Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndinamusirira Chifukwa Sanasinthe Maganizo Ake”

“Ndinamusirira Chifukwa Sanasinthe Maganizo Ake”

“Ndinamusirira Chifukwa Sanasinthe Maganizo Ake”

M’CHAKA cha 2006, Günter Grass, wolemba mabuku wa ku Germany amenenso mu 1999 anapata mphoto yapamwamba ya Nobel chifukwa cha mabuku ake, anatulutsa buku la mbiri ya moyo wake. M’bukulo, iye anafotokozamo za nthawi imene anaitanidwa kuti akakhale msilikali wa dziko la Germany. M’buku lomweli, iye anafotokozamonso za munthu wina amene anachita zinthu zimene zinam’khudza kwambiri, moti panopa amakumbukirabe ngakhale kuti patha zaka zoposa 60. Ndi munthu yekhayo amene anakhalabe wokhulupirika panthawi yomwe ankazunzidwa.

M’nkhani ina yomwe inasindikizidwa m’nyuzipepala ya Frankfurter Allgemeine Zeitung, Grass anafotokoza za munthu wochititsa chidwiyu, amene anakana kumenya nawo nkhondo. Grass ananena kuti munthuyu “sanatsatire maganizo alionse omwe anali ofala panthawiyo, kaya a chipani cha Nazi, achikomyunizimu, kapena achisosholizimu. Iye anali wa Mboni za Yehova.” Grass sanakumbukire dzina la wa Mboni ameneyu, amene iye ankangomutcha kuti ‘Zimenezi sitichita.’ Anthu ochita kafukufuku wa zimene Mboni za Yehova zinkachita anapeza kuti dzina la munthuyu ndi Joachim Alfermann. Iye anamenyedwa mobwerezabwereza ndiponso ankachititsidwa manyazi. Kenako anam’tsekera m’ndende mwayekhayekha. Koma Alfermann sanasinthe maganizo ake ndipo anakanitsitsa kumenya nawo nkhondo.

Grass anati: “Ndinamusirira chifukwa sanasinthe maganizo ake. Ndinadzifunsa kuti: Kodi akutha bwanji kupirira zonsezi? N’chiyani chimamuthandiza?” Pambuyo popirira kwanthawi yaitali zinthu zimene anthu ankamuchitira pofuna kuti asakhalenso wokhulupirika kwa Mulungu, Alfermann anatumizidwa ku ndende yozunzirako anthu ya Stutthof, mu February 1944. Iye anamasulidwa mu April 1945, ndipo pambuyo pa nkhondoyo anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova mpaka pamene anamwalira mu 1998.

Alfermann anali mmodzi wa Mboni pafupifupi 13,400 zimene zinachitiridwa nkhanza chifukwa cha chikhulupiriro chawo ku Germany ndi m’mayiko ena amene ankalamulidwa ndi chipani cha Nazi. Mbonizi zinatsatira lamulo la m’Baibulo loti zisamalowerere ndale ndiponso zisamamenye nawo nkhondo. (Mateyo 26:52; Yohane 18:36) Mboni pafupifupi 4,200 zinatumizidwa ku ndende zozunzirako anthu, ndipo Mboni 1,490 zinafa. Ngakhale panopa, anthu ambiri amene si Mboni amasirira Mboni za Yehova chifukwa chakuti zimakhalabe zokhulupirika.

[Chithunzi patsamba 32]

Joachim Alfermann