Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Londolani Kuwala

Londolani Kuwala

Londolani Kuwala

NSANJA zimene zimakhala ndi nyale yolondolera anthu oyenda pa nyanja zapulumutsa miyoyo ya anthu ambiri. Koma munthu wapaulendo yemwe watopa kwambiri, akaona kuwala pamtunda wautali amadziwa kuti kuwalako si kukum’chenjeza chabe za malo oopsa. Koma kukum’thandizanso kudziwa kuti watsala pang’ono kufika. Mofanana ndi zimenezo, Akhristu masiku ano, akuyandikira mapeto a ulendo wawo wautali wodutsa m’dziko loopsa lomwe lili mumdima wauzimu. M’Baibulo anthu onse omwe sachita zimene Mulungu amafuna akuyerekezeredwa ndi “nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi uve.” (Yesaya 57:20) Anthu a Mulungu akukhala pamodzi ndi anthu oterewa. Komabe, iwo ali ndi chiyembekezo chabwino cha chipulumutso. Ndipo kwa iwo, chiyembekezo chimenechi chili ngati kuwala kodalirika. (Mika 7:8) Chifukwa cha Yehova ndiponso Mawu ake olembedwa, “kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima.”​—Salmo 97:11. *

Komabe, Akhristu ena alola kudodometsedwa ndi zinthu zina mpaka kuchoka m’kuwala kwa Yehova. Zinthu zimenezi ndi monga kukonda chuma, chiwerewere, ngakhalenso mpatuko, zomwe tingaziyerekezere ndi miyala yoopsa chifukwa zachititsa kuti chikhulupiriro chawo chisweke ngati ngalawa. N’zoonadi, monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, anthu ena masiku ano “chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.” (1 Timoteyo 1:19; 2 Petulo 2:13-15, 20-22) Dziko latsopano lingayerekezeredwe ndi doko limene tikupita. Popeza kuti tatsala pang’ono kufika, zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati wina atasiya kuyanjidwa ndi Yehova.

Samalani Kuti ‘Chikhulupiriro Chanu Chisasweke Ngati Ngalawa’

Kale, ngalawa inkatha kuyenda bwinobwino m’katikati mwa nyanja, koma n’kusweka itangotsala pang’ono kufika ku doko. Mofananamo, kwa anthu ambiri, “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu ndi nthawi yoopsa kwambiri, m’mbiri yonse ya anthu. Baibulo limafotokoza molondola kuti masiku amenewa ndi “nthawi yovuta,” makamaka kwa Akhristu odzipereka.​—2 Timoteyo 3:1-5.

N’chifukwa chiyani masiku amenewa ali ovuta? Satana akudziwa kuti wangotsala ndi “kanthawi kochepa” kolimbana ndi anthu a Mulungu. Choncho, iye akuyesetsa kwambiri pankhondo yoti aswe chikhulupiriro chawo. (Chivumbulutso 12:12, 17) Komabe, sikuti ife tangokhala opanda thandizo ndiponso chitsogozo. Nthawi zonse Yehova ndi pothawira pa anthu amene amatsatira uphungu wake. (2 Samueli 22:31) Iye watipatsa zitsanzo zotichenjeza zimene zimavumbula machenjera oipa a Satana. Tsopano, tiyeni tione zitsanzo ziwiri zokhudza mtundu wa Isiraeli pamene unatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa.​—1 Akorinto 10:11; 2 Akorinto 2:11.

Atayandikira Dziko Lolonjezedwa

Motsogoleredwa ndi Mose, Aisiraeli anatha kutuluka m’dziko la Iguputo. Posapita nthawi, anayandikira malire a kum’mwera a Dziko Lolonjezedwa. Kenako, Mose anatuma amuna 12 kuti akazonde dzikolo. Amuna 10 opanda chikhulupiriro anabweretsa uthenga wosalimbikitsa, ndipo anati Aisiraeli sangapambane ngati atamenyana ndi Akanani chifukwa anthu ake anali “aatali misinkhu” ndiponso anali akatswiri pomenya nkhondo. Kodi zimenezi zinawakhudza bwanji Aisiraeli? Nkhaniyi imanena kuti iwo anayamba kudandaulira Mose ndi Aroni kuti: “Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chawo. . . . Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo.”​—Numeri 13:1, 2, 28-32; 14:1-4.

Tangoganizani! Anthuwa anali atadzionera okha Yehova akugonjetsa mochititsa manyazi Iguputo, ufumu wa mphamvu kwambiri padziko lonse nthawi imeneyo, mwa kuwakantha ndi miliri 10 yoopsa kwambiri komanso chozizwitsa chochititsa mantha kwambiri pa Nyanja Yofiira. Ndipo Dziko Lolonjezedwa linali pafupi kwambiri moti anafunika kungoyenda ngati ngalawa imene ikuyenda molunjika kuwala kwa pa doko limene ikupita. Koma iwo ankaona kuti Yehova sangathe kugonjetsa timaufumu ting’onoting’ono komanso togawikana ta Akanani. N’zosachita kufunsa kuti Mulungu, Yoswa ndiponso Kalebe, anakhumudwa kwambiri ndi kupanda chikhulupiriro kumeneku, chifukwa Yoswa ndi Kalebe, omwe anakazonda nawo dziko la Kanani, ankaliona ngati “mkate [kwa Aisiraeli]”. Ndipotu, anthu awiriwa ankadziwa zoona zenizeni chifukwa anali atayenda m’dziko la Kanani. Anthuwo atalephera kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa ndi Kalebe anakhala nawo m’chipululu zaka zambirimbiri, koma sanafere limodzi ndi anthu opanda chikhulupirirowo. Yoswa ndi Kalebe anatsogolera m’badwo wotsatira kuchoka m’chipululu n’kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 14:9, 30) Koma atayandikiranso Dziko Lolonjezedwalo, Aisiraeli anakumana ndi chiyeso cha mtundu wina. Kodi anachita bwanji?

Balaki, mfumu ya a Moabu, anauza mneneri wonyenga Balamu kuti atemberere Aisiraeli. Komabe, Yehova analepheretsa zimenezi mwakuchititsa Balamu kuwadalitsa m’malo mowatemberera. (Numeri 22:1-7; 24:10) Komatu, Balamu sanalekere pomwepo, koma anapeza njira ina yolepheretsera anthu a Mulunguwo kulandira dzikolo. Kodi njirayo inali yotani? Anawakopa kuti achite chiwerewere ndiponso kulambira Baala. Ngakhale kuti Aisiraeli ambiri sanagwere m’tchimoli, anthu 24,000 anakopeka nalo. Iwo anachita chiwerewere ndi akazi achimoabu ndiponso anayamba kupembedza nawo Baala wa ku Peori.​—Numeri 25:1-9.

Tangoganizani! Ambiri mwa Aisiraeli amenewa anali ataona Yehova akuwatsogolera bwinobwino kudutsa “m’chipululu chachikulu ndi choopsa chija.” (Deuteronomo 1:19) Koma ali pafupi kulandira cholowa chawo, anthu a Mulungu okwana 24,000 anatsatira zilakolako zathupi n’kuphedwa ndi Yehova. Ilitu ndi chenjezo lamphamvu kwa atumiki a Mulungu masiku ano pamene angotsala pang’ono kulandira cholowa chawo chamtengo wapatali.

Satana sakufunikira njira zatsopano pamene akuyesayesa komaliza kulepheretsa atumiki a Yehova a masiku ano kuti alandire mphoto yawo. Mofanana ndi mmene zinalili ndi Aisiraeli atayandikira koyamba Dziko Lolonjezedwa, nthawi zambiri Satana amayesetsa kuchititsa atumiki a Mulungu kukhala amantha ndiponso okayikakayika. Amatero mwa kuchititsa anthu ena kuwaopseza, kuwazunza kapena kuwanyoza. Ndipo Akhristu ena agonja chifukwa cha zimenezi. (Mateyo 13:20, 21) Njira ina imene amakonda kugwiritsa ntchito ndiyo kusokoneza maganizo a anthu pankhani ya makhalidwe. Nthawi zina, anthu amene alowa mumpingo wachikhristu ndi zolinga zoipa, amayesa kusokoneza maganizo a anthu ofooka mwauzimu, ndiponso amene sakulondola ndi mtima wonse kuwala kwa Mulungu.​—Yuda 8, 12-16.

Kwa anthu omwe ali paubwenzi wolimba ndi Mulungu ndiponso amene ndi atcheru kwambiri, kulowa pansi kwa makhalidwe m’dzikoli ndi umboni wosatsutsika wakuti Satana sakugona tulo pantchito yake. Iye akudziwa kuti posachedwapa sadzathanso kusokoneza atumiki okhulupirika a Mulungu. Choncho, ino ndi nthawi yoti tikhale tcheru mwauzimu ndi zochita za Satana.

Zimene Zingatithandize Kukhala Tcheru Mwauzimu

Mtumwi Petulo anafotokoza kuti mawu aulosi a Mulungu ali ngati “nyale imene ikuwala mumdima,” chifukwa amathandiza Akhristu kuona ndiponso kumvetsa za kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu. (2 Petulo 1:19-21) Anthu amene amakonda Mawu a Mulungu ndiponso kuwalola kuti apitirize kuwatsogolera, amaona kuti Yehova amawongola mayendedwe awo. (Miyambo 3:5, 6) Chifukwa chokhala ndi chiyembekezo, anthu oyamikira amenewa ‘amaimba ndi mtima wosangalala,’ koma anthu osadziwa Yehova kapena amene asiyiratu njira zake, ali ndi “mtima wachisoni,” ndiponso ‘n’ngosweka mzimu.’ (Yesaya 65:13, 14) Choncho, ngati tiphunzira Baibulo mwakhama ndiponso kuchita zimene tikuphunzirazo, nthawi zonse maganizo athu adzakhala pa zinthu zodalirika zimene tikuyembekezera, osati pa zosangalatsa zakanthawi za m’dongosolo lino la zinthu.

Pemphero nalonso n’lofunika kwambiri kuti tikhalebe atcheru mwauzimu. Pamene ankanena za mapeto a dongosolo lino, Yesu anati: “Chotero khalani maso, muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) Onani kuti Yesu ananena kuti “muzipemphera mopembedzera,” zimene zikutanthauza kupemphera ndi mtima wofunitsitsa. Yesu anadziwa kuti m’nthawi yovuta ino n’zosavuta kuti anthu ataye mwayi wopeza moyo wosatha. Kodi mapemphero anu amasonyeza kuti mukufunitsitsadi kukhalabe atcheru mwauzimu?

Tisaiwale kuti nthawi yoopsa kwambiri ya ulendo wokalandira cholowa chathu ingakhale pamene tayandikira mapeto. Motero, tiyeni tiyesetse kukhala tcheru kuti tisasiye kulondola kuwala komwe kungatitsogolere ku chipulumutso.

Chenjerani ndi Kuwala Konyenga

Kalekale, vuto lina limene anthu oyenda pa ngalawa ankakumana nalo linali zimene anthu oipa ankachita usiku, kukakhala kopanda mwezi pamene oyendetsa ngalawa ankavutika kuona gombe. Anthu oipawa ankatha kuika nyale m’gombe loopsa kuti oyendetsa ngalawa asochere. Ngalawa za anthu amene apusitsidwa mwanjira imeneyi zinkatha kusweka, katundu wawo n’kubedwa ndipo anthu a m’ngalawazo ankatha kuphedwa.

N’chimodzimodzinso ndi zimene Satana, yemwe ndi “mngelo wa kuwala” konyenga amachita. Iye akufuna kusokoneza ubwenzi wa pakati pa Mulungu ndi anthu Ake. Mdyerekezi angagwiritse ntchito “atumwi onama” ndi “atumiki a chilungamo” ampatuko kuti anyenge anthu osazindikira. (2 Akorinto 11:13-15) Oyendetsa ngalawa atcheru kwambiri ndiponso odziwa bwino ntchito yawo sankapusitsidwa chisawawa ndi kuwala konyenga. Mofananamo, Akhristu “amene pogwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira, aphunzitsa lunthalo kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika,” sasocheretsedwa ndi anthu amene amalimbikitsa ziphunzitso zonyenga ndiponso zoipa kwambiri.​—Aheberi 5:14; Chivumbulutso 2:2.

Oyendetsa ngalawa ankayenda ndi chikalata chosonyeza malo amene muli nsanja za nyale yolondolera anthu oyenda pa nyanja. Chikalatacho chinkafotokoza maonekedwe a nyale iliyonse. Buku lina limati: “Oyendetsa ngalawa ankazindikira nyale iliyonse imene angaione, komanso ankadziwa kuti tafika pa malo akutiakuti, chifukwa cha maonekedwe a nyaleyo komanso mothandizidwa ndi chikalatacho.” (The World Book Encyclopedia) Umu ndi mmenenso zimakhalira ndi Mawu a Mulungu. Mawu amenewa amathandiza anthu okonda choonadi kuzindikira kulambira koona ndiponso kuzindikira anthu amene akulambira moona, makamaka m’masiku otsiriza ano pamene Yehova wachititsa kuti kulambira koonako kukhale kokwezeka kuposa chipembedzo chonyenga. (Yesaya 2:2, 3; Malaki 3:18) Posonyeza kusiyana pakati pa kulambira koona ndi konyenga lemba la Yesaya 60:2, 3 limati: “Mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.”

Chikhulupiriro cha anthu ambiri ochokera m’mitundu yonse, amene akupitirizabe kutsogoleredwa ndi kuwala kwa Yehova, sichidzasweka pamene akuyandikira mapeto a ulendo wawo. M’malo mwake, iwo adzadutsa bwinobwino m’masiku otsalawa a dongosolo lino la zinthu n’kulowa m’dziko latsopano lamtendere.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti “kuwala” m’njira zosiyanasiyana zophiphiritsa. Mwachitsanzo, Baibulo limati Mulungu ndi kuwala. (Salmo 104:1, 2; 1 Yohane 1:5) Ndiponso limayerekezera kuwala ndi mfundo zonena za Mulungu zopezeka m’Mawu ake. (Yesaya 2:3-5; 2 Akorinto 4:6) Pa utumiki wake padziko lapansi, Yesu anali kuwala. (Yohane 8:12; 9:5; 12:35) Ndipo otsatira a Yesu analamulidwa kuti aonetse kuwala kwawo.​—Mateyo 5:14, 16.

[Chithunzi patsamba 15]

Mofanana ndi oyendetsa ngalawa, Akhristu amakhala osamala kuti asasocheretsedwe ndi kuwala konyenga