Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mverani Chikumbumtima Chanu

Mverani Chikumbumtima Chanu

Mverani Chikumbumtima Chanu

‘Anthu amitundu amene alibe chilamulo [cha Mulungu] amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo.’​—AROMA 2:14.

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri achita zotani pofuna kuthandiza anzawo? (b) Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Malemba zimene zimasonyeza mtima wofuna kuthandiza ena?

MNYAMATA wina wazaka 20 yemwe amadwala khunyu, anagwera m’njanji pamalo odikirira sitima. Bambo wina ataona zimenezi, anasiya ana ake aakazi, n’kuthamangira pamene panagwera mnyamatayo. Anam’kokera m’kangalande kapakati panjanjizo, n’kumutsamira pomuteteza kuti sitima yomwe inkadutsa pamwamba pawo isamugunde. Anthu ena anganene kuti bamboyo ndi wolimba mtima. Komatu mwiniwakeyo anati: “Munthu amafunika kuchita zinthu zoyenera. Inetu kunali kukoma mtima basi. Osati kufuna kutchuka kapena kutamandidwa ayi.”

2 N’kutheka kuti mukudziwa munthu wina amenenso anaika moyo wake pachiswe pofuna kuthandiza ena. Izi n’zimene ambiri anachita panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iwo ankabisa anthu osawadziwa n’komwe. Kumbukiraninso zimene zinachitikira mtumwi Paulo ndi anzake 275, chombo chawo chitasweka pa Melita, kufupi ndi chilumba cha Sisile. Anthu akumeneko anathandiza alendowo, n’kuwasonyeza “kukoma mtima kwa umunthu kwapadera.” (Machitidwe 27:27–28:2) Taganizirani za mtsikana wachiisiraeli amene ngakhale kuti mwina sanaike moyo wake pachiswe, anakomera mtima mmodzi mwa anthu a ku Suriya amene anam’tenga ukapolo. (2 Mafumu 5:1-4) Ndipo taganiziraninso za fanizo la Yesu lodziwika kwambiri lonena za Msamariya wachifundo. Wansembe wina ndiponso Mlevi wina sanafune kuthandiza Myuda mnzawo amene anatsala pang’ono kufa, koma Msamariya wina anayesetsa kuti am’thandize. Kwa zaka zambiri, anthu amitundu yambiri akhudzidwa mtima kwambiri ndi fanizo limeneli.​—Luka 10:29-37.

3, 4. Kodi mtima wosadzikonda umene anthu ambiri ali nawo umatsutsa bwanji chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka?

3 N’zoona kuti tikukhala ‘m’nthawi yovuta’ ndipo anthu ambiri ndi “oopsa” komanso “osakonda zabwino.” (2 Timoteyo 3:1-3) Komabe, kodi sitinaonepo anthu akuchita zinthu mokomerana mtima, ndipo mwinanso mokomera mtima ifeyo? Sizachilendo kuona anthu akuthandizana, ngakhale kuti mwina zingawachititse kuika moyo wawo pachiswe, ndipo ena amati mtima woterewu ndi “umunthu.”

4 Anthu amitundu ndiponso zikhalidwe zonse ali ndi mtima wofuna kuthandizana ngakhale kuti kuchita zimenezo kungawatayitse zambiri. Mtima umenewu umatsutsana ndi mfundo yakuti anthu anachokera ku zinyama. Katswiri wina wa maphunziro a chibadwa cha anthu, dzina lake Francis S. Collins, yemwe anatsogolera kafukufuku wina amene boma la United States linachita pofuna kumvetsa za chibadwa cha anthu, anati: “Mtima wosadzikonda umatsutsana ndi chiphunzitso chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. . . . Sizingatheke kuti munthu, amene akatswiri a chiphunzitsochi amanena kuti ali ndi majini odzikonda, akhale ndi mtima wosadzikonda.” Iye ananenanso kuti: “Anthu ena amalolera kutaya zinthu zambiri pofuna kuthandiza anthu osawadziwa n’komwe. . . . Ndipo zimenezi sizingafotokozedwe ndi chiphunzitso cha Darwin,” chakuti zamoyo zinachita kusanduka.

‘Zimene Chikumbumtima Chimatiuza’

5. Kodi zikuoneka kuti anthu amachita zinthu motani nthawi zambiri?

5 Dr. Collins anatchulapo mbali ina ya mtima wathu wosadzikonda, yomwe ndi “chikumbumtima chimene chimatiuza kuti tithandize ena ngakhale kuti sitilipidwapo chilichonse.” * Potchula za “chikumbumtima,” Dr. Collins akutikumbutsa mfundo ina imene mtumwi Paulo anatchula. Iye anati: “Nthawi zonse anthu a mitundu amene alibe chilamulo akamachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo, anthu amenewa, ngakhale kuti alibe chilamulo, ali chilamulo kwa iwo eni. Amenewa ndiwo amasonyeza kuti mfundo za m’chilamulo zinalembedwa m’mitima mwawo, pamene chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomereza.”​—Aroma 2:14, 15.

6. N’chifukwa chiyani anthu onse adzadziyankhira mlandu kwa Mlengi?

6 M’kalata imene Paulo analembera Aroma, anasonyeza kuti anthufe tidzadziyankhira mlandu kwa Mulungu chifukwa chakuti zimene timaona zimasonyeza makhalidwe Ake ndiponso kuti Iye alipo. Umu ndi mmene zakhalira “chilengedwere dziko kumka m’tsogolo.” (Aroma 1:18-20; Salmo 19:1-4) N’zoona kuti anthu ambiri amanyalanyaza Mlengi wawo n’kukhala ndi makhalidwe oipa. Komatu, Mulungu amafuna kuti anthu adziwe kuti iye ndi wolungama, n’kulapa zochita zawo zoipa. (Aroma 1:22–2:6) Ayuda anayenera kuchita zimenezi, popeza kuti anapatsidwa Chilamulo cha Mulungu kudzera mwa Mose. Komabe, ngakhale anthu amene analibe “mawu opatulika a Mulungu” anafunika kuvomereza kuti Mulungu alipo.​—Aroma 2:8-13; 3:2.

7, 8. Kodi mtima wofunitsitsa kuti zinthu zichitike mwachilungamo ndi wofala motani, ndipo kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?

7 Chifukwa chachikulu chimene chiyenera kuchititsa tonse kuvomereza kuti kuli Mulungu n’kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene amafuna n’chakuti tili ndi nzeru yachibadwa yotizindikiritsa chabwino ndi choipa. Anthufe timafunitsitsa kuti zinthu zizichitika mwachilungamo ndipo umenewu ndi umboni wakuti tili ndi chikumbumtima. Tayerekezerani kuti mukuona ana ali pamzere kudikirira kuti akwere katungwe. Kenako, mwana wina akulowerera anzakewo kutsogolo. Ambiri mwa anawo akunena kuti, ‘N’kulakwatu kumeneku!’ Ndiyeno, tadzifunsani kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani ana ambiri angosonyezera pamodzi kuti ali ndi mtima wofunitsitsa kuti zinthu zichitike mwachilungamo?’ Izi zikusonyeza kuti anawo ali ndi chikumbumtima. Paulo analemba kuti: ‘Nthawi zonse anthu amitundu amene alibe chilamulo amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo.’ Iye sananene kuti, “Nthawi zina,” ngati kuti amachita mwakamodzikamodzi. Iye anati “nthawi zonse,” kusonyeza kuti zimachitika kawirikawiri. Izi zikusonyeza kuti anthu ‘amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo,’ kutanthauza kuti chikumbumtima chawo chimawachititsa zinthu mogwirizana ndi zimene timawerenga m’malamulo a Mulungu.

8 Zikuoneka kuti anthu m’mayiko ambiri amachita zinthu motsatira chikumbumtima. Mphunzitsi wina wa pa yunivesite ya Cambridge anafotokoza kuti ena mwa malamulo a Ababulo, Aiguputo ndi Agiriki komanso Aaborijini a ku Australia ndiponso Amwenye a ku America, “ankaletsa kuponderezana, kupha munthu, chinyengo, koma ankalimbikitsa kukomera mtima achikulire, ana, ndiponso ofooka.” Ndipo Dr. Collins analemba kuti: “Zikuoneka kuti anthu onse ali ndi nzeru yachibadwa yozindikira chabwino ndi choipa.” Kodi zimenezi sizikukukumbutsani mfundo ya pa Aroma 2:14?

Kodi Chikumbumtima Chanu Chimagwira Ntchito Motani?

9. Kodi chikumbumtima n’chiyani, ndipo chingatithandize motani tisanachite zinthu?

9 Baibulo limasonyeza kuti chikumbumtima ndi maganizo achibadwa oona ndi kusinkhasinkha zochita zathu. Chimakhala ngati mawu a mumtima mwathu otiuza kuti zomwe tikuchita n’zabwino kapena zoipa. Paulo ankanena zimenezi pamene anati: “Chikumbumtima changa chikuchitira umboni pamodzi ndi ine mwa mzimu woyera.” (Aroma 9:1) Mwachitsanzo, tisanachite zinthu zimene zingafune kuti tisankhe chabwino kapena choipa, chikumbumtima chingatithandize kuona bwino zinthuzo. Ndipo tingadziwe zotsatira za zimene tikufuna kuchita ndiponso mmene tingamvere ngati titazichita.

10. Kodi kawirikawiri chikumbumtima chimagwira ntchito motani?

10 Koma kawirikawiri chikumbumtima chimatitsutsa titachita kale zinthu zinazake. Pamene ankathawa Mfumu Sauli, Davide anapeza mpata wochita zinthu zimene zinali zosalemekeza mfumu yoikidwa ndi Mulungu. Koma pambuyo pochita zinthuzo, “mtima wa Davide unam’tsutsa.” (1 Samueli 24:1-5; Salmo 32:3, 5) Chikumbumtima n’chimene chinam’tsutsa Davide, ngakhale kuti lembali silikutchula mawu oti “chikumbumtima.” Mofanana ndi zimenezi, tonsefe chikumbumtima chathu chinatitsutsapo. Pambuyo pochita zinthu zinazake tinavutika mumtima n’kumaona kuti sitinachite bwino. Anthu ena amene anazemba kulipira msonkho anavutikapo ndi chikumbumtima moti pambuyo pake analipira msonkhowo. Ena aululapo kwa mwamuna kapena mkazi wawo kuti anachita chigololo. (Aheberi 13:4) Komatu, munthu akachita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake amakhala wosangalala ndiponso amakhala ndi mtendere wamumtima.

11. Kodi kuchita zinthu mongotsatira chikumbumtima kungakhale koopsa motani? Perekani chitsanzo.

11 Ndiyeno kodi ndi bwino kuti tizingochita zinthu motsatira chikumbumtima? N’zoona kuti kumvera chikumbumtima kumathandiza, koma nthawi zina chikumbumtimacho chingatisokoneze kwambiri. Inde, mawu a “munthu wathu wa m’kati” angatisocheretse. (2 Akorinto 4:16) Taganizirani chitsanzo ichi. Baibulo limatiuza za Sitefano, amene anali wodzipereka kwambiri potsatira Khristu, ndiponso “wodzala ndi chisomo ndi mphamvu.” Koma Ayuda ena anam’tulutsa mu Yerusalemu ndipo anamupha mwa kum’ponya miyala. Saulo (yemwe pambuyo pake anadzakhala mtumwi Paulo) anali pomwepo ndipo “anali kuvomereza za kupha Sitefano.” Zikuoneka kuti Ayudawo ankaona kuti akuchita zoyenera ndipo chikumbumtima chawo sichinkawatsutsa. N’chimodzimodzinso ndi Saulo, yemwe pambuyo pochita zimenezi anali “chilusirebe poopseza ndi kufuna kupha ophunzira a Ambuye.” Mosakayikira, nayenso chikumbumtima chake sichinkamuuza zolondola.​—Machitidwe 6:8; 7:57–8:1; 9:1.

12. Kodi chimodzi mwa zinthu zimene zingachititse chikumbumtima chathu kukhala chabwino kapena choipa n’chiyani?

12 Kodi n’chiyani chinasokoneza chikumbumtima cha Saulo. Chinthu choyamba chingakhale anthu amene ankacheza nawo. Ambirife tinalankhulapo ndi munthu wina patelefoni, amene mawu ake ankafanana kwambiri ndi a bambo ake. Mwina n’chibadwa cha mwanayo kuti mawu ake azimveka choncho, komanso n’kutheka kuti anachita kutengera mmene bambo akewo amalankhulira. N’chimodzimodzinso ndi Saulo. Iye ayenera kuti anatengera zochita za Ayuda amene ankadana ndi Yesu ndiponso kutsutsa zimene ankaphunzitsa. (Yohane 11:47-50; 18:14; Machitidwe 5:27, 28, 33) Zoonadi, n’kutheka kuti zimene chikumbumtima cha Saulo chinkamuuza zinali zogwirizana ndi zochita za anzakewo.

13. Kodi dera limene munthu akukhala lingakhudze bwanji chikumbumtima chake?

13 Chinanso chimene chingachititse kuti chikumbumtima cha munthu chikhale chabwino kapena choipa ndi chikhalidwe kapena dera lomwe munthuyo akukhala. Zimenezi zimafanana ndi mmene kalankhulidwe ka munthu kamasinthira malingana ndi dera limene amakhala. (Mateyo 26:73) Izi ziyenera kuti n’zimene zinachitikira Asuri akale. Iwo ankadziwika kuti anali anthu okonda nkhondo, ndipo zinthu zimene ankazokota m’malo osiyanasiyana zimasonyeza iwo akuzunza akapolo awo. (Nahumu 2:11, 12; 3:1) Baibulo limati Anineve a m’masiku a Yona sankadziwa “kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.” Izi zikutanthauza kuti iwo sankatha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi zolakwika pamaso pa Mulungu. N’zodziwikiratu kuti chikumbumtima cha munthu wokulira mu Nineve chikanatha kusokonezeka. (Yona 3:4, 5; 4:11) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano munthu angakhale ndi chikumbumtima chogwirizana ndi zochita za anthu amene amakhala nawo.

Mmene Tingakhalire ndi Chikumbumtima Chabwino

14. Kodi chikumbumtima chathu chimagwirizana motani ndi lemba la Genesis 1:27?

14 Yehova anapatsa Adamu ndi Hava mphatso ya chikumbumtima, ndipo ife tinatengera kwa iwo. Lemba la Genesis 1:27 limanena kuti munthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. Izi sizitanthauza kuti tili ndi thupi lofanana ndi Mulungu, chifukwa Iye ndi mzimu. Koma zimatanthauza kuti tili ndi makhalidwe, kuphatikizapo chikumbumtima chimene chimatithandiza kusankha zochita. Zimenezi zikutithandiza kuona njira imodzi imene ingatithandize kuti tikhale ndi chikumbumtima champhamvu, ndiponso chodalirika. Tingatero mwa kuphunzira kwambiri za Mlengi, ndiponso kumuyandikira kwambiri.

15. Kodi kudziwa Atate wathu kungatipindulitse m’njira iti?

15 Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndiye anatipatsa moyo, choncho iye ali ngati Atate wa tonsefe. (Yesaya 64:8) Akhristu okhulupirika, kaya akuyembekezera kukakhala kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi laparadaiso, angatchule Mulungu kuti Atate. (Mateyo 6:9) Tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kuyandikira kwa Atate wathuyu ndi kuphunzira maganizo ndiponso mfundo zake. (Yakobe 4:8) Komatu anthu ambiri alibe chidwi chochita zimenezi. Iwo ali ngati Ayuda amene Yesu anawauza kuti: “Inu simunamvepo mawu ake nthawi ina iliyonse, kapena kuona thupi lake. Mawu akenso sanakhazikike mwa inu.” (Yohane 5:37, 38) N’zoona kuti sitinamvepo mawu enieni a Mulungu, koma tingadziwe maganizo ake mwa kuwerenga mawu ake, ndipo tikatero tingathe kufanana naye ndiponso kuganiza monga mmene iye amaganizira.

16. Kodi nkhani ya Yosefe imasonyeza motani kufunika kophunzitsa ndi kumvera chikumbumtima chathu?

16 Nkhani ya Yosefe m’nyumba ya Potifara imasonyeza zimenezi. Mkazi wa Potifara anayesa kunyengerera Yosefe kuti agone naye. Ngakhale kuti panthawiyo kunalibe buku lililonse la Baibulo, ndiponso Malamulo Khumi anali asanaperekedwe, Yosefe anakana, n’kunena kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) Sikuti iye anayankha chonchi pofuna kusangalatsa achibale ake ayi, chifukwa iwo ankakhala kutali kwambiri. Kwenikweni, iye ankafuna kusangalatsa Mulungu. Yosefe ankadziwa kuti maganizo a Mulungu pankhani ya ukwati ndi oti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi, ndiponso kuti awiriwo amakhala “thupi limodzi.” Komanso mwinamwake anali atamvapo mmene Abimeleki anamvera atauzidwa kuti Rebeka ndi wokwatiwa. Abimeleki anaona kuti kukwatira Rebeka kukanakhala kulakwa, ndipo kukanabweretsa mavuto pa anthu ake. Ndipotu Yehova anadalitsa zotsatira za nkhaniyi, zomwe zinasonyeza kuti Iye amadana ndi chigololo. Kudziwa zinthu zonsezi, kuyenera kuti kunachititsa chikumbumtima chake kukhala champhamvu, ndipo anakana kuchita chiwerewere.​—Genesis 2:24; 12:17-19; 20:1-18; 26:7-14.

17. Pankhani yofanana ndi Atate wathu, kodi ifeyo tili ndi mwayi wotani kusiyana ndi Yosefe?

17 Kunena zoona, ife tili ndi mwayi waukulu. Tili ndi Baibulo lonse, lomwe lingatiphunzitse mmene Atate wathu amaganizira ndiponso mmene amamvera, komanso zinthu zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Tikaphunzira kwambiri Malemba, timayandikiranso kwambiri kwa Mulungu ndiponso timafanana naye kwambiri. Tikamachita zimenezi, chikumbumtima chathu chizitilimbikitsa kuchita zinthu mogwirizana kwambiri ndi maganizo ndiponso chifuniro cha Atate wathu.​—Aefeso 5:1-5.

18. Mosaganizira mmene moyo wathu unalili kale, kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chikhale chodalirika kwambiri?

18 Nanga bwanji za khalidwe la anthu otizinga? N’kutheka kuti zochita zathu zimagwirizana ndi maganizo ndiponso zochita za achibale athu komanso dera limene tinakulira. Motero, mwina zimene chikumbumtima chathu chimatiuza zingakhale zolakwika, chifukwa chakuti tinatengera zochita za anthu omwe tinkakhala nawo. N’zoona kuti sitingasinthe zinthu zimene zinachitika kale; koma tingakonze zoti tizisankha anzathu ndiponso malo amene angathandize kuti chikumbumtima chathu chikhale chabwino. Zimene zingatithandize kwambiri ndi kukhala ndi Akhristu odzipereka kwambiri amene akhala akuyesetsa kwanthawi yaitali kuti afanane ndi Atate wathu. Misonkhano ya mpingo ndiponso kucheza kumene kumakhalapo misonkhanoyo isanayambe kapena itatha, zimatithandiza kwambiri. Tingakhale ndi mwayi woona mmene Akhristu anzathu amaganizira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene aphunzira m’Baibulo. Komanso tingaone kuti iwo ndi ofunitsitsa kumvera, chikumbumtima chawo chikamawalimbikitsa kuchita zinthu mogwirizana ndi maganizo a Mulungu. M’kupita kwanthawi, zimenezi zidzatithandiza kukhala ndi chikumbumtima chogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, ndipo tidzafanana kwambiri ndi Mulungu. Chikumbumtima chikamagwirizana ndi mfundo za Atate wathu ndipo tikamatsatira chitsanzo chabwino cha Akhristu anzathu, chikumbumtima chathucho chidzakhala chodalirika kwambiri ndiponso tidzakhala ofunitsitsa kuchimvera.​—Yesaya 30:21.

19. Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana zinthu ziti zokhudza chikumbumtima chathu?

19 Komabe, ena zimawavuta kuti nthawi zonse azitsatira zimene chikumbumtima chawo chikuwauza. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zinthu zina zimene zakhala zikuchitikira Akhristu. Mwa kuganizira zinthu zimenezi, tingathe kuona ntchito ya chikumbumtima, zinthu zimene zimachititsa kuti chikumbumtima cha anthu chizisiyana, ndiponso zimene tingachite kuti tizilabadira kwambiri chikumbumtima chathu.​—Aheberi 6:11, 12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mofanana ndi zimenezi, Owen Gingerich, katswiri wa zakuthambo wa pa yunivesite ya Harvard, analemba kuti: “Mtima wosadzikonda ungatichititse kufunsa funso limene . . . asayansi sangaliyankhe mwa kungophunzira za nyama. Yankho logwira mtima lingapezeke mwa kuphunzira zinthu zina ndipo lingakhudze makhalidwe amene Mulungu anapatsa anthu, kuphatikizapo chikumbumtima.”

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani anthu amitundu yonse ali ndi chikumbumtima?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisamangotsatira chikumbumtima?

• Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

Davide anavutika ndi chikumbumtima . . .

koma sizinali choncho ndi Saulo wa ku Tariso

[Chithunzi patsamba 24]

Tingathe kuphunzitsa chikumbumtima chathu