Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Cholinga Chabwino Pamoyo

Kufunafuna Cholinga Chabwino Pamoyo

Kufunafuna Cholinga Chabwino Pamoyo

“Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.”​—SALMO 150:6.

1. Fotokozani zimene wachinyamata wina anachita pofunafuna cholinga chabwino pamoyo.

“NDINAPHUNZIRA udokotala n’cholinga choti ndizithandiza anthu. Ndinkaonanso kuti ndidzakhala munthu wosangalala chifukwa cha ndalama zomwe ndingapeze ndi ulemu umene anthu azidzandipatsa ndikakhala dokotala,” anatero Seung Jin, yemwe anakulira ku Korea. * Iye anapitiriza kuti: “Koma ndinakhumudwa nditaona kuti ndi zinthu zochepa kwambiri zimene dokotala angachite kuti athandize anthu. Kenako, ndinayamba kuphunzira luso la zojambulajambula koma ndinaonanso ngati ndine wodzikonda chifukwa lusoli silinkathandiza ena kwenikweni. Pambuyo pake ndinayamba uphunzitsi koma ndinaonanso kuti ndinkangothandiza anthu kudziwa zinthu popanda kuwathandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe.” Mofanana ndi anthu ena ambiri, Seung Jin ankafunafuna cholinga chabwino pamoyo wake.

2. (a) Kodi kukhala ndi cholinga pamoyo kumatanthauza chiyani? (b) Kodi timadziwa bwanji kuti Mlengi wathu anali ndi cholinga potiika padziko pano?

2 Kukhala ndi cholinga chenicheni pamoyo kumatanthauza kudziwa chifukwa chimene tikukhalira ndi moyo ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi chifukwacho. Kodi anthu angakhaledi ndi cholinga chimenechi? Inde, nzeru komanso chikumbumtima zimene tili nazo, zimasonyeza kuti Mlengi wathu ali ndi cholinga chabwino kwambiri chomwe anatiikira padzikoli. Apatu, n’zodziwikiratu kuti tingapeze ndiponso kukwaniritsa cholinga chathu chenicheni ngati tikhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mlengiyo.

3. Kodi cholinga cha Mulungu pa anthu chimaphatikizapo chiyani?

3 Baibulo limasonyeza kuti cholinga cha Mulungu kwa ife chimaphatikizapo zinthu zambiri. Mwachitsanzo anthufe tinalengedwa modabwitsa ndipo umenewu ndi umboni wakuti Mulungu ndi wachikondi chopanda dyera. (Salmo 40:5; 139:14) Choncho, kukhala ndi moyo mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu kumatanthauza kukonda ena mmene Mulungu amachitira. (1 Yohane 4:7-11) Kumatanthauzanso kumvera malangizo a Mulungu omwe amatithandiza kukhala ndi moyo mogwirizana ndi cholinga chake chachikondi.​—Mlaliki 12:13; 1 Yohane 5:3.

4. (a) Kodi chofunika n’chiyani kuti munthu akhale ndi cholinga chabwino pamoyo? (b) Kodi cholinga chofunika kwambiri chimene aliyense ayenera kukhala nacho n’chiti?

4 Cholinga chinanso cha Mulungu ndi chakuti anthufe tizikhala mosangalala ndiponso mwamtendere ndi anzathu komanso ndi zolengedwa zina zonse. (Genesis 1:26; 2:15) Nangano, tingatani kuti tizikhala mosangalala, motetezeka ndiponso mwamtendere? Mofanana ndi mwana amene amasangalala ndipo amamva kuti ndi wotetezeka akakhala pafupi ndi makolo ake, nafenso timakhala ndi zolinga zabwino pamoyo tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. (Aheberi 12:9) Mulungu amachititsa kuti ubwenzi umenewu utheke mwa kulola kuti timuyandikire ndiponso mwa kumvetsera mapemphero athu. (Yakobe 4:8; 1 Yohane 5:14, 15) ‘Tikamayenda ndi Mulungu’ m’chikhulupiriro ndiponso tikakhala naye paubwenzi, Atate wathu wakumwambayu amasangalala komanso amalemekezedwa. (Genesis 6:9; Miyambo 23:15, 16; Yakobe 2:23) Ichitu ndi cholinga chofunika kwambiri chimene aliyense ayenera kukhala nacho. Wamasalmo analemba kuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.”​—Salmo 150:6.

Kodi Inuyo Muli ndi Cholinga Chotani Pamoyo Wanu?

5. N’chifukwa chiyani n’kupanda nzeru kukhala ndi moyo wongofunafuna zinthu zakuthupi?

5 Mbali ina ya cholinga cha Mulungu kwa ife ndi yakuti tizidzisamalira ndiponso kusamalira mabanja athu mwakuthupi komanso mwauzimu. Komatu, m’pofunika kuchita zinthu mwanzeru kuti kusamalira zofunika zakuthupi kusasokoneze zinthu zauzimu zomwe ndi zofunika kwambiri. (Mateyo 4:4; 6:33) N’zomvetsa chisoni kuti moyo wa anthu ambiri ndi wongofuna kukhala ndi zinthu zakuthupi basi. Koma n’kupanda nzeru kukhala ndi moyo wongofunafuna zinthu zakuthupi. Kafukufuku wina wa posachedwapa ku Asia, wasonyeza kuti anthu ambiri olemera amaona kuti “n’ngosatetezeka ndiponso ovutika maganizo ngakhale kuti amapatsidwa ulemu komanso amatha kuchita zinthu zambiri chifukwa cha chuma chawocho.”​—Mlaliki 5:11.

6. Kodi Yesu anapereka malangizo otani pankhani yofunafuna chuma?

6 Yesu ananena za “chinyengo champhamvu cha chuma.” (Maliko 4:19) Kodi chuma n’chonyenga motani? Chimaoneka ngati chingabweretse chisangalalo koma si zoona. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva.” (Mlaliki 5:10) Kodi n’zotheka kufunafuna chuma uku ukutumikira Mulungu ndi mtima wonse? Ayi n’zosatheka. Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Yesu sanalimbikitse otsatira ake kukundika chuma padzikoli koma “kumwamba,” kutanthauza kupanga dzina labwino ndi Mulungu amene “amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”​—Mateyo 6:8, 19-25.

7. Kodi tingatani kuti ‘tigwire zolimba moyo weniweniwo’?

7 Mtumwi Paulo analembera Timoteyo malangizo amphamvu pankhani imeneyi. Iye anamuuza kuti: “Lamula achuma, . . . kuti asadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale . . . , akhale . . . owolowa manja, okonzeka kugawana ndi ena, kudzisungira okha maziko abwino a tsogolo lawo, kuti akagwire zolimba moyo weniweniwo.”​—1 Timoteyo 6:17-19.

Kodi “Moyo Weniweniwo” N’chiyani?

8. (a) N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amafunafuna chuma ndi ulemu? (b) Kodi anthu otere sazindikira chiyani?

8 Anthu ambiri akamva za “moyo weniweniwo” amaganiza za moyo wosangalala komanso kukhala ndi katundu wambiri. Magazini ina ya ku Asia inanena kuti: “Anthu amene amaonera mafilimu kapena TV amayamba kusirira zimene akuonerazo, n’kumalakalaka atakhala nazo.” Ambiri amakhala ndi cholinga chopeza zinthu zimenezi pamoyo wawo. Ambiri awononga unyamata wawo, thanzi lawo, mabanja ndiponso makhalidwe awo auzimu chifukwa chofunafuna zinthu zimenezi. Ndi anthu ochepa chabe amene amazindikira kuti maganizo ofuna chuma amangosonyeza “mzimu wa dziko,” kapena kuti maganizo amene amachititsa anthu ambiri kuchita zinthu zosemphana ndi chifuniro cha Mulungu. (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2) M’pake kuti anthu ambiri masiku ano sakhala osangalala.​—Miyambo 18:11; 23:4, 5.

9. Kodi n’chiyani chimene anthu sangathe kuchita, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Nanga bwanji za anthu amene amafuna kuthandiza ena mwa kuyesetsa kuthetsa njala, matenda ndi chinyengo? Iwo amachita bwino ndipo amathandiza anthu ambiri. Komatu, ngakhale akuyesetsa kutero sangasinthe dongosolo lino n’kukhala labwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” yemwe ndi Satana, ndipo iye safuna kuti lisinthe.​—1 Yohane 5:19.

10. Ndi liti pamene anthu okhulupirika adzakhale ndi “moyo weniweniwo”?

10 Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati chiyembekezo cha munthu chili pa moyo uno wokha. Paulo analemba kuti: “Ngati tayembekeza Khristu m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.” Anthu amene amakhulupirira kuti moyo ndi uno wokha, ali ndi maganizo akuti, “tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa.” (1 Akorinto 15:19, 32) Koma pali chiyembekezo cha “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo [la Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Panthawi imeneyo, Akhristu adzasangalala ndi “moyo weniweniwo,” womwe ndi “moyo wosatha,” ndipo adzakhala angwiro kumwamba kapena padziko lapansi molamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu.​—1 Timoteyo 6:12.

11. N’chifukwa chiyani kugwira ntchito yopititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu ndi cholinga chabwino kwambiri?

11 Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetseretu mavuto onse a anthu. Choncho kugwira ntchito yopititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu ndi cholinga chabwino kwambiri chimene aliyense afunika kukhala nacho. (Yohane 4:34) Tikatero, tidzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wakumwamba. Timasangalalanso kutumikira pamodzi ndi abale ndi alongo ambiri amene ali ndi cholinga chimenechi.

Kudzipereka pa Zinthu Zoyenera

12. Kodi moyo m’dongosolo lino ukusiyana bwanji ndi “moyo weniweniwo”?

12 Baibulo limanena kuti dzikoli “likupita limodzi ndi chilakolako chake.” Choncho, palibe mbali ya dziko la Satanali imene idzapulumuka kuphatikizapo kutchuka ndiponso chuma, ‘koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhalabe kosatha.’ (1 Yohane 2:15-17) Mosiyana ndi chuma chosadalirika, ulemu wakanthawi, ndiponso chisangalalo chochepa cha m’dzikoli, ‘moyo weniweni,’ womwe ndi moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu, n’ngokhalitsa ndipo tidzaupeza ngati tikhala odzipereka pa zinthu zoyenera.

13. Kodi banja lina linatani kuti likhale lodzipereka pa zinthu zoyenera?

13 Taganizirani za Henry ndi Suzanne. Iwo amakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo la Mulungu lakuti iye adzathandiza anthu amene amaika patsogolo Ufumu wake. (Mateyo 6:33) Choncho, iwo anasankha kukhala m’nyumba yotsika mtengo, m’malo moti onse azigwira ntchito yolembedwa kuti apeze ndalama zolipilira nyumba. Zimenezi zinawathandiza kukhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu pamodzi ndi ana awo aakazi awiri. (Aheberi 13:15, 16) Mnzawo wina sanamvetse zimene anachitazi, ndipo poganiza kuti akuwafunira zabwino anauza Suzanne kuti: “Suzanne ngati ukufuna kukhala m’nyumba yabwino tangozisiya zinazi.” Koma Henry ndi Suzanne anadziwa kuti kuika Yehova patsogolo “kuli ndi lonjezo la moyo uno ndi umene ukubwerawo.” (1 Timoteyo 4:8; Tito 2:12) Ana awo atakula anakhala atumiki a nthawi zonse achangu kwambiri. Banja lonse likuona kuti silinataye chilichonse chofunika, m’malo mwake linapindula kwambiri chifukwa cha cholinga chawo chofuna kupeza “moyo weniweniwo.”​—Afilipi 3:8; 1 Timoteyo 6:6-8.

‘Tisaligwiritse Ntchito Mokwanira Dzikoli’

14. Kodi pangakhale ngozi yotani ngati tiiwala cholinga chathu pamoyo?

14 Pangakhale ngozi yaikulu ngati tiiwala cholinga chathu, n’kusiya kugwiritsitsa “moyo weniweniwo.” Tingathe ‘kutengeka ndi nkhawa, chuma, ndi zosangalatsa za moyo uno.’ (Luka 8:14) Kufunitsitsa chuma komanso “nkhawa za moyo,” zingachititse munthu kutengeka kwambiri ndi dongosolo lino la zinthu. (Luka 21:34) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amatanganidwa kwambiri ndi moyo wofuna chuma moti “asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo,” mpaka kufika powononga ubwenzi wawo wamtengo wapatali ndi Yehova. Iyitu ndi ngozi yaikulu imene athu omwe asiya ‘kugwira zolimba moyo wosatha’ amakumana nayo.​—1 Timoteyo 6:9, 10; Miyambo 28:20.

15. Kodi banja lina linapindula bwanji chifukwa ‘chosagwiritsa ntchito mokwanira dzikoli’?

15 Paulo anapereka malangizo akuti: “Amene amagwiritsa ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsa ntchito mokwanira.” (1 Akorinto 7:31) Keith ndi Bonnie anatsatira malangizo amenewa. Keith anati: “Ndinakhala wa Mboni za Yehova nditangomaliza maphunziro a udokotala wa mano. Ndinali ndi mwayi wothandiza anthu ambiri odwala n’kumapeza ndalama zochuluka, koma zimenezi zikanasokoneza moyo wathu wauzimu. Choncho ndinasankha kuthandiza anthu ochepa n’cholinga choti ndizikhala ndi nthawi yochita zinthu zauzimu ndiponso yocheza ndi banja langa kuphatikizapo ana athu aakazi asanu. Ngakhale kuti tinkakhala ndi ndalama zochepa, tinaphunzira kuzigwiritsa ntchito mwanzeru ndipo nthawi zonse tinkapeza zinthu zofunika. Banja lathu linali logwirizana ndiponso losangalala kwambiri. Kenako tonse tinayamba utumiki wa nthawi zonse. Tsopano ana athuwo anakwatiwa ndipo akusangalala m’mabanja mwawo. Atatu mwa iwo ali ndi ana. Nawonso mabanja awo ndi osangalala chifukwa akupitirizabe kuika chifuniro cha Yehova patsogolo.”

Ikani Cholinga cha Mulungu Poyamba M’moyo Wanu

16, 17. Tchulani anthu a m’Baibulo omwe anali ndi luso losiyanasiyana, komanso zinthu zimene amakumbukiridwa nazo.

16 Baibulo lili ndi zitsanzo za anthu amene anakhala mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu ndi amene sanatero. Zimene timaphunzira pa zitsanzo zimenezi n’zothandiza anthu amisinkhu yonse, azikhalidwe zosiyanasiyana ndiponso a moyo wosiyanasiyana. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:6, 11) Nimrode anamanga mizinda yaikulu motsutsana ndi cholinga cha Yehova. (Genesis 10:8, 9) Komabe, pali anthu ena ambiri omwe ndi zitsanzo zabwino. Mwachitsanzo, cholinga cha Mose pamoyo sichinali choti apitirize kukhala ndi udindo wolemekezeka ku Iguputo. Koma anaona kuti utumiki umene Mulungu anam’patsa unali “chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo.” (Aheberi 11:26) N’kutheka kuti Luka yemwe anali dokotala, anathandiza Paulo ndi anthu enanso pamene ankadwala. Koma zinthu zabwino kwambiri zimene anachita zinali kulalikira ndiponso kulemba Baibulo. Ponena za Paulo, iye sankadziwika ngati katswiri wa Chilamulo koma monga mmishonale, “mtumwi weniweni wotumidwa kwa mitundu ina.”​—Aroma 11:13.

17 Davide amakumbukiridwa monga “munthu wa pamtima [pa Mulungu],” osati ngati mkulu wa asilikali kapena woimba ndi kupeka nyimbo. (1 Samueli 13:14) Timadziwa Danieli osati monga mkulu wa boma la Ababulo, koma chifukwa cha utumiki wake monga mneneri wokhulupirika wa Yehova. Estere sitim’dziwa ngati mfumukazi ya Perisiya, koma monga chitsanzo cha munthu wachikhulupiriro ndi wolimba mtima. Petulo, Andreya, Yakobe ndi Yohane amadziwika monga atumwi a Yesu osati ngati asodzi odziwa bwino ntchito yawo. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi cha Yesu, yemwe amadziwika monga “Khristu” osati “mmisiri wa matabwa.” (Mateyo 16:16; Maliko 6:3) Anthu onsewa anazindikira kuti ngakhale anali ndi luso, chuma kapena udindo m’dzikoli, kutumikira Mulungu kunayenera kukhala cholinga chawo chachikulu pamoyo. Iwo anadziwa kuti cholinga chabwino ndiponso chopindulitsa kwambiri chinali kukhala munthu woopa Mulungu.

18. Kodi Mkhristu wina wachinyamata anasankha kuchita chiyani pamoyo wake ndipo anazindikira chiyani?

18 Seung Jin amene tam’tchula kumayambiriro uja anazindikira mfundo imeneyi. Iye anati: “M’malo mogwira ntchito ya udokotala, yojambula zithunzi kapena uphunzitsi, ndinasankha kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwanga kwa Mulungu. Panopa, ndikutumikira kudera limene kulibe anthu okwanira ophunzitsa Baibulo, ndipo ndikuthandiza anthu kuyenda m’njira ya kumoyo wosatha. Poyamba ndinkaona kuti utumiki wa nthawi zonse sufuna zinthu zambiri. Koma tsopano ndili ndi zochita zambiri kuposa kale lonse, monga kusintha khalidwe langa ndi kuphunzitsa anthu azikhalidwe zosiyanasiyana. Ndikuona kuti kuika patsogolo cholinga cha Yehova m’moyo wathu ndi njira yabwino kwambiri.”

19. Kodi tingapeze bwanji cholinga chenicheni pamoyo?

19 Akhristufe tapatsidwa uthenga wopulumutsa moyo ndipo tapatsidwanso chiyembekezo cha chipulumutso. (Yohane 17:3) Choncho, ‘tisalandire kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtima kumeneko.’ (2 Akorinto 6:1) M’malo mwake, tiyenera kugwiritsa ntchito moyo wathu wamtengo wapatali kulemekeza Yehova. Tiyeni tilalikire uthenga umene umabweretsa chisangalalo panopa komanso umene umatsogolera ku moyo wosatha. Tikatero tidzavomereza mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ndipo tidzakhala ndi cholinga chenicheni pamoyo wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Mayina ena tawasintha.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi cholinga chofunika kwambiri chimene tiyenera kukhala nacho ndi chiti?

• N’chifukwa chiyani kufunafuna chuma n’kupanda nzeru?

• Kodi “moyo weniweniwo” umene Mulungu walonjeza n’chiyani?

• Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito moyo wathu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Akhristu afunika kudzipereka pa zinthu zoyenera