Phunzitsani Ana Anu Kukonda Mulungu ndi Mtima Wonse
Phunzitsani Ana Anu Kukonda Mulungu ndi Mtima Wonse
MASIKU ANO, n’zovuta kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. (Salmo 16:8) Mogwirizana ndi ulosi wa Baibulo, tikukhala mu “nthawi yovuta.” Anthu ambiri ‘amakonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.’ (2 Timoteyo 3:1-5) Ndithudi, ndi anthu ochepa okha masiku ano amene amakondadi Mulungu.
N’zovuta kuti mwana ayambe yekha kukonda Yehova Mulungu. Ana ayenera kuchita kuphunzitsidwa zimenezi. Koma kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kukonda Mulungu?
Muzilankhulana Momasuka
Tingathandize ana athu kukonda Mulungu ndi mtima wawo wonse ngati ifenso timatero. (Luka 6:40) Izi n’zimene Baibulo limauza makolo. Limati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.”—Deuteronomo 6:4-7.
Tingaphunzitse bwanji mwana wathu kukonda Mulungu ndi mtima wake wonse? Choyamba, tiyenera kudziwa zimene zili mu mtima mwake. Chachiwiri, tiyenera kusonyeza zimene zili mu mtima mwathu.
Popita ku Emau limodzi ndi ophunzira ake awiri, Yesu Khristu anawalimbikitsa kunena zimene zinali mu mtima mwawo. Atamvetsera zimene ananena, iye anawongolera maganizo awo olakwika mwa kuwafotokozera Malemba. Kenako ophunzirawo ananena kuti: “Kodi mitima yathu sinali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe?” Chimenechi ndi chitsanzo cha kulankhulana momasuka. (Luka 24:15-32) Kodi tingadziwe bwanji zimene zili mu mtima wa mwana wathu?
Posachedwapa, tinafunsa makolo ena, amene ana awo panopa ndi achikulire kapena achinyamata akuluakulu ndipo ndi zitsanzo zabwino mumpingo, kuti afotokoze kufunika kolankhulana momasuka. Mwachitsanzo, tinafunsa Glen, bambo yemwe walera bwino ana anayi ku Mexico. * Iye anati: “Kuti makolo ndi ana awo azilankhulana momasuka pamafunika khama. Ine ndi mkazi wanga tinkapewa kuwononga nthawi yathu pa zinthu zosafunika kwambiri kuti tikhale ndi nthawi yambiri yocheza ndi ana athu. Pamene anali achinyamata, tinkacheza nawo nkhani ina iliyonse imene yabwera m’maganizo mwawo mpaka nthawi yokagona. Panthawi ya chakudyanso, tinkachita chimodzimodzi. Tinkamvetsera nkhani zawo n’kuzindikira mavuto amene anali nawo ndipo kenako tinkawawongolera mwachikondi. Nthawi zambiri tinkachita zimenezi popanda iwo kudziwa.”
Kuti tizilankhulana momasuka ndi ana athu, timafunikanso kunena zimene zili mu mtima mwathu. Yesu anati: “Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino cha mtima wake, . . . pakuti pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Luka 6:45) Toshiki, yemwe ana ake atatu akuchita utumiki wa nthawi zonse ku Japan, anati: “Ndinkawauza chimene chinandipangitsa kuyamba kukhulupirira Yehova ndiponso chifukwa chake ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti iye alipo. Ndinkawafotokozeranso mmene zinthu zomwe ndaona pa moyo wanga zandithandizira kudziwa kuti Baibulo ndi loona ndiponso kuti malangizo ake ndi abwino kwambiri.” Mayi wina wa ku Mexico, dzina lake Cindy, anati: “Mwamuna wanga ankakonda kupemphera ndi ana athu. Pamene anawo ankamva mapemphero ake ochokera pansi pa mtima, ankadziwa kuti Yehova ndi weniweni.”
Chitsanzo Chathu N’chofunika Kwambiri
Zochita zathu n’zofunika kwambiri kuposa Yohane 14:31.
mawu athu chifukwa n’zimene zimasonyeza ana athu kuti timakondadi Mulungu. Anthu ankazindikira kuti Yesu Khristu ankakondadi Yehova akaona kuti iyeyo amamvera Mulungu. Yesu anati: “Kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atateyo anandipatsa.”—Wa Mboni za Yehova wina ku Wales, dzina lake Gareth, anati: “Ana athu ayenera kuona kuti timakonda Yehova ndi kuti timayesetsa kutsatira zimene iye amafuna. Mwachitsanzo, ana anga amaona kuti pomvera zimene Mulungu amatiuza, ndimavomereza zolakwa zanga. Panopa, iwonso amayesetsa kuchita zimenezi.”
Mwamuna wina wa ku Australia, dzina lake Greg, anati: “Tinkafuna kuti ana athu aone kuti choonadi n’chofunika kwambiri pamoyo wathu. Tisanasankhe zinthu zokhudza ntchito ndi zosangalatsa, timaganizira kaye ngati zinthuzi zingasokoneze zinthu zachikhristu. Ndife osangalala kuona kuti mwana wathu wa zaka 19 ali ndi maganizo omwewa pamene akuchita upainiya wothandiza.”
Muzithandiza Ana Anu Kudziwa Mulungu
N’zovuta kukonda kapena kukhulupirira munthu yemwe sitimudziwa bwino. Pofuna kuti Akhristu a ku Filipi akulitse chikondi chawo pa Yehova, mtumwi Paulo anawalembera kuti: “Ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino lomwe.” (Afilipi 1:9) Bambo wa ana anayi ku Peru, dzina lake Falconerio, anati: “Kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo nthawi zonse ndi ana kumawathandiza kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Ndinkati ndikalephera kuphunzira ndi ana anga, ndinkaona chikhulupiriro chawo chikufooka.” Munthu wina ku Australia, dzina lake Gary, anati: “Ndimakonda kusonyeza ana anga mmene ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwira. Ndimawathandizanso kuona ubwino wogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Kuchita phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse n’kumene kwathandiza ana athu kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu.”
Ana amasangalala kuphunzira ndipo zinthu zimawafika pa mtima ngati pamene akuphunzira ali aufulu ndi omasuka bwino. (Yakobe 3:18) Makolo a ana anayi ku Britain, Shawn ndi Pauline, anati: “Pochita phunziro la Baibulo la banja, tinkayesetsa kuti tisakalipire ana athu ngakhale ngati atayamba kufuntha. Tinkachititsa phunzirolo mosiyanasiyana. Nthawi zina tinkauza anawo kuti asankhe zimene tiphunzire. Nthawi zinanso tinkaonera mavidiyo opangidwa ndi gulu la Yehova. Poonera vidiyo, tinkatha kuiimitsa kapena kuibweza kuti tikambirane zimene taonerazo.” Mayi wina wa ku Britain, dzina lake Kim, anati: “Ndimakonzekera bwino phunziro la banja kuti ndifunse mafunso abwino, othandiza ana anga kuganiza. Tikamaphunzira aliyense amakhala wosangalala, ndipo timaseka kwambiri.”
Muzisankha Anthu Abwino Ocheza Nawo
Ana athu angaphunzire kukonda kwambiri Yehova ndi choonadi ngati amacheza ndi anthu okonda Mulungu. Pangafunike khama kuti tipezere ana athu anthu abwino amene angacheze ndi kusewera nawo. Komabe, khama lanu silipita pachabe. Ndi bwinonso kuyesetsa kuti ana athu adziwane ndi a Mboni za Yehova amene akuchita utumiki wa nthawi zonse. Ambiri amene akuchita utumiki wa nthawi zonse akutero chifukwa chakuti ankacheza ndi atumiki a Mulungu achangu. Mlongo wina amene ndi mmishonale anati: “Makolo anga ankaitana apainiya kuti adzadye nafe kunyumba kwathu. Iwowo anali osangalala kwambiri pochita utumiki wawo ndipo zimenezi zinandipangitsa kufuna kutumikira Mulungu ngati iwowo.”
N’zoona kuti ana athu angatengere zinthu zabwino kapena zoipa. Zimakhala zovuta kuphunzitsa bwino ana athu ngati iwowo akucheza ndi anthu olakwika. (1 Akorinto 15:33) Pamafunika luso kuti tiphunzitse ana athu kupewa kucheza ndi anthu amene sakonda kapena kudziwa Yehova. (Miyambo 13:20) Shawn, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Tinaphunzitsa ana athu kucheza bwino ndi anzawo kusukulu koma kuti macheza awo azithera komweko. Ana athu anamvetsa chifukwa chake sankayenera kuchita nawo masewera ena ndi zinthu zina zosakhudzana ndi maphunziro.”
Kufunika Kophunzitsa Ana
Tikamaphunzitsa ana athu kufotokoza zimene amakhulupirira, amasangalala kulankhula za chikondi chawo pa Mulungu. Bambo wina ku United States, dzina lake Mark, anati: “Timafuna kuti ana athu aziona kuti atha kulalikira nthawi ina iliyonse, osati kokha pamene akupita ku utumiki wa kumunda. Choncho, tikapita kwina kukasangalala monga kupaki, kunyanja kapena kokaona nkhalango, timapita ndi Baibulo ndi mabuku olifotokoza ndipo timakambirana ndi anthu zinthu zimene timakhulupirira. Anawo amasangalala kwambiri kulalikira m’njira imeneyi. Nawonso amalankhula ndi anthuwo za chikhulupiriro chawo.”
Mtumwi Yohane, anathandiza anthu ambiri kukonda Mulungu. Ponena za iwowo, analemba kuti: “Palibe chondisangalatsa koposa zinthu zimenezi, kumva kuti ana anga [auzimu] akuyendabe m’choonadi.” (3 Yohane 4) Ifenso tingasangalale ngati tiphunzitsa ana athu kukonda Mulungu ndi mtima wawo wonse.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mayina ena tawasintha.
[Zithunzi patsamba 9]
Pamafunika khama kuti tizilankhulana ndi ana athu momasuka nkhani za chikhulupiriro chathu
[Chithunzi patsamba 10]
Phunzitsani ana anu kulankhula za chikondi chawo pa Mulungu
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of Green Chimneys Farm