Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Amene Timalimbana Nawo Popereka Uthenga Wabwino

Mavuto Amene Timalimbana Nawo Popereka Uthenga Wabwino

Mavuto Amene Timalimbana Nawo Popereka Uthenga Wabwino

GALIMOTO yathu ikuyandikira pa rodibuloko imene pali anthu pafupifupi 60 okhala ndi mfuti. Anthuwo ndi amuna, akazi, ndi achinyamata. Ena avala zachisilikali, ena zovala wamba, koma ambiri anyamula mfuti zoopsa. Akuoneka kuti akudikira kuti tifike. Kunotu kuli nkhondo yapachiweniweni.

Tayenda kwa masiku anayi, ndipo galimoto yathu yanyamula mabuku ofotokoza Baibulo olemera matani 10. Komabe, sitikudziwa ngati atilole kudutsa. Mwina afuna ndalama, mwinanso zitenga nthawi yaitali kwambiri kuti akhulupirire kuti ulendo wathu ndi wamtendere.

Mwamuna wina amene kwa iye kuombera mfuti si nkhani, akuwombera mfuti yake m’mwamba pofuna kutionetsa kuti iye ndiye wamkulu pano. Ataona mafoni athu a m’manja, akulamula kuti timupatse. Titazengereza pang’ono, iye akupereka chizindikiro chakuti tikalimbalimba, aticheka pa khosi. Titaona zimenezo, sitikuchitira mwina koma kumupatsa mafoni athuwo.

Kenako, tikuona mkazi wina atavala zachisilikali akubwera potero atanyamula mfuti. Akuti ameneyu ndi sekiritale, ndipo nayenso akufuna kuti timupatseko kanthu. Kuno moyo ndi wovuta ndipo munthu amafunika kenakake kangachepe. Msilikali wina akutenga jerikani yake n’kuyamba kupopa mafuta m’galimoto yathu. Titadandaula, akutiuza kuti akungochita zimene wauzidwa. Motero, tikungomuyang’ana n’kumapempherera kuti ena asatengere nzeru zakezo.

Pamapeto pake, akutilola kuti tidutse ndipo tikupitiriza ulendo wathu. Zitatero, mtima wathu ukukhala pansi. Zinali zoopsa, koma zochitika ngati zimenezi tazizolowera. Zili choncho chifukwa chakuti kuyambira April 2002 mpaka January 2004, tinayenda maulendo 18 kuchokera ku Douala m’dziko la Cameroon, kupita ku Bangui likulu la dziko la Central African Republic. Paulendo wamakilomita 1,600 umenewu, timadziwa kuti chilichonse chingathe kuchitika. *

Joseph ndi Emmanuel, madalaivala amene amapitapita kumeneku, anati: “Pamaulendo amenewa taphunzirapo zinthu zambiri. Taphunzira kuti tikakumana ndi mavuto, ndi bwino kusatekeseka komanso kupemphera chamumtima mobwerezabwereza. Wamasalmo anati: ‘Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa; munthu adzandichitanji?’ Timayesetsa kukhala ndi mtima umenewu. Timakhulupirira kuti Yehova akudziwa kuti ulendo wathu ndi wokapereka uthenga wopatsa anthu chiyembekezo chimene akufunikira kwambiri.”​—Salmo 56:11.

Mboni za Kumayiko Ena Zikuthandiza Kupereka Chakudya Chauzimu

Anthu ambiri kuno amakonda kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Timanyamula mabuku amene cholinga chake ndicho kuthandiza anthu kuthetsa njala yawo yauzimu. (Mateyo 5:3; 24:14) Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kuno ku Cameroon imatumiza mabuku kwa ofalitsa Ufumu oposa 30,000 ndiponso kwa anthu ena achidwi akunoko. Imatumizanso mabuku ku mayiko ena anayi oyandikana ndi dziko la Cameroon.

Mabukuwa amakhala atayenda mtunda wautali. Ambiri amasindikizidwa ku England, Finland, Germany, Italy, ndi Spain. Kenako amatumizidwa pa sitima yapamadzi kuchokera ku France. Pamilungu iwiri iliyonse, chikontena chimodzi cha thiraki chodzaza mabuku ofotokoza Baibulo chimafika pa doko la Douala.

Ndiye amanyamula chikontenacho pa thiraki n’kuchipititsa ku ofesi ya nthambi. Kumeneko amakalongedza mabukuwo mogwirizana ndi kumene akupita. Ntchito yotumiza mabukuwa kumadera a m’midzi ndi yovuta kwambiri. Koma kuchita zimenezi ndi mbali yopititsa uthenga wabwino “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Ofesi ya nthambi imadalira abale odzipereka omwe amalolera kuyenda ulendo woopsa umenewu. Mwanjira imeneyi, anthu ambiri a m’chigawo chapakati cha ku Africa kuno amalandira mabuku ofotokoza Baibulo.

Mmene Ulendowu Umakhalira

Ku Cameroon, Chad, Equatorial Guinea, Gabon, ndi ku Central African Republic mabuku amayenda pa galimoto. Tiyeni tikwere nawo galimoto imodzi yotereyi. Tayerekezerani kuti mwakhala m’galimoto ndi madalaivala, ndipo mwakonzekera ulendo wovuta koma wosangalatsa wamasiku 10 kapena kuposerapo.

Paulendowu pamakhala madalaivala 6. Iwo ndi amuna olimba, odalirika, oleza mtima, ndipo amavala bwino. Nthawi zina amavala zovala za kuno ku Africa, koma nthawi zina amavala shati ndi tayi. M’mbuyomu, akuluakulu oona za katundu wolowa ndi kutuluka m’dziko ananenapo kuti: “Taonani mmene galimoto yawo ilili yaukhondo ndipo madalaivala ake ndi ooneka bwino. Zikufanana ndendende ndi zithunzi za m’mabuku awo.” Ngakhale zili choncho, chofunika kwambiri kuposa maonekedwe awo ndi mtima wawo wodzipereka kupita kwina kulikonse kukatumikira anzawo.​—Salmo 110:3.

Tikunyamuka ku Douala pafupifupi 6 koloko m’mamawa, ndipo dzuwa langotuluka kumene. Tikutero kuti tisakumane ndi galimoto zambiri mumzinda wodzaza anthu umenewu. Titadutsa mlatho pafupi ndi ofesi ya nthambi ndi kutuluka mu mzinda wamagalimoto ambiriwu, tikulowera kum’mawa kupita ku Yaoundé, likulu la dziko la Cameroon. Kumeneku ndi kumene tiyambire kusiya mabuku.

Madalaivala onse 6 angathe kukuuzani kuti si ntchito yamasewera kuyendetsa thiraki itanyamula mabuku olemera matani 10. Kwa masiku atatu oyambirira, tikukumana ndi mavuto ochepa chabe chifukwa tikuyenda m’misewu yatala, koma m’pofunikabe kusamala. Kenako kukugwa chimvula chadzaoneni. Kuyambira pamenepa, msewu ndi wopanda tala. Tikuyenda pang’onopang’ono chifukwa tikuvutika kuona, msewu ndi woterera, ndiponso wamabampu. Dzuwa latsala pang’ono kulowa tsopano. Choncho tikuima n’kudya, ndipo kenako tikudzikakamiza kugona m’galimoto titapachika miyendo molozetsa ku galasi lakutsogolo. Moyo waketu ndi umenewu pamaulendo oterewa.

Tsopano kwacha, ndipo tikupitiriza ulendo wathu. Mmodzi wa madalaivala ali tcheru kuonetsetsa kuti msewuwo uli bwanji. Tikangoyandikira kwambiri ngalande, akumatichenjeza mwamsanga kuti tisamale. Madalaivala amadziwa kuti galimoto ikangolowa m’ngalande, ndiye kuti basi mutchona. Tsopano talowa m’dziko la Central African Republic koma tikupeza kuti misewu yake n’chimodzimodzi basi. Tikuyenda mtunda wamakilomita 650, ndipo mtunda wonsewo tikuona mapiri okongola komanso owirira. Galimoto yathu ikuyenda pang’onopang’ono kudutsa m’midzi ndipo tikuona ana, achikulire, ndi amayi ataberekera ana akutibayibitsa. Chifukwa cha nkhondo yapachiweniweni, m’misewu mulibe galimoto zambiri, ndipo anthu akutiyang’anitsitsa modabwa.

Nkhani Zolimbikitsa

Janvier, mmodzi wa madalaivala, akutiuza kuti ngakhale kuti iwo sakhala ndi nthawi yambiri paulendowu, amaimabe m’midzi kuti apume ndi kugawira mabuku. Iye akuti: “Ku Baboua tinkayesetsa kulankhula ndi munthu wina wogwira ntchito pachipatala amene ankachita chidwi kwambiri ndi uthenga wa Ufumu. Ndipo tinkaphunzira naye Baibulo mwachidule. Tsiku lina tinamuonetsa iyeyo ndi banja lake kaseti ya vidiyo ya Nowa. Anaitana anzake ndi achinansi, ndipo nyumba yake inadzaza anthu ofuna kuonerera. Aliyense anali atamvapo za Nowa, koma tsopano anatha kuonerera nkhani yake yonse. Tinakhudzidwa kwambiri kuona chidwi cha anthuwa. Titamaliza, anaphika chakudya chapadera pofuna kuyamikira, ndipo anatilimbikitsa kuti tigone konko. Chifukwa choti ulendowo unali wautali, sitikanatha kugona. Komabe tinasangalala kuti tauza anthu odzichepetsawa uthenga wabwino.”

Dalaivala wina, dzina lake Israel, akusimba zimene zinachitika pa ulendo wina wopita ku Bangui, kumene tikupitaku. Iye akuti: “Titayandikira kwambiri mzinda wa Bangui, tinaona kuti marodibuloko ayamba kuchuluka. Mwayi wake, asilikali ambiri anali ansangala ndipo anakumbukira kuti galimoto yathuyi inadutsapo pa malowa m’mbuyomo. Anatipatsa pokhala, ndipo analandira mabuku athu. Iwo amaona kuti mabuku ndi ofunikira kwambiri, choncho akalandira buku lililonse, amalembamo dzina lawo, tsiku limene alandira bukulo, ndiponso dzina la munthu amene wawapatsa bukulo. Ena mwa asilikaliwo ali ndi achibale awo a Mboni ndipo n’chifukwa chakenso anali ansangala.”

Joseph, yemwe wakhala zaka zambiri akuyendetsa galimoto, akufotokoza kuti chinthu chimene chimamusangalatsa kwambiri pa maulendowa ndi zimene zimachitika akafika kumene akupita. Iye akukumbikira ulendo wina wotere ponena kuti: “Titangotsala pang’ono kufika ku Bangui, tinaimbira telefoni abale athu kumeneko kuwauza kuti tifika posachedwa. Iwo anatiperekeza mumzindawo, ndi kutithandiza pokasainitsa mapepala osiyanasiyana kuboma. Titafika, anthu onse paofesi yanthambi anabwera n’kudzatikumbatira mwansangala. Abale ochokera m’mipingo yapafupi anabwera kudzathandiza kutsitsa ndi kulongedza makatoni a Mabaibulo, mabuku, timabuku, ndi maganizi moti tinamaliza ntchitoyi m’maola ochepa chabe.”

Joseph akupitiriza kunena kuti: “Nthawi zina pa katundu amene tinkanyamula pankakhalanso mphatso monga zovala, nsapato, ndi zinthu zina zokapatsa ana. Zonsezi zinkapita ku dziko loyandikana nalo la Democratic Republic of Congo. Zinalitu zosangalatsa kwambiri kuona abale akulandira mphatsozi chimwemwe chitadzaza tsaya.”

Titapuma tsiku limodzi, tikuonaona galimoto yathu n’kuyambapo ulendo wobwerera. Tikudziwa kuti tikumana ndi mavuto kutsogoloko, komano mavutowo sangapose chisangalalo chimene takhala nacho kunoko.

Pali zinthu zambiri zofoola monga kutalika kwa ulendowu, mvula yamphamvu, misewu yoipa, kuphwa kwa matayala, ndiponso kuwonongeka kwa galimoto. Nthawi zambiri amakumananso ndi asilikali ena ovuta. Komabe palibe chinthu china chimene chimasangalatsa madalaivalawa koposa kupereka uthenga wabwino wa Ufumu ku madera akumidzi amenewa n’kuona mmene ukukhudzira anthu amene akuulandira.

Mwachitsanzo, chifukwa cha ntchito imeneyi, m’mudzi wina ku Central African Republic pafupi ndi malire a dziko la Sudan, muli bambo yemwe tsopano amawerenga Baibulo lomasuliridwa mwamakono. Mkazi wake amawerenga magazini ongotuluka kumene a Nsanja ya Olonda, ndipo ana awo amasangalala kwambiri ndi buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. * Banja limeneli ndi anthu enanso ambiri a m’midziyi amalandira chakudya chauzimu chimenechi, monganso amachitira abale ndi alongo okhala m’mizinda yambiri ikuluikulu. Izitu n’zosangalatsa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuyambira nthawi imeneyi achita zambiri kuti akhwimitse chitetezo mumsewu wa pakati pa Douala ndi Bangui.

^ ndime 25 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CAMEROON

Douala

CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

Bangui

[Chithunzi patsamba 9]

Joseph

[Chithunzi patsamba 9]

Emmanuel

[Chithunzi patsamba 10]

Ofesi ya nthambi ya m’dziko la Central African Republic, ku Bangui

[Chithunzi patsamba 10]

Kutsitsa katundu ku Bangui