Wolamulira Wachuma Sanasankhe Bwino
Wolamulira Wachuma Sanasankhe Bwino
WOLAMULIRA wachuma wachinyamata anali wokonda chilungamo, womvera malamulo, ndiponso wokonda kupembedza. Iye atabwera kwa Yesu, anagwada pansi n’kufunsa kuti: “Mphunzitsi wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”
Poyankha, Yesu anauza mnyamatayo kuti afunikira kutsatira malamulo a Mulungu ngati akufuna moyo wosatha. Atafunsa kuti malamulo ake ndi ati, Yesu anati: “Usaphe munthu, Usachite chigololo, Usabe, Usapereke umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amayi wako, komanso, Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.” Amenewa anali malamulo akuluakulu a m’Chilamulo cha Mose. Kenako mnyamatayo anati: “Ndakhala ndikuzitsatira zonsezi; n’chiyaninso chimene ndikupereweza?”—Mateyo 19:16-20.
Yesu “anam’konda” mnyamatayo ndipo anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita, kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndi kupatsa ndalamazo osauka, pamenepo chuma udzakhala nacho kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”—Maliko 10:17-21.
Yesu anamusiya mnyamatayo ndi ntchito yaikulu kwambiri yosankha chochita. Kodi iye anatani? Kodi anapereka chuma chake n’kukhala wotsatira wa Yesu, kapena anakakamirabe chuma chake? Kodi anasankha chuma cha padziko lapansi kapena chuma chakumwamba? Sizinali zophweka kuti asankhe chimodzi. N’zowonekeratu kuti mnyamatayu ankakonda zinthu zauzimu, chifukwa ankatsatira Chilamulo ndipo anafunsa mafunso ofuna kudziwa zimene angachite kuti Mulungu am’konde. Ndiyeno kodi anasankha chiyani? Iye “anachoka ali wachisoni, pakuti anali ndi katundu wochuluka.”—Maliko 10:22.
Wolamulira wachinyamata ameneyu sanasankhe bwino. Akanakhala wotsatira wa Yesu
wokhulupirika, akanapeza moyo wosatha umene iye ankafuna. Baibulo silifotokoza zimene kenako zinachitikira mnyamatayu. Koma zimene tikudziwa n’zakuti, patatha zaka pafupifupi 40, asilikali Achiroma anawononga Yerusalemu ndi madera ambiri a Yudeya. Panthawi imeneyi, Ayuda ambiri anataya chuma ndiponso moyo wawo.Mosiyana ndi wolamulira wachinyamatayu, mtumwi Petulo ndi ophunzira ena anasankha mwanzeru. Iwo ‘anasiya zinthu zonse’ ndi kutsatira Yesu. Anasankha bwino kwambiri! Yesu anawauza kuti adzalandira zinthu zambiri kuposa zimene iwo anasiya. Koposa zonse, adzalandira moyo wosatha. Iwo sanasankhe molakwika moti n’kunong’oneza bondo.—Mateyo 19:27-29.
Tonsefe timasankha zochita pamoyo wathu, zina zazing’ono, zina zazikulu. Kodi Yesu anatipatsa malangizo otani pankhani yosankha zochita? Kodi musankha kumvera malangizo ake? Ngati mutatero, mudzadalitsidwa kwambiri. Tiyeni tione mmene tingatsatirire Yesu ndiponso mmene tingapindulire ndi zimene iye ananena.