Tsanzirani Wopanga Ophunzira Waluso
Tsanzirani Wopanga Ophunzira Waluso
“Samalani ndi kamvedwe kanu.”—LUKA 8:18.
1, 2. N’chifukwa chiyani muyenera kutsatira zimene Yesu ankachitira anthu muutumiki wake?
YESU KHRISTU anauza otsatira ake kuti: “Samalani ndi kamvedwe kanu.” (Luka 8:16-18) Ponena mawu amenewa iye anali kukwaniritsa udindo wake monga Mphunzitsi ndiponso Wopanga Ophunzira Waluso. Mfundo imeneyi ikukhudza utumiki wanu monga Mkhristu. Mukasamalira zinthu zimene Mulungu amaphunzitsa ndiponso chifuniro chake, mumazigwiritsa ntchito pamoyo wanu ndipo mumakhala wogwira mtima kwambiri polengeza Ufumu. N’zoona kuti masiku ano simungamve mawu enieni a Yesu, koma mungathe kuwerenga Malemba ndi kumva zimene iye ananena ndi kuchita. Kodi Malemba amatiuza zotani pankhani ya zimene Yesu ankachitira anthu muutumiki wake?
2 Yesu anali wogwira mtima kwambiri polengeza uthenga wabwino ndiponso pophunzitsa anthu choonadi cha m’Malemba. (Luka 8:1; Yohane 8:28) Ngakhale kuti ntchito yopanga ophunzira imafuna kulalikira ndi kuphunzitsa, Akhristu ena amalalikira mogwira mtima koma amavutika kuti aphunzitse anthu mogwira mtima. Kulalikira kumaphatikizapo kulengeza uthenga, koma kuphunzitsa anthu za Yehova ndiponso zolinga zake kumafuna kuti munthu wopanga ophunzira adziwane bwino ndi wophunzirayo. (Mateyo 28:19, 20) Tingachite zimenezi potsanzira Yesu Khristu, Mphunzitsi ndiponso Wopanga Ophunzira Waluso.—Yohane 13:13.
3. Kodi kutsanzira Yesu kungakuthandizeni motani pantchito yopanga ophunzira?
3 Ngati mutsanzira njira zimene Yesu ankaphunzitsira, mudzachita zinthu mogwirizana ndi malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitirizani kuyenda mwanzeru kwa akunja, ndipo muzidziwombolera nthawi yopezeka. Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akolose 4:5, 6) Ngakhale kuti m’pofunika khama kuti mutsanzire Yesu pantchito yopanga ophunzira, kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muziphunzitsa mogwira mtima chifukwa mudzatha ‘kuyankha wina aliyense’ mogwirizana ndi vuto lake.
Yesu Ankalimbikitsa Ena Kulankhula
4. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ankakonda kumvetsera ena?
4 Kuyambira ali mwana, Yesu ankakonda kumvetsera anthu akamalankhula ndiponso kuwalimbikitsa kuti afotokoze maganizo awo. Mwachitsanzo, ali ndi zaka 12, makolo ake anam’peza ali pakati pa aphunzitsi kukachisi, “kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.” (Luka 2:46) Yesu sanapite ku kachisi n’cholinga chokachititsa manyazi aphunzitsiwo ngakhale kuti iye ankadziwa zambiri. Ngakhale kuti ankafunsanso mafunso, iye anapita ku kachisiko n’cholinga chokamvetsera. N’kutheka kuti Mulungu ndiponso anthu ankamukonda chifukwa chakuti ankakonda kumvetsera ena.—Luka 2:52.
5, 6. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankamvetsera zonena za anthu amene ankawaphunzitsa?
5 Atabatizidwa ndi kudzozedwa kukhala Mesiya, Yesu anapitirizabe kumvetsera zonena za anthu ena. Iye sankangophunzitsa mosaganizira anthu amene abwera kudzamumvetsera. Nthawi zambiri, ankadukiza kulankhula, n’kufunsa maganizo awo, ndi kumvetsera mayankho awo. (Mateyo 16:13-15) Mwachitsanzo, Lazaro yemwe anali mlongo wa Marita atamwalira, Yesu anauza Marita kuti: “Aliyense amene ali moyo ndi kukhulupirira mwa ine sadzafa konse.” Kenako, anam’funsa kuti: “Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Mosakayikira, Yesu anamvetsera pamene Marita ankayankha kuti: “Inde, Ambuye; ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu.” (Yohane 11:26, 27) Yesu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kumva Marita akufotokoza chikhulupiriro chake motere.
6 Ophunzira ambiri atasiya kutsatira Yesu, iye anafuna kumva maganizo a atumwi ake. Motero, anawafunsa kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” Simoni Petulo anam’yankha nati: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha; ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:66-69) Mosakayikira, Yesu anasangalala kwambiri ndi mawu amenewa, ndipo nanunso mungasangalale kwambiri kumva munthu amene mukuphunzira naye Baibulo akunena mawu ngati amenewa.
Yesu Ankamvetsera Mwaulemu
7. N’chifukwa chiyani Asamariya ambiri anakhulupirira Yesu?
7 Chinthu china chimene chinachititsa kuti Yesu akhale wogwira mtima popanga ophunzira n’chakuti iye ankaganizira anthu ndiponso ankawamvetsera mwaulemu. Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu analalikira mkazi wachisamariya pafupi ndi chitsime cha Yakobo, ku Sukari. Pokambirana naye, Yesu ankamupatsa mpata mkaziyo kuti alankhule ndipo Yesu ankamvetsera zonena zake. Atachita zimenezi, Yesu anaona kuti mkaziyo ndi wokonda kulambira ndipo anamuuza kuti Mulungu amafuna kuti anthu azimulambira ndi mzimu ndi choonadi. Yesu anamusonyeza ulemu ndi chidwi moti mkaziyo anakauza anthu ena za Yesu. Zitatero, “Asamariya ambiri ochokera mu mzindawo anakhulupirira mwa iye chifukwa cha mawu a mayi” ameneyu.—Yohane 4:5-29, 39-42.
8. Popeza kuti anthu amakonda kufotokoza maganizo awo, kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji kuti muyambe kukambirana nawo muutumiki?
8 Anthu amakonda kufotokoza maganizo awo. Mwachitsanzo, anthu a ku Atene ankakonda kufotokoza maganizo awo komanso kumvetsera zinthu zatsopano. Zimenezi zinathandiza mtumwi Paulo kukamba nkhani yogwira mtima pa Areopagi mumzinda umenewu. (Machitidwe 17:18-34) Poyamba kukambirana ndi munthu muutumiki munganene kuti: “Ndabwera kuti ndimve maganizo anu pankhani iyi.” Mvetserani maganizo a munthuyo pankhaniyo ndipo perekani ndemanga kapena funso pamaganizo akewo. Ndiyeno, mokoma mtima musonyezeni zimene Baibulo limanena.
Yesu Ankadziwa Zoyenera Kunena
9. Kodi Yesu anatani ‘asanasanthule Malemba momveka bwino’ kwa Keleopa ndi mnzake?
9 Yesu sankasowa chonena. Kuwonjezera pa kumvetsera zonena za ena, iye ankadziwa Mateyo 9:4; 12:22-30; Luka 9:46, 47) Taonani chitsanzo ichi: Patangopita nthawi yochepa Yesu ataukitsidwa, ophunzira ake awiri anali paulendo, kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Emau. Uthenga Wabwino umati: “Ali mkati mokambirana ndi kufunsana, Yesu mwiniyo anafika ndi kumayenda nawo limodzi; koma m’maso mwawo sanathe kumuzindikira. Iye anati kwa iwo: ‘Kodi ndi nkhani zanji zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?’ Iwo anangoima chilili ndi nkhope zachisoni. Poyankha, mmodzi dzina lake Keleopa anati kwa iye: ‘Kodi iwe ukukhala wekha m’Yerusalemu monga mlendo, moti sukudziwa zimene zachitika mmenemo m’masiku amenewa?’ Iye anati kwa iwo: ‘Zinthu zotani?’” Mphunzitsi Waluso anawamvetsera pamene ankafotokoza kuti Yesu wa ku Nazarete anaphunzitsa anthu, anachita zozizwitsa ndipo kenako anaphedwa. Ophunzirawo ananenanso kuti panthawiyo ena anali kunena kuti iye waukitsidwa. Yesu anapatsa Keleopa ndi mnzake mpata wofotokoza maganizo awo. Kenako, anawafotokozera zinthu zimene anayenera kudziwa, ‘n’kuwasanthulira Malemba momveka bwino.’—Luka 24:13-27, 32.
zimene anthu akuganiza ndipo ankadziwiratu zoyenera kunena. (10. Pamene muli mu utumiki, kodi mungatani kuti mudziwe maganizo a munthu pankhani yachipembedzo?
10 N’kutheka kuti simungadziwe maganizo alionse amene munthu wina ali nawo pankhani yachipembedzo. Kuti mudziwe maganizo ake, mungam’fotokozere kuti mumasangalala kumva maganizo a anthu pankhani ya pemphero. Kenako, mungam’funse kuti, “Kodi mukuganiza kuti pali aliyense amene amamvetsera mapemphero?” Yankho lake lingakuthandizeni kudziwa maganizo ake ndiponso zinthu zina zokhudza chipembedzo chake. Ngati munthuyo amakonda kupembedza, mungamvenso maganizo ake ena mwa kum’funsa kuti, “Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamvetsera mapemphero onse, kapena pali mapemphero ena amene sakondwera nawo?” Mafunso ngati amenewa angathandize kuti mucheze naye momasuka. Ngati ndi bwino kum’sonyeza zimene Malemba amanena pankhaniyo, onetsetsani kuti mukuchita zinthu mosamala, osati motsutsa zimene iye amakhulupirira. Akasangalala ndi zimene mwakambirana naye, mwina angakuuzeni kuti mudzacheze nayenso. Koma tiyerekeze kuti wakufunsani funso limene simungathe kuyankha. Zikatero, mungakafufuze yankho n’kudzabweranso kudzam’fotokozera “chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho, koma . . . ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.”—1 Petulo 3:15.
Yesu Ankaphunzitsa Anthu Oyenera
11. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupeza anthu oyenera kuwaphunzitsa?
11 Yesu anali wangwiro, ndipo ankatha kuzindikira anthu oyenera kuwaphunzitsa. Koma ife, timavutika kwambiri kuti tipeze anthu a “maganizo oyenerera moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48) Ndi mmenenso zinalili ndi atumwi amene Yesu anawauza kuti: “Mukalowa mu mzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera.” (Mateyo 10:11) Mofanana ndi atumwi a Yesu, nanunso mukufunika kufufuza anthu ofuna kumvetsera ndiponso kuphunzira choonadi cha m’Malemba. Mungapeze anthu oyenera mwa kumvetsera mwatcheru anthu onse amene mwakumana nawo, ndi kuzindikira maganizo a munthu aliyense.
12. Kodi mungatani kuti mupitirize kuthandiza munthu wachidwi?
12 Mukasiyana ndi munthu amene wasonyeza kuti ali ndi chidwi ndi uthenga wa Ufumu, ndi bwino kupitiriza kuganizira mfundo za choonadi cha m’Baibulo zimene munthuyo akufunika kuphunzira. Kulemba zinthu zimene mwaona pambuyo pokambirana naye uthenga wabwino, kungakuthandizeni kuti mupitirize kuthandiza munthuyo mwauzimu. Pamaulendo obwereza, muzimvetsera mwatcheru n’cholinga choti mudziwe zikhulupiriro, maganizo, ndiponso moyo wa munthuyo.
13. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa mmene munthu amaonera Baibulo?
13 Kodi mungachite chiyani pofuna kulimbikitsa munthu kuti akufotokozereni mmene amaonera Mawu a Mulungu? M’madera ena, zimakhala zothandiza kufunsa funso lakuti, “Kodi mumaona kuti Baibulo n’lovuta kulimvetsa?” Nthawi zambiri, yankho la munthu limasonyeza mmene amaonera zinthu zauzimu. Njira ina ndi yowerenga lemba ndi kufunsa kuti, “Kodi mukuimva bwanji mfundo imeneyi?” Mofanana ndi Yesu, nanunso mungachite zambiri muutumiki wanu mwa kufunsa mafunso abwino. Komabe, m’pofunika kusamala.
Yesu Ankafunsa Mafunso Mwanzeru
14. Popanda kupanikiza anthu ndi mafunso, kodi mungasonyeze motani kuti muli ndi chidwi chodziwa maganizo awo?
14 Pamene mukusonyeza kuti muli ndi chidwi chodziwa maganizo a ena, ndi bwino kuti musawachititse manyazi. Tsatirani mmene Yesu ankachitira. Iye sikuti ankangofunsa mafunso mwachisawawa, koma ankafunsa mafunso othandiza munthu kuganiza. Komanso, Yesu ankamvetsera mokoma mtima, zomwe zinkatsitsimula anthu oona mtima ndiponso zinkawapangitsa kuti akhale omasuka. (Mateyo 11:28) Anthu onse ankamasuka kum’fotokozera nkhawa zawo. (Maliko 1:40; 5:35, 36; 10:13, 17, 46, 47) Ngati mukufuna kuti anthu azimasuka kulankhula nanu mmene amaonera Baibulo ndiponso zimene limaphunzitsa, musamawapanikize ndi mafunso.
15, 16. Kodi mungatani kuti muyambe kukambirana ndi anthu nkhani zokhudza chipembedzo?
15 Kuwonjezera pa kufunsa mafunso mwanzeru, mungalimbikitse munthu kuti azilankhula mwa kuyambitsa nkhani imene ingam’sangalatse ndiyeno n’kumvetsera maganizo ake. Mwachitsanzo, Yesu anauza Nikodemo kuti: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.” (Yohane 3:1-3) Mawu amenewa anam’chititsa chidwi kwambiri Nikodemo, moti anafotokozera Yesu maganizo ake ndiponso anamvetsera zomwe Yesu ankanena. (Yohane 3:4-20) Mwina nanunso mungalimbikitse anthu kulankhula ngati mutachita zimenezi.
16 Masiku ano, ku Africa kuno, kummawa kwa Europe, ndiponso ku Latin America kukuyambika zipembedzo zambiri zatsopano, ndipo ndi nkhani imene anthu akuikambirana kwambiri. M’madera ngati amenewa, n’zosavuta kuyamba kukambirana ndi munthu ngati mutanena kuti: “Zikundidetsa nkhawa kuona kuti pali zipembedzo zambiri chonchi. Koma ndikuyembekezera kuti posachedwapa anthu amitundu yonse adzagwirizana n’kuyamba kulambira koona. Kodi inu mukufuna kudzaona zimenezi zikuchitika?” Mwa kutchula mfundo inayake yochititsa chidwi yokhudza chikhulupiriro chanu, mungalimbikitse munthu kufotokoza maganizo ake. Ndipo anthu savutika kuyankha mafunso amene ali ndi mayankho awiri oti asankhepo limodzi. (Mateyo 17:25) Mwininyumba akayankha funso lanu, mungamuwerengere lemba limodzi kapena awiri. (Yesaya 11:9; Zefaniya 3:9) Mukamamvetsera mosamala n’kuona m’mene munthuyo akuyankhira, mungathe kudziwa zoyenera kudzanena paulendo wotsatira.
Yesu Ankamvetsera Zonena za Ana
17. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankachita chidwi ndi ana?
17 Yesu ankachitanso chidwi ndi ana. Iye ankadziwa masewera amene ana ankachita komanso zimene ankakonda kulankhula. Nthawi zina ankaitana ana. ( Luka 7:31, 32; 18:15-17) Ena mwa anthu amene ankamvetsera Yesu analinso ana. Pamene ana anakuwa kutamanda Mesiya, Yesu anamva ndipo anafotokoza kuti Malemba ananeneratu zimenezi. (Mateyo 14:21; 15:38; 21:15, 16) Masiku ano ana ambiri akukhala ophunzira a Yesu. Kodi ana amenewa mungawathandize bwanji?
18, 19. Kodi mungatani kuti muthandize mwana wanu mwauzimu?
18 Kuti muthandize mwana wanu mwauzimu, muyenera kumamvetsera akamalankhula. Muyenera kudziwa ngati ali ndi maganizo osemphana ndi zolinga za Yehova. Kaya mwanayo anena zotani, muyenera kupereka yankho lolimbikitsa. Ndiyeno, mungam’thandize pogwiritsa ntchito malemba kuti adziwe maganizo a Yehova pankhaniyo.
19 Kufunsa mafunso kumathandizanso. Koma mofanana ndi akuluakulu, ana safuna kuwapanikiza ndi mafunso. M’malo mowapanikiza ndi mafunso ovuta, mutha kungowauza zinthu zochepa zokhudza inuyo. Mogwirizana ndi nkhani imene mukukambirana mungawauze mmene inuyo munkaganizira komanso zifukwa zake. Ndiyeno mungawafunse kuti: “Kodi iweyo ukuganizanso choncho?” Zimene mwana wanu angayankhe zingathandize kwambiri kuti muyambe kukambirana mfundo zolimbikitsa za m’Malemba.
Pitirizani Kutsatira Chitsanzo cha Wopanga Ophunzira Waluso
20, 21. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera pamene tikupanga ophunzira?
20 Kumvetsera mosamala n’kofunika pamene mukukambirana ndi ana anu kapena anthu ena. Zimasonyeza kuti mumawakonda. Mukamamvetsera mumasonyeza kudzichepetsa ndiponso kulemekeza ndi kuganizira munthu amene akulankhulayo. Choncho, kuti munthu amvetsere ayenera kuchita chidwi ndi zolankhula za anthu ena.
21 Pamene muli muutumiki wachikhristu pitirizani kumvetsera zonena za anthu. Mukamatero, mungathe kudziwa mfundo za choonadi cha m’Baibulo zimene zingawasangalatse. Kenako, yesetsani kutsatira njira zimene Yesu ankagwiritsa ntchito pophunzitsa. Mukatero, mudzakhala osangalala ndiponso okhutira chifukwa chotsatira chitsanzo cha Wopanga Ophunzira Waluso.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yesu ankatani kuti alimbikitse ena kufotokoza maganizo awo?
• N’chifukwa chiyani Yesu ankamvetsera anthu amene ankawaphunzitsa?
• Kodi mungagwiritse ntchito motani mafunso pamene muli mu utumiki?
• Kodi mungatani kuti muthandize ana mwauzimu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 28]
Pamene mukulalikira muyenera kumvetsera zolankhula za ena
[Chithunzi patsamba 30]
Tikamathandiza ana mwauzimu timatsatira chitsanzo cha Yesu