Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumangoganizira za Lero Zokha Basi?

Kodi Mumangoganizira za Lero Zokha Basi?

Kodi Mumangoganizira za Lero Zokha Basi?

“SINDITAYA nthawi kuganizira za m’tsogolo chifukwa zimakhala zitafika kale ndisanamalize n’komwe kuganiza.” Anthu ambiri amati mawu otchukawa ananenedwa ndi katswiri wa sayansi Albert Einstein. Enanso ambiri amaganiza chimodzimodzi. Iwo amati: “Palibe chifukwa chodzivutitsira ndi kuganiza za m’tsogolo.” Mwina munamvaponso anthu akunena kuti: “Osalimbana ndi zambiri.” “Ganizirani za lero basi.” “Iwalani za mawa.”

Maganizo amenewa si achilendo. Anthu akale otchedwa Aepikuleya anali ndi mawu akuti: “Idya, imwa, sangalala. Zina zonse zilibe ntchito.” Anthu ena a m’nthawi ya mtumwi Paulo analinso ndi maganizo ofanana ndi amenewa. Iwo ankati: “Tiyeni tidye ndi kumwa, popeza mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Iwo ankakhulupirira kuti moyo umene ulipo ndi wokhawu basi. Choncho ankalimbikitsa maganizo akuti tizisangalala nawo mmene tingathere.

Komabe, kwa anthu ambiri padziko pano, n’zosatheka n’komwe kukhala ndi moyo womangosangalala. Tsiku lililonse pamoyo wawo, amangokhalira kuvutika. Ndiye angavutikirenji n’kuganizira za mawa pamene akudziwa kale kuti mawalo mavuto akuwadikirira?

Kodi Tiziganizira za Mawa?

Ngakhalenso anthu amene alibe mavuto ambiri saona chifukwa chodzivutitsira ndi kuganizira za mawa. Ena amaona kuti anthu amene amaganizira za m’tsogolo amangotaya nthawi chifukwa amadzakhumudwa zinthuzo zikalephereka. Ngakhale Yobu, anakhumudwa kwambiri ataona kuti zinthu zimene ankaganizira zalephereka n’kusokonezeratu tsogolo lake ndi la banja lake.​—Yobu 17:11; Mlaliki 9:11.

Wolemba ndakatulo wina wa ku Scotland, dzina lake Robert Burns, anayerekezera vuto lathuli ndi vuto la mbewa inayake imene iye anaiphwasulira chisa chake mwangozi akulima ndi pulawo. Mbewayo inabulika n’kuthawa, nyumba yakeyo itawonongedwa. Ataona zimenezi, iye anati: ‘Umutu ndi mmene zimakhalira tikakumana ndi vuto loposa msinkhu wathu. Ngakhale titayesetsa motani kuti tilithetse, siziphula kanthu.’

Ndiye kodi kuganizira za mawa n’kungodzivutitsa? Ayi, chifukwatu kusakonzekera bwino zinthu kumabweretsa mavuto aakulu. Mwachitsanzo, n’zoona kuti palibe munthu amene akanaletsa mphepo yamkuntho yotchedwa Katrina, imene inasakaza kwambiri mzinda wina wa ku America. Komatu kukonzekera kukanathandiza kuti mphepoyo isawononge kwambiri mzindawo ndi kusowetsa mtendere anthu ambiri.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi ndi nzeru kumangoganizira za lero zokha basi n’kuiwala za mawa? Tawerengani zimene nkhani yotsatirayi ikunena pa mfundo imeneyi.

[Zithunzi patsamba 3]

“Idya, imwa, sangalala. Zina zonse zilibe ntchito”

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi inuyo mukuona kuti kukonzekera kukanathandiza kuti mphepo ya Katrina isawononge kwambiri?

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Coast Guard Digital