Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mphatso Yamtengo Wapatali” ya Anthu a ku Poland

“Mphatso Yamtengo Wapatali” ya Anthu a ku Poland

“Mphatso Yamtengo Wapatali” ya Anthu a ku Poland

PA July 6, 1525, Albrecht yemwe anali kalonga wa ku Hohenzollern, analengeza zoti dziko lake likhala la chipembedzo cha Lutheran. Choncho, dziko la Prussia lomwe panthawiyo linali kachigawo ka ufumu wa Poland, linakhala dziko loyamba ku Ulaya, kuvomereza mfundo za Martin Luther.

Albrecht ankafuna kuti mzinda wa Königsberg, umene unali likulu la chigawo chakum’mawa kwa dziko la Prussia, ukhale chimake cha Chipolotesitanti. Iye anakhazikitsa yunivesite mu mzindawo ndipo analimbikitsa ntchito yosindikiza mabuku a chipembedzo cha Lutheran m’zinenero zosiyanasiyana. M’chaka cha 1544, Albrecht analamulanso kuti anthu a ku Poland omwe anali m’dziko lake, azimvetsera mavesi a m’Malemba Oyera m’chinenero chawo. Koma panthawiyo panalibe Baibulo la Chipolishi.

Baibulo la Chinenero Chimene “Anthu Wamba Amalankhula”

Kuti athetse vutoli, Albrecht anayamba kufufuza munthu amene angathe kumasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chipolishi. Cha m’ma 1550, iye analemba ntchito Jan Seklucjan yemwe anali wolemba mabuku, ndipo ankagulitsa ndi kusindikiza mabuku. Seklucjan anamaliza maphunziro ake pa yunivesite ya Leipzig ndipo ankadziwika kuti ndi munthu wokonda kukhumudwitsa Tchalitchi cha Katolika chifukwa chofalitsa mfundo za Chipolotesitanti. Ndipotu, anali atapitapo ku Königsberg pothawa kuzengedwa mlandu wofalitsa zikhulupiriro zake pankhani ya chipembedzo.

Jan Seklucjan anali ndi chidwi chofuna kutulutsa Baibulo m’Chipolishi. Patangotha chaka chimodzi atapatsidwa ntchito yomasulira ija, Seklucjan anasindikiza Baibulo la Uthenga Wabwino wa Mateyo. Baibulo limeneli linali ndi ndemanga zatsatanetsatane ndiponso mavesi ena anali ndi mawu m’mphepete mwake ofotokoza mavesiwo. Patangotha nthawi yochepa, Seklucjan anasindikiza Baibulo la Mauthenga Abwino onse anayi. Pasanathe n’komwe zaka zitatu atatulutsa Baibulo limeneli, anasindikizanso Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu.

Kuti Baibuloli likhale lolondola, munthu amene analimasulirayo ankagwiritsanso ntchito malemba achigiriki. Komanso mawu oyamba m’Baibulo limene analisindikiza mu 1551 ananena kuti anagwiritsanso ntchito Mabaibulo a Chilatini ndiponso “Mabaibulo a zinenero zina.” Stanisław Rospond, yemwe analemba buku la Studies on the Polish Language of the 16th Century, anafotokoza kuti Baibulo limeneli linamasuliridwa “mosangalatsa ndi motsatirika bwino.” Rospond ananenanso kuti womasulirayo sanagwiritse ntchito “mawu ovuta kumva.” Koma anayesetsa kugwiritsa ntchito Chipolishi chimene “anthu wamba amalankhula.”

Ngakhale kuti Seklucjan ndiye anatsogolera ntchito yomasulirayo, pali umboni wosonyeza kuti si iye amene anamasulira Baibuloli. Ndiyeno kodi ndani amene analimasulira? Anali Stanisław Murzynowski. Zikuoneka kuti Murzynowski anali asanakwanitse n’komwe zaka 25 panthawi imene Seklucjan anapatsidwa ntchito yovutayi.

Murzynowski sanabadwire m’tawuni, koma atakula ndithu, bambo ake anam’tumiza ku mzinda wa Königsberg kuti akaphunzire Chigiriki ndi Chiheberi. Kenako Murzynowski anakaphunzira pa yunivesite ya Wittenberg ku Germany komwe zikuoneka kuti anakumana ndi Martin Luther. Mnyamatayu ankamvetsera nkhani za Philipp Melanchthon yemwe mosakayikira anam’thandiza kuti adziwe bwino Chigiriki ndi Chiheberi. Atapitanso ku Italy kukapitiriza maphunziro ake, Murzynowski anabwerera ku Königsberg kumene anakagwira ntchito kwa Albrecht.

Maria Kossowska, m’buku lake lakuti The Bible in the Polish Language ananena kuti: “Murzynowski anagwira ntchito yake bwino lomwe ndiponso mwakhama, koma sanafune kudzitchukitsa kapena kudzipezera ulemu ndipo sanapemphe kuti dzina lake lilembedwe patsamba loyamba la Baibulolo.” Ndipo ponena za nkhawa imene anali nayo, mnyamatayu anati: “Sinditha kulemba bwinobwino Chilatini kapena Chipolishi.” Komabe, ngakhale kuti Murzynowski ankadzikayikira chonchi, iye anathandiza kwambiri kuti Mawu a Mulungu ayambe kupezeka m’Chipolishi. Pofotokoza za Baibulo limene anamasulira, mnzake amene anagwira naye ntchitoyo, Seklucjan ananena kuti Baibulolo ndi “mphatso yamtengo wapatali” ya anthu a ku Poland.

Imodzi mwa Mphatso Zamtengo Wapatali

Pamasuliridwa Mabaibulo enanso ambiri kuchokera pamene Baibulo loyamba la Chipolishi limeneli linamasuliridwa. M’chaka cha 1994, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chipolishi ndipo Baibulo lonse la New World Translation of the Holy Scriptures linatulutsidwa mu 1997. Omasulira ake sanafune kudzitchukitsa ndipo anamasulira Mawu a Mulungu molondola komanso mmene anthu wamba amalankhulira masiku ano, osati mmene ankalankhulira zaka za m’ma 1500.

Masiku ano Baibulo lonse kapena zigawo zake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,400. Ngati m’chinenero chanu muli ndi Mawu a Mulungu omasuliridwa molondola, imeneyo ndiye kuti ndi mphatso yanu yamtengo wapatali kwambiri, imene Yehova Mulungu wakupatsani kuti ikutsogolereni.​—2 Timoteyo 3:15-17.

[Chithunzi patsamba 20]

Mwala wachikumbutso cha Stanisław Murzynowski, amene anamasulira “Chipangano Chatsopano” m’Chipolishi

[Chithunzi patsamba 21]

Chaputala chachitatu cha buku la Mateyo lomwe Stanisław Murzynowski anamasulira

[Mawu a Chithunzi]

Dzięki uprzejmości Towarzystwa Naukowego Płockiego