“Choonadi N’chiyani?”
“Choonadi N’chiyani?”
KAZEMBE wachiroma Pontiyo Pilato ndiye anafunsa Yesu funsoli monyoza. Iye sankafuna yankho ndipo Yesu sanamuyankhe. Mwinamwake, Pilato ankaona kuti n’zosatheka kudziwa choonadi.—Yohane 18:38.
Anthu ambiri masiku ano monga atsogoleri achipembedzo, aphunzitsi ndiponso andale ali ndi maganizo ngati a Pilato pankhani ya choonadi. Amakhulupirira kuti choonadi, makamaka pankhani ya makhalidwe ndi zinthu zauzimu, chimasinthasintha. Ngati zili choncho, ndiye kuti munthu aliyense angamasankhe yekha chabwino ndi choipa. (Yesaya 5:20, 21) Ndiponso, anthu angasiye kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene makolo awo kale ankatsatira poganiza kuti tsabola wakale sawawa.
Tiyeni tione mawu amene anachititsa Pilato kufunsa funso limeneli. Yesu anali atanena kuti: “Chimene ndinabadwira, ndi chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu sankaona kuti n’zovuta kudziwa choonadi. Iye analonjeza ophunzira ake kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.
Kodi choonadi tingachipeze kuti? Panthawi ina, Yesu popemphera kwa Mulungu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi” (Yohane 17:17) Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndipo lili ndi choonadi chomwe chimapereka malangizo odalirika ndiponso chiyembekezo cha moyo wosatha.—2 Timoteyo 3:15-17.
Pilato analibe chidwi chophunzira za choonadi. Nanga bwanji inuyo? Bwanji osafunsa Mboni za Yehova kuti mudziwe “choonadi” chimene Yesu ankaphunzitsa? Iwo angasangalale kukuuzani za choonadi chimenechi.