Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Siliva Ndi Wanga, Golidi Ndi Wanga”

“Siliva Ndi Wanga, Golidi Ndi Wanga”

“Siliva Ndi Wanga, Golidi Ndi Wanga”

M’ZAKA za m’ma 500 B.C.E., Mfumu Koresi ya ku Perisiya inatulutsa anthu a Mulungu omwe anamangidwa ku Babulo. Anthu ambiri anabwerera ku Yerusalemu kuti akamangenso kachisi wa Yehova, amene anali atasanduka bwinja. Anthu obwererawo analibe chuma, ndipo anali ndi adani amene ankalimbana nawo pantchitoyo. Motero, ena mwa anthu omanga kachisiyo ankakayikira zoti adzamaliza ntchito yofunika kwambiriyi.

Ndiyeno Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Hagai kuwatsimikizira omangawo kuti Iye ali nawo. Mulungu anati: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” Hagai analimbikitsa omangawo kuti asade nkhawa poganizira mavuto awo azachuma. Iye anawauza kuti: “Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:7-9) Patangotha zaka zisanu kuchokera pamene Hagai ananena mawu olimbikitsawa, ntchitoyo inamalizidwa.​—Ezara 6:13-15.

Mawu a Hagai alimbikitsanso atumiki a Mulungu masiku ano pogwira ntchito zikuluzikulu zokhudzana ndi kulambira Yehova. Mu 1879, gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru litayamba kufalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda, yomwe panthawiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence, magaziniyi inati: “Sitikayikira kuti YEHOVA ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa magazini ino ya ‘Zion’s Watch Tower,’ motero sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi. Mwiniwakeyo, amene ananena kuti: ‘Siliva ndi golidi yense wa m’mapiri ndi wanga,’ akadzalephera kupereka ndalama zokwanira, tidzadziwa kuti nthawi yosiya kufalitsa magaziniyi yakwana.”

Magazini ya Nsanja ya Olonda ikufalitsidwabe mpaka pano. Magazini yoyamba inali ya Chingelezi, ndipo anasindikiza magazini 6,000 okha. Masiku ano avereji ya magazini amene amasindikizidwa pa Nsanja ya Olonda iliyonse imene yatuluka ndi 28,578,000, ndipo amatuluka m’zinenero 161. * Avereji ya magazini amene amasindikizidwa pa Galamukani! iliyonse imene yatuluka ndi 34,267,000, ndipo amatuluka m’zinenero 80. Magazini ya Galamukani! ndi inzake ya magazini ya Nsanja ya Olonda.

Mboni za Yehova zimagwira ntchito zambiri zomwe cholinga chake n’chofanana ndi cholinga cha Nsanja ya Olonda. Cholinga chimenechi ndi kukweza Yehova monga Mfumu ya chilengedwe chonse ndiponso kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wake. (Mateyo 24:14; Chivumbulutso 4:11) Masiku ano Mboni za Yehova zimakhulupirira zimene magazini ino inanena mu 1879. Zimakhulupirira kuti Mulungu ndi amene akutsogolera ntchito yawo, motero pazipezeka ndalama zoyendetsera ntchito imene iye wavomereza. Komano, kodi ndalama zoyendetsera ntchito za Mboni za Yehova zimachokera kuti kwenikweni? Nanga ndi ntchito ziti zimene iwowa akuchita pofuna kulalikira uthenga wabwino padziko lonse?

Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Mboni za Yehova Zimachokera Kuti?

A Mboni za Yehova akamalalikira nthawi zambiri anthu amawafunsa kuti, “Kodi mumalipidwa?” Yankho n’lakuti ayi salipidwa. Iwowa amapereka nthawi yawo kwaulere. Amatha maola ambiri akufotokozera ena za Yehova ndiponso za lonjezo la Baibulo lonena za tsogolo labwino. Iwo amatero chifukwa choyamikira zimene Mulungu wawachitira ndiponso mmene uthenga wabwino wawasinthira kuti akhale ndi moyo wabwino. Motero, amafuna kuuza ena zinthu zabwino zimenezi. Potero, amatsatira mfundo imene Yesu ananena kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyo 10:8) Chifukwa chofunitsitsa kuchitira umboni Yehova ndi Yesu, iwowa amagwiritsa ntchito ndalama zam’thumba mwawo n’cholinga chofuna kuuza ena zimene amakhulupirira, ngakhale ngati enawo amakhala kutali kwambiri.​—Yesaya 43:10; Machitidwe 1:8.

Ntchito yolalikirayi n’njaikulu zedi moti imafuna ndalama zankhaninkhani. Zili choncho chifukwa choti, kuti itheke pamafunika zinthu zambiri monga makina osindikizira mabuku, maofesi, Malo a Misonkhano, ndiponso nyumba za amishonale. Kodi ndalama zake zimachokera kuti? Zinthu zonsezi zimayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. Mboni za Yehova siziika lamulo loti anthu m’mipingo yawo azipereka ndalama zothandizira ntchito za gulu lawo, ndipo sizilipiritsa mabuku amene zimagawira. Munthu akafuna kuthandiza pantchito yawo yophunzitsayi, Mbonizo zimayamikira kwambiri kulandira thandizolo. Imodzi mwa ntchito zothandiza pa kulalikira uthenga wabwino padziko lonse ndi yomasulira mabuku. Tsopano tiyeni tione mmene ntchito imeneyi imayendera.

Kumasulira Mabuku M’zinenero 437

Kwa zaka zambiri, mabuku a Mboni za Yehova akhala m’gulu la mabuku omasuliridwa m’zinenero zambiri padziko lonse. Mboni zamasulira timapepala, timabuku, magazini, ndi mabuku m’zinenero 437. Komano monga mukudziwira, ntchito yomasulira imalira zambiri, monga mmene zililinso ndi mbali zina zothandiza pantchito yolalikira uthenga wabwino. Kodi ntchito yomasulira imayenda m’ndondomeko yotani?

Akonzi a mabuku a Mboni za Yehova akamaliza kulemba nkhani inayake m’Chingelezi, amaitumiza pa kompyuta kupita ku magulu a omasulira ophunzitsidwa bwino, omwe ali m’mayiko osiyanasiyana. Gulu lililonse la omasulira limamasulira chimodzi mwa zinenero zimene mabukuwa amamasuliridwa. Malingana ndi kuchuluka kwa mabuku amene akumasulira komanso chinenero chawo, maguluwa amakhala ndi anthu 5 kapena mpaka 25.

Akamaliza kumasulira nkhani iliyonse amaionanso n’kukonza paliponse pamene palakwika ndipo amaiwerenganso. Cholinga chawo chimakhala kufotokoza bwinobwino mfundo zonse zimene zatchulidwa m’Chingelezi. Iyi ndi ntchito yovuta pa zifukwa zingapo. Mwachitsanzo, akamamasulira nkhani yokhala ndi mawu ovuta, omasulira ndiponso owerenga aja amayenera kufufuza kwambiri kuti amvetse bwino nkhaniyo (kaya ndi ya Chingelezi, kapena yomasuliridwa kale m’zinenero zina monga Chifalansa, Chirasha, kapena Chisipanishi). Amatero pofuna kuti amasulire molondola. Mwachitsanzo, m’magazini ya Galamukani! mukakhala nkhani inayake yovuta kapena yonena za mbiri yakale, pamafunika kuifufuza kwambiri.

Omasulira ambiri amagwira ntchito ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Ena amagwira ntchitoyi nthawi zonse ndipo ena amangothandiza. Ena amakhalanso m’madera amene anthu amalankhula chinenero chimene amamasuliracho. Omasulirawa salipidwa ayi. Ndipo omasulira amene amagwira ntchitoyi nthawi zonse, amangopatsidwa pogona, chakudya ndi ndalama zochepa zongogulira zinthu zina zofunika kwambiri pa moyo wawo. Padziko lonse, pali Mboni pafupifupi 2,800 zimene zimachita ntchito yomasulira. Pakali pano, maofesi a nthambi 98 a Mboni za Yehova ali ndi magulu omasulira ndipo maofesi ena amayang’anira magulu oterewa amene ali m’madera ena. Mwachitsanzo, ofesi ya nthambi ya ku Russia imayang’anira omasulira oposa 230 a nthawi zonse ndi ongothandiza omwe. Ndipo omasulirawa amamasulira zinenero zoposa 30, kuphatikizapo zinenero zina zosadziwika kwambiri ku Russia, monga Chichuvashi, Chioseshiya, ndi Chiwiga.

Kuyesetsa Kuti Azimasulira Bwino

Aliyense amene anayesapo kuphunzira chinenero china amadziwa bwino lomwe kuti sizophweka kumasulira bwinobwino mfundo zovuta kufotokoza. Cholinga cha womasulirayo chimakhala choti afotokoze bwinobwino mfundo zonse zimene zili ku Chingelezi koma panthawi yomweyonso amafuna kuti nkhaniyo iziwerengeka mosavuta, ngati kuti inalembedwa m’chinenero chomwecho. Pamenepa pamagona luso zedi. Pamatenga zaka zambiri kuti womasulira adziwe bwino ntchitoyi, ndipo Mboni za Yehova zimaphunzitsa omasulirawa nthawi ndi nthawi. Nthawi zina magulu omasulirawa amalandira alangizi amene amawathandiza kunola luso lawo lomasulira ndi logwiritsira ntchito kompyuta.

Ntchito yophunzitsa omasulirayi ikuthandiza kwambiri. Mwachitsanzo, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Nicaragua inanena kuti: “Kwanthawi yoyamba, omasulira Chimisikito aphunzitsidwa dongosolo lofunika kutsatira pomasulira komanso njira zosiyanasiyana zothandiza kumasulira bwino. Mlangizi wawo anachokera ku ofesi ya nthambi ya ku Mexico. Zimenezi zathandiza kwambiri kuti omasulirawa azichita bwino ntchito yawo. Tsopano ayamba kumasulira bwino kwambiri.”

Mawu Okhudza Mtima

Cholinga cha ntchito yokonza Mabaibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zosiyanasiyana ndicho kufika pa mtima anthu omwe amalankhula ndi kumva bwino zinenerozo. Izitu n’zimene zikuchitika. M’chaka cha 2006, Mboni za Yehova ku Bulgaria zinasangalala kwambiri pamene Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chibugariya. Ofesi ya nthambi ya ku Bulgaria inanena kuti inalandira mauthenga ambiri oyamikira Baibuloli. Anthu m’mipingo ya Mboni za Yehova kumeneko amanena kuti “tsopano Baibulo limawakhudzadi mtima, sikuti amangomva chabe ayi.” Munthu wina wachikulire wochokera mu mzinda wa Sofia anati: “Ndakhala ndikuwerenga Baibulo kwazaka zambiri, koma sindinawerengepo Baibulo losavuta kumva ngati limeneli. Ili ndi Baibulo lom’fikadi munthu pamtima.” Munthu winanso wa ku Albania anayamikira atalandira Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu la Chiabaniya. Iye anati: “Mawu a Mulungu akumveka bwino zedi m’Chiabaniya! Apatu Yehova akutilankhula m’chinenero chathuchathu. Ndithu, uwu ndi mwayi wosasimbika!”

Pangatenge zaka zingapo kuti gulu la omasulira Baibulo limasulire Baibulo lonse lathunthu. Koma tikaona anthu mamiliyoni akuyamba kumvetsetsa Mawu a Mulungu, kodi tingatsutse kuti khama limeneli limapindula?

“Ndife Antchito Anzake a Mulungu”

Monga mukudziwira, ntchito yomasulira ndi mbali imodzi chabe ya ntchito zambiri zothandiza kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino iziyenda bwinobwino. Kulemba, kusindikiza, ndiponso kutumiza mabuku ofotokoza Baibulo pamodzi ndi ntchito zosiyanasiyana zochitika pa ofesi ya nthambi, m’madera, ndiponso m’mipingo ya Mboni za Yehova zimafuna khama komanso ndalama zambiri ndithu. Komabe anthu a Mulungu ‘amadzipereka eni ake’ kuchita ntchito imeneyi. (Salmo 110:3) Iwo amaona kuti ndi mwayi wapadera kuti iwowo pawokha angathe kuthandiza nawo pantchitoyi ndipo amaona kuti n’chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuti pochita zimenezi Yehova amawaona ngati “antchito anzake.”​—1 Akorinto 3:5-9.

N’zoona kuti iye amene anati “siliva ndi wanga, golidi ndi wanga” sadalira thandizo lathu la ndalama kuti achite ntchito yake. Koma Yehova walemekeza atumiki ake powapatsa mwayi wothandiza nawo kuyeretsa dzina lake mwa kupereka ndalama zothandizira ntchito yolalikira choonadi chopulumutsa miyoyo “ku mitundu yonse.” (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Kodi zimenezi sizikukulimbikitsani kuchita zonse zimene mungathe kuti muthandizepo pa ntchito imeneyi? Ntchitoyitu siidzabwerezedwanso mpaka kalekale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Zinenero zimenezi zatchulidwa pa tsamba 2 la magazini ino.

[Bokosi patsamba 18]

“AMATITHANDIZA KUTI TIZIGANIZA MWAKUYA”

Mtsikana wina wazaka 14 analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Cameroon. M’kalatayo analembamo kuti: “Nditagula zonse zofunika kusukulu chaka chino, ndinagulitsa mabuku awiri a kalasi imene ndinali chaka chatha. Mabukuwa ndinawagulitsa ma franc 2,500 [madola asanu]. Landirani ndalama zimenezi pamodzinso ndi zina ma franc 910 [pafupifupi madola awiri] zimene ndinkasunga. Ndikufuna kukulimbikitsani kuti mupitirize ntchito yabwino imene mukuchita. Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha magazini anu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Magazini amenewa amatithandiza kuti tiziganiza mwakuya.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

ANAPEREKA MPHATSO YAPADERA KWAMBIRI

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico inalandira kalata yoyamikira yochokera kwa kamnyamata kazaka 6, dzina lake Manuel, yemwe amakhala ku Chiapas. Popeza sadziwa kulemba, mnzake anam’lembera kalatayo. Manuel anati: “Agogo anga anandipatsa nkhumba yaikazi. Itabereka, ndinasankha kamwana kathanzi kwambiri n’kukasamalira bwinobwino, mothandizidwa ndi abale a mumpingo wathu. Ndine wosangalala kwambiri kukutumizirani ndalama zimene ndinapeza nditagulitsa nkhumba imeneyi. Inali yolemera mapaundi 220 [makilogalamu 100], ndipo ndinaigulitsa ma peso 1,250 [madola 110]. Gwiritsirani ntchito ndalamazo pa ntchito ya Yehova.”

[Bokosi patsamba 19]

“MUGWIRITSE NTCHITO NDALAMA ZIMENEZI POMASULIRA BAIBULO”

M’chaka cha 2005, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chiyukireniya, pamsonkhano wachigawo ku Ukraine. Tsiku lotsatira anapeza kuti m’bokosi la zopereka muli kapepala kolembedwa kuti: “Ndili ndi zaka 9. Ndikufuna kukuthokozani kwambiri chifukwa cha Malemba Achigiriki. Mayi anga anatipatsa ndalama zoti ineyo ndi mng’ono wanga, tikwerere basi popita kusukulu. Koma titaona kuti kunja sikukugwa mvula, tinaganiza zongoyenda wapansi, n’kusunga ndalama izi; zokwana ma hryvnia 50 [madola 10]. Ine ndi mng’ono wanga tikufuna kuti mugwiritse ntchito ndalamazi pomasulira Baibulo lonse m’Chiyukireniya.”

[Bokosi pamasamba 20, 21]

NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amaika padera ndalama, kapena kuti amachita bajeti, kuti aziponya ndalama mwakutimwakuti m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyo 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha ndalama zimene mukufuna kupereka ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti a ku Banki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu a ku banki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo mu kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke monga mphatso, malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo panthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ku boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, inuyo mukadzamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapenanso mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762 111

[Zithunzi patsamba 19]

Omasulira Chimisikito, ku ofesi ya nthambi ya ku Nicaragua