Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Valani Kudzichepetsa’

‘Valani Kudzichepetsa’

‘Valani Kudzichepetsa’

SAULO anali munthu wochokera mumzinda wotchuka kwambiri. Ankaonedwanso ngati munthu wapamwamba chifukwa anali nzika ya Roma ndipo n’zosakayikitsa kuti ankachokeranso m’banja lodziwika. Iyeyu anali munthu wophunzira kwambiri malinga ndi maphunziro a panthawiyo, ankalankhula zinenero zosachepera pa ziwiri, komanso anali m’gulu lachipembedzo la Afarisi, lomwe linali lotchuka kwambiri pakati pa Ayuda.

Saulo anaphunzira khalidwe lonyoza anthu wamba ndiponso lodzikweza chifukwa chodziona kuti iyeyo ndi wolungama. (Luka 18:11, 12; Machitidwe 26:5) Afarisi anzake anali anthu odzitukumula ndiponso okonda maudindo ndi kutchulidwa mayina aulemu. (Mateyo 23:6, 7; Luka 11:43) N’kutheka kuti Saulo anali munthu wodzikuza chifukwa chokhala ndi Afarisiwa. Tikudziwa kuti Saulo anazunza Akhristu kwadzaoneni. Patapita zaka zambiri, atayamba kutchedwa mtumwi Paulo, iye anachita kunena yekha kuti anali munthu “wonyoza ndi wozunza ndiponso wachipongwe.”​—1 Timoteyo 1:13.

Inde, panthawiyi Saulo anali atasinthiratu khalidwe lake n’kukhala Mkhristu, n’kumatchedwa kuti mtumwi Paulo. Monga mtumwi wachikhristu, ananena modzichepetsa kuti iye anali ‘munthu wochepa pomuyerekezera ndi wochepetsetsa wa oyera onse.’ (Aefeso 3:8) Paulo anachita zazikulu pantchito yolengeza uthenga wabwino, koma sanadzitame ayi. M’malo mwake, anapereka ulemu wonse kwa Mulungu. (1 Akorinto 3:5-9; 2 Akorinto 11:7) Paulo yemweyo ndiye analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”​—Akolose 3:12.

Kodi malangizo amenewa angagwirenso ntchito masiku ano? Kodi kudzichepetsa kuli ndi phindu lililonse? Kodi kudzichepetsa si kufooka?

Mlengi Wamphamvuyonse Ndi Wodzichepetsa

Sitingakambirane nkhani ya kudzichepetsa popanda kuganizira mmene Mulungu amaionera. N’chifukwa chiyani? Chifukwa choti iye ndiye Mfumu yathu komanso Mlengi wathu. Mulungu sali ngati ife ayi, ndipo ifeyo tiyenera kuvomereza kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kuchita ndipo timadalira Mulungu pa moyo wathu wonse. Kalelo, munthu wina wanzeru, dzina lake Elihu, ananena kuti: “Kunena za Wamphamvuyonse, sitingam’santhule; ndiye wa mphamvu yoposa.” (Yobu 37:23) Izitu n’zoona chifukwa tikangoganizira za kukula kwa chilengedwe chonse timaona kuti ndife ochepa zedi. Mneneri Yesaya anati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”​—Yesaya 40:26.

Ngakhale kuti Yehova Mulungu ndi wamphamvuyonse, iye ndi wodzichepetsa. Mfumu Davide anapemphera kwa Yehova motere: “Munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.” (2 Samueli 22:36) Tinganene kuti Mulungu ndi wodzichepetsa chifukwa choti, ngakhale kuti anthu ndi apansi kwambiri poyerekezera ndi iyeyo, iye amaganizira anthu onse amene amayesetsa kumusangalatsa ndipo amawachitira chifundo. Zili ngati kuti Yehova amawerama kumwambako kuti afikire anthu oopa Mulungu pansi pano, n’kuwasonyeza kukoma mtima kwake.​—Salmo 113:5-7.

Chinanso n’chakuti Yehova amasangalala kwambiri akaona atumiki ake akudzichepetsa. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo kwake.” (1 Petulo 5:5) Pankhani ya mmene Mulungu amaonera kudzikuza, wolemba Baibulo wina anati: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.” (Miyambo 16:5) Komano, n’chifukwa chiyani tikunena kuti munthu wodzichepetsa si wofooka?

Kodi Kudzichepetsa Sikutanthauza Chiyani?

Kudzichepetsa sikutanthauza kunyozeka ayi. Pakati pa mitundu ina ya anthu akale, munthu wodzichepetsa ankakhala kapolo basi, chifukwa ankaoneka kuti ndi munthu wachabechabe ndiponso womvetsa chisoni. Koma Baibulo limasonyeza kuti kudzichepetsa kumachititsa munthu kuyamba kulemekezedwa. Mwachitsanzo, munthu wanzeru analemba kuti: “Mphoto ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” (Miyambo 22:4) Ndipo pa Salmo 138:6, timawerenga kuti: “Angakhale Yehova n’ngokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziwira kutali.”

Sikuti munthu akadzichepetsa ndiye kuti alibe luso kapena kuti sangachite zinthu zotamandika. Mwachitsanzo, Yesu Khristu sanakane kuti ndi Mwana wobadwa yekha wa Yehova, ndipo sanabise kuti utumiki wake padziko lapansi unali wofunika kwambiri. (Maliko 14:61, 62; Yohane 6:51) Komabe, Yesu anasonyeza kudzichepetsa potamanda Atate wake pazinthu zonse zimene Yesuyo anachita ndiponso pogwiritsira ntchito mphamvu zake potumikira komanso kuthandiza ena, osawapondereza ayi.

Kudzichepetsa Sikusonyeza Kufooka

N’zosakayikitsa kuti m’nthawi yake, Yesu Khristu anali wodziwika ndi “ntchito zamphamvu” zimene ankachita. (Machitidwe 2:22) Komabe, kwa anthu ena iye anali “wolubukira anthu,” kapena kuti wonyozeka kuposa wina aliyense. (Danieli 4:17) Yesu ankakhala moyo wonyozeka komanso ankakonda kuphunzitsa anthu za kufunika kokhala munthu wodzichepetsa. (Luka 9:48; Yohane 13:2-16) Komatu kudzichepetsa kwakeku sikunam’pangitse kukhala munthu wofooka ayi. Iye sanachite mantha poikira kumbuyo dzina la Atate wake ndi kukwaniritsa utumiki wake. (Afilipi 2:6-8) M’Baibulo Yesu amafanizidwa ndi mkango wopanda mantha. (Chivumbulutso 5:5) Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza kuti khalidwe lodzichepetsa limasonyeza mphamvu ndiponso kulimba mtima.

Tikamayesetsa kukhala anthu odzichepetsadi, timazindikira kuti kukhala ndi khalidwe limeneli sikophweka ayi. Nthawi zonse timafunika kuti tizigonjera zimene Mulungu akufuna, osati kumangochita zinthu zimene zili zophweka kwa ifeyo, kapena kungotsata zilakolako zathu ayi. Kukhala wodzichepetsa kumafuna kulimba mtima, chifukwa munthu amafunika kuiwalako kaye zofuna zake, n’cholinga choti atumikire Yehova ndi kuchita kaye zofuna za ena.

Ubwino wa Kudzichepetsa

Munthu akakhala wodzichepetsa sakhala wodzikweza kapena wodzimva. Munthu amakhala ndi mtima wodzichepetsa ngati wakhala pansi n’kuona bwinobwino zinthu zimene amachita bwino, zimene sachita bwino, zimene wakwanitsapo kuchita ndiponso zinthu zimene walephera. Paulo anapereka malangizo abwino kwambiri pankhaniyi polemba kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire koposa mmene muyenera kudziganizira; koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.” (Aroma 12:3) Munthu aliyense amene amatsatira malangizo amenewa amakhala akusonyeza kudzichepetsa.

Timasonyezanso kudzichepetsa ngati tikuchitadi zinthu zosonyeza kuti tikuika patsogolo zofuna za ena osati zathu ayi. Mouziridwa ndi Mulungu, Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Musachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, mukumaona ena kukhala okuposani.” (Afilipi 2:3) Zimenezi n’zogwirizana ndi lamulo limene Yesu anapatsa ophunzira ake, lakuti: “Wamkulu koposa pakati panu akhale mtumiki wanu. Aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.”​—Mateyo 23:11, 12.

Inde, Mulungu amaona kuti munthu wodzichepetsa n’ngolemekezeka kwambiri. Wophunzira Yakobe anagogomezera mfundo imeneyi polemba kuti: “Dzichepetseni pamaso pa Yehova, ndipo iye adzakukwezani.” (Yakobe 4:10) Kodi ndani amene sangafune kuti Mulungu amukweze?

Chifukwa chosadzichepetsa, anthu akhala akusemphana maganizo kwambiri. Koma kudzichepetsa kumachititsa kuti zinthu ziyende bwino. Timasangalala podziwa kuti tikuchita zimene Mulungu amafuna. (Mika 6:8) Timakhalanso ndi mtendere chifukwa choti nthawi zambiri munthu wodzichepetsa amakhala wachimwemwe ndi wosangalala kusiyana ndi munthu wodzikuza. (Salmo 101:5) Tikakhala odzichepetsa zinthu zimatiyendera bwino pochita zinthu ndi anthu ena monga achibale athu, anzathu, ndi anthu amene timagwira nawo ntchito, motero timasangalala pochita zinthuzo. Anthu odzichepetsa amapewa kuchita zinthu zovutitsa ena. Iwo safuna kukwiyitsa anzawo, zomwe zingachititse kuti asiye kugwirizana.​—Yakobe 3:14-16.

Inde, kudzichepetsa ndi njira yabwino kwambiri yothandiza kuti tizikhala bwino ndi anthu anzathu. Kungatithandize kuti tilimbane ndi mavuto amene timakumana nawo chifukwa cha kufala kwa khalidwe lodzikonda ndiponso lokonda kupikisana ndi ena. Mtumwi Paulo anathandizidwa ndi Mulungu n’kusiya khalidwe lake lodzikweza. Ifenso tingachite bwino kwambiri ngati titayesetsa kuthetsa khalidwe lililonse lodzikuza kapena lodziona kuti ndife oposa ena. Baibulo limachenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” (Miyambo 16:18) Tikatsatira chitsanzo cha Paulo ndiponso malangizo ake, tingathe kuona kuti ‘kuvala kudzichepetsa’ n’chinthu chanzeru kwambiri.​—Akolose 3:12.

[Chithunzi patsamba 4]

Paulo anakwanitsa kuthetsa khalidwe lake lodzikuza

[Chithunzi patsamba 7]

Kudzichepetsa kumatithandiza kukhala bwino ndi ena

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Anglo-Australian Observatory/​David Malin Images