Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Popeza kuti Ayuda analamulidwa kuti asamadye “kanthu ka chotupitsa” pa Pasika, n’chifukwa chiyani poyambitsa mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake, Yesu anagwiritsa ntchito vinyo, yemwe ankafunika kuwira popanga?​—Eksodo 12:20; Luka 22:7, 8, 14-20.

Mwambo wa Pasika, womwe unkachitika pokumbukira kutuluka kwa ana a Isiraeli mu Iguputo, unakhazikitsidwa mu 1513 B.C.E. Popereka malangizo a mwambowu, Yehova anati: “Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa.” (Eksodo 12:11, 20) Lamuloli linangokhudza mtundu wa mkate umene anayenera kudya pa Pasika. Silinatchulepo za vinyo.

Chifukwa chachikulu chimene analetsera chotupitsa n’chakuti, Aisiraeli anafunika kutuluka mofulumira mu Igupto. Lemba la Eksodo 12:34 limafotokoza kuti: “Anthu anatenga mtanda wawo usanatupe, ndi zoumbiramo zawo zomangidwa m’zovala zawo pa mapewa awo.” M’tsogolo mwake, kusagwiritsa ntchito chotupitsa pamwambowu kukanakumbutsa mibadwo yotsatira mfundo yofunika imeneyi.

M’kupita kwa nthawi, anthu anayamba kuona chotupitsa monga chizindikiro cha uchimo ndi kuwonongeka. Mwachitsanzo, ponena za munthu wachiwerewere mumpingo wachikhristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse?” Kenako anati: “Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu waperekedwa kale monga nsembe yathu ya pasika. Chotero tiyeni tichite chikondwererochi, osati ndi chofufumitsa chakale, kapena chofufumitsa choimira zoipa ndi uchimo, koma ndi makeke osafufumitsa oimira kuona mtima ndi choonadi.” (1 Akorinto 5:6-8) Choncho mkate wopanda chotupitsa unali chizindikiro choyenera cha thupi la Yesu lopanda uchimo, lomwe anali nalo padziko lapansi.​—Aheberi 7:26.

Zikuoneka kuti Ayuda anayamba okha kugwiritsa ntchito vinyo pa mwambo wa Pasika. Iwo anayamba kuchita zimenezi atabwera kuchokera kuukapolo wa ku Babulo. Baibulo silinatsutse zimenezi, ndipo panalibe cholakwika chilichonse kuti Yesu agwiritse ntchito vinyo paphwando la Pasika. Komanso, kuwira kumene kunkachitika popanga vinyo kalelo kunali kosiyana ndi kufufumitsa mkate. Pofufumitsa mkate pankafunika kuthira yisiti kapena zofufumitsa zina. Vinyo wopangidwa ndi mpesa sankafunika kuthira zinthu ngati zimenezi. Madzi a zipatso za mpesa ankatha kuwira paokha. Choncho, sizikanatheka kuwasunga osawira kuchokera nthawi yokolola mpesa, m’miyezi ya September mpaka October, kufika nthawi ya Pasika, m’March kapena April.

Choncho, pamene Yesu anagwiritsa ntchito vinyo monga chizindikiro cha pa Chikumbutso, sanachite zinthu zosemphana ndi malangizo onena za chotupitsa pa Pasika. Vinyo aliyense wofiira wosathira chilichonse ndi woyenera kugwiritsa ntchito monga chizindikiro cha “magazi a mtengo wapatali,” a Khristu.​—1 Petulo 1:19.