Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musamangogoma ndi Chilengedwe Dziwaninso Mlengi

Musamangogoma ndi Chilengedwe Dziwaninso Mlengi

Musamangogoma ndi Chilengedwe Dziwaninso Mlengi

MWINA munamvapo za katswiri wa ku Italy wa zojambula ndi zosemasema dzina lake Michelangelo. Ngakhale ngati zojambula zake zotchukazo simunazionepo pamasom’pamaso, mungavomereze zimene ananena katswiri wina wa mbiri ya za anthu aluso, zoti munthu walusoyu “analibe mnzake pa luso lake.” Palibe angatsutse zoti Michelangelo anali waluso. Kodi alipo munthu wanzeru zake amene angagome ndi zojambula za Michelangelo koma n’kutsutsa zoti iyeyu anali munthu waluso logometsa?

Ndiyeno taganizirani za zinthu zamoyo zochuluka mosaneneka za padziko pano, zomwe n’zopangidwa m’njira yovuta kwambiri kumvetsa. M’pake kuti magazini ina inagwira mawu a pulofesa wa sayansi ya zamoyo, yemwe anati: “Sayansi ya zamoyo imapereka umboni wosonyeza kuti zamoyo zinalengedwa mwaluso.” Iye anapitiriza kuti: “Zamoyo zosiyanasiyana zimapereka umboni wosatsutsika wakuti zinalengedwa mogometsa.” (The New York Times) Ndiyeno kodi munthu wanzeru angagome ndi chilengedwe koma n’kukana kuvomereza kuti kuli mlengi?

Mtumwi Paulo, yemwe anali wokonda kuchita chidwi ndi zinthu zimene ankaona, anatchulapo za anthu amene ankalambira “chilengedwe ndi kuchichitira utumiki wopatulika m’malo mochita zimenezo kwa Iye amene anazilenga.” (Aroma 1:25) Chifukwa choti nthawi zambiri amamva zoti zamoyo zinangokhalako zokha, anthu ena amakana kapena amalephera kuona kuti luso logometsa la m’chilengedwe limasonyeza kuti kuli mlengi. Koma kodi mfundo yoti zamoyo zinangokhalako zokha posintha kuchokera ku zinthu zina ndi yogwirizana ndi sayansi yeniyeni? Taonani zimene ananena Christoph Schönborn, bishopu wamkulu wachikatolika ku Vienna, zomwe zinalembedwa m’nyuzipepala ina. Iye anati: “Mfundo iliyonse yotsutsa kapena yonyalanyaza umboni wamphamvu umene ulipo wakuti zamoyo zinachita kulengedwa, siyogwirizana ndi sayansi, koma ndi yongopeka basi.”​—The New York Times

Kodi Zimenezi Zingasokonezeke Sayansi?

Komabe, pali ena amene amaona kuti kuvomereza umboni woti kuli Mlengi “kungasokoneze zimene asayansi akufufuza.” Nkhani ya m’magazini ina inatchulapo mfundo imeneyi ponena kuti kuvomereza zimenezi “kungachititse kuti asayansi asiye kuvutika n’kufufuza zinthu zatsopano zokhudza chilengedwe, chifukwa angathe kumangonena kuti ‘mlengi ndiye anazipanga basi.’” (New Scientist) Koma kodi zimenezi n’zomveka? Ayi. Ndipotu kunena zoona, kuvomereza zoti kuli mlengi kungalimbikitse kwambiri sayansi. Kungatero motani?

Kwenikweni, kukhulupirira zoti chilengedwe chonsechi komanso zamoyo zonse padziko pano zinangokhalako pazokha, kumatsekereza njira iliyonse imene ingakhalepo yothandiza kuti timvetse bwinobwino zinthu zimenezi. Komano, kuvomereza kuti pali Mlengi wanzeru amene analenga zinthu zonsezi kungatithandize kuti tiyesetse kufufuza nzeru zake ndi mmene zimagwirira ntchito m’chilengedwe. Taganizirani izi: Kudziwa kuti Leonardo da Vinci ndiye anajambula chithunzi chotchuka cha “Mona Lisa” sikunachititse kuti akatswiri a mbiri ya za anthu aluso asiye kufufuza njira ndiponso zipangizo zimene iyeyu ankagwiritsira ntchito. Chimodzimodzinso ndi ifeyo; kuvomereza kuti kuli Mlengi kusatifooketse kuti tisiye kufufuza mozama zinthu zakuya zimene analenga.

Baibulo silifooketsa anthu ofuna kufufuza zinthu, m’malo mwake limalimbikitsa anthu kufufuza mayankho a mafunso okhudza sayansi ndiponso zinthu zauzimu. Mfumu yakale Davide, inaganizira mozama za thupi lake, ndipo inaona kuti linapangidwa mwaluso zedi. Motero, mfumuyo inati: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Kwenikweni, Baibulo limanena kuti Mlengi anafunsa Yobu kuti: “Kodi unalingalira utali wa dziko la pansi pano?” (Yobu 38:18, Malembo Oyera) Ndithu, mawu amenewa sakusonyeza kuti Baibulo likuletsa kufufuza zinthu. Ndipotu pamenepa, Mlengi Wamkuluyu kwenikweni ankalimbikitsa kufufuza chilengedwe chake. Taganiziraninso zimene mneneri Yesaya analemba, zimene zimatilimbikitsa kudziwa bwino Mlengi wa zinthu zimene timaonazi. Yesaya anati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo.” Kenaka lemba la Yesaya 40:26 likutchula mfundo yakuti chilengedwe chonse chinapangidwa ndi Mlengi wamphamvu zosaneneka. Mfundo imeneyi ndi yogwirizana ndi zimene asayansi apeza.

N’zoona kuti zinthu zina zokhudza chilengedwe zingativute kumvetsa. Izi zili choncho chifukwa choti nzeru zathu zili ndi malire ndipo pali zinthu zina zokhudza dzikoli zimene sitizidziwa. Yobu ankamvetsa mfundo imeneyi. Iye anatama Mlengi, amene amachititsa kuti dziko lathuli lizitha kukhala molenjekeka mlengalenga ndiponso kuti lizikutidwa ndi mitambo yamvula. (Yobu 26:7-9) Yobu anazindikira kuti Yehova anapanga zodabwitsa zambiri “koma zomwe tizipenya n’zazing’onotu.” (Yobu 26:14, Malembo Oyera) N’zosakayikitsa kuti Yobu ankafuna kudziwa zambiri zokhudza zinthu zimene anali kuona. Ndipo Davide anavomereza kuti pali malire a zimene iyeyo angathe kumvetsa, ponena kuti: “Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwiza: Kundikhalira patali, sindifikirako.”​—Salmo 139:6.

Kuvomereza kuti kuli Mlengi sikungalepheretse sayansi kupita patsogolo. N’zoona kuti kufufuza n’cholinga chomvetsa bwino zinthu zachilengedwe ndiponso zauzimu kulibe malire ndipo sikudzatha mpaka muyaya. Mfumu ina yakale yomwe inali yotchuka chifukwa cha nzeru zake zakuya inalemba modzichepetsa kuti: “Waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”​—Mlaliki 3:11.

Kodi Amangotchula Mulungu Akasowa Mfundo Yogwira Mtima?

Anthu ena amatsutsa mfundo yoti zinthu zinachita kulengedwa, ponena kuti palibe umboni woti kuli Mulungu, ndipo amati Mulungu amangotchulidwa “polephera kufokotoza” zinthu zimene asayansi sanazitulukire. Kwenikweni mfundo ya anthu amenewa ndi yakuti amene amatchula zoti kuli Mlengi amatero chifukwa chosowa mfundo yogwira mtima, motero akapeza chilichonse chovuta kufotokoza amangothamangira kunena kuti chinapangidwa ndi Mulungu basi. Komano kodi ndi zinthu zotani zimene zili zovuta kufotokoza? Kodi ndi zinthu zing’onozing’ono ndiponso zosafunika kwenikweni zimene timalephera kuzimvetsa? Ayi, zimenezi ndi mfundo zikuluzikulu zomwe Darwin anayambitsa ponena kuti zamoyo zinangokhalako zokha. Asayansi samvetsa mfundo zimenezi akatsatira mfundo yakuti zamoyo zinangokhalako zokha. Kunena mosapita m’mbali, asayansi okhulupirira mfundo zopanda umboni ndiwo kwenikweni akusowa mfundo yogwira mtima. Motero akapeza chilichonse chovuta kufotokoza amangothamangira kunena kuti chinangokhalako chokha basi, monga ananenera Darwin.

Mlengi amene amatchulidwa m’Baibulo si Mulungu wongotchulidwa posowa mfundo ina yogwira mtima. Komano iyeyu ndiyedi analenga zinthu zonse m’chilengedwe. Wamasalmo anagogomezera kwambiri mfundo yakuti Yehova ndiye analenga zonse. Iye anati: “Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu: M’kuunika kwanu tidzaona kuunika.” (Salmo 36:9) Baibulo limanenanso momveka bwino kuti iye ndiye anapanga “kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhalamo.” (Machitidwe 4:24; 14:15; 17:24) M’pake kuti mphunzitsi wina wakale ananena kuti Mulungu “analenga zinthu zonse.”​—Aefeso 3:9.

Kuphatikiza pamenepo, Mulungu anakhazikitsa “malamulo a thambo,” omwe ndi malamulo amene amayendetsa zinthu zonse m’chilengedwe. Asayansi sanafikebe pomvetsa bwinobwino malamulo amenewa. (Yobu 38:33, Malemba Oyera) Mulungu analenga zinthu zonse mwadongosolo ndiponso ndi cholinga, ndipo anakwanitsa cholinga chake chopanga dziko lapansi kuti muzikhala zamoyo zosiyanasiyana.

Kugwiritsa Ntchito Nzeru Zanu Zachibadwa

Pomaliza, tiyenera kuganizira za nzeru zimene tonsefe timakhala nazo, ngakhale popanda kupita kusukulu. Ponena za mmene tingadziwire kuti mfundo zosiyanasiyana za sayansi n’zoona kapena ayi, wasayansi wina dzina lake John Horgan anati: “Ngati palibe umboni weniweni wotsimikizira mfundo za sayansizo, tisamachite manyazi kungogwiritsira ntchito nzeru zimene tonsefe timakhala nazo, ngakhale popanda kupita kusukulu.”

Kodi n’zomveka kunena kuti zamoyo zinangokhalako zokha basi kapenanso kuti zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zopanda moyo? Ngakhale kuti anthu ambiri amakhulupirira zimenezi, palinso anthu ena ambiri anzeru, kuphatikizapo asayansi, omwe amakhulupirira kuti pali Mlengi wanzeru. Pulofesa wina wa sayansi ananena kuti anthu ambiri padziko pano “mwanzeru zawo, sakayika ngakhale pang’ono kuti zamoyo zinachita kulengedwa.” N’chifukwa chiyani amatero? N’chifukwa choti anthu ambiri angavomereze mawu a Paulo akuti: “Inde, nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake.” (Aheberi 3:4) Baibulo limasonyeza kuti si nzeru kuvomereza kuti nyumba imafunikira woimanga koma n’kumatsutsa zoti selo, yomwe ndi yopangidwa movuta kumvetsa kwambiri, inangokhalako yokha basi.

Baibulo limanena izi pofotokoza anthu amene amati kulibe Mlengi: “Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.” (Salmo 14:1) Pamenepa wamasalmo akutsutsa anthu amene sanakhulupirirebe zoti kuli Mlengi. Anthu ena amangoyendera mfundo zowakomera iwowo basi osati zimene zikuonekeratu kuti n’zoona. Koma munthu wanzeru, ndiponso woganiza bwino amadzichepetsa n’kuvomereza kuti kuli Mlengi.​—Yesaya 45:18.

Anthu ambiri oganiza bwino amakhutira kwambiri ndi umboni umene ulipo woti kuli Mlengi Wamkulu.

Mungathe Kudziwa Mlengi

Ngati tikuvomereza kuti tinachita kulengedwa, kodi tinalengedwa chifukwa chiyani? Kodi cholinga cha moyo wathu n’chiyani? Sayansi payokha yalephera kuyankha mafunso amenewa momveka. Komatu nkhani zikuluzikulu ngati zimenezi zimafunika mayankho ogwira mtima. Baibulo lingatithandize kwambiri kupeza mayankho otere. Limati Yehova ndi Mlengi komanso amachita zinthu ndi zolinga zomveka. Malemba amasonyeza cholinga cha Mulungu polenga anthu, ndipo amatipatsa chiyembekezo chosangalatsa cha m’tsogolo.

Komabe kodi Yehova ndi ndani kwenikweni? Kodi iyeyu ndi Mulungu wotani? Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuti mum’dziwe bwino Mlengi Wamkulu. Mungathe kuphunzira za dzina lake, makhalidwe ake ndiponso mmene wakhala akuchitira zinthu ndi anthu. Pophunzira Mawu ake, Baibulo, mungathe kuona kuti kugoma ndi chilengedwe chake sikokwanira. M’pofunikanso kumutamanda monga Mlengi.​—Salmo 86:12; Chivumbulutso 4:11.

[Chithunzi patsamba 4]

Michelangelo

[Zithunzi patsamba 5]

Kukhulupirira zoti kuli Mlengi kumagwirizana ndi sayansi yeniyeni

[Chithunzi patsamba 6]

Kuchuluka ndiponso kusiyanasiyana kwa zamoyo kumapereka umboni wakuti panagona luso polenga mitundu yosiyanasiyana ya zinthu

[Zithunzi patsamba 7]

Sipangakhale chilengedwe popanda mlengi