Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anali Ndi Baibulo Lakelake?

Kodi Yesu Anali Ndi Baibulo Lakelake?

Kodi Yesu Anali Ndi Baibulo Lakelake?

AYI, Yesu analibe Baibulo. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa choti m’nthawi ya Yesu kunalibe Baibulo lathunthu monga masiku ano. Komano m’masunagoge munkasungidwa mipukutu yokhala ndi mabuku amene panopo anaikidwa pamodzi n’kukhala Baibulo. M’sunagoge wa ku Nazarete, Yesu anawerenga mpukutu wa buku la Yesaya. (Luka 4:​16, 17) Mtumwi Paulo anamva ‘Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zikuwerengedwa’ pamene anali mu mzinda wa Antiokeya, ku Pisidiya. (Machitidwe 13:​14, 15) Ndipo mtumwi Yakobe anati zolemba za Mose “zimawerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.”​—Machitidwe 15:21.

Kodi anthu ena m’nthawi ya atumwi anali ndi mipukutu yawoyawo ya Malemba Oyera? Zikuoneka kuti mdindo wa ku Itopiya yemwe ankagwira ntchito m’nyumba ya Mfumukazi Kandake anali ndi mpukutu wakewake. Tikutero chifukwa choti pamene Filipo anakumana naye pamsewu wa ku Gaza, iyeyu n’kuti ‘ali chikhalire akuyenda m’galeta lake, akuwerenga mokweza m’buku la mneneri Yesaya.’ (Machitidwe 8:​26-30) Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti amubweretsere “mipukutu, makamaka ija ya zikopa.” (2 Timoteyo 4:13) Ngakhale kuti Paulo sananene kuti inali mipukutu ya chiyani, zikuoneka kuti iyi inali mipukutu ya Malemba Achiheberi.

Alan Millard, yemwe ndi pulofesa wa zinenero monga Chiheberi anati, n’kutheka kuti Ayuda, amene ankakhala ndi mipukutu yawoyawo ya Malemba anali “anthu apamwamba a ku Palestina, kapena anthu amene ankadziona kuti ndi a maphunziro apamwamba, Afarisi enaake ndi aphunzitsi monga Nikodemo.” Mwa zina, chinkapangitsa zimenezi chinali mtengo wa miputukuyo. Pulofesa Millard uja anati, “mpukutu wa Yesaya wokha unkatha kugulitsidwa madinari 6 kapena 10,” ndipo anatinso Baibulo lathunthu la Chiheberi “linkadzaza mipukutu 15 kapena 20,” ndipo kuti munthu agule pankafunika ndalama zokwana theka la malipiro ake a pachaka.

Baibulo silinena kuti Yesu kapena ophunzira ake anali ndi Mabaibulo awoawo. Komabe palibe angatsutse kuti Yesu ankadziwa bwino Malemba, ndipo ankatha kunena mfundo za m’Malemba kapena kutchula Malemba enaake pamtima. (Mateyo 4:​4, 7, 10; 19:​4, 5) Zimenezitu ziyenera kutilimbikitsa kwambiri masiku ano kudziwa bwino Baibulo, chifukwa choti ambirife tingathe kukwanitsa kuligula ndiponso limapezeka mosavuta.