Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziganiziranso za Mawa

Muziganiziranso za Mawa

Muziganiziranso za Mawa

“MUSADE nkhawa za tsiku lotsatira,” anatero Yesu Khristu m’nkhani yake yotchuka, imene anakamba ali paphiri, ku Galileya. Malingana ndi Baibulo la Chipangano Chatsopano Cholembedwa M’Chicheŵa Chamakono, Yesu anapitiriza ndi mawu akuti: “Za maŵa n’zamaŵa.”​—Mateyo 6:34.

Kodi mukuganiza kuti mawu akuti “za maŵa n’zamaŵa” akutanthauza chiyani? Kodi akusonyeza kuti muzingoganizira za lero zokha basi n’kuiwala za mawa? Kodi zimenezi n’zimenedi Yesu komanso otsatira ake ankakhulupirira?

‘Lekani Kuda Nkhawa’

Werengani nokha zimene Yesu ananena pa Mateyo 6:25-32. Zina mwa zomwe ananena ndi izi: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu chimene mudzadya kapena chimene mudzamwa, kapena matupi anu chimene mudzavala. . . . Onetsetsani mbalame za mlengalenga, pajatu sizifesa kapena kukolola kapena kututira m’nkhokwe ayi; komabe Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. . . . Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa? Komanso pa nkhani ya zovala, n’chifukwa chiyani mukuda nkhawa? Phunzirani ku maluwa akuthengo, mmene akukulira; sagwira ntchito, ndiponso sawomba nsalu . . . Choncho musamade nkhawa n’kumati, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti amitundu akufunafuna mwakhama zinthu zonse zimenezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti zinthu zonsezi inu mukuzisowa.”

Yesu anamaliza mbali imeneyi ya nkhani yake potchula mfundo ziwiri. Yoyamba inali yakuti: “Pitirizani kufuna ufumu [wa Mulungu] choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” Yachiwiri inali yakuti: “Choncho musade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira patsikulo.”​—Mateyo 6:33, 34.

Atate Wanu Akudziwa Zimene Mukufunikira

Kodi mukuganiza kuti pamenepa Yesu anali kuletsa ophunzira ake, ngakhalenso alimi, kuti asiye ‘kufesa, kukolola kapena kututira dzinthu m’nkhokwe’? Kapenanso kodi ankawaletsa ‘kugwira ntchito, ndiponso kuwomba nsalu’ kuti akhale ndi zovala? (Miyambo 21:5; 24:30-34; Mlaliki 11:4) Ayi ndithu. Chifukwatu ngati iwowa akanasiya kugwira ntchito, n’zosachita kufunsa kuti ‘akanayamba kupemphapempha m’nyengo yamasika,’ posowa chakudya kapena chovala.​—Miyambo 20:4.

Nanga bwanji za nkhani ya nkhawa? Kodi Yesu ankatanthauza kuti anthuwo akanatha kupeweratu nkhawa? Zimenezo n’zosatheka. Ngakhale Yesu amene, anavutika kwambiri ndi maganizo komanso nkhawa atatsala pang’ono kugwidwa.​—Luka 22:44.

Apatu Yesu ankangotchula mfundo yofunika kwambiri kuiganizira, yakuti nkhawa sizingakuthandizeni kuthana ndi mavuto alionse. Mwachitsanzo, simungatalikitse moyo wanu ndi nkhawa. Yesu anati nkhawa singathe ‘kuwonjezera pa msinkhu wanu mkono umodzi.’ (Mateyo 6:27) Ndipotu kukhala ndi nkhawa kwa nthawi yaitali kungathe kukufupikitsirani moyo wanu.

Motero malangizo a Yesuwo anali othandiza kwambiri. Zinthu zambiri zimene timada nazo nkhawa sizichitika n’komwe. Nduna yaikulu yakale ya dziko la Britain, dzina lake Winston Churchill, inazindikira zimenezi panthawi yovuta ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ponena za zinthu zina zimene zinkamudetsa nkhawa panthawiyo iye anati: “Ndikamaganizira za zinthu zambiri zimene zinkandidetsa nkhawa panthawiyi, ndimakumbikira nkhani ya gogo winawake amene atatsala pang’ono kumwalira, ananena kuti pamoyo wake wakhala ndi mavuto ambiri. Ambiri mwa mavuto akewo sanakumane nawo n’komwe ayi, koma ankangowaganizira basi.” N’zoona kuti n’chinthu chanzeru kusada nkhawa ndi za mawa, makamaka ngati zimenezi zingachititse kuti tiyambe kuda nkhawa kwambiri.

‘Pitirizani Kufuna Ufumu wa Mulungu Choyamba’

Kwenikweni, Yesu sankangonena chabe za nkhawa yokhudza zinthu zofunika pamoyo wawo. Iye ankadziwa kuti nkhawa yokhudza kupeza zinthu zofunikira pamoyo kapenanso chuma ndi zosangalatsa, ingaiwalitse munthu zinthu zofunikira kwambiri. (Afilipi 1:10) Mwina mungaganize kuti: ‘Kodi palinso zinthu zina zofunika kuposa kupeza zinthu zofunikira pamoyo?’ Inde zilipo. Ndipo zimenezi ndi zinthu zauzimu zokhudza kulambira Mulungu. Yesu anagogomezera mfundo yakuti chinthu chofunikira kwambiri pamoyo ndicho ‘kufuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake.’​—Mateyo 6:33.

M’nthawi ya Yesu, anthu ambiri ankalimbana kwambiri ndi kufuna chuma. Komabe, Yesu analimbikitsa anthu amene ankamvera nkhani yakewo kuti asakhale otero. Poti anali anthu odzipereka kwa Mulungu, anayenera kutsatira malangizo akuti “opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—Mlaliki 12:13.

Anthuwa akanati aziganizira kwambiri za chuma, ndiye kuti “nkhawa za m’dongosolo lino la zinthu ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma,” zikanawasokonezeratu mwauzimu. (Mateyo 13:22) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopanda nzeru ndi zopweteka, zimene zimaponya anthu ku chiwonongeko chotheratu.” (1 Timoteyo 6:9) Pofuna kuwathandiza kupewa “msampha” umenewu, Yesu anauza anthu om’tsatira kuti Atate wawo wakumwamba akudziwa kuti iwo amafunikira zinthu zonsezi. Motero Iye aziwasamala monga amachitira ndi “mbalame za mlengalenga.” (Mateyo 6:26, 32) M’malo movutika kwambiri ndi nkhawa, iwo anayenera kuchita zonse zimene akanatha n’kusiya zonse m’manja mwa Yehova.​—Afilipi 4:6, 7.

Ponena kuti “za maŵa n’zamaŵa,” Yesu ankangotanthauza kuti tisamawonjezere mavuto a lero poda nkhawa kwambiri ndi zimene zingadzachitike mawa. Baibulo lina limamasulira mawuwa motere: “Musadere nkhawa ndi za mawa; chifukwa mawa lidzakhala ndi nkhawa zake zokwanira. Musawonjezere mavuto ena pa mavuto amene tsiku lililonse limakhala nawo.”​—Mateyo 6:34, Today’s English Version.

“Ufumu Wanu Ubwere”

Komano kusada nkhawa kwambiri ndi za mawa sikutanthauza kuti tiiwaliretu za mawazo. Yesu sanalimbikitse ophunzira ake kuchita zimenezi. M’malo mwake, iye anawalimbikitsa kuti aziganizira kwambiri zam’tsogolo. Inde, panalibe vuto kupempherera zofuna zawo za panthawiyo, monga chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku. Koma anayenera kuyamba kaye kupempherera zam’tsogolo. Zimenezi zinaphatikizapo kupempherera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere ndiponso kuti chifuniro chake chichitike.​—Mateyo 6:9-11.

Tisakhale ngati anthu a m’nthawi ya Nowa. Iwo anali otanganidwa kwambiri ndi “kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa” moti “sanazindikire” zimene zichitike patsogolo. Kodi mapeto ake anaona zotani? “Chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo.” (Mateyo 24:36-42) Mtumwi Petro anagwiritsira ntchito nkhani imeneyi pofuna kutikumbutsa kuti tiziganizira za mawa pamoyo wathu. Iye analemba kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu. Teroni poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.”​—2 Petulo 3:5-7, 11, 12.

Kundikani Chuma Kumwamba

Inde, tiziyesetsa “kukumbukira nthawi zonse” tsiku la Yehova. Zimenezi zidzatithandiza kwambiri kugwiritsira ntchito bwino nthawi, mphamvu, luso, chuma, ndiponso nzeru zathu. Tisamalimbane kwambiri ndi kufunafuna zinthu zakuthupi, kaya n’zofunikiradi kapena zongosangalala nazo chabe, mpaka kufika posowa nthawi yokwanira yochitira ntchito zosonyeza ‘kudzipereka kwa Mulungu.’ Mwina kuganizira za lero zokha kumathandiza panthawi imeneyoyo, koma kuthandiza kwake sikokhalitsa ayi. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti njira yabwino kwambiri ndiyo ‘kukundika chuma chathu kumwamba,’ osati padziko lapansi pano.​—Mateyo 6:19, 20.

Yesu anagogomezera mfundo imeneyi mu fanizo limene ananena la munthu yemwe ankakonza zodzachita zinthu zazikulu m’tsogolo. Komabe zinthuzo sizinali zokhudzana ngakhale pang’ono ndi ubwenzi wake ndi Mulungu. Fanizolo limati munthuyo anakolola zinthu zambiri. Motero iye anaganiza zophwasula nkhokwe zake zakale n’kumanga zina zikuluzikulu ndi cholinga choti azikhala moyo wamwanaalirenji, womangodya, kumwerera n’kumangosangalala basi. Nanga kodi pamenepa panali vuto lililonse? Inde, chifukwatu munthuyo anafa asanadyerere n’komwe thukuta lakelo. Komanso vuto lalikulu linali lakuti anafa asanapange ubwenzi ndi Mulungu. Yesu anamaliza fanizoli ndi mawu akuti: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”​—Luka 12:15-21; Miyambo 19:21.

Kodi Inuyo Mutani?

Musachite zinthu ngati munthu ameneyu. Fufuzani kuti mudziwe zimene Mulungu wakonzera anthu m’tsogolo ndipo sinthani moyo wanu kuti ugwirizane ndi zimenezo. Mulungu sanabisire anthu za cholinga chake cha m’tsogolo. Mneneri Amosi anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Zimene Yehova waulula kwa anthu kudzera mwa aneneri ake, zili m’Baibulo, lomwe ndi mawu ake ouziridwa.​—2 Timoteyo 3:16, 17.

Chimodzi mwa zinthu zimenezi n’chokhudza zimene zichitike posachedwapa zomwe zidzasinthiratu dziko lonse lapansi m’njira yomwe siinachitikepo ndi kale lonse. Yesu anati: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino.” (Mateyo 24:21) Palibe munthu amene angaletse chisautso chimenechi. Ndipotu Akhristu oona sangafune n’komwe kuti chisautso chimenechi chisachitike. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti chisautso chachikulu chidzathetsa mavuto onse padziko lapansi, ndi kukhazikitsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zimene zikutanthauza boma latsopano la kumwamba ndi dziko latsopano la anthu olungama. M’dziko latsopanolo, Mulungu “adzapukuta msozi uliwonse m’maso [mwa anthu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:1-4.

Kodi simukuona kuti ndi bwino kuyesetsa kufufuza zimene Baibulo limanena za nkhaniyi? Ngati mungafunikire thandizo, uzani Mboni za Yehova zakwanuko kapena lembani kalata kwa ofalitsa magazini ino. Choncho, yesetsani kuti musamangoganizira za lero zokha basi, koma muziganiziranso za tsogolo labwino limene Mulungu wakonza.

[Zithunzi patsamba 7]

‘Lekani kuda nkhawa . . . Tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso’