N’zotheka Kukhala ndi Moyo Wosangalala
N’zotheka Kukhala ndi Moyo Wosangalala
ANTHU ambiri amangokhalira kufunafuna ndalama ndi zinthu zoti agule. Pomwe ena amafuna kutchuka kwambiri m’dzikoli. Ena amafuna kupititsa patsogolo luso lawo. Ndipo pali anthu enanso amene cholinga chawo ndi kuthandiza anthu basi. Koma anthu ambiri sadziwa cholinga cha moyo.
Nanga bwanji inuyo? Kodi munaganizapo mozama za cholinga cha moyo wanu? Taganizirani zimene anthu akhala akuyesetsa kuti achite, ndiyeno muone ngati zimapangitsadi moyo kukhala waphindu. Kodi n’chiyani chingapangitse moyo wa munthu kukhala waphindu?
Kodi Ndalama ndiponso Zosangalatsa N’zofunika Kwambiri?
Pa Mlaliki 7:12 Baibulo limati: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” N’zoona kuti ndalama zimathandiza. Ndalama n’zofunika pamoyo wathu, makamaka kuti munthu asamalire banja lake.—1 Timoteyo 5:8.
Nthawi zina moyo sungakhale wosangalatsa popanda ndalama. Yesu Khristu ananena kuti analibiretu poti n’kutsamiritsa mutu wake. Koma nthawi zina ankadya chakudya komanso kumwa zakumwa zabwino kwambiri. Iye analinso ndi chovala chamtengo wapatali.—Mateyo 8:20; Yohane 2:1-11; 19:23, 24.
Komatu sikuti cholinga cha Yesu chinali kusangalala kokhakokha. Panali zinthu zimene ankaona kuti ndi zofunika kwambiri. Yesu anati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu Luka 12:13-21.
zimene ali nazo.” Kenako anafotokoza fanizo la munthu wina wachuma amene munda wake unabereka bwino. Munthuyo anati: “Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi? . . . Ndidzapasula nkhokwe zanga ndi kumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo; ndipo ndidzauza moyo wanga kuti: ‘Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri; ungoti phee tsopano, udye, umwe, usangalale.’” N’chifukwa chiyani maganizo a munthu ameneyu anali olakwika? Fanizoli likupitiriza kuti: “Mulungu anati kwa iye, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna. Nanga chuma chimene wakundikachi chidzakhala cha ndani?’” Ngakhale munthuyu akanasunga zokolola zakezo, atamwalira sizikanatheka kuti asangalale ndi chuma chimene anaunjikacho. Pomaliza fanizolo Yesu anati: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”—N’zoona kuti anthufe timafunika ndalama komanso kusangalala. Koma ndalama ndiponso zosangalatsa, si zinthu zofunika kwambiri pamoyo. Chofunika kwambiri chomwe tiyenera kuyesetsa kuchita ndicho kukhala wolemera kwa Mulungu, kutanthauza kuti kukhala ndi moyo wosangalatsa Mulungu.
Kodi Kutchuka N’kofunika?
Anthu ambiri cholinga chawo ndi kufuna kutchuka basi. Kuchita zinthu n’cholinga choti anthu adzatikumbukire sikulakwa kwenikweni. Baibulo limati: “Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.”—Mlaliki 7:1.
Patsiku lomwalira, mbiri ya munthu imakhala itadziwika. Ngati ali ndi mbiri yabwino tsiku limene wamwalira limaposa tsiku limene anabadwa. Zili choncho chifukwa patsiku lobadwa analibe mbiri iliyonse.
Mfumu Solomo ndi amene analemba buku la m’Baibulo la Mlaliki. Mchimwene wake, wobadwa ku banja lina la bambo wake, dzina lake Abisalomu ankafuna kutchuka. Koma zikuoneka kuti ana aamuna atatu a Abisalomu, amene akanatenga dzina lake, anamwalira akadali aang’ono. Kodi zitatero Abisalomu anatani? Malemba amanena kuti: ‘Abisalomu . . . anadziutsira choimiritsa chili m’chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha.’ (2 Samueli 14:27; 18:18) Panopa chipilala chimene anamangacho kulibe. Ndipo anthu amene amaphunzira Baibulo amakumbukira Abisalomu monga munthu woukira amene anafuna kulanda ufumu wa bambo ake, Davide.
Masiku ano, anthu ambiri amafuna kuti adzakumbukiridwe ndi zinthu zimene achita. Iwo amafuna kupatsidwa ulemu ndi anthu, ngakhale kuti zimene anthuwo amafuna zimasintha m’kupita kwanthawi. Koma kodi chimachitika n’chiyani ndi kutchuka? M’buku lina, Christopher Lasch analemba kuti: “Masiku ano munthu sangatchuke kwanthawi yaitali. Chifukwa chakuti nthawi zambiri munthu amakhala wotchuka ngati akuoneka wachinyamata, wachikoka, kapena ngati amachita zinthu
zosiyana ndi ena. Ndipo anthu otchuka amada nkhawa kuti mwina sakhalanso otchuka.”(The Culture of Narcissism) Zotsatira zake n’zakuti anthu ambiri otchuka amayamba kuchita zinthu zowononga moyo wawo monga kuledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Motero si bwino kuti cholinga chathu chikhale kufuna kutchuka.Nanga kodi tiyenera kukhala ndi mbiri yabwino kwa ndani? Ponena za anthu amene ankasunga malamulo ake, Yehova kudzera mwa mneneri Yesaya anati: ‘Iwo ndidzawapatsa m’nyumba yanga ndi m’kati mwa makoma anga malo, ndi dzina. . . . Ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa.’ (Yesaya 56:4, 5) Mulungu amasangalala ndi anthu omwe amamumvera ndipo adzawapatsa ‘malo ndi dzina.’ Mulungu sadzaiwala dzina lawo ndipo iwo sadzawonongedwa. Baibulo limatilimbikitsa kuti tipange dzina labwino, kutanthauza kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova, Mlengi wathu.
Yesaya ankalosera za nthawi imene anthu okhulupirika adzalandire “moyo wosatha” m’Paradaiso padziko lapansi. “Moyo wosatha” m’Paradaiso ameneyu ndiwo “moyo weniweniwo,” womwe Mulungu ankafuna kuti anthu akhale nawo pamene anawalenga. (1 Timoteyo 6:12, 19) M’malo mokhala moyo umene udzatha posachedwapa ndiponso wosasangalatsa, tiyeni tiyesetse kuti tidzapeze moyo wosatha.
Luso Kapena Kuthandiza Ovutika N’zosakwanira
Anthu ambiri aluso amayesetsa kuti apititse patsogolo luso lawo. Koma moyo uno n’ngwaufupi kwambiri moti zimenezi sizingatheke. Hideo yemwe tam’tchula m’nkhani yoyamba ija anayesetsa kupititsa patsogolo luso lake ali ndi zaka 90. Ngakhale munthu amene wapititsa patsogolo kwambiri luso lake, angalephere kuchita zinthu zina zimene ankatha kuchita ali wachinyamata. Koma bwanji atakhala ndi moyo wosatha? Mukuganiza kuti angafike pati ndi luso lake?
Nanga bwanji za anthu amene cholinga chawo ndi kuthandiza ovutika? Anthu amene amayesetsa kuthandiza ovutika pogwiritsa ntchito chuma chawo amachita bwino kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Zimakhaladi zosangalatsa ngati munthu ali ndi mtima wothandiza ena. Koma kodi munthu mmodzi angathandize anthu angati pamoyo wake wonse? Anthufe tingachite zinthu zochepa chabe pothandiza anzathu. Ngakhale munthu atamapereka mphatso zochuluka motani, sangapeze chinthu chofunika kwambiri pamoyo wa munthu chimene anthu ambiri amachinyalanyaza ndipo ambiri alibe.. Kodi chinthu chofunika kwambiri chimenechi n’chiyani?
Pezani Chinthu Chofunika Kwambiri Pamoyo
Paulaliki wa paphiri Yesu anatchula chinthu chofunika kwambiri pamoyo wamunthu. Iye anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mateyo 5:3) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, munthu sangakhale ndi moyo wosangalala chifukwa cha chuma, kutchuka, luso, kapena kuthandiza ovutika. Munthu amakhala ndi moyo wosangalala ngati apeza zosowa zake zauzimu zomwe ndi kulambira Mulungu.
Mtumwi Paulo analimbikitsa anthu osadziwa Mlengi kuti am’fufuze. Iye anati: “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi. Iye anakhazikitsanso nthawi zoikika ndi kuika malire a pokhalapo anthu. Anatero kuti anthuwo afunefune Mulungu, ngati angam’papase ndi kum’pezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. Pakuti mwa iye tili ndi moyo, timayenda, ndi kukhalapo.”—Machitidwe 17:26-28.
Tikakhala ndi cholinga cholambira Mulungu woona tidzakhala ndi moyo wosangalala. Tikatero tidzakhalanso ndi mwayi wodzapeza “moyo weniweniwo.” Taganizirani za Teresa
amene anatchuka kwambiri pa TV. Pa anthu akuda a ku America amene ankachita masewero pa TV, iye anali woyamba kutchuka kwambiri. Koma pasanapite nthawi yaitali, iye anasiya kuchita masewero amenewa. N’chifukwa chiyani anasiya? Iye anati: “Ndaona kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo ndi njira yabwino kwambiri.” Teresa sanafune kuti awononge ubwenzi wake ndi Mulungu chifukwa chochita nawo masewero amene ankalimbikitsa chiwerewere ndi chiwawa. Iye anasiya kuchita masewero a pa TV n’kuyamba kuchita zinthu zofunika kwambiri. Anakhala mlaliki wanthawi zonse wa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, n’kumathandiza anthu ena kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.Teresa atasiya kuchita masewero a pa TV, mnzake wina ananena kuti: “Ndinakhumudwa kwambiri kuona akusiya ntchito imene ndinkaona kuti inali yabwino kwambiri. Koma kunena zoona Teresa anapeza chinthu chachikulu komanso chofunika kwambiri.” Teresa anamwalira pangozi. Atamwalira, mnzake uja ananenanso kuti: “Teresa anali munthu wosangalala ndipo palibenso china chimene munthu ungafune pa moyo kuposa zimenezi. Koma ambirife sitiganiza choncho.” Anthu amene amaona kuti ubwenzi wawo ndi Mulungu ndi wamtengo wapatali amakhala ndi chiyembekezo choti akamwalira adzaukitsidwa mu Ufumu wa Mulungu.—Yohane 5:28, 29.
Mlengi ali nalo cholinga dziko lapansili ndiponso anthu. Iye amafuna kuti inuyo mudziwe cholinga chimenechi ndi kudzakhala kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansili. (Salmo 37:10, 11, 29) Ino ndi nthawi yodziwa bwino Yehova, yemwe ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, ndiponso yodziwa cholinga chake kwa inuyo. Amboni za Yehova kwanuko ndi okonzeka kukuthandizani kudziwa zinthu zimenezi. Tikukulimbikitsani kuti mulankhule nawo kapena kulembera kalata akonzi a magazini ino.
[Chithunzi patsamba 5]
N’chifukwa chiyani maganizo a munthu wachuma wa m’fanizo la Yesu anali olakwika?
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi mungakonde kudzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi?