Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza “Zinthu Zozama za Mulungu”

Kufufuza “Zinthu Zozama za Mulungu”

Kufufuza “Zinthu Zozama za Mulungu”

“Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”​—1 AKORINTO 2:10.

1. Tchulani mfundo zina za choonadi cha m’Baibulo zomwe munthu amene wayamba kumene kuphunzira Baibulo amasangalala nazo.

AMBIRIFE tingakumbukire mmene tinasangalalira pamene tinayamba kuphunzira choonadi. Tinazindikira za kufunika kwa dzina la Yehova, chifukwa chimene walolera kuti anthu azivutika, chifukwa chimene anthu ena amapitira kumwamba, ndiponso tsogolo la anthu ena onse okhulupirika. N’kutheka kuti kale tinkawerenga Baibulo, koma sitinkazindikira zinthu zimenezi, monga momwe zilili ndi anthu ambiri. Tinali ngati munthu wina amene wayamba ulendo wake m’bandakucha. Atangonyamuka, iye sakutha kuona zinthu zambiri chifukwa cha mdima. Koma pamene dzuwa likutuluka, iye akuyamba kuona zinthu bwinobwino. Ndipo dzuwa litakwera, iye akutha kuona zinthu ngakhale zimene zili patali. Umu ndi mmenenso zinalili ndi ifeyo, munthu wina atayamba kutithandiza kumvetsa Malemba. Inali nthawi yoyamba kuti tione “zinthu zozama za Mulungu.”​—1 Akorinto 2:8-10.

2. N’chifukwa chiyani kusangalala kwathu pophunzira Mawu a Mulungu kulibe malire?

2 Komabe, kodi ndi bwino kukhutira ndi mfundo zoyambirira zokha za choonadi cha m’Baibulo? Mawu akuti “zinthu zozama za Mulungu” amatanthauza nzeru za Mulungu zimene Akhristu amazimvetsa mothandizidwa ndi mzimu woyera, koma anthu ena sazindikira nzeru zimenezi. (1 Akorinto 2:7) Kufufuza nzeru za Mulungu kulibe malire ndipo n’kosangalatsa kwambiri. Sitingadziwe nzeru zonse za Mulungu. Ndipo ngati tipitiriza kufufuza “zinthu zozama za Mulungu,” tingapitirize kusangalala monga momwe tinachitira titaphunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo.

3. Kodi kumvetsa bwino chifukwa chimene timakhulupirira zinthu zina n’kofunika motani?

3 Kodi n’chifukwa chiyani timafunika kumvetsa “zinthu zozama” zimenezi? Kumvetsa zimene timakhulupirira ndiponso zifukwa zake timakhulupirira zimenezo, kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. Malemba amatiuza kuti tizigwiritsa ntchito “luntha [lathu] la kulingalira” kuti ‘tizindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.’ (Aroma 12:1, 2) Kumvetsa chifukwa chimene Yehova amafunira kuti titsatire mfundo zinazake pamoyo wathu kumatilimbikitsa kumumvera. Motero, kudziwa “zinthu zozama” kungatithandize kuti tisagonje pamene tikuyesedwa kuti tichite zoipa ndiponso kungatilimbikitse kukhala “achangu pa ntchito zabwino.”​—Tito 2:14.

4. Kodi kuphunzira Baibulo kumatanthauza chiyani?

4 Timafunika kuphunzira kuti timvetse bwino zinthu zozama. Komatu, kuphunzira n’kosiyana ndi kungowerenga. Kuphunzira kumatanthauza kuganizira mozama mfundo inayake kuti tione kugwirizana kwake ndi mfundo zina zimene tikuzidziwa kale. (2 Timoteyo 1:13) Kumaphatikizapo kuona zifukwa zake afotokoza choncho. Pophunzira Baibulo tiyenera kusinkhasinkha za mmene mfundozo zingatithandizire kusankha zinthu mwanzeru komanso mmene tingathandizire nazo anthu ena. Komanso, popeza kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa” tiyenera kuphunzira “mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (2 Timoteyo 3:16, 17; Mateyo 4:4) Kuphunzira Baibulo kumasangalatsa ngakhale kuti kumafuna khama, ndipotu kumvetsa “zinthu zozama za Mulungu” sikovuta kwambiri.

Yehova Amathandiza Anthu Odzichepetsa Kuti Amvetse

5. Ndi anthu ati omwe angamvetse “zinthu zozama za Mulungu”?

5 Ngakhale kuti mwina simunapite patali ndi maphunziro kapena simunazolowere kuwerenga, musaganize kuti simungamvetse “zinthu zozama za Mulungu.” Pamene Yesu anali padziko lapansi Yehova sanaulule zolinga zake kwa anthu anzeru ndi ozindikira koma kwa anthu wamba ndi osaphunzira. Iwo anali odzichepetsa moti akanatha kuphunzitsidwa ndi mtumiki wa Mulungu. Powayerekeza ndi anthu ophunzira, iwo anali ngati tiana. (Mateyo 11:25; Machitidwe 4:13) Ponena za “zimene Mulungu wakonzera om’konda,” mtumwi Paulo anati: “Mulungu anaululira ifeyo zinthu zimenezi, chifukwa mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”​—1 Akorinto 2:9, 10.

6. Kodi lemba la 1 Akorinto 2:10 limatanthauza chiyani?

6 Kodi mzimu wa Mulungu umafufuza motani “zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu”? M’malo moulula choonadi kwa Mkhristu aliyense payekha, Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kutsogolera gulu lake limene limathandiza anthu a Mulungu kuti amvetse Baibulo. (Machitidwe 20:28; Aefeso 4:3-6) Anthu m’mipingo yonse padziko lapansi amaphunzira Baibulo m’njira yofanana. M’kupita kwanthawi amakhala ataphunzira mfundo zambiri za m’Baibulo lonse. Mzimu woyera umathandiza anthu kudzera m’mipingo imeneyi kuti akhale ndi mtima umene ungawathandize kuti amvetse “zinthu zozama za Mulungu.”​— Machitidwe 5:32.

Kodi “Zinthu Zozama za Mulungu” N’chiyani?

7. N’chifukwa chiyani anthu ambiri samvetsa “zinthu zozama za Mulungu”?

7 Sitiyenera kuganiza kuti “zinthu zozama” ndi zovuta kumvetsa. Anthu ambiri sadziwa “zinthu zozama za Mulungu” osati chifukwa chakuti nzeru ya Mulungu ndi yovuta kumvetsa, koma chifukwa chakuti Satana amanyenga anthu kuti azikana thandizo limene Yehova akupereka kudzera m’gulu Lake.​—2 Akorinto 4:3, 4.

8. M’chaputala chachitatu cha kalata yopita kwa Aefeso, kodi Paulo anatchulamo zinthu zozama ziti?

8 M’chaputala chachitatu cha kalata yopita kwa Aefeso, Paulo anasonyeza kuti zina mwa “zinthu zozama za Mulungu” ndi mfundo za choonadi zimene ambiri mwa anthu a Yehova amazimvetsa, monga za Mbewu yolonjezedwa, kusankhidwa kwa anthu opita kumwamba, ndiponso za Ufumu wa Mesiya. Paulo analemba kuti: “M’mibadwo ina, chinsinsi chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene chaululidwira tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa mzimu. Chinsinsi chimenechi ndicho chakuti, anthu a mitundu nawonso akhale odzalandira cholowa, nakhalenso ziwalo za thupi ndiponso otenga mbali m’lonjezo limodzi nafe, mogwirizana ndi Khristu Yesu.” Paulo ananena kuti anapatsidwa ntchito ‘yoonetsa anthu mmene chinsinsi chopatulikacho chikuyendetsedwera. Kuyambira kalekale, chinsinsi chimenechi chakhala chobisika mwa Mulungu.’​—Aefeso 3:5-9.

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudziwa “zinthu zozama za Mulungu” ndi mwayi wamtengo wapatali?

9 Paulo anapitiriza kufotokoza chifuniro cha Mulungu kuti: “Amene ali m’malo akumwamba, tsopano adziwe mbali zambirimbiri za nzeru ya Mulungu kudzera mwa mpingo.” (Aefeso 3:10) Angelo amapindula kwambiri akamaona ndi kuzindikira nzeru ya Yehova pamene akutsogolera mpingo wachikhristu. Ndi mwayi wamtengo wapatali kuti tikudziwa zinthu zimene angelo nawonso amachita nazo chidwi. (1 Petulo 1:10-12) Kenako, Paulo ananena kuti tiyenera kuchita khama kuti ‘tidziwe bwino lomwe m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama,’ kwa zinthu zimene Akhristu amakhulupirira. (Aefeso 3:11, 18) Tsopano tiyeni tione zitsanzo za zinthu zozama zomwe n’kutheka kuti sitinaziganizirepo.

Zitsanzo za Zinthu Zozama

10, 11. Malingana ndi Malemba, kodi ndi liti pamene Yesu anakhala mbali yoyamba ya “mbewu” ya ‘mkazi’ wakumwamba wa Mulungu?

10 Timadziwa kuti Yesu ndi mbali yoyamba ya “mbewu” ya ‘mkazi’ wakumwamba wa Mulungu wotchulidwa pa Genesis 3:15. Pofuna kudziwa zambiri, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi liti pamene Yesu anakhala Mbewu yolonjezedwa? Kodi anakhala Mbewuyo nthawi ina asanabwere pa dziko lapansi, kapena pamene anabadwa padziko lapansi? Kodi mwina ndi paubatizo wake, kapena ataukitsidwa kwa akufa?’

11 Mulungu anali atalonjeza kuti mbali yakumwamba ya gulu lake, yomwe ulosiwo unaitcha ‘mkazi,’ idzabala mbewu imene idzalalire mutu wa njoka. Koma panatha zaka zambiri, ndipo mkazi wa Mulungu sanabale mbewu imene ikanatha kuwononga Satana ndi ntchito zake. N’chifukwa chake ulosi wa m’buku la Yesaya unanena kuti mkaziyo ndi ‘wosabala’ ndiponso “wosauka m’mzimu.” (Yesaya 54:1, 5, 6) M’kupita kwanthawi, Yesu anabadwa ku Betelehemu. Koma Yesu atabatizidwa, n’kudzozedwa ndi mzimu kuti akhale mwana wa Mulungu, m’pamene Yehova ananena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga.” (Mateyo 3:17; Yohane 3:3) Apa, mbali yoyamba ya “mbewu” ya mkazi inadziwika. Kenako, anthu otsatira Yesu nawonso anadzozedwa ndi mzimu woyera. Tsopano, ‘mkazi’ wa Yehova, amene kwanthawi yaitali anali ngati ‘wosabala, anaimba’ mosangalala.​—Yesaya 54:1; Agalatiya 3:29.

12, 13. Kodi ndi malemba ati amene amasonyeza kuti Akhristu onse odzozedwa padziko lapansi amapanga gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

12 Chitsanzo chachiwiri cha zinthu zozama zimene tazindikira chikukhudza cholinga cha Mulungu chosankha anthu 144,000. (Chivumbulutso 14:1, 4) Timamvetsa ndipo timavomereza kuti odzozedwa onse omwe ali padziko lapansi amapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” yemwe Yesu anati adzapatsa “chakudya” antchito ake a pakhomo. (Mateyo 24:45) Kodi ndi malemba ati m’Baibulo amene amatsimikizira kuti zimenezi ndi zoona? Kodi n’kutheka kuti Yesu ankanena za Mkhristu aliyense wolimbikitsa abale ake mwauzimu?

13 Mulungu anauza anthu a mtundu wa Isiraeli kuti: “Inu ndinu mboni zanga . . . ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.” (Yesaya 43:10) Koma pa Nisani 11, m’chaka cha 33 C.E., Yesu anauza atsogoleri a Aisiraeli kuti Mulungu anakana kuti mtundu wawo ukhale mtumiki Wake. Iye anati: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” Yesu anauza khamu la anthu kuti: “Tamverani! Nyumba yanu akunyanyalirani.” (Mateyo 21:43; 23:38) Nyumba ya Isiraeli sinakhale yokhulupirika ndiponso yanzeru monga kapolo wa Yehova. (Yesaya 29:13, 14) Kenako tsiku lomwelo, Yesu anafunsa kuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?” Pofunsa izi, iye ankatanthauza kuti, ‘Kodi ndi mtundu uti wanzeru umene udzalowe m’malo mwa Isiraeli ndi kukhala kapolo wokhulupirika wa Mulungu?’ Mtumwi Petulo anayankha funsoli pamene analimbikitsa mpingo wa Akhristu odzozedwa kuti: “Inu ndinu . . . ‘mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera.’” (1 Petulo 1:4; 2:9) Mtundu wauzimu umenewu, womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu,” unakhala kapolo watsopano wa Yehova. (Agalatiya 6:16) Anthu onse a mtundu wa Isiraeli wakale anali ngati “mtumiki” mmodzi, nawonso Akhristu onse odzozedwa omwe ali padziko lapansi pano panthawi ina iliyonse, amapanga “kapolo [mmodzi] wokhulupirika ndi wanzeru.” Tili ndi mwayi wamtengo wapatali wopatsidwa “chakudya” kudzera mwa kapolo wa Mulungu.

Mungasangalale Kwambiri ndi Phunziro Laumwini

14. Nchifukwa chiyani munthu amakhala wosangalala akamaphunzira Baibulo m’malo mongowerenga chabe?

14 Timasangalala kwambiri tikamvetsa mfundo inayake ya m’Malemba chifukwa zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. N’chifukwa chake kuphunzira Baibulo kumakhala kosangalatsa kusiyana ndi kungowerenga chabe. Choncho, ndi bwino kuti powerenga mabuku achikhristu tizidzifunsa kuti: ‘Kodi mfundo imeneyi ikugwirizana bwanji ndi zimene ndikudziwa kale pankhaniyi? Kodi ndi Malemba kapena mfundo zina ziti zomwe ndingaziganizire zogwirizana ndi zimene nkhaniyi ikunena?’ Ngati pali mfundo zina zimene mufunika kufufuza, lembani funso limene mukufuna kudzapeza yankho lake, ndiyeno dzafufuzeni nkhaniyo paphunziro lanu nthawi ina.

15. Kodi ndi nkhani ngati ziti zimene munthu angasangalale nazo pophunzira, ndipo angatani kuti apindule nazo kwanthawi yaitali?

15 Kodi ndi nkhani ngati ziti zimene mungafufuze n’kusangalala nazo? Kufufuza zinthu ngati mapangano osiyanasiyana amene Mulungu anachita pofuna kuthandiza anthu n’kolimbikitsa kwambiri. Mungalimbitse chikhulupiriro chanu mwa kuphunzira ulosi wonena za Yesu Khristu kapena kuphunzira vesi ndi vesi mabuku osiyanasiyana a m’Baibulo onena za ulosi. Chikhulupiriro chanu chingalimbenso ngati muphunzira mbiri yamakono ya Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom ngati lilipo m’chinenero chimene mumamva. * Komanso kuwerenga “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” m’magazini am’mbuyomu a Nsanja ya Olonda kungakuthandizeni kumvetsa Malemba ena. Pamene mukuwerenga, khalani ndi chidwi choona mfundo za m’Malemba zimene zikugwiritsidwa ntchito poyankha funso lililonse. Izi zingakuthandizeni kuphunzitsa luntha lanu losiyanitsa zinthu ndiponso kukulitsa luso lanu la kuzindikira. (Aheberi 5:14) Pamene mukuphunzira, muzilemba mfundo zosiyanasiyana m’Baibulomo kapena papepala, n’cholinga choti inuyo komanso anthu ena omwe mungawathandize apindule kwanthawi yaitali ndi phunzirolo.

Thandizani Ana Anu Kusangalala Pophunzira Baibulo

16. Kodi mungawathandize bwanji ana anu kusangalala pophunzira Baibulo?

16 Makolo angathandize kwambiri ana awo kukulitsa cholinga chawo chokhala paubwenzi ndi Mulungu. Musaganize kuti ana sangathe kumvetsa zinthu zozama. Mutapatsa ana anu nkhani yoti afufuze pokonzekera phunziro la Baibulo labanja, mungathe kuwafunsa zimene aphunzira. Mungakonzenso zoti nthawi zina paphunziro labanja ana aziyeserera mmene angafotokozere za chikhulupiriro chawo kwa otsutsa ndiponso kutsimikizira kuti zimene amaphunzitsidwa ndi zoona. Komanso, mungagwiritse ntchito kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ * powaphunzitsa za malo otchulidwa m’Baibulo ndiponso pomveketsa bwino mfundo zimene mukuphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu.

17. N’chifukwa chiyani m’pofunika kusamala pankhani yophunzira ndi kufufuza mfundo za m’Baibulo patokha?

17 Mungasangalale ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chanu pophunzira ndi kufufuza mfundo za m’Baibulo panokha, koma samalani kuti kuchita zimenezi kusakulepheretseni kukonzekera misonkhano ya mpingo. Misonkhano ndi njira ina imene Yehova akutilangizira kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Komabe, kufufuza nkhani zimenezi kungakuthandizeni kuti muzipereka ndemanga zogwira mtima, monga pa Phunziro la Buku la Mpingo kapena panthawi ya mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

18. N’chifukwa chiyani khama lomwe munthu angachite pophunzira “zinthu zozama za Mulungu” silipita pachabe?

18 Kuphunzira mozama Mawu a Mulungu kungatithandize kuyandikira kwa Yehova. Posonyeza phindu la kuphunzira koteroko, Baibulo limati: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eniake.” (Mlaliki 7:12) Motero, khama limene mungachite n’cholinga choti mumvetse bwino zinthu zauzimu silipita pachabe. Baibulo limalonjeza anthu amene amafufuza mwakhama kuti: ‘Udzam’dziwadi Mulungu.’​—Miyambo 2:4, 5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi “zinthu zozama za Mulungu” n’chiyani?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kuphunzira zinthu zozama?

• N’chifukwa chiyani Akhristu onse ali ndi mwayi womvetsa “zinthu zozama za Mulungu”?

• Kodi mungatani kuti mupindule kwambiri ndi “zinthu zozama za Mulungu”?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi ndi liti pamene Yesu anakhala Mbewu yolonjezedwa?

[Chithunzi patsamba 31]

Makolo angapatse ana awo nkhani zoti afufuze pokonzekera phunziro labanja