Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Chonde Landirani Kamphatso Kangaka”

“Chonde Landirani Kamphatso Kangaka”

“Chonde Landirani Kamphatso Kangaka”

MAWU amenewa analembedwa m’kalata imene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia inalandira, limodzi ndi bokosi lalikulu la masokosi.

Amene anatumiza mphatsoyi ndi mayi wina wazaka 67 dzina lake Alla. Iye ndi wa Mboni za Yehova ndipo ali mu mpingo wina kummawa kwa dziko la Russia. Alla wakhala akutumikira Yehova kwazaka zoposa 10. Iye wakhala akulalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu. Koma mwadzidzidzi anadwala matenda amene anapha ziwalo zake zina. Chifukwa cha chikondi, Alla anachita zinthu zofanana ndi zimene Dolika, mkazi wachikhristu wa m’nthawi ya atumwi, ankachita. Iye ankapangira Akhristu anzake zovala.​—Machitidwe 9:36, 39.

M’kalatayo, Alla analemba kuti: “Miyendo yanga sigwira ntchito, koma manja anga ndi abwinobwino. Choncho ndimalalikira kudzera m’makalata.” Iye anapitiriza kuti: “Ndinaganiza kuti popeza manja anga akugwirabe ntchito ndi bwino kuti ndiluke masokosi. Ndikufuna kuti masokosi amenewa aperekedwe kwa abale ndi alongo amene akukagwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’madera ozizira monga kummawa kwa dziko lino ndiponso ku Siberia.”

Ponena za otsatira ake enieni, Yesu Khristu anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chikondi ngati chimene Alla anasonyeza ndi chizindikiro cha ophunzira enieni a Yesu.