Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Surakusa Mzinda Womwe Paulo Anaima Paulendo Wake

Surakusa Mzinda Womwe Paulo Anaima Paulendo Wake

Surakusa Mzinda Womwe Paulo Anaima Paulendo Wake

CHA m’ma 59 C.E., chombo china chinanyamuka kuchoka ku chilumba chapanyanja ya Mediterranean, chotchedwa Melita, kupita ku Italiya. Chombocho chinali ndi chizindikiro cha “Ana a Zeu,” milungu imene ankati inkateteza anthu oyenda pa nyanja. Munthu amene analemba nawo Baibulo, dzina lake Luka, anafotokoza kuti chombocho chinakocheza “pa doko ku Surakusa,” kum’mwera chakum’mawa kwa chilumba cha Sisile ndipo ‘chinakhala pamenepo masiku atatu.’ (Machitidwe 28:11, 12) Paulendowo, Luka anali ndi Alisitakasi ndiponso mtumwi Paulo, yemwe anatengedwa kuti akam’zenge mlandu ku Roma.​—Machitidwe 27:2.

Sitikudziwa ngati Paulo analoledwa kutsika chombocho ku Surakusa. Koma ngati iye kapena anzake omwe anali naye paulendowo anatsika chombocho, kodi n’kutheka kuti anaona chiyani pachilumbachi?

M’nthawi za Agiriki ndi Aroma, mzinda wa Surakusa unali wosasiyana kwambiri ndi mizinda ya Atene ndi Roma. Malingana ndi mbiri yakale, Akorinto ndiwo anayamba kumanga mzindawu mu 734 B.C.E. Nthawi zina, zinthu zinkayenda bwino mumzinda wa Surakusa ndiponso anthu ena otchuka kwambiri kalelo anabadwira mu mzindawu. Ena mwa iwo ndi wolemba masewero, dzina lake Epicharmus ndiponso katswiri wa masamu, dzina lake Archimedes. Mu 212 B.C.E., Aroma anagonjetsa mzinda wa Surakusa.

Mutapita ku mzinda wamakono wa Surakusa, mungakakhale ndi chithunzithunzi cha mmene mzindawu unalili m’masiku a Paulo. Mzindawu unagawidwa pawiri. Mbali ina inali pa chilumba chaching’ono cha Ortygia, ndipo mbali inayo inali pa chilumba chachikulu, cha Sisile. N’kutheka kuti chombo chimene munali Paulo chinakocheza pa chilumba cha Ortygia.

Masiku ano, pachilumbachi pali mabwinja a kachisi wa mulungu wotchedwa Apollo, yemwe anamangidwa motsatira mmene Agiriki akale ankamangira akachisi pachilumba cha Sisile. Kachisiyu anamangidwa m’ma 500 B.C.E. Palinso zipilala za kachisi wa mulungu wamkazi wotchedwa Athena, amene anamangidwa m’ma 400 B.C.E., koma kenako anadzakhala mbali ya tchalitchi chachikulu.

Ntchito zambiri mumzindawu zimachitikira pa chilumba chachikulu chija, ndipo kumeneko n’komwe kuli malo oonetserako zinthu zakale, otchedwa Neapolis. Kufupi ndi khomo lolowera ku malowa, kuli bwalo lamasewero lachigiriki. Bwaloli ndi limodzi mwa mabwalo ochititsa chidwi achigiriki omwe adakalipo mpaka pano. Popeza kuti linayang’ana chakunyanja, bwaloli linali malo abwino kwambiri ochitirako masewero osiyanasiyana. Chakum’mwera kwenikweni kwa Neapolis kuli bwalo lalikulu lamasewero lachiroma, lomwe linamangidwa m’ma 200 C.E. Bwaloli ndi lozungulira ngati dzira, ndipo ndi la mamita 140 m’litali, ndi mamita 119 m’lifupi, komanso ndi lachitatu pa mabwalo aakulu kwambiri ku Italiya.

Ngati muli ndi mwayi wokaona mzinda wa Surakusa, mungakakhale pa mpando wa m’mphepete mwa nyanja pachilumba cha Ortygia, n’kutsegula Baibulo pa Machitidwe 28:12, n’kuyerekezera kuti mukuona mtumwi Paulo atakwera chombo chomwe chikubwera kudzakocheza pa dokoli.

[Chithunzi/​Mapu patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Melita

Sisile

Surakusa

ITALIYA

Regiamu

Puteyoli

Roma

[Chithunzi patsamba 30]

Bwinja la bwalo lamasewero lachigiriki ku Surakusa