Ndipo anali oti abereke ana osangalala komanso opanda mavuto. Chiyambi cha munthu chinalidi chabwino kwambiri.​—Genesis 1:31.

Chiyambi cha Mavuto

4. Kuona mmene mbiri yonse ya anthu yakhalira, kodi tingati chiyani?

4 Komabe, tikaona mmene moyo wa munthu wakhalira m’mbiri yonse, n’zoonekeratu kuti penapake zinthu zinalakwika kwambiri. Zinthu zoipa zakhala zikuchitika, ndipo anthu avutika kwambiri. Kuyambira kalekale, mbadwa zonse za Adamu ndi Hava zakhala zikudwala, kukalamba, ndi kufa. Dziko lapansi sililinso paradaiso wa anthu osangalala. Lemba la Aroma 8:22 limafotokoza bwino mmene zinthu zilili kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka mpaka pano.”

5. Kodi makolo athu oyamba anachita chiyani kuti ayambitse nawo mavuto?

5 Yehova sindiye wachititsa kuti mavuto akhaleko kwa nthawi yonseyi. (2 Samueli 22:31) Koma anthu ndiwo anayambitsa nawo mavuto. Iwo “achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.” (Salmo 14:1) Makolo athu oyamba anapatsidwa zinthu zonse zabwino pachiyambi. Koma kuti zinthu zimenezi zipitirire, iwo anayenera kumvera Mulungu. Komabe, Adamu ndi Hava anapandukira Yehova. Popeza kuti makolo athu oyambawo anakana Yehova, iye anasiya kuwathandiza ndipo sanapitirize kukhala angwiro. Anayamba kukalamba ndipo kenako anamwalira. Choncho, iwo anatisiyira kupanda ungwiro.​—Genesis 3:17-19; Aroma 5:12.

6. Kodi Satana anayambitsa nawo motani mavuto?

6 Winanso amene anayambitsa nawo mavuto ndi mngelo amene anadzakhala Satana Mdyerekezi. Iye analengedwa ndi ufulu wosankha zochita. Komabe, anagwiritsa ntchito molakwa ufuluwo chifukwa chofuna kulambiridwa. Anachita zimenezi ngakhale kuti ndi Yehova yekha amene ayenera kulambiridwa, osati zolengedwa zake. Anali Satana yemweyo amene anasonkhezera Adamu ndi Hava kupandukira Yehova, powauza kuti ‘adzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.’​—Genesis 3:5.

Yehova Yekha Ndiye Ali ndi Ufulu Wolamulira

7. Kodi zotsatira zake za kupandukira Yehova zimasonyeza chiyani?

7 Zotsatira za kupanduka kwawoko zimasonyeza kuti Yehova, monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndiye ali ndi ufulu wolamulira ndipo ndi ulamuliro wake wokha umene uli wolungama. Zaka zikwi zambiri zapitazi zasonyeza kuti Satana, amene anakhala “wolamulira wa dzikoli,” wakhazikitsa ulamuliro woipa, wopanda chilungamo ndi wankhanza womwe si ulamuliro wabwino m’pang’ono pomwe. (Yohane 12:31) Nawonso ulamuliro wolephera wa anthu otsogozedwa ndi Satana womwe wakhalapo nthawi yaitali, wasonyeza kuti anthu sangathe kulamulirana mwachilungamo. (Yeremiya 10:23) Choncho, ulamuliro uliwonse umene anthu angakhazikitse popanda Yehova, ndi wolephera. Ndipo umboni wosatsutsika wa zimenezi, ndi zimene zachitika m’mbiri yonse ya anthu.

8. Kodi cholinga cha Yehova n’chiyani pa maulamuliro onse a anthu, ndipo adzakwaniritsa bwanji cholinga chakecho?

8 Panopo, popeza kuti Yehova walola anthu kuyesa kudzilamulira popanda iye kwa zaka zikwi zambiri, sitingamuimbe mlandu ngati atachotsa maulamuliro onse padziko lapansi ndi kukhazikitsa boma lake. Pankhani imeneyi, ulosi umati: “Masiku a mafumu aja [maulamuliro a anthu] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [boma lake la kumwamba lolamulidwa ndi Khristu] woti sudzawonongeka ku nthawi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ulamuliro wa ziwanda ndi wa anthu udzathera pompo, ndipo ndi Ufumu wakumwamba wa Mulungu wokha umene udzalamulira dziko lapansi. Khristu ndiye adzakhale Mfumu, ndipo adzalamulira limodzi ndi anthu okhulupirika okwana 144,000 otengedwa pa dziko lapansi.​—Chivumbulutso 14:1.

Mavuto Ali ndi Ubwino Wake

9, 10. Kodi Yesu anapindula bwanji ndi mavuto amene anakumana nawo?

9 N’zochititsa chidwi kuona ziyeneretso za amene adzalamulira mu Ufumu wakumwamba. Choyamba, Khristu Yesu anasonyeza kuti ndi woyenerera kukhala Mfumu. Kwa zaka zosawerengeka, anali limodzi ndi Yehova kuchita chifuniro cha Atate akewo, ndipo anali “mmisiri” wake. (Miyambo 8:22-31) Yehova atakonza zoti Yesu abwere padziko lapansi pano, iye anavomera ndi mtima wonse. Ali padziko lapansi pano anachita khama kuuza ena za ulamuliro wa Yehova ndi Ufumu wake. Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino tonsefe cha mmene tingagonjerere ulamuliro umenewo ndi moyo wonse.​—Mateyo 4:17; 6:9.

10 Yesu anazunzidwa, ndipo pamapeto pake anaphedwa. Koma pochita utumiki wake, anatha kuona mmene anthu kulikonse ankavutikira. Kodi kuona zimenezi komanso kuvutika kwake kunali ndi phindu lililonse? Inde, chifukwa lemba la Aheberi 5:8 limati: “Ngakhale anali Mwana [wa Mulungu], anaphunzira kumvera mwa mavuto amene anakumana nawo.” Zimene Yesu anakumana nazo padziko lapansi zinamuthandiza kukhala munthu womvetsa mavuto a ena ndi wachifundo. Anadzionera yekha ndi maso ake mavuto a anthu moti anatha kumvera chisoni anthu ovutika ndipo anazindikira kufunika kwa udindo wake wowawombola. Taonani mmene mtumwi Paulo anasonyezera zimenezi m’buku la Aheberi. Anati: “Anayenera ndithu kukhala ngati ‘abale’ ake m’zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu. Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yachiyanjanitso yophimba machimo a anthu. Popeza kuti iye mwini anavutika poyesedwa, amatha kuthandiza iwo amene akuyesedwa.” “Sitili ndi mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu, koma amene wayesedwa m’zonse ngati ifeyo, napezekabe wopanda uchimo. Choncho, tiyeni tifike ndi ufulu wa kulankhula ku mpando wachifumu wa kukoma mtima kwa m’chisomo, kuti tikalandire chifundo ndi kukoma mtima kwa m’chisomo kotithandiza panthawi yake.”​—Aheberi 2:17, 18; 4:14-16; Mateyo 9:36; 11:28-30.

11. Kodi mavuto amene anthu odzakhala mafumu ndi ansembe akumana nawo padziko lapansi, adzawathandiza bwanji polamulira?

11 N’chimodzimodzinso ndi a 144,000 amene “anagulidwa” kuchokera pa dziko lapansi kukalamulira limodzi ndi Khristu Yesu mu Ufumu wakumwamba. (Chivumbulutso 14:4) Anthu onsewa anabadwira padziko lapansi pompano, anakulira m’dziko lomweli lamavuto, ndipo nawonso anavutika. Ambiri a iwo anazunzidwa, ndipo ena anaphedwa kumene chifukwa chokhala okhulupirika kwa Yehova ndi kutsatira Yesu. Koma ‘sanachite manyazi ndi kuchitira umboni za Ambuye wawo, ndipo anatenga nawo mbali pakumva zowawa chifukwa cha uthenga wabwino.’ (2 Timoteyo 1:8) Chifukwa cha zimene anakumana nazo ali pa dziko lapansi, iwo ndi oyenerera kwambiri kuweruza anthu, ndipo adzachita zimenezi ali kumwamba. Padziko lapansi pano, iwo aphunzira kukhala achisoni, okoma mtima, ndi okonda kuthandiza anthu.​—Chivumbulutso 5:10; 14:2-5; 20:6.

Anthu Oyembekezera Kukhala pa Dziko Lapansi Amasangalala

12, 13. Kodi anthu oyembekeza kukhala padziko lapansi, angapindule bwanji ndi mavuto?

12 Kodi anthu amene akuyembekeza kukhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi lopanda matenda, chisoni, ndi imfa, angapindule ndi mavuto mwanjira iliyonse? Sikuti mavuto paokha ndi abwino. Koma tikamapirira mavutowo, makhalidwe athu abwino angakule ndipo tingakhale osangalala.

13 Pankhani imeneyi, Mawu a Mulungu amati: “Ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe osangalala.” “Ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu, khalani osangalala.” (1 Petulo 3:14; 4:14) “Osangalala muli inu pamene anthu akunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, lumphani ndi chisangalalo, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.” (Mateyo 5:11, 12) “Ali wosangalala munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira kolona wa moyo.”​—Yakobe 1:12.

14. Kodi anthu olambira Yehova akamakumana ndi mavuto, amasangalala chifukwa chiyani?

14 Ndithudi, kukumana ndi mavuto pakokha sindiko kumatipatsa chisangalalo. M’malo mwake, timasangalala podziwa kuti tikuvutika chifukwa chochita chifuniro cha Yehova ndi kutsatira chitsanzo cha Yesu. Mwachitsanzo, atumwi ena anagwidwa ndi kupita nawo ku khoti lalikulu la Ayuda kumene anapezeka ndi mlandu wolalikira za Yesu Khristu. Anakwapulidwa ndipo kenako anamasulidwa. Koma kodi iwo anamva bwanji? Baibulo limati iwo “anachoka pamaso pa Bungwe Lalikulu la Ayuda, ali osangalala chifukwa anayesedwa oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina lake.” (Machitidwe 5:17-41) Sikuti iwo anasangalala ndi kukwapulidwako. Koma anasangalala podziwa kuti zimenezo zinachitika chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Yehova ndi kutsatira kwawo mapazi a Yesu.​—Machitidwe 16:25; 2 Akorinto 12:10; 1 Petulo 4:13.

15. Kodi kupirira kwathu mavuto panopa kungadzatithandize bwanji m’tsogolo?

15 Ngati tipirira popanda kudandaula kapena kukhumudwa pamene anthu akutitsutsa kapena kutizunza, timaphunzira kukhala ndi mtima wopirira kwambiri. Zimenezi zidzatithandiza kupirira mavuto m’tsogolo. Timawerenga kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwa kuti chikhulupiriro chanu choyesedwacho, chimabala chipiriro.” (Yakobe 1:2, 3) Nalonso lemba la Aroma 5:3-5 limatiuza kuti: “Tiyeni tikondwere pamene tili m’zisautso, popeza tikudziwa kuti chisautso chimabala chipiriro; kenako chipiriro chimabala chivomerezo kwa Mulungu; chivomerezocho chimabala chiyembekezo, ndipo chiyembekezocho sichigwiritsa mwala.” Choncho, tikamapirira kwambiri mayesero amene timakumana nawo panopa chifukwa chokhala Akhristu, tidzakhala okonzeka kupirira mayesero aakulu amene tingakumane nawo m’dongosolo loipa la zinthuli.

Yehova Adzatibwezera Zonse

16. Kodi Yehova adzawachitira chiyani mafumu ndi ansembe am’tsogolo chifukwa cha kuvutika kwawo?

16 Ngakhale ngati titataya katundu wathu potsutsidwa kapena kuzunzidwa chifukwa chokhala Akhristu, tiyenera kusangalalabe podziwa kuti Yehova adzatibwezera zonse. Mwachitsanzo, polembera amene anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba, mtumwi Paulo anati: “Munalola mokondwa katundu wanu kufunkhidwa, podziwa kuti inuyo muli ndi chuma chopambana ndi chokhalitsa” cholamulira mu Ufumu wa Mulungu. (Aheberi 10:34) Ndipo chimwemwe chawo chidzakhala chachikulu pamene motsogoleredwa ndi Yehova ndi Khristu, adzathandiza kubweretsa madalitso osaneneka kwa anthu m’dziko latsopano. Mawu amene mtumwi Paulo anauza Akhristu okhulupirika ndi oona. Iye anati: “Ndikuona kuti masautso amene tili nawo tsopano sali kanthu powayerekeza ndi ulemerero umene tidzaonekera nawo.”​—Aroma 8:18.

17. Kodi Yehova adzawachitira chiyani anthu oyembekezera kukhala padziko lapansi amene akumutumikira mokhulupirika?

17 Chimodzimodzinso anthu amene akuyembekezera kukhala pa dziko lapansi. Kaya ataya zotani kapena adzimana zinthu zotani chifukwa chotumikira Yehova, iye adzawabwezera zoposa zonsezo m’tsogolo. Adzawapatsa moyo wosatha ndiponso wangwiro m’paradaiso padziko lapansi. M’dziko latsopanolo, Yehova “adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Limenelitu ndi lonjezo labwino kwambiri. Palibe chilichonse chimene tingadzimane kapena kutaya m’dziko lino chifukwa cha Yehova, chimene chingapose moyo wabwino umene adzapatsa atumiki ake okhulupirira amene amapirira mavuto.

18. Kodi Yehova kudzera m’Mawu ake amatipatsa lonjezo lotonthoza lotani?

18 Mavuto aliwonse amene tingapirire m’tsogolomu sadzatilepheretsa kusangalala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Moyo wabwino umene tidzakhala nawo m’dziko latsopano udzaposa mavuto onse amene tikukumana nawo. Lemba la Yesaya 65:17, 18 limatiuza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ichi ndichilenga.” N’chifukwa chake Yakobe, m’bale wake wa Yesu, anati: “Anthu amene anapirira timawatcha osangalala.” (Yakobe 5:11) Zoonadi, tikamapirira mokhulupirika mavuto amene timakumana nawo, timapindula panopa komanso m’tsogolo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi anthu anayamba bwanji kuvutika?

• Kodi mavuto angakhale ndi ubwino wotani kwa odzalamulira dziko lapansi ndiponso kwa nzika zake?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusangalala ngakhale ngati tikuvutika?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 27]

Makolo athu oyamba anali ndi tsogolo labwino kwambiri

[Chithunzi patsamba 29]

Yesu adzakhala Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe wabwino chifukwa anadzionera yekha mavuto a anthu

[Chithunzi patsamba 31]

Atumwi ‘anasangalala chifukwa anayesedwa oyenera kuchitiridwa chipongwe’ chifukwa cha chikhulupiriro chawo