Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzina la Mulungu mu Nyimbo za ku Russia

Dzina la Mulungu mu Nyimbo za ku Russia

Dzina la Mulungu mu Nyimbo za ku Russia

MU 1877, woimba wina wotchuka wa ku Russia, dzina lake Modest Mussorgsky analemba buku la nyimbo zakwaya zokhala ndi nkhani za m’Baibulo. M’kalata yopita kwa mnzake, iye analemba kuti: “M’bukumu ndalembamo nyimbo ina yofotokoza za Yoswa (yakuti Jesus Navinus) mogwirizana ndendende ndi nkhani ya m’Baibulo. Ndailembanso mogwirizana ndi ndondomeko ya malo onse amene Yoswa anadutsa ndi ankhondo ake polowerera dziko la Kanani.” M’nyimbo zake zina, kuphatikizapo nyimbo yakuti “Kuwonongedwa kwa Sanakeribu,” Mussorgsky analembamonso nkhani ndiponso anthu otchulidwa m’Baibulo.

N’zochititsa chidwi kuti m’nyimbo yofotokoza za Yoswa ija ndiponso m’nyimbo ya “Kuwonongedwa kwa Sanakeribu,” yomwe anaitulutsa mu 1874, Mussorgsky anatchula Mulungu pogwiritsa ntchito katchulidwe ka Chirasha ka dzina lenileni la Mulungu, limene pa Chiheberi limalembedwa ndi zilembo zinayi. Zilembo zake ndizo יהוה (YHWH) ndipo m’Malemba Achiheberi zimapezeka pafupifupi nthawi 7,000.

Motero, nyimbo zimene Mussorgsky analembazi zimasonyeza kuti kalekale chisanafike n’komwe chaka cha 1900, anthu a ku Russia ankadziwa dzina la m’Baibulo la Mulungu lakuti Yehova. Zimenezi n’zomveka, chifukwa chakuti kalekale Yehova anauza Mose kuti: “Ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo.”​—Eksodo 3:15.

[Chithunzi patsamba 32]

Sukulu ya St. Petersburg Conservatory mu 1913. Kusukulu imeneyi amaphunzitsa nyimbo ndipo n’kumene amasungako buku la nyimbo za Mussorgsky

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Sheet music: The Scientific Music Library of the Saint-Petersburg State Conservatory named after N.A. Rimsky-Korsakov; street scene: National Library of Russia, St. Petersburg